Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuukitsidwa kwa Lazaro

Kuukitsidwa kwa Lazaro

Zoti Achinyamata Achite

Kuukitsidwa kwa Lazaro

Malangizo: Chitani zotsatirazi pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI YOHANE 11:1-45.

Werengani vesi 21. Kodi mukuganiza kuti Malita ankamva bwanji, nanga mukawerenga vesi 32 mukuganiza kuti Mariya ankamva bwanji?

․․․․․

Kodi mukawerenga pa vesi 33 ndi 35? n’kuona mmene Yesu anamvera, mukuganiza kuti iye anali munthu wotani?

․․․․․

Mukawerenga vesi 43 ndi 44, mukuganiza kuti Lazaro anamva bwanji ataukitsidwa nanga mukuganiza kuti anthu ena amene analipo anamva bwanji?

FUFUZANI MOZAMA.

Ulendo wa ku Betaniya unali wa masiku awiri. Ndiyeno kodi n’chifukwa chiyani Yesu anaganiza zopita mochedwa? (Werenganinso vesi 6.)

․․․․․

Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Mariya ndi Malita anali anthu okonda zinthu zauzimu? (Luka 10:38, 39; Yohane 11:24)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Yesu ankaukitsa anthu ngakhale kuti iyeyo ankadziwa kuti anthuwo adzafabe m’tsogolo? (Maliko 1:41, 42; Yohane 5:28, 29; 11:45)

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PANKHANI YOTI . . .

Yesu ali ndi mphamvu youkitsa anthu akufa komanso amafunitsitsa kuwaukitsa.

․․․․․

Yesu amamva chisoni kwambiri akaona anthu akulira maliro.

․․․․․

KODI NDANI AMENE INUYO MUNGAKONDE KUDZAKUMANA NAYE AKADZAUKITSIDWA?

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․