Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kubadwa Mwatsopano Ndi Nkhani Yoti Munthu Amachita Kusankha Yekha?

Kodi Kubadwa Mwatsopano Ndi Nkhani Yoti Munthu Amachita Kusankha Yekha?

Kodi Kubadwa Mwatsopano Ndi Nkhani Yoti Munthu Amachita Kusankha Yekha?

KODI ndani amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano? Alaliki ena achikhristu akamalimbikitsa anthu kuti abadwe mwatsopano, amagwiritsa ntchito mawu a Yesu akuti: “Anthu inu muyenera kubadwanso.” (Yohane 3:7) Alaliki amenewa amagwiritsa ntchito mawu akuti “muyenera kubadwanso” ngati lamulo. Motero, iwo amalalikira kuti munthu aliyense ayenera kumvera Yesu ndi kuchita zinthu zonse zimene iwo amati n’zofunika kuti munthu abadwe mwatsopano. Iwo amakhala akutanthauza kuti kubadwa mwatsopano ndi nkhani yoti munthu akhoza kusankha yekha. Koma kodi maganizo amenewa akugwirizana ndi zimene Yesu anauza Nikodemo?

Tikawerenga mosamala mawu a Yesu, timaona kuti iye sanaphunzitse kuti munthu aliyense ayenera kusankha yekha kuti abadwe mwatsopano kapena ayi. Tikutero chifukwa chakuti mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “kubadwanso” angamasuliridwenso kuti “kubadwa kuchokera kumwamba.” * Mogwirizana ndi mawu amenewa, kubadwa mwatsopano kumachokera “kumwamba,” kapena kuti “kwa Atate.” (Yohane 19:11; Yakobe 1:17) Choncho, Mulungu ndi amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano.​—1 Yohane 3:9.

Tikamakumbukira mawu akuti “kuchokera kumwamba,” sizingativute kumvetsa mfundo yakuti munthu sangasankhe yekha kuti abadwe mwatsopano. Taganizirani zimene zinachitika kuti mubadwe. Kodi munachita kusankha nokha? Ayi, chifukwa makolo anu ndi amene anachititsa kuti mubadwe. Mofanana ndi zimenezi, tingabadwe mwatsopano pokhapokha ngati Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wa kumwamba, wachititsa kuti tibadwe mwatsopano. (Yohane 1:13) N’chifukwa chake mtumwi Petulo anati: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti mwa chifundo chake chachikulu, anatibala mwatsopano.”​—1 Petulo 1:3.

Kodi Ndi Lamulo?

Ena angadabwe kuti, ‘Ngati zili zoona kuti palibe munthu amene amasankha yekha kubadwanso, n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti: “Anthu inu muyenera kubadwanso”?’ Funso limeneli n’lomveka. Komabe mawu amene Yesu ananenawa akanakhala kuti ndi lamulo, ndiye kuti iye analamula zinthu zimene sitingathe kuchita. Choncho, mfundo yakuti limeneli ndi lamulo ndi yosamveka. Nangano kodi mawu akuti “muyenera kubadwanso” akutanthauza chiyani kwenikweni?

Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “muyenera kubadwanso,” amasonyeza kuti mawuwa si lamulo. Choncho, pamene Yesu ananena kuti “muyenera kubadwanso,” ankangotchula mfundo yofunika osati kupereka lamulo. Malinga ndi Baibulo lina, iye anati: “M’pofunika kuti mubadwe kuchokera kumwamba.”​—Yohane 3:7, Modern Young’s Literal Translation.

Kuti timvetse bwino nkhaniyi, tiyerekezere kuti mumzinda winawake muli sukulu ya ana ochokera kumayiko ena. Tsiku lina pasukulupo pakufika mwana wina wam’dziko lomwelo n’kuuza mphunzitsi wamkulu kuti: “Ndabwera kuti ndidzalembetse nawo sukulu.” Mphunzitsi wamkuluyo akumuyankha kuti: “Kuti uyambe sukulu pano, uyenera kukhala wochokera kudziko lina.” Pamenepa sikuti mphunzitsiyu akulamula mwanayu kuti “akhale wochokera kudziko lina.” Koma akungomuuza zomuyeneretsa kuti alembedwe sukulu. Mofanana ndi zimenezi, pamene Yesu ananena kuti “anthu inu muyenera kubadwanso,” sikuti ankapereka lamulo. Koma iye ankangonena zinthu zoyenera zimene zingathandize kuti munthu ‘adzalowe mu Ufumu wa Mulungu.’

Mawu akuti Ufumu wa Mulungu, omwe ndi omalizira palembali, akutithandiza kupeza yankho la funso linanso lokhudza kubadwa mwatsopano. Funso lake n’lakuti, Kodi cholinga cha kubadwa mwatsopano n’chiyani? Kudziwa yankho la funso limeneli n’kofunika kwambiri chifukwa kungatithandize kumvetsa bwino tanthauzo la kubadwa mwatsopano.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mabaibulo ena anamasulira lemba la Yohane 3:3 m’njira imeneyi. Mwachitsanzo, Baibulo lina limati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa kuchokera kumwamba.”​—A Literal Translation of the Bible.

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi kubadwa mwatsopano n’kofanana bwanji ndi kubadwa kwenikweni?