Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zisanu Zotilimbikitsa Kuopa Mulungu Osati Anthu

Mfundo Zisanu Zotilimbikitsa Kuopa Mulungu Osati Anthu

Mfundo Zisanu Zotilimbikitsa Kuopa Mulungu Osati Anthu

MNYAMATA wina anadabwa kwambiri ndi zimene anamva. Iye anaphunzira zinthu zambiri atakambirana ndi anthu awiri a Mboni za Yehova. Kwanthawi yaitali iye ankadzifunsa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika. Koma pa tsikuli anapeza mayankho a m’Baibulo. Iye sankadziwa kuti Baibulo lili ndi mfundo zolimbikitsa ndi zosangalatsa.

Patangopita mphindi zochepa chichokereni a Mboniwo, mayi yemwe anali mwiniwake wa nyumba imene mnyamatayo ankakhalamoyo analowa molusa n’kufunsa kuti: “Anabwera aja ndi ndani?”

Mnyamatayo anadabwa kwambiri ndipo sanayankhe.

Kenako mayiwo ananena mokalipa kuti: “Ndikuwadziwa amene aja. Ndikadzangowaonanso pakhomo pano, ndidzakuthamangitsa m’nyumba ino wamva!”

Kenako anamenyetsa chitseko n’kutuluka.

Akhristu Oona Amadziwa Kuti Amadedwa

Zimene wachinyamata ameneyu anakumana nazo sizodabwitsa. Baibulo limafotokoza kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Kuyambira kale, Akhristu oona sakondedwa ndi anthu ambiri. N’chifukwa chiyani? Mtumwi Yohane anauza Akhristu anzake kuti: “Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu, koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Baibulo limatinso Satana Mdyerekezi ali ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Yohane 5:19; 1 Petulo 5:8) Kuopa anthu ndi njira imodzi imene Satana amagwiritsira ntchito kwambiri.

Ngakhale Yesu Khristu, amene anachita zabwino zambiri ndipo sanachite tchimo lililonse, anasekedwa ndi kuzunzidwa. Iye anati: “Anadana nane popanda chifukwa.” (Yohane 15:25) Usiku woti afa mawa, Yesu anakonzekeretsa ophunzira ake, powauza kuti: “Ngati dziko lidana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu. Kumbukirani mawu ndinakuuzani aja, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, adzakuzunzani inunso.”​—Yohane 15:18, 20.

Chifukwa cha zimenezi, ambiri anazengereza kuyamba kulambira koona. Baibulo limanena kuti pa anthu onse amene ankafuna Yesu panthawi inayake, “panalibe amene anali kulankhula poyera za iye chifukwa choopa Ayuda.” (Yohane 7:13; 12:42) Atsogoleri a chipembedzo a m’nthawi imeneyo ankaopseza kuti achotsa mumpingo munthu aliyense wokhulupirira Khristu. Motero ambiri analephera kukhala Akhristu chifukwa choopa anthu.​—Machitidwe 5:13.

Patsogolo pake Chikhristu chitakhazikitsidwa, Baibulo limati Akhristu a ku Yerusalemu anakumana ndi “chizunzo chachikulu.” (Machitidwe 8:1) Ndipotu mu Ufumu wonse wa Aroma, Akhristu ankazunzidwa. Anthu ena otchuka a ku Roma anauza mtumwi Paulo kuti: “Timadziwa kuti gulu la mpatuko limeneli amalinenera zoipa kwina kulikonse.” (Machitidwe 28:22) Inde, Akhristu oona anazunzidwa kwambiri.

Masiku anonso, Satana amagwiritsirabe ntchito mantha otere pofuna kulepheretsa anthu ambiri kukhala otsatira enieni a Khristu. Anthu oona mtima amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova amatsutsidwa ndi kusekedwa kusukulu, kuntchito, kumene akukhala, kapenanso ndi anzawo. Motero angaope kuti anzawo awathawa, anthu asiya kuwalemekeza, kapena asowa owathandiza pankhani ya zachuma. M’madera ena akumidzi, alimi amaopa kuti anzawo angakane kuwathandiza kukolola kapena kuteteza ziweto zawo. Komabe, pali anthu ambirimbiri amene alimba mtima, kuyamba kukhulupirira Mulungu n’kumakhala moyo mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, potsanzira Yesu Khristu. Ndipo Yehova wawadalitsa pochita zimenezi.

Zifukwa Zoopera Mulungu Osati Anthu

Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziopa Mulungu, osati munthu. Limati: “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” (Salmo 111:10) Awa si mantha osafunika aja ayi, koma ndi mantha oopa kukhumudwitsa Mulungu wathu, yemwe ali Wopatsa moyo. Mantha amenewa amayenderana kwambiri ndi chikondi. Komano kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuopa Mulungu osati munthu? Tiyeni tionepo zifukwa zisanu.

1 Yehova ndiye Wamphamvuyonse. Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Tikamaopa Mulungu, timasonyeza kuti timalambira iyeyo, Wamphamvuyonse amene amaona ‘amitundu monga dontho la m’mtsuko.’ (Yesaya 40:15) Chifukwa choti Mulungu ndi Wamphamvuyonse, iye ali ndi mphamvu zogonjetsera “chida [chilichonse] chosulidwira” anthu okhulupirika kwa iye. (Yesaya 54:17) Komanso chifukwa choti iyeyo ndi amene adzasankhe anthu oyenerera kulandira moyo wosatha, n’chinthu chanzeru kusalola china chilichonse kutilepheretsa kuphunzira za iye ndi kuchita chifuniro chake.​—Chivumbulutso 14:6, 7.

2 Mulungu amatithandiza ndi kutiteteza. Pa Miyambo 29:25, Baibulo limati: “Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” Kuopa anthu kumatchera msampha chifukwa choti kungatichititse kuti tibwerere m’mbuyo pankhani youza anthu za chikhulupiriro chathu mwa Mulungu. Mulungu amatitsimikizira kuti ali ndi mphamvu zotha kutipulumutsa ponena kuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”​—Yesaya 41:10.

3 Mulungu amakonda anthu amene amayandikira kwa iye. Mtumwi Paulo analemba mawu okhudza mtima awa: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, kapena moyo, kapena angelo, kapena maboma, kapena zinthu zimene zilipo, kapena zinthu zam’tsogolo, kapena mphamvu, kapena msinkhu, kapena kuya, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:37-39) Tikaphunzira kukhulupirira ndi kumvera Mulungu, tingathe kuyamba kukondedwa ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ameneyu, yemwe chikondi chake n’chosalephera. Uwutu ndi mwayi wosaneneka.

4 Timayamikira zinthu zonse zimene Mulungu watichitira. Yehova ndiye Mlengi wathu, amene anatipatsa moyo. Anatipatsanso zonse zofunika pa moyo kuphatikizaponso zinthu zimene zimachititsa kuti tizisangalala ndi moyo n’kumaumva kukoma. Ndithu, iye ndiye Wopereka wa mphatso iliyonse yabwino. (Yakobe 1:17) Davide, anali munthu wokhulupirika ndipo ankayamikira kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu. Iye anati: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife . . . Zindichulukira kuziwerenga.”​—Salmo 40:5.

5 Ena amene amatitsutsa amatha kusintha. Mungathe kuthandiza anthu amene amakutsutsani posagonja ndiponso kupitirizabe kuopa ndi kukonda Mulungu. Taganizirani za abale ake a Yesu. Poyamba, iwo sankamukhulupirira, ndipo ankati: “Wachita misala.” (Maliko 3:21; Yohane 7:5) Koma patsogolo pake, Yesu atafa n’kuuka, ambiri a iwo anayamba kumukhulupirira. Moti abale ake awiri a Yesu, Yakobo ndi Yuda, analemba nawo Malemba. Nayenso Saulo ankazunza Akhristu modetsa nkhawa koma pambuyo pake anadzakhala mtumwi Paulo. Anthu ena amene amativutitsa panopa adzafika pozindikira kuti tikutsatiradi choonadi cha m’Baibulo chifukwa cha kusasunthika kwathu.​—1 Timoteyo 1:13.

Mwachitsanzo mayi wina wa ku Africa konkuno, dzina lake Aberash ankapemphera kuti apeze choonadi. Atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova achibale ake komanso atsogoleri a chipembedzo chake anayamba kulimbana naye koopsa. Achibale ake ena amene ankaphunziranso anasiya chifukwa choopa anthu. Koma iye anapempha Yehova kuti amupatse mphamvu komanso kuti amuthandize kukhala wolimba mtima ndipo anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Achibale ake okwana 8 analimba mtima n’kuyambiranso kuphunzira Baibulo ndipo akupita patsogolo kwambiri.

Mukhoza Kuthetsa Vuto la Kuopa Anthu

Kuti musakodwe mumsampha wa kuopa anthu, muyenera kukulitsa chikondi chanu kwa Mulungu. Mungakulitse chikondichi mwa kuwerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha malemba monga Aheberi 13:6. Lembali limati: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Angandichite chiyani munthu?” Kumbukirani mfundo zonse zosonyeza kuti kuopa Mulungu osati anthu ndi chinthu choyenera komanso chanzeru.

Musaiwalenso madalitso amene mungapeze chifukwa chotsatira mfundo zimene mwaphunzira m’Baibulo. Mungathe kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Mungapeze nzeru zokuthandizani kuthana ndi mavuto a pamoyo wanu. Mungakhale ndi chiyembekezo chabwino ngakhale kuti zinthu zikuipiraipira m’dzikoli. Komanso mungathe kupemphera kwa Mulungu wamphamvuyonse panthawi iliyonse.

Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.” (1 Yohane 2:17) Ino ndi nthawi yoti tikhalebe olimba ndiponso oopa Mulungu. M’malo moopa anthu mungathe kumvera zimene Mulungu akukupemphani. Iye akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Kuchita zimene Mulungu watipemphazi ndi mwayi wosaneneka.

Kumbukirani kuti palibe munthu amene angakupatseni zimene Mulungu walonjeza kuti adzapereka kwa anthu amene amamuopa. Mawu ake amati: “Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”​—Miyambo 22:4.

[Chithunzi patsamba 14]

Chifukwa cha kulimba mtima kwa Aberash, abale ake 8 akupitiriza kuphunzira Baibulo