Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Satana anachotsedwa liti kumwamba?​—Chiv. 12:1-9.

Buku la Chivumbulutso silimatchula mwachindunji nthawi imene Satana anachotsedwa kumwamba, koma limatchula zinthu zofunika kwambiri zimene zingatithandize kudziwa nthawi imene zimenezi zinachitika. Chinthu choyamba ndicho kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya ndipo kenaka “kunabuka nkhondo kumwamba.” Pa nkhondoyo Satana anagonjetsedwa n’kuchotsedwa kumwambako.

Malemba amasonyeza momveka bwino kuti mu 1914 “nthawi zoikika za amitundu” zinatha ndipo Ufumu unakhazikitsidwa. * (Luka 21:24) Kodi nkhondo yochotsa Satana kumwamba inayamba zimenezi zitangochitika?

Lemba la Chivumbulutso 12:4 limati “Chinjokacho [Satana] chinangoimabe pamaso pa mkazi uja amene anali pafupi kubereka, kuti akabereka, chimudye mwana wakeyo.” Zimenezi zikusonyeza kuti Satana ankafunitsitsa kuwonongeratu Ufumuwo utangobadwa kumene. Ngakhale kuti Yehova anachitapo kanthu kuti zolinga za Satana zisatheke, Satana anachitabe khama kuti awononge Ufumu umene unali utangokhazikitsidwa kumenewo. N’chifukwa chake “Mikayeli ndi angelo ake” sanachedwechedwe koma anathamangitsa “chinjoka ndi angelo ake” kuwachotsa kumwambako n’cholinga choti Ufumuwo usawonongedwe. Izi zikutipatsa chithunzi chakuti Satana anachotsedwa kumwamba Ufumu utangokhazikitsidwa kumene mu 1914.

Mfundo ina imene tiyenera kuiganizira ndi yokhudza kuuka kwa Akhristu odzozedwa. Malemba amasonyeza kuti kuuka kumeneku kunayamba Ufumu utangokhazikitsidwa kumene. * (Chiv. 20:6) Baibulo silinena kuti Khristu anali ndi abale ake ena pomenyana ndi chinjoka ndiponso ziwanda. Zimenezi zikutanthauza kuti pa nthawi imene abale ake a Khristu anayamba kuuka, nkhondo yochotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba iyenera kuti inali itatha.

Motero, Baibulo silitchula nthawi yeniyeni imene Satana ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba. Komabe, umboni umasonyeza kuti kuchotsedwa kwa Satana kumwamba kunachitika Yesu Khristu atangoikidwa kumene kukhala Mfumu kumwamba mu 1914.

[Mawu a M’munsi]