Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira “Khristu”?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira “Khristu”?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira “Khristu”?

“Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha . . . ndi kunditsatira mosalekeza.”​—LUKA 9:23.

1, 2. Kodi kukambirana zifukwa zotichititsa kutsatira “Khristu” n’kofunika motani?

YEHOVA amasangalala kwambiri akaona inu atsopano ndi achinyamatanu pa gulu la anthu amene amamulambira. Pitirizani kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano yachikhristu nthawi zonse, ndi kudziwa bwino choonadi chopatsa moyo chopezeka m’Mawu a Mulungu. Pamene mukuchita zimenezi muyenera kuganizira mozama mawu a Yesu akuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo tsiku ndi tsiku, ndi kunditsatira mosalekeza.” (Luka 9:23) Pamenepa Yesu akutiuza kuti tiyenera kudzikana tokha ndi kukhala otsatira ake. Motero m’pofunika tione kuti n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira “Khristu.”​—Mat. 16:13-16.

2 Kodi zimenezi zikukhudza bwanji enafe amene tayamba kale kutsatira mapazi a Yesu Khristu? Baibulo limatilimbikitsa kuti “pitirizani kutero mowonjezereka.” (1 Ates. 4:1, 2) Kaya tayamba choonadi posachedwapa, kaya tinayamba kale kwambiri, kuganizira zifukwa zimene tiyenera kutsatira Khristu kungatithandize kugwiritsa ntchito malangizo a Paulo. Zimenezi zingatithandize kuyamba kutsatira kwambiri Khristu pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Tiyeni tione zifukwa zisanu zotichititsa kutsatira Khristu.

Kuti Yehova Akhale Bwenzi Lathu Lapamtima

3. Tchulani njira ziwiri zimene zingatithandize kumudziwa bwino Yehova.

3 ‘Ataimirira pakati pa bwalo la Areopagi,’ Paulo analankhula ndi anthu a ku Atene, kuti: “[Mulungu] anakhazikitsanso nthawi zoikika ndi kuika malire a pokhalapo anthu. Anatero kuti anthuwo afunefune Mulungu, ngati angam’papase ndi kum’pezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:22, 26, 27) Tonsefe tikhoza kufika pomudziwa bwino Mulungu ngati titam’funafuna. Mwachitsanzo tikayang’ana zinthu zachilengedwe, tikhoza kuphunzira makhalidwe a Mulungu ndiponso mphamvu zake. Kunena zoona, munthu akaganizira bwino za chilengedwechi amaphunzira zambiri zokhudza Mlengi. (Aroma 1:20) M’mawu ake Baibulo, Yehova wafotokozanso zinthu zambiri zotithandiza kumudziwa bwino. (2 Tim. 3:16, 17) Tikamaganizira kwambiri ‘ntchito zimene Yehova wachita,’ tikhoza kumudziwa bwino kwambiri.​—Sal. 77:12.

4. Kodi kutsatira Khristu kungatithandize bwanji kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

4 Njira yabwino kwambiri yotithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiyo kutsatira Khristu. Tangoganizirani ulemerero umene Yesu anali nawo pa nthawi imene anali ndi Atate wake ‘dziko lisanakhaleko.’ (Yoh. 17:5) Iye ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Chiv. 3:14) Popeza ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” Yesu anakhala ndi Atate wake Yehova kwa zaka zankhaninkhani. Pa nthawi imeneyo sikuti ankangokhala ndi Atate wake osachita chilichonse. Yesu anali bwenzi lapamtima la Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, ankagwira ntchito limodzi mosangalala, ndipo ubwenzi wawo unali wolimba kuposa ubwenzi wina uliwonse. Yesu ankaona mmene Atate wake ankachitira zinthu. Ankadziwanso mmene ankamvera pa zochitika zosiyanasiyana. Anaphunzira makhalidwe a atate wake komanso anatengera kwambiri zonse zimene anaphunzira kwa Atate wakewo. Izi zinachititsa kuti Mwana womverayu azichita zinthu zofanana ndendende ndi zimene Atate wake ankachita moti Baibulo limati iye ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akol. 1:15) Ngati titsatira Yesu mosamalitsa, Yehova adzakhala bwenzi lathu lapamtima.

Kuti Tithe Kutsanzira Kwambiri Yehova

5. N’chiyani chingatithandize kutsanzira Yehova kwambiri ndipo n’chifukwa chiyani mukutero?

5 Anthufe tinalengedwa ‘m’chifanizo cha Mulungu, monga mwa chikhalidwe chake,’ choncho tingathe kusonyeza makhalidwe amene Mulungu ali nawo. (Gen. 1:26) Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti akhale “otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aef. 5:1) Kutsatira Khristu kungatithandize kuti tizitsanzira Yehova, yemwe ndi Atate wake. Tikutero chifukwa chakuti Yesu anasonyeza bwino nzeru ya Mulungu, mmene amamvera komanso makhalidwe ake. Iye anafotokozanso bwino kwambiri za Yehova kuposa mmene munthu wina aliyense angafotokozere. Kuwonjezera pa kudziwitsa anthu dzina la Yehova, Yesu ali padziko lapansi anachitanso zinthu zina. Iye anathandiza anthu kudziwa kuti Mulungu ndi wotani. (Werengani Mateyo 11:27.) Anatero mwa zochita zake, zolankhula zake zimene anaphunzitsa komanso chitsanzo chake.

6. Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zimatiuza chiyani za Yehova?

6 Yesu anaphunzitsa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita komanso anaphunzitsa mmene Iye amamvera akamaona anthu omulambira. (Mat. 22:36-40; Luka 12:6, 7; 15:4-7) Mwachitsanzo, Yesu atatchula lamulo lakuti “usachite chigololo,” lomwe ndi limodzi mwa Malamulo Khumi, anafotokozanso mmene Mulungu amamvera munthu akamaganizira zinthu zimene patsogolo pake zingam’chititse chigololo. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.” (Eks. 20:14; Mat. 5:27, 28) Afarisi ankaphunzitsa zinthu zolakwika pofotokozera Chilamulo. Iwo ankaphunzitsa kuti, “uzikonda mnansi wako ndi kudana naye mdani wako.” Koma Yesu anafotokoza mmene Yehova amaonera nkhaniyi ponena kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mat. 5:43, 44; Eks. 23:4; Lev. 19:18) Kumvetsa bwino maganizo a Mulungu, mmene amamvera komanso zimene amafuna kuti tizichita, kungatithandize kumutsanzira bwino kwambiri.

7, 8. Kodi chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa chiyani za Yehova?

7 Yesu anapereka chitsanzo chotithandiza kuona makhalidwe a Atate wake. Tikamawerenga m’mabuku a uthenga wabwino timamva mmene Yesu ankachitira zinthu. Iye ankachitira chifundo anthu ovutika, ankaganizira anthu odwala, komanso ophunzira ake atadzudzula ana aang’ono iye anakwiya. Izitu zikusonyeza bwino kwambiri mmene Yehova amamvera. (Maliko 1:40-42; 10:13, 14; Yoh. 11:32-35) Taganizirani mmene zochita za Yesu zimatithandizira kudziwa makhalidwe akuluakulu a Mulungu. Zozizwitsa zimene Khristu anachita zimatithandiza kudziwa mphamvu zosaneneka zimene iye anapatsidwa. Komabe sanagwiritsire ntchito mphamvuzo pochita zinthu zodzipindulitsa kapena zovulaza ena. (Luka 4:1-4) Ndipotu anasonyezeratu kuti amakonda kwambiri chilungamo pamene anathamangitsa m’kachisi amalonda amene ankadyera anthu masuku pamutu. (Maliko 11:15-17; Yoh. 2:13-16) Iye ankawafika anthu pamtima ndi zimene ankaphunzitsa komanso mawu ake okopa. Anasonyezeratu kuti pa nkhani ya nzeru anali “woposa Solomo.” (Mat. 12:42) Yesu anasonyeza chikondi chosaneneka popereka moyo wake kuti apulumutse ena, moti mpake kuti Baibulo limati “palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi.”​—Yoh. 15:13.

8 Mwana wa Mulungu anasonyeza bwino makhalidwe a Yehova mwa zolankhula zake komanso zochita zake moti ankanenadi zoona pamene anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Werengani Yohane 14:9-11.) Motero munthu akamatsatira Khristu ndiye kuti akutsanzira Yehova.

Yesu Ndi Wodzozedwa wa Yehova

9. Kodi Yesu anakhala liti Wodzozedwa wa Mulungu ndipo zimenezi zinachitika motani?

9 Taganizirani zimene zinachitika mu 29 C.E., Yesu ali ndi zaka 30. Iye anapita kwa Yohane Mbatizi. “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo; pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatera pa iye.” Apatu m’pamene iye anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Ndipo nthawi yomweyo Yehova ananena kuti Yesu ndi wodzozedwa wake. Iye anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:13-17) Chimenechitu ndi chifukwa chomveka chotsatirira Khristu.

10, 11. (a) Ponena za Yesu kodi mawu akuti “Khristu” amalembedwa m’njira ziti? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira Yesu Khristu?

10 M’Baibulo mawu akuti “Khristu” amalembedwa m’njira zosiyanasiyana akamanena za Yesu. Njira zake ndi izi: Yesu Khristu, Khristu Yesu ndiponso Khristu. Pamene anadzitchula kuti “Yesu Khristu,” Yesu anagwiritsira ntchito njira yoyamba ndi dzina kenako udindo wake. Popemphera kwa Atate wake iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yoh. 17:3) Katchulidwe kameneka kamachititsa kuti anthu aganizire kwambiri za munthu amene anatumidwa ndi Mulungu n’kudzakhala Wodzozedwa wake. Tikanena kuti “Khristu Yesu” ndiye kuti tayamba ndi udindo kenako dzina. Izi zimachititsa kuti anthu aganizire kwambiri za udindowo osati za munthuyo. (2 Akor. 4:5) Koma tikangoti “Khristu” ndiye kuti nkhani ndi ya udindo wokhawo basi ndipo zimachititsanso kuti anthu aganizire za udindo wa Yesu monga Mesiya.​—Mac. 5:42.

11 Ponena za Yesu, kaya dzina la udindo lakuti “Khristu” lalembedwa motani, mfundo yaikulu ndi yakuti: Ngakhale kuti Mwana wa Mulungu anabwera padzikoli ngati munthu n’kuthandiza anthu kudziwa chifuniro cha Mulungu, iye sanali munthu wamba kapena mneneri wamba. Koma anali Wodzozedwa wa Yehova. Choncho tiyenera kum’tsatiradi.

Yesu Ndi Njira Yokhayo Yopezera Chipulumutso

12. Kodi ndi mawu otani amene Yesu ananena kwa Tomasi amene amagwiranso ntchito kwa ife?

12 Tiyenera kutsatira Mesiya pa chifukwa chinanso chofunika kwambiri chimene Yesu anatchula polankhula ndi atumwi ake okhulupirika, patangotsala maola ochepa chabe Yesuyo asanaphedwe. Poyankha funso la Tomasi lokhudza zimene Yesu ananena zakuti akupita kukawakonzera malo, Yesu anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 14:1-6) Pa nthawiyi Yesu ankalankhula ndi atumwi ake 11 okhulupirika. Iye anawalonjeza malo kumwamba, koma mawu akewa amagwiranso ntchito kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 10; 21:1-4) N’chifukwa chiyani tikunena choncho?

13. Kodi mawu akuti Yesu ndi “njira” amatanthauza chiyani?

13 Yesu Khristu ndi “njira.” Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ndi munthu yekhayo amene tingadzereko kuti tim’fikire Mulungu. Choncho popemphera, tiyenera kudzera m’dzina la Yesu kuti tisakayike ngakhale pang’ono kuti Atate atipatsa chilichonse chimene tapempha mogwirizana ndi chifuniro Chake. (Yoh. 15:16) Komabe, mawu akuti Yesu ndi “njira” ali ndi tanthauzo linanso. Uchimo unachititsa kuti anthu atalikirane ndi Mulungu. (Yes. 59:2) Yesu anapereka “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Motero, Baibulo limafotokoza kuti: “Magazi a Yesu . . . akutiyeretsa uchimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Choncho Mwana wa Mulungu anatsegula njira yogwirizanitsanso anthu ndi Mulungu. (Aroma 5:8-10) Kuti tikhale ndi ubwenzi weniweni ndi Mulungu tiyenera kukhulupirira Yesu ndi kumumvera.​—Yoh. 3:36.

14. Kodi mawu akuti Yesu ndi “choonadi” amatanthauza chiyani?

14 Yesu ndi “choonadi” chifukwa choti nthawi zonse ankalankhula zoona ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi, komanso chifukwa choti pali maulosi ambirimbiri onena za Mesiya amene anakwaniritsidwa mwa iyeyo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa iye.” (2 Akor. 1:20) Ngakhale “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera,” womwe unali m’Chilamulo cha Mose, unakwaniritsidwa mwa Khristu Yesu. (Aheb. 10:1; Akol. 2:17) Maulosi onse amakhudza Yesu, ndipo amatithandiza kuzindikira udindo wake, womwe ndi wofunikira kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Yehova. (Chiv. 19:10) Tiyenera kutsatira Mesiya kuti tidzapeze madalitso Mulungu akamadzakwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga anthu.

15. Kodi mawu akuti Yesu ndi “moyo” amatanthauza chiyani?

15 Yesu ndi “moyo” chifukwa choti iye anagula mtundu wonse wa anthu ndi magazi ake opatsa moyo, ndipo moyo wosatha ndi mphatso imene Mulungu amapereka “kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Komanso Yesu ndi “moyo” kwa anthu amene anamwalira. (Yoh. 5:28, 29) Ndiye taganiziraninso zimene adzachite akadzakhala mkulu wa ansembe, mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000. Pa nthawiyi anthu onse amene Yesu azidzawalamulira padziko lapansi, adzawawombola ku uchimo ndi imfa.​—Aheb. 9:11, 12, 28.

16. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira Yesu?

16 Motero tingaone kuti yankho la Yesu pa funso limene Tomasi anafunsa likutikhudza kwambiri. Yesu ndi njira, choonadi ndi moyo. Iye ndi amene Mulungu anamutuma padziko pano kuti dziko lipulumutsidwe kudzera mwa iye. (Yoh. 3:17) Ndipo palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa iye. Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Mac. 4:12) Motero kaya poyamba tinkakhulupirira zotani, chinthu chanzeru panopo ndicho kuyamba kukhulupirira Yesu kuti atitsogolere ku moyo.​—Yoh. 20:31.

Talamulidwa Kumvera Khristu

17. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Mwana wa Mulungu?

17 Petulo, Yohane, ndi Yakobe anaona kusandulika kwa Yesu. Pa nthawi imeneyo, iwo anamva mawu ochokera kumwamba, akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndinam’sankha. Mumvereni iye.” (Luka 9:28, 29, 35) Kumvera lamulo lakuti timvere Mesiya ndi nkhani yofunika kwambiri.​—Werengani Machitidwe 3:22, 23.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvera Yesu Khristu?

18 Kumvera Yesu kumatanthauzanso ‘kumuyang’anitsitsa ndi kutsatira chitsanzo chake mozama.’ (Aheb. 12:2, 3) Choncho, ndi bwino kuti “tisamalire mwapadera” zinthu zokhudza iyeyo zimene timawerenga m’Baibulo ndi m’mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” komanso zimene timamva kumisonkhano yachikhristu. (Aheb. 2:1; Mat. 24:45) Poti ndife nkhosa zake, tiziyesetsa kumumvera ndi kumutsatira.​—Yoh. 10:27.

19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirizebe kutsatira Khristu?

19 Kodi n’zotheka kum’tsatira Khristu nthawi zonse, ngakhale titakumana ndi zovuta zazikulu kwambiri? Inde n’zotheka mwa ‘kugwiritsitsabe chitsanzo cha mawu opindulitsa,’ potsatira zimene timaphunzira komanso potsatira “chikhulupiriro ndi chikondi zomwe zili mwa Khristu Yesu.”​—2 Tim. 1:13.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi kutsatira “Khristu” kungatithandize bwanji kuti Yehova akhale bwenzi lathu lapamtima?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikamatsanzira Yesu timakhalanso tikutsanzira Yehova?

• Kodi Yesu ndi ‘njira, choonadi ndi moyo’ motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Wodzozedwa wa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Zimene Yesu ankaphunzitsa zimasonyeza kaganizidwe kapamwamba ka Yehova

[Chithunzi patsamba 30]

Tiyenera kutsatira mokhulupirika Wodzozedwa wa Yehova

[Chithunzi patsamba 32]

Yehova ananena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga . . . mumvereni iye”