Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalani Maso”

“Khalani Maso”

“Khalani Maso”

“Mapeto a zinthu zonse ayandikira. . . . Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.”​—1 PET. 4:7.

1. Kodi mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankaphunzitsa inali yotani?

PAMENE Yesu Khristu anali padziko lapansi, mfundo yaikulu ya zimene ankaphunzitsa inali Ufumu wa Mulungu. Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu umenewu posonyeza kuti iye ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso poyeretsa dzina lake. N’chifukwa chake, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mat. 4:17; 6:9, 10) Posachedwapa, boma la Ufumu limeneli lidzawononga dziko la Satanali ndipo kenako lidzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chikuchitika padziko lonse lapansi. Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [omwe alipowa]. Nudzakhala chikhalire.”​—Dan. 2:44.

2. (a) Kodi otsatira a Yesu akanadzadziwa bwanji za kukhalapo kwake mu Ufumu? (b) Kodi chizindikiro chimenechi chinali kudzasonyezanso chiyani?

2 Chifukwa chakuti Ufumu wa Mulungu unali wofunika kwambiri kwa otsatira a Yesu, iwo anamufunsa kuti: “Chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:3) Panafunikira chizindikiro chooneka chifukwa kukhalapo kwa Khristu mu Ufumu wake kunali kudzakhala kosaoneka kwa anthu a padziko lapansi. Chizindikirochi chinali kudzakhala ndi mbali zosiyanasiyana zimene Malemba analosera. Choncho, otsatira a Yesu okhala panthawi imeneyo akanadzatha kuzindikira kuti iye wayamba kulamulira kumwamba. Chizindikirochi chinali kudzasonyezanso kuyambika kwa nthawi imene Baibulo limati “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipa lomwe lilipoli.​—2 Tim. 3:1-5, 13; Mat. 24:7-14.

Tiyenera Kukhala Maso M’masiku Otsiriza Ano

3. N’chifukwa chiyani Akhristu anafunika kukhala maso?

3 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho khalani oganiza bwino, ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” (1 Pet. 4:7) Otsatira a Yesu anafunika kukhala maso, kuonetsetsa zochitika padzikoli zosonyeza kuti Yesu wayamba kulamulira mu Ufumu wake. Ndipo iwo anafunika kukhala maso kwambiri pamene mapeto a dongosolo loipali anali kuyandikira. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Khalani maso, pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwini nyumba [kudzapereka chiweruzo padziko la Satanali].”​—Maliko 13:35, 36.

4. Kodi mmene atumiki a Yehova amaonera zochitika padzikoli zimasiyana bwanji ndi mmene anthu amene ali mbali ya dziko la Satanali amaonera? (Onani bokosi.)

4 Anthu ambiri akulamulidwa ndi Satana, ndipo sali maso kuti adziwe tanthauzo la zochitika padzikoli. Iwo sazindikira kukhalapo kwa Khristu mu Ufumu wake. Koma otsatira enieni a Khristu akhala ali maso ndipo azindikira tanthauzo lenileni la zimene zakhala zikuchitika zaka 100 zapitazi. Kuyambira chaka cha 1925, Mboni za Yehova zazindikira kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse komanso zinthu zina zimene zinachitika pambuyo pake, ndi umboni wosatsutsika wakuti kukhalapo kwa Khristu mu Ufumu wake kumwamba kunayamba mu 1914. Ndipo masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipali, lolamulidwa ndi Satana, anayambira pamenepo. Anthu ambiri ozindikira amadziwa kuti mmene zinthu zinalili nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanachitike, n’zosiyana kwambiri ndi mmene zakhalira kuyambira pamene nkhondoyo inachitika, ngakhale kuti sadziwa tanthauzo la zimenezi.​—Onani bokosi lakuti  “Nthawi Imene Mavuto Anayamba.”

5. N’chifukwa chiyani tifunika kukhalabe maso?

5 Papita zaka pafupifupi 100 tsopano, padzikoli pakuchitika zinthu zoopsa kwambiri ndipo zimenezi zikusonyeza kuti tili m’masiku otsiriza. Kwangotsala nthawi yochepa kwambiri kuti Yehova alamule Khristu kutsogolera magulu amphamvu a angelo kuti awononge dziko la Satana. (Chiv. 19:11-21) Akhristu oona akuuzidwa kuti akhalebe maso. Choncho, m’pofunika kwambiri panopa kukhala maso chifukwa tikuyembekezera mapeto a dongosolo lino. (Mat. 24:42) Tiyenera kukhalabe maso, ndipo motsogoleredwa ndi Khristu, tiyenera kugwira ntchito imene ikufunika kuchitidwa padziko lonse lapansi.

Ntchito ya Padziko Lonse

6, 7. Kodi ntchito yolalikira Ufumu yapita bwanji patsogolo m’masiku otsiriza?

6 Ntchito imene atumiki a Yehova ayenera kuchita, inaloseredwa ngati mbali ya chizindikiro chakuti tili m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipali. Pamene Yesu anatchula zinthu zosiyanasiyana zochitika m’nthawi yamapeto, ananenanso za ntchito ya padziko lonse imeneyi. Mu ulosi umenewu, iye ananenanso mfundo yofunika iyi: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”​—Mat. 24:14.

7 Taganizirani mfundo zina zokhudza mbali imeneyi ya ulosi wa Yesu. Pamene masiku otsiriza anayamba mu 1914, anthu olengeza uthenga wabwino anali ochepa. Koma panopa chiwerengero chakwera kwambiri. Pali Mboni za Yehova zoposa 7,000,000 zimene zikulalikira padziko lonse, ndipo zili m’mipingo yoposa 100,000. Ndiponso anthu okwana 10,000,000 anasonkhana ndi Mboni za Yehova mu 2008, pa Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Chiwerengero chimenechi ndi chachikulu kwambiri poyerekezera ndi cha mu 2007.

8. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ikupitabe patsogolo ngakhale kuti Satana akuyesetsa kuilepheretsa?

8 Kunena zoona, umboni wokwanira wonena za Ufumu wa Mulungu ukuperekedwa m’mitundu yonse, dongosolo lino lisanathe. Izi zikuchitika ngakhale kuti Satana ndi “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akor. 4:4) Satana ndi amene akuyendetsa zinthu pankhani ya ndale, zipembedzo, zamalonda, komanso njira zimene dziko loipali limafalitsira nkhani. Ndiyeno kodi n’chiyani chachititsa kuti ntchito yolalikira imeneyi ipite patsogolo chonchi? N’chifukwa chakuti Yehova akutithandiza. Ndipotu ntchito yolalikira Ufumu ikupitabe patsogolo modabwitsa kwambiri ngakhale kuti Satana akuyesetsa kuilepheretsa.

9. N’chifukwa chiyani kupita kwathu patsogolo mwauzimu n’kodabwitsa kwambiri?

9 Kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira Ufumu, kuchuluka kwa anthu a Yehova ndiponso kudziwa kwawo bwino Mulungu ndi chifuniro chake, n’kodabwitsa kwambiri. Popanda thandizo la Mulungu, lomwe likuphatikizapo kutitsogolera ndi kutiteteza, ntchito yolalikira siikanatheka. (Werengani Mateyo 19:26.) Chifukwa cha mzimu woyera wa Mulungu umene ukugwira ntchito m’mitima ya anthu amene ali maso komanso ofunitsitsa kutumikira, sitikukayikira kuti ntchito yolalikira imeneyi ipitirirabe kuyenda bwino mpaka kuimaliza, ndipo “kenako mapeto adzafika.” Nthawi yamapeto imeneyi ikufulumira kwambiri.

“Chisautso Chachikulu”

10. Kodi Yesu ananena chiyani za chisautso chachikulu chimene chikubwera?

10 Dongosolo loipali lidzatha pa “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:14) Baibulo silitiuza kuti chisautsocho chidzatenga nthawi yaitali bwanji, koma Yesu ananena kuti: “Panthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:21) Tikaganizira za chisautso chimene dzikoli lakumana nacho kale, monga nkhondo yachiwiri ya padziko lonse pamene anthu pakati pa 50 miliyoni ndi 60 miliyoni anafa, chisautso chimene chikubwerachi chidzakhala choopsa kwambiri. Chisautsochi chidzafika pachimake pankhondo ya Aramagedo. Panthawi imeneyi, Yehova adzalamula magulu ake a nkhondo kuti awononge chilichonse chotsala m’dongosolo la Satanali.​—Chiv. 16:14, 16.

11, 12. Kodi n’chiyani chimene chidzasonyeza kuyamba kwa chisautso chachikulu?

11 Ngakhale kuti ulosi wa Baibulo sunena nthawi yeniyeni imene mbali yoyamba ya chisautso chachikulu idzayambe, ulosiwu umatiuza zochitika zoopsa zimene zidzasonyeza kuyamba kwake. Chisautso chidzayamba pamene maboma andale adzaukira ndi kuwononga zipembedzo zonse zonyenga. Ulosi wa Baibulo pa Chivumbulutso chaputala 17 ndi 18, umayerekezera chipembedzo chonyenga ndi mkazi wachiwerewere amene wakhala akuchita dama ndi maboma andale a dziko lapansi. Lemba la Chivumbulutso 17:16 limasonyeza kuti posachedwapa, maboma andale ‘adzadana naye mkazi wachiwerewereyo. Adzamusakaza ndi kum’siya wamaliseche. Adzadya minofu yake ndi kumunyeketsa ndi moto.’

12 Nthawi ikadzakwana yakuti Mulungu awononge zipembedzo zonyenga, ‘Mulungu adzaika izi m’mitima yawo [olamulira andale] kuti achite monga mwa maganizo ake.’ (Chiv. 17:17) Choncho tinganene kuti chiwonongeko chimenechi chidzachokera kwa Mulungu. Chidzakhala chiweruzo chake pa zipembedzo zonyenga zimene kwa nthawi yaitali, zakhala zikuphunzitsa zinthu zotsutsana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso kuzunza atumiki ake. Anthu ambiri m’dzikoli sakuzindikira kuti chipembedzo chonyenga chikuyembekezera chiwonongeko chimenechi. Koma atumiki okhulupirika a Yehova akudziwa zimenezi, ndipo m’masiku otsiriza ano, akhala akuuzabe anthu za chiwonongekochi.

13. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mapeto a chipembedzo chonyenga adzachitika m’nthawi yochepa?

13 Panthawi imeneyo, anthu sadzamvetsa kuona chipembedzo chonyenga chitawonongedwa. Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti ngakhale ena mwa “mafumu a dziko lapansi” adzanena zokhudza chiwonongeko chimenechi kuti: “Kalanga ine, kalanga ine, . . . chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!” (Chiv. 18:9, 10, 16, 19) Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “ola limodzi” posonyeza kuti zidzachitika m’nthawi yochepa.

14. Kodi adani a Yehova akadzaukira atumiki ake, iye adzatani?

14 Tikudziwa kuti pambuyo poti chipembedzo chonyenga chawonongedwa, atumiki a Yehova, omwe akhala akulengeza uthenga wa chiweruzo chake, adzaukiridwa. (Ezek. 38:14-16) Kuukira kumeneku kukadzayamba, anthu oukirawo adzakhala ngati aputa Yehova, amene amalonjeza kuti adzateteza atumiki ake okhulupirika. Yehova anati: “Ndanena mu nsanje yanga, ndi m’moto wa kuzaza kwanga. . . . Motero adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Werengani Ezekieli 38:18-23.) Mulungu ananena m’Mawu ake kuti: ‘Iye wokhudza inu [atumiki ake okhulupirika], akhudza mwana wa m’diso [langa].’ (Zek. 2:8) Choncho, adani a Yehova akadzayamba kuzunza atumiki ake padziko lonse, iye sadzawalekerera. Iye adzachitapo kanthu ndipo zimenezi zidzayambitsa mbali yomaliza ya chisautso chachikulu, imene idzakhala Aramagedo. Molamulidwa ndi Khristu, angelo amphamvu adzapereka chiweruzo cha Yehova padziko la Satanali.

Kodi Zimenezi Ziyenera Kutikhudza Bwanji?

15. Kodi kudziwa kuti mapeto a dongosolo loipali ayandikira kwambiri kuyenera kutikhudza bwanji?

15 Kodi kudziwa kuti mapeto a dongosolo loipali ayandikira kwambiri kuyenera kutikhudza bwanji? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu.” (2 Pet. 3:11) Mawu amenewa akutsindika mfundo yakuti tiyenera kukhala maso ndiponso kuonetsetsa kuti khalidwe lathu likugwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Ndiponso tiyenera kuonetsetsa kuti pamoyo wathu tikuchita ntchito za kudzipereka kwa Mulungu posonyeza kuti timakonda Yehova. Ntchito zimenezi zikuphatikizapo kuyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, mapeto asanafike. Petulo analembanso kuti: “Mapeto a zinthu zonse ayandikira. . . . Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” (1 Pet. 4:7) Timayandikira kwa Yehova ndikusonyeza kuti timamukonda mwa kupitirizabe kupemphera kwa iye, kuti atitsogolere ndi mzimu wake woyera komanso mpingo wake wa padziko lonse.

16. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira kwambiri malangizo a Mulungu?

16 M’nthawi yoopsa ino, tiyenera kutsatira kwambiri malangizo a m’Mawu a Mulungu akuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, podziwombolera nthawi yoyenerera chifukwa masikuwa ndi oipa.” (Aef. 5:15, 16) Masiku ano, kuipa kwachuluka kwambiri kuposa kale. Satana akugwiritsa ntchito zinthu zambiri kuti alepheretse anthu kuchita chifuniro cha Yehova kapenanso kuti awadodometse. Monga atumiki a Mulungu, tikudziwa zimenezi, ndipo sitikufuna kuti chinthu chilichonse chitisiyitse kukhala okhulupirika kwa Mulungu wathu. Tikudziwanso zimene zichitike posachedwapa, ndipo timadalira Yehova ndi zimene akufuna kuchita.​—Werengani 1 Yohane 2:15-17.

17. Kodi anthu opulumuka Aramagedo adzatani akadzaona abale awo ataukitsidwa?

17 Nthawi idzafika pamene Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake losangalatsa, loukitsa anthu amene anamwalira, chifukwa Baibulo limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Taonani kuti Baibulo likuchita kutsindika kuti: “Kudzakhala kuuka.” Sitiyenera kukayikira lonjezo limeneli, chifukwa Yehova ndi amene wanena. Lemba la Yesaya 26:19 limati: “Akufa anu adzakhala ndi moyo. . . . Ukani muimbe, inu amene mukhala m’fumbi.” Mawu amenewa anakwaniritsidwa koyamba koma mophiphiritsa pamene anthu akale a Mulungu anabwerera kwawo, ndipo zimenezi zikutipangitsa kukhulupirira kuti m’dziko latsopano, akufa adzauka. Ndipotu zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona anthu amene adzaukitsidwe akukumananso ndi abale awo. Inde, mapeto a dziko la Satanali ali pafupi ndipo dziko latsopano la Mulungu layandikira kwambiri. Ndiyetu m’pofunika kwambiri kuti tikhalebe maso.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankaphunzitsa inali yotani?

• Kodi ntchito yolalikira Ufumu yafika pati masiku ano?

• N’chifukwa chiyani kukhala maso ndi kofunika kwambiri panopa?

• Kodi lonjezo la pa Machitidwe 24:15 limakulimbikitsani bwanji?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 16, 17]

 NTHAWI IMENE MAVUTO ANAYAMBA

Mu 2007, Alan Greenspan, yemwe kwa zaka pafupifupi 20 anali tcheyamani wa bungwe limene limayang’anira mabanki akuluakulu ku United States, la Federal Reserve Board, analemba buku lakuti The Age of Turbulence: Adventures in a New World. M’bukuli, iye anafotokoza kusiyana kwakukulu pakati pa mmene zinthu zinalili chaka cha 1914 chisanafike, ndi mmene zakhalira chiyambire chaka chimenechi. Greenspan anati:

“Mbiri imasonyeza kuti chaka cha 1914 chisanafike, dziko linkaoneka kuti likupita patsogolo ndipo zinkaoneka kuti anthu tsopano akulemekezana kwambiri komanso kutukuka. Zinthu zinkaoneka kuti zikuyenda bwino mwakuti anthu ankaganiza kuti moyo ukhala wabwino kwambiri. Ndipo zinkaoneka kuti anthu akusiya nkhanza. . . . Luso lopanga zinthu linapita patsogolo kwambiri padziko lonse m’zaka za m’ma 1800, ndipo zimenezi zinachititsa kuti kubwere njanji, telefoni, magetsi, kanema, galimoto, ndi ziwiya zamakono za m’nyumba zosiyanasiyana. Sayansi ya zamankhwala, zakudya zopatsa thanzi, ndiponso kupezeka kwa madzi abwino akumwa zinathandiza kuti anthu azikhala ndi moyo zaka zambiri . . . Aliyense ankaganiza kuti chitukuko chimenechi chipitirira.”

Koma . . . “Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inachititsa anthu kuti asiye kulemekezana komanso inachititsa kuti chitukuko chibwerere m’mbuyo kuposa mmene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, imene inapha anthu ambirimbiri, inachitira. Nkhondo yoyamba inachititsa anthu kuti asakhalenso ndi chiyembekezo. Ndimakumbukira kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanachitike, anthu ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera ndipo panalibe chosokoneza. Masiku ano tikuona zinthu mosiyana kwambiri ndi mmene anthu ankaonera zinthu zaka 100 zapitazo, ndipo mmene tikuonera zinthu masiku ano ndi mmene zililidi. Kodi uchigawenga, kutentha kwa dziko, kapena kuyambiranso kwa mfundo zolimbikitsa ufulu wa anthu wamba, ziwononga zinthu nthawi ino yolimbikitsa chitukuko cha padziko lonse, ngati mmene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inawonongera? Palibe angapereke yankho lenileni.”

Greenspan amakumbukira mawu a Pulofesa Benjamin Anderson (1886-1949), yemwe anali mphunzitsi wake wa zachuma panthawi imene anali ku yunivesite. Pulofesayo anati: “Anthu achikulire amene angathe kukumbukira ndi kumvetsa mmene zinthu zinalili padzikoli, nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanachitike, amalakalaka nthawi imeneyo. Panthawiyo kunali chitetezo champhamvu kuposa nthawi ina iliyonse pambuyo pa nkhondo.”​—Economics and the Public Welfare.

Mawu ngati amenewa ananenedwanso ndi G. J. Meyer, m’buku lake limene linatuluka mu 2006. (A World Undone) M’bukuli iye anati: “Anthu amati zinthu zikuluzikulu zomwe zachitika m’mbuyomu ‘zinasintha chilichonse.’ Izi ndi zoonadi tikaganizira za Nkhondo Yaikulu [1914-1918] yomwe inachita zimenezi. Nkhondo imeneyi inasinthadi chilichonse: osati malire okha, maboma ndi tsogolo la mayiko, komanso mmene anthu akhala akuonera dzikoli ndiponso moyo wawo kuchokera nthawi imeneyo. Nkhondoyi inasintha zinthu kwambiri, mwakuti dzikoli linasiyana kwambiri ndi mmene linalili nkhondoyo isanachitike.”

[Chithunzi patsamba 18]

Pa Aramagedo, Yehova adzagwiritsa ntchito angelo amphamvu