Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Olungama Adzatamanda Mulungu Kosatha

Olungama Adzatamanda Mulungu Kosatha

Olungama Adzatamanda Mulungu Kosatha

“Wolungama adzakumbukika . . . Chilungamo chake chikhalitsa kosatha.”​—SAL. 112:6, 9.

1. (a) Kodi anthu onse amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama ali ndi tsogolo labwino lotani? (b) Kodi zimenezi zikubweretsa funso lotani?

ANTHU amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Iwo mosangalala adzaphunzira makhalidwe abwino a Yehova kosatha. Panopa iwo akamaphunzira zambiri za ntchito za Mulungu za kulenga, amamutamanda kwambiri. “Chilungamo” ndi chofunika kwambiri kuti anthu akhale ndi tsogolo labwino, ndipo zimenezi zafotokozedwa mobwerezabwereza mu Salmo 112. Koma kodi Yehova Mulungu, yemwe ndi woyera ndi wachilungamo, angaone bwanji anthu ochimwa ngati olungama? Ngakhale kuti timayesetsa kwambiri kuchita zabwino, timalakwitsa ndipo nthawi zina zolakwa zathu zimakhala zazikulu.​—Aroma 3:23; Yak. 3:2.

2. Kodi ndi zozizwitsa ziwiri ziti zimene Yehova anachita chifukwa cha chikondi chake?

2 Mwachikondi, Yehova anakonza njira yabwino kwambiri. Kodi iye anatani? Choyamba, iye anachita chozizwitsa mwa kusamutsira moyo wa Mwana wake wokondedwa m’mimba mwa namwali, kuti abadwe monga munthu wangwiro. (Luka 1:30-35) Kenako adani atapha Yesu, Yehova anachita chozizwitsa china chapadera. Mulungu anaukitsa Yesu n’kukhala cholengedwa chauzimu chaulemerero.​—1 Pet. 3:18.

3. N’chifukwa chiyani Mulungu anali wosangalala kupatsa Mwana wake mphoto ya moyo wakumwamba?

3 Yehova anapatsa Yesu chinthu chamtengo wapatali chimene Mwana wakeyu analibe asanabwere padziko lapansi. Iye anam’patsa moyo wosakhoza kuwonongeka kumwamba. (Aheb. 7:15-17, 28) Yehova anasangalala kuchita zimenezi chifukwa Yesu anakhalabe wokhulupirika pamene anali kukumana ndi mayesero ovuta kwambiri. Chifukwa cha kukhulupirika kwake, Yesu anathandiza kwambiri Atate wake kuyankha bodza la Satana lakuti, anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera osati chifukwa cha chikondi chenicheni.​—Miy. 27:11.

4. (a) Kodi Yesu atabwerera kumwamba, anatichitira chiyani, ndipo Yehova anatani? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zimene Yehova ndi Yesu akuchitirani?

4 Atapita kumwamba, Yesu anachitanso zinthu zina. Iye ‘anaonekera pamaso pa Mulungu mwiniyo kaamba ka ife’ ndi mtengo wa “magazi a iye mwini.” Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wachifundo, analandira nsembe yamtengo wapatali ya Yesu monga “nsembe yachiyanjanitso yophimba machimo athu.” Choncho, tingachite “utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo” ndi ‘zikumbumtima zoyera.’ Ndiyetu nafenso tili ndi chifukwa chomveka chonenera mawu a mu Salmo 112 akuti: “Haleluya.”​Aheb. 9:12-14, 24; 1 Yoh. 2:2.

5. (a) Kodi tiyenera kutani kuti tikhalebe olungama pamaso pa Mulungu? (b) Kodi Salmo 111 ndi Salmo 112 analembedwa motani?

5 Kuti tikhalebe olungama pamaso pa Mulungu, tiyenera kupitirizabe kukhulupirira magazi a Yesu. Tisamalole tsiku kudutsa popanda kuthokoza Yehova chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife. (Yoh. 3:16) Tifunikanso kupitirizabe kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuyesetsa kwambiri pamoyo wathu kutsatira zimene mawuwo amanena. Salmo 112 lili ndi malangizo abwino kwa anthu onse amene akufuna kukhalabe ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu. Salmo limeneli likugwirizana ndi Salmo 111. Masalmo awiri onsewa amayamba ndi mawu akuti, “Haleluya,” kapena kuti “Tamandani Ya, anthu inu!” Kenako mawuwa amatsatiridwa ndi ziganizo 22, ndipo m’chinenero cha Chiheberi, chiganizo chilichonse chinayamba ndi chimodzi mwa zilembo 22 za alifabeti ya Chiheberi. *

Chifukwa Chokhalira Osangalala

6. Kodi n’chifukwa chiyani “munthu” woopa Mulungu wonenedwa mu Salmo 112 ndi wodala?

6 “Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Mbewu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.” (Sal. 112:1, 2) Onani kuti wamasalmoyu choyamba akutchula “munthu” mmodzi, ndipo kenako m’mbali yachiwiri ya vesi 2 akusintha n’kunena za anthu ambiri kuti, “oongoka mtima.” Zimenezi zikusonyeza kuti Salmo 112 likunenanso za gulu la anthu. N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito Salmo 112:9 ponena za Akhristu m’nthawi ya atumwi. (Werengani 2 Akorinto 9:8, 9.) Salmo limeneli likusonyeza bwino kwambiri mmene otsatira Khristu padziko lapansi masiku ano angakhalire osangalala.

7. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu afunika kumuopa moyenera, ndipo kodi inuyo muyenera kumva bwanji mumtima mwanu ndi malamulo a Mulungu?

7 Monga mmene Salmo 112:1 likunenera, Akhristu oona amenewa amasangalala kwambiri akamayenda ‘moopa Yehova.’ Mantha oyenera amenewa, osafuna kukhumudwitsa Yehova, amawathandiza kukana mzimu wa dziko la Satanali. Iwo ‘amakondwera kwambiri’ kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kumvera malamulo ake. Malamulo amenewa akuphatikizapo lamulo lolalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi. Akhristu oona amayesetsa kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse ndipo amachenjeza oipa za tsiku la Mulungu la chiweruzo limene likubwera.​—Ezek. 3:17, 18; Mat. 28:19, 20.

8. (a) Kodi anthu odzipereka a Mulungu masiku ano adalitsidwa bwanji chifukwa cha changu chawo? (b) Kodi anthu odzakhala padziko lapansi akuyembekezera madalitso otani?

8 Chifukwa chomvera malamulowa, atumiki a Mulungu padziko lonse panopa aposa 7 miliyoni. Kodi ndani angatsutse zoti anthu a Mulungu akhala ‘amphamvu pa dziko lapansi’? (Yoh. 10:16; Chiv. 7:9, 14) Ndipotu Mulungu akamadzakwaniritsa cholinga chake, anthu amenewa ‘adzadalitsidwa’ kwambiri. Monga gulu, anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, adzatetezedwa pa “chisautso chachikulu” chikubwerachi, ndipo adzapanga “dziko latsopano” mmene “mudzakhala chilungamo.” M’kupita kwa nthawi, anthu opulumuka pa Aramagedo ‘adzadalitsidwa’ m’njira zinanso zambiri. Iwo adzakhala okonzeka kulandira anthu ambirimbiri amene adzaukitsidwe. Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri. Kenako, anthu amene ‘amakondwera kwambiri’ ndi malamulo a Mulungu adzafika pokhala angwiro ndipo adzasangalala kosatha ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—2 Pet. 3:13; Aroma 8:21.

Njira Yabwino Yogwiritsira Ntchito Chuma

9, 10. Kodi Akhristu oona akhala akugwiritsa ntchito bwanji chuma chawo chauzimu, ndipo chilungamo chawo chidzakhala bwanji chikhalire?

9 “M’nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire. Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.” (Sal. 112:3, 4) M’nthawi za m’Baibulo, atumiki ena a Mulungu anali olemera. Ndipotu ngakhale popanda kukhala ndi chuma chakuthupi, anthu amene Mulungu amakondwera nawo amakhalabe olemera. Zoona zake n’zakuti, anthu ambiri amene amadzichepetsa pamaso pa Mulungu angathe kukhala osauka ndiponso ooneka onyozeka pamaso pa anthu ena, ngati mmene zinalili m’nthawi ya Yesu. (Luka 4:18; 7:22; Yoh. 7:49) Koma kaya munthu akhale wolemera kapena wosauka, n’zotheka kukhala wolemera mwauzimu.​—Mat. 6:20; 1 Tim. 6:18, 19; werengani Yakobe 2:5.

10 Akhristu odzozedwa limodzi ndi anzawo a nkhosa zina, saumira chuma chawo chauzimu. M’malomwake, iwo akhala ‘akuunikira’ m’dziko lamdima la Satanali monga “kuunika kotulukira oongoka mtima.” Iwo amachita zimenezi pothandiza anthu ena kuti apindule ndi chuma chauzimu chomwe ndi nzeru ndi kudziwa Mulungu. Otsutsa akhala akuyesetsa kuletsa ntchito yolalikira Ufumu koma alephera. M’malomwake, zipatso za ntchito ya chilungamo imeneyi ‘zidzakhala chikhalire.’ Mwa kupirira pokumana ndi mayesero ndi kukhalabe olungama, atumiki a Mulungu angayembekezere kukhala mpaka muyaya kapena kuti ‘kukhala chikhalire.’

11, 12. Kodi anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito chuma chawo chakuthupi m’njira monga ziti?

11 Anthu a Mulungu, kaya odzozedwa a gulu la kapolo kapena a “khamu lalikulu,” asonyeza kuti ndi oolowa manja pankhani ya zinthu zakuthupi. Lemba la Salmo 112:9 limati: “Anagawagawa, anapatsa aumphawi.” Masiku ano, Akhristu oona nthawi zambiri amapatsa Akhristu anzawo zinthu zakuthupi ndiponso amapatsa ngakhale anthu oyandikana nawo amene akufunikira thandizo. Iwo amaperekanso chuma chawo chakuthupi pofuna kuthandiza anthu amene agweredwa tsoka. Monga mmene Yesu anasonyezera, Akhristuwa akamachita zimenezi amakhala osangalala.​—Werengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:7.

12 Ndiponso taganizirani kuchuluka kwa ndalama zimene zimafunika kuti magazini ino ifalitsidwe m’zinenero 172. Anthu amene amalankhula zambiri mwa zinenerozi ndi osauka. Taganiziraninso kuti magazini ino imapezeka m’zilembo za akhungu, komanso m’zinenero zamanja zimene anthu osamva ndiponso osalankhula amagwiritsa ntchito.

Wachifundo Ndiponso Wachilungamo

13. Kodi ndani amene ali zitsanzo zabwino pankhani ya kupatsa mwachifundo, ndipo tingawatsanzire bwanji?

13 “Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa.” (Sal. 112:5) Mwina mwaonapo kuti anthu ambiri amene amathandiza anzawo, nthawi zambiri sachita zimenezi chifukwa cha chifundo. Anthu ena amathandiza pofuna kungoonetsa kuti ali ndi zinthu zambiri kuposa ena, kapena chifukwa chongokakamizika. Sizisangalatsa kulandira thandizo kuchokera kwa munthu amene amakuonani kuti ndinu wotsika kapena amene amakupangitsani kudziona kuti ndinu wovutitsa kapena wosowetsa mtendere. Mosiyana ndi zimenezi, zimasangalatsa kwambiri kulandira thandizo kuchokera kwa munthu amene ndi wachifundo. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya chifundo. Iye amapatsa mosangalala. (1 Tim. 1:11; Yak. 1:5, 17) Nayenso Yesu Khristu anasonyeza ndendende chifundo cha Atate wake. (Maliko 1:40-42) Choncho, kuti Mulungu azitiona monga olungama, tiyenera kupatsa mosangalala ndi mwachifundo, makamaka tikamapereka thandizo lauzimu kwa anthu anzathu muutumiki wakumunda.

14. Kodi tingachite zinthu mwachilungamo pa zinthu monga ziti?

14 “Adzalimbika nawo mlandu wake poweruzidwa,” kapena kuti amachita zinthu mwachilungamo. (Sal. 112:5) Mogwirizana ndi ulosi, gulu la mdindo wokhulupirika likusamalira zinthu za Mbuye wake mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova. (Werengani Luka 12:42-44.) Zimenezi zimaonekera m’malangizo a m’Malemba amene akulu amapatsidwa, ndipo akuluwa nthawi zina amathandiza anthu ena mumpingo amene achita machimo aakulu. Kuchita zinthu mwachilungamo kumaonekeranso m’malangizo a m’Baibulo amene gulu la kapolo limapereka a mmene mipingo yonse, nyumba za amishonale ndi za Beteli, ziyenera kugwirira ntchito. Chilungamo n’chofunika osati kwa akulu okha, koma ngakhalenso kwa Akhristu ena akamachita zinthu ndi abale awo auzimu komanso anthu osakhulupirira. Zimenezi zikuphatikizapo nkhani za malonda.​—Werengani Mika 6:8, 11.

Madalitso a Wolungama

15, 16. (a) Kodi mbiri yoipa imene ikuchitika padzikoli imawakhudza bwanji anthu olungama? (b) Kodi atumiki a Mulungu atsimikiza kupitirizabe kuchita chiyani?

15 “Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha. Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake n’ngokhazikika, wokhulupirira Yehova. Mtima wake n’ngochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo om’sautsa.” (Sal. 112:6-8) Panopa, padzikoli pali mbiri yoipa kwambiri kuposa m’mbuyo monsemu. Pali zinthu monga nkhondo, uchigawenga, matenda achilendo ndiponso matenda akale amene akuyambiranso, kuphwanya malamulo, umphawi, komanso kuwonongeka kwa mpweya, malo ndi madzi. Anthu amene Mulungu akuwaona kuti ndi olungama amavutikanso ndi mbiri yoipa imeneyi, koma iwo saopa. M’malomwake, mitima yawo ndi ‘yokhazikika’ ndiponso ‘yochirikizika.’ Iwo saopa akaganizira za m’tsogolo chifukwa amadziwa kuti dziko latsopano la Mulungu, limene mudzakhala chilungamo, lili pafupi. Kukachitika tsoka, iwo amatha kupirira chifukwa chodalira thandizo la Yehova. Iye nthawi zonse salola kuti olungama ake ‘agwedezeke.’ Iye amawathandiza ndi kuwapatsa mphamvu kuti apirire.​—Afil. 4:13.

16 Anthu amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama akulimbana ndi mavuto monga kudedwa ndiponso mabodza amene otsutsa amafalitsa, koma zimenezi sizinawachititse ndipo sizidzawachititsa Akhristu oona kusiya kulalikira. M’malomwake atumiki a Mulungu ndi okhazikika ndipo sasunthika pa ntchito imene Yehova wawapatsa, yomwe ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira mwa anthu onse amene amamvetsera. N’zosakayikitsa kuti olungama azitsutsidwa kwambiri pamene mapeto akuyandikira. Chidani chimenechi chidzafika pachimake Satana Mdyerekezi, monga Gogi wa Magogi, akadzaukira atumiki a Mulungu padziko lonse. Panthawi imeneyo ‘tidzaona otisautsa’ akugonjetsedwa mochititsa manyazi. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kuona dzina la Yehova litayeretsedwa kotheratu.​—Ezek. 38:18, 22, 23.

‘Adzakwezeka ndi Ulemu’

17. Kodi wolungama ‘adzakwezeka ndi ulemu’ motani?

17 Zidzakhalatu zosangalatsa anthu onse akamadzatamanda Yehova, popanda kutsutsidwa ndi Mdyerekezi komanso dziko lake. Chisangalalo chimenechi chidzakhala mphoto yosatha ya anthu onse amene akuyesetsabe kukhala olungama pamaso pa Mulungu. Iwo sadzagonjetsedwa, chifukwa Yehova analonjezanso kuti, “nyanga” ya olungama “idzakwezeka ndi ulemu.” (Sal. 112:9) Munthu wolungama wa Yehova adzasangalala kwambiri kuona adani onse a Yehova, amene savomereza kuti iye ndiye woyenera kulamulira, akugonjetsedwa.

18. Kodi mawu omaliza a Salmo 112 adzakwaniritsidwa bwanji?

18 “Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.” (Sal. 112:10) Anthu onse omwe akupitirizabe kutsutsa anthu a Mulungu, posachedwapa ‘adzasungunuka’ ndi nsanje komanso chidani chawo. Zimene amakhumba zoti ntchito yathu isapitirire, zidzatha iwowo akamadzawonongedwa pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwerachi.​—Mat. 24:21.

19. Kodi tikutsimikiza za chiyani?

19 Kodi inuyo mudzakhala m’gulu la anthu opulumuka panthawi yogonjetsa adani imeneyi? Nanga mutamwalira dziko la Satanali lisanathe chifukwa cha matenda kapena ukalamba, kodi mudzakhala m’gulu la “olungama” amene adzaukitsidwe? (Mac. 24:15) Mungayankhe kuti inde, ngati mofanana ndi anthu amene akuimiridwa ndi “munthu” wolungama wonenedwa mu Salmo 112, mukupitirizabe kukhulupirira nsembe ya dipo la Yesu ndiponso kutsanzira Yehova. (Werengani Aefeso 5:1, 2.) Yehova adzaonetsetsa kuti wakumbukira anthu olungama amenewa ndipo sadzaiwala ntchito zawo zolungama. Inde, Yehova adzawakumbukira ndi kuwakonda kosatha.​—Sal. 112:3, 6, 9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kugwirizana kwa masalmo amenewa kumaonekera ndi mmene analembedwera komanso ndi zimene mavesi ake amanena. “Munthu” woopa Mulungu wonenedwa mu Salmo 112 akutsatira makhalidwe a Mulungu amene afotokozedwa mowatamanda mu Salmo 111. Zimenezi zimaoneka poyerekezera Salmo 111:3, 4 ndi Salmo 112:3, 4.

Mafunso Owasinkhasinkha

• Tchulani zina mwa zifukwa zimene tingafuulire kuti “Haleluya”!

• Kodi masiku ano pakuchitika zinthu zotani zimene zikupangitsa Akhristu oona kusangalala kwambiri?

• Kodi Yehova amakonda kupatsa kotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 25]

Kuti tikhalebe olungama pamaso pa Mulungu, tiyenera kukhulupirira magazi a Yesu

[Zithunzi patsamba 26]

Ndalama zoperekedwa ndi mtima wonse zingathandize pakachitika tsoka ndiponso pantchito yofalitsa mabuku ofotokoza Baibulo