Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali “Nthawi Yokhala Chete”

Pali “Nthawi Yokhala Chete”

Pali “Nthawi Yokhala Chete”

“MWAMBI wina wa ku Asia umati: “Kulankhula kuli ngati siliva, ndipo kukhala chete kuli ngati golide.” Pa Chichewa palinso mwambi wofanana ndi umenewu, wakuti: “Kukhala chete n’kulankhula komwe.” Ndipo Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru, anati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake . . . mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.”​—Mlal. 3:1, 7.

Kodi ndi nthawi iti imene munthu ayenera kutonthola, kapena kuti kukhala chete? M’Baibulo, mawu oti “kukhala chete,” kapena kuti “kutonthola,” amapezeka nthawi zopitirira 100. Nkhani zonse zimene zili ndi mawu amenewa zimasonyeza phindu la kukhala chete m’njira zitatu. Tiyeni tione bwinobwino mmene kukhala chete kumasonyezera ulemu, nzeru ndi kuzindikira, komanso mmene kumapatsira munthu mpata wosinkhasinkha.

Kumasonyeza Ulemu

Kukhala chete kumasonyeza ulemu. Mneneri Habakuku anati: “Yehova ali m’Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.” (Hab. 2:20) Anthu amene amalambiradi Yehova ayenera ‘kuyembekeza ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.’ (Maliro 3:26) Wamasalmo analemba kuti: “Khala chete mwa Yehova, num’lindirire Iye: Usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m’njira yake.”​—Sal. 37:7.

Kodi n’zotheka kutamanda Yehova popanda kulankhula? Inde n’zotheka. Mwachitsanzo, timagoma kwambiri tikaona kukongola kwa chilengedwe moti nthawi zina timachita kusowa chonena. Ndiyeno kodi kugoma kumeneku si umboni wakuti tikutamanda mlengi wathu chamumtima? Mawu oyamba amene Davide analemba mu Salmo lina, ndi akuti: “M’Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu: Adzakuchitirani Inu chowindachi.”​—Sal. 65:1.

Popeza Yehova ndi woyenera kulemekezedwa, tiyenera kulemekezanso mawu ake. Mwachitsanzo, pamene Mose mneneri wa Mulungu ankalankhula mawu omaliza kwa Aisiraeli, iye ndi ansembe analangiza anthu onse amene anasonkhana kuti: “Khalani chete . . . muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu.” Ngakhale ana awo ankayenera kumvetsera mwatcheru Aisiraeliwo akasonkhana pomvetsera Chilamulo cha Mulungu chikuwerengedwa. Mose anati: “Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono . . . kuti aphunzire.”​—Deut. 27:9, 10; 31:11, 12.

Masiku anonso n’chinthu choyenera kwa anthu olambira Yehova kumvetsera mwaulemu malangizo amene amalandira pa misonkhano yachikhristu, ngakhale misonkhano ikuluikulu. Ndithu, kunong’onezana nkhani zosafunika kwenikweni pa nthawi imene choonadi chamtengo wapatali cha m’Baibulo chikufotokozedwa pa msonkhano, n’kusalemekeza Mawu a Mulungu ndiponso gulu lake. Panthawi imeneyi tiyenera kukhala chete n’kumamvetsera.

Ngakhale pokambirana ndi munthu mmodzi, kumvetsera bwino kumasonyeza kuti ndife aulemu. Mwachitsanzo, Yobu anauza anthu amene ankamutsutsa kuti: “Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine.” Yobu ankaonetsetsa kuti wakhala chete n’kumamvetsera pamene iwo akulankhula. Ndipo itafika nthawi yake yoti alankhule, iye anawauza kuti: “Khalani chete, ndilekeni, kuti ndinene.”​—Yobu 6:24; 13:13.

Kumasonyeza Nzeru Ndiponso Kuzindikira

Baibulo limati: “Wokhala chete achita mwanzeru.” Limanenanso kuti: “Wozindikira amatonthola.” (Miy. 10:19; 11:12) Taonani chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu pa nkhaniyi. Iye anasonyeza nzeru ndiponso kuzindikira pokhala chete. Atazindikira kuti palibe chimene akanalankhula kuti asinthe maganizo oipa a adani ake, Yesu “anangokhala chete.” (Mat. 26:63) Kenako, akuimbidwa mlandu pamaso pa Pilato, Yesu anangokhala chete kuti ntchito zake, zimene anthuwo anali kuzidziwa, zimuchitire umboni.​—Mat. 27:11-14.

Ndi bwino kuti ifenso tizisamala polankhula, makamaka ena akatichitira zamtopola. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.” (Miy. 14:29) Popanda kuganiza mosamala tikakwiya ndi zinazake, tingalankhule mokhadzula ndipo tingadzanong’oneze bondo pambuyo pake. Mawu amene tingalankhule angakhale opanda nzeru ndipo zimenezi zingachititse kuti tisakhale ndi mtendere mumtima.

Kusamala polankhula tikakhala pakati pa anthu oipa kumaonetsa kuti ndife ozindikira. Anthu akamatinyoza mu utumiki, nthawi zina ndi bwino kungokhala chete. Ndi bwinonso kukhala chete anzathu kusukulu kapena kuntchito akamakamba nthabwala zoipa kapena akamatukwana. Izi zimasonyeza kuti sitisangalala ndi zinthu zoterozo. (Aef. 5:3) Wamasalmo analemba kuti: “Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham’kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.”​—Sal. 39:1.

Munthu “wozindikira” saulula chinsinsi. (Miy. 11:12) Mkhristu woona saulula zinthu zachinsinsi chifukwa cholephera kudzigwira. Makamaka akulu ayenera kusamala kwambiri pa nkhani imeneyi chifukwa kupanda kutero anthu mumpingo sangawakhulupirire.

Monga tanenera kale, kukhala chete n’kulankhula komwe ndipo nthawi zina kungakhale ndi zotsatira zabwino. Wolemba mabuku wina wa m’ma 1800, dzina lake Sydney Smith, anafotokoza motere za munthu wina wa m’nthawi yake: “Akamakamba nkhani, nthawi zina amangokhala phee ndipo izi zimachititsa kuti uzisangalala kumumvetsera.” Izi n’zimene zimafunika munthu akamakambirana ndi mnzake. Munthu wodziwa kulankhula bwino ndi anthu amapereka mpata woti winayo alankhule.

Solomo anachenjeza kuti: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.” (Miy. 10:19) Motero munthu wosalankhulalankhula amapewa kulankhula mopanda nzeru. Ndipotu “ngakhale chitsiru chikatonthola achiyesa chanzeru; posunama ali wochenjera.” (Miy. 17:28) Choncho tiyenera kupempha Yehova kuti ‘asunge pakhomo pa milomo yathu.’​—Sal. 141:3.

Kumatipatsa Mpata Wosinkhasinkha

Ponena za munthu amene amachita chilungamo, Malemba amatiuza kuti: “M’chilamulo [cha Mulungu] amalingirira usana ndi usiku.” (Sal. 1:2) Kodi pa nkhani yosinkhasinkha, ndi nthawi iti imene ili yabwino kwambiri?

Isake mwana wa Abulahamu, “anatuluka kulingalira m’munda madzulo.” (Gen. 24:63) Iye anasankha nthawi yabwino komanso malo aphee kuti asinkhesinkhe. Mfumu Davide ankasinkhasinkhanso usiku, kunja kuli zii. (Sal. 63:6) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, nayenso ankayesetsa kupeza nthawi yokhala kwayekha kumapiri, kuchipululu, ndi malo ena abata kuti asinkhesinkhe.​—Mat. 14:23; Luka 4:42; 5:16.

Kukhala chete kumatithandiza m’njira zambiri. Munthu akakhala chete amatha kudzifufuza bwinobwino ndipo zimenezi zingamuthandize kuti akhale munthu wabwino. Kukhala chete kumathandizanso kuti munthu akhale ndi mtendere wa mumtima. Kusinkhasinkha tili pa malo abata kumatithandiza kukhala odzichepetsa ndiponso kungatithandize kuganizira zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu.

M’nkhani ino taona kuti kukhala chete n’kwabwino. Koma palinso “nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:7) Masiku ano atumiki oona a Mulungu amatanganidwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyo 24:14) Izi zikuchititsa kuti pakhale chisangalalo chachikulu kwambiri pamene chiwerengero cha atumikiwo chikuwonjezereka. (Mika 2:12) Choncho tiyeni tiyesetse kulalikira nawo mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu n’kumalankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu. Pamene tikugwira ntchito yofunika imeneyi, tiyenera kusonyezanso pa moyo wathu kuti timadziwa mfundo yakuti nthawi zina kukhala chete n’kofunika.

[Chithunzi patsamba 3]

Pa misonkhano yathu tiyenera kukhala chete n’kumamvetsera mwatcheru

[Chithunzi patsamba 4]

Mu utumiki tiyenera kukhala chete, anthu akamatinenera mawu achipongwe

[Chithunzi patsamba 5]

Kukhala chete kumatipatsa mpata wosinkhasinkha