Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Yesu popemphera anatchula Yehova kuti “Abba, Atate”?

Mawu a Chialamu akuti ʼab·baʼʹ amatanthauza “Atate.” Mawuwa amapezeka malo atatu m’Baibulo ndipo anagwiritsidwa ntchito m’pemphero potchula Atate wakumwamba, Yehova. Kodi mawuwa ankatanthauza chiyani?

Buku lina limati: “M’nthawi ya Yesu, mawu akuti ʼabbāʼ ankagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi ana poitana bambo awo mwaulemu ndiponso mwachikondi.” (The International Standard Bible Encyclopedia) Mawuwa anali ena mwa mawu oyamba amene mwana ankalankhula pophunzira kulankhula. Yesu anagwiritsa ntchito mawuwa popemphera kwa Atate ake mochokera pansi pamtima. Ali m’munda wa Getsemane patangotsala maola ochepa kuti aphedwe, Yesu popemphera anatchula Yehova kuti, “Abba, Atate.”​—Maliko 14:36.

Buku lija limanenanso kuti: “Mawu otchulira Mulungu akuti ʼAbbāʼ sapezeka kawirikawiri m’mabuku a Ayuda a m’nthawi ya ulamuliro wa Agiriki ndi Aroma. Izi zinali chonchi chifukwa iwo ankaona kuti n’kupanda ulemu kutchula Mulungu ndi mawu amenewa.” Komabe bukuli limanenanso kuti; “Yesu . . . anagwiritsa ntchito mawu amenewa m’pemphero pofuna kutsimikizira kuti iye amagwirizana kwambiri ndi Mulungu.” Mawu akuti “Abba” amapezekanso m’mabuku awiri a m’Baibulo omwe analembedwa ndi mtumwi Paulo ndipo amasonyeza kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankatchula mawuwa popemphera.​—Aroma 8:15; Agalatiya 4:6.

N’chifukwa chiyani mbali ina ya Baibulo inalembedwa m’Chigiriki?

Mtumwi Paulo ananena kuti Ayuda “anaikizidwa mawu opatulika a Mulungu.” (Aroma 3:1, 2) N’chifukwa chake mbali yoyambirira ya Baibulo inalembedwa m’Chiheberi, chomwe chinali chinenero cha Ayuda. Koma Malemba Achikhristu analembedwa m’Chigiriki. * Nanga n’chifukwa chiyani analembedwa m’Chigiriki osati m’Chiheberi?

M’zaka za m’ma 300 B.C.E., asilikali a Alesandro Wamkulu ankalankhula Chigiriki chakale chosiyanasiyana. Panthawi imene Alesandro ankagonjetsa maulamuliro ena, Chigiriki chosiyanasiyanachi anachiphatikiza n’kupanga Chigiriki chosavuta chotchedwa Koine, ndipo anthu a m’mayiko ambiri anayamba kuchilankhula. Panthawiyi, Ayuda ambiri ankakhala m’mayiko osiyanasiyana. Patapita zaka zambiri ukapolo wa ku Babulo utatha, Ayuda ena sanabwerere kwawo ku Palestina. M’kupita kwa nthawi, Ayuda ambiri anaiwala kulankhula Chiheberi n’kuyamba kulankhula Chigiriki. (Machitidwe 6:1) Pofuna kuthandiza Ayuda amenewa, Malemba Achiheberi anamasuliridwa mu Baibulo lotchedwa Septuagint, lomwe linalembedwa m’Chigiriki chosavuta kumva chotchedwa Koine.

Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linafotokoza kuti: “Chigiriki chinali ndi mawu ambiri osiyanasiyana katchulidwe kake ndiponso anthu a m’mayiko osiyanasiyana sankavutika kuchimva.” Chinenero chimenechi chili ndi mawu ochuluka, malamulo a kalembedwe osavuta, komanso mawu ake ena angatanthauze zinthu zingapo. Chifukwa cha zimenezi, “anthu a m’mayiko osiyanasiyana ankalankhulana m’chinenerochi ndipo n’chifukwa chake Akhristu ankachigwiritsa ntchito.” (Dictionnaire de la Bible) Choncho, mpake kuti Malemba Achikhristu analembedwa m’Chigiriki.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mbali zochepa za Malemba a Chiheberi zinalembedwa m’Chialamu. Zikuoneka kuti poyamba Uthenga wabwino wa Mateyo unalembedwa m’Chiheberi ndipo kenako Mateyo anadzaumasulira m’Chigiriki.

[Chithunzi patsamba 13]

Chidutswa cha Baibulo la Chigiriki Lotchedwa Septuagint

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of Israel Antiquities Authority