Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amuna, Tsanzirani Chikondi cha Khristu

Amuna, Tsanzirani Chikondi cha Khristu

Amuna, Tsanzirani Chikondi cha Khristu

TSIKU loti afa mawa, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:34, 35) Akhristu oona ayeneradi kukondana.

Paulo analembera amuna achikhristu omwe ndi okwatira kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Kodi mwamuna wachikhristu yemwe mkazi wake ndi mtumiki wa Yehova wodzipereka angatsatire bwanji malangizo a m’Malemba amenewa?

Khristu Ankasamalira Mpingo

Baibulo limati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. Amene akonda mkazi wake adzikonda iye mwini, pakuti palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.” (Aef. 5:28, 29) Yesu ankakonda kwambiri ophunzira ake ndipo ankawaona kuti ndi amtengo wapatali. Iye ankawasamalira. Ngakhale kuti ophunzira akewo ankalakwitsa zinthu zina, iye anali woleza ndipo ankawakomera mtima. Pofuna kuti “alandire mpingowo uli wokongola mwaulemerero,” iye ankaganizira kwambiri za makhalidwe abwino a ophunzira akewo.​—Aef. 5:27.

Khristu ankachita zinthu zosonyeza kuti ankakonda mpingo, motero mwamuna ayeneranso kusonyeza kuti amakonda mkazi wake mwa zochita ndi zolankhula zake zomwe. Mkazi akamamva mawu achikondi kawirikawiri kwa mwamuna wake, amamva bwino kwambiri ndipo amasangalala. Koma ngakhale pakhomo patakhala pa mwanaalirenji, mkazi amakhala wosungulumwa ndipo sakhala wachimwemwe ngati mwamuna wake amangomunyalanyaza.

Kodi mwamuna amasonyeza bwanji kuti amasamalira mkazi wake? Akakhala pagulu, amanena monyadira kuti mkazi wanga ndi uyu, ndipo amayamikira kwambiri zabwino zimene mkaziyo amachita. Iye sachita manyazi kuuza ena ngati mkazi wakeyo wathandiza kwambiri kuti zina zake ziyende bwino m’banjamo. Akakhala awiriwiri, mkaziyo amafunika azimva kuti mwamuna wake amamukonda. Zinthu ngati kum’sisita, kum’mwetulira, kum’kumbatira ndiponso kumuyamikira zingaoneke ngati zazing’ono koma zimachititsa mkazi kumva bwino.

‘Sanachite Manyazi Kuwatcha “Abale”’

Yesu Khristu ‘sanachite manyazi kuwatcha [Akhristu odzozedwa] “abale.”’ (Aheb. 2:11, 12, 17) Ngati ndinu mwamuna wachikhristu muzikumbukira kuti mkazi wanuyo ndi mlongonso. Kaya mkazi wanuyo anabatizidwa mutakwatirana kale kapena ayi, dziwani kuti kudzipereka kwake kwa Yehova kumaposa malumbiro amene anapanga tsiku la ukwati wanu. M’bale amene akuchititsa misonkhano amatchula mkazi wanu kuti “mlongo uje.” Sikuti mkazi wanuyo amakhala mlongo mukakhala ku Nyumba ya Ufumu kokha. Iye amakhalanso mlongo wanu mukakhala kunyumba. Motero n’koyenera kuti muzimuchitira zabwino ndiponso muzimulemekeza mukakhala kunyumba, ngati mmene mumachitira mukakhala ku Nyumba ya Ufumu.

Ngati muli ndi maudindo ambiri kumpingo, nthawi zina mungaone kuti n’zovuta kuti muzipeza nthawi yosamaliranso maudindo am’banja. Choncho muzigwirizana ndi akulu ndiponso atumiki othandiza komanso kuphunzitsa ena mmene angagwirire ntchito zina. Izi zingakuthandizeni kuti muzipeza nthawi yokhala ndi mkazi wanu, yemwe ndi mlongo amene muyenera kumuthandiza kwambiri. Kumbukirani kuti pali abale ambiri amene angathe kusamalira maudindo amene inu mumasamalira kumpingo. Koma dziwani kuti pali zinthu zina zokhudza mkazi wanuyo zimene ndi inu nokha amene mungazisamalire.

Ndiponso inuyo ndinu mutu wa mkazi wanu. Baibulo limati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akor. 11:3) Popeza ndinu mutu, kodi muyenera kuchita zinthu motani? Muyenera kuchita zinthu mwachikondi osati kumangomuuza kuti, ‘Pajatu ine ndi mutu ndiye uzindimvera.’ Njira yabwino yosonyezera umutu ndi kutsanzira Yesu Khristu pochita zinthu ndi mkazi wanu.​—1 Pet. 2:21.

‘Ndinu Mabwenzi Anga’

Yesu anatchula ophunzira ake kuti mabwenzi. Iye anawauza kuti: “Sindikutchanso inu kuti akapolo, chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” (Yoh. 15:14, 15) Yesu ndi ophunzira ake ankakambirana momasuka ndiponso ankachitira zinthu limodzi. “Yesunso ndi ophunzira” ake anaitanidwa kuphwando la ukwati ku Kana. (Yoh. 2:2) Iwo analinso ndi malo amene ankakonda kupitako monga ngati ku munda wa Getsemane. Baibulo limati: “Nthawi zambiri Yesu anali kukumana ndi ophunzira ake kumeneko.”​—Yoh. 18:2.

Mkazi ayenera kudzimva kuti mwamuna wake ndi mnzake wapamtima. Choncho m’pofunika kuti mwamuna ndi mkazi wake azikhala mosangalala, azitumikira Mulungu limodzi komanso azisangalala pophunzira Baibulo limodzi. Azikhala limodzi, kuyenda limodzi, kucheza limodzi ndi kudya limodzi. Kungokhala anthu okwatirana sikokwanira ayi, muyeneranso kumagwirizana kwambiri monga munthu ndi mnzake wapamtima.

“Anawakonda Mpaka Mapeto”

Yesu ‘anakonda ophunzira ake mpaka mapeto.’ (Yoh. 13:1) Amuna ena amalephera kutsanzira Khristu pa nkhani imeneyi. Ena mpaka amafika posiya ‘mkazi wa ubwana wawo’ n’kutenga wina, mwina wachitsikana.​—Mal. 2:14, 15.

Koma pali amuna ena amene amatsanzira Khristu. Mwachitsanzo, mkazi wa Willi atadwala anafunika chisamaliro kwa zaka zambiri. Kodi Willi anamva bwanji ndi vuto limeneli? Iye anati: “Nthawi zonse ndimaona kuti mkazi wanga ndi mphatso yochokera kwa Mulungu yomwe ndimaiyamikira kwambiri. Ndipotu zaka 60 zapitazo ndinalonjeza kuti ndidzamusamalira zivute zitani. Sindidzaswa lonjezo limeneli.”

Choncho, amuna achikhristunu tsanzirani chikondi cha Khristu. Muzisamalira kwambiri kapena kuti kuchengeta mkazi wanu woopa Mulungu, yemwe ndi mlongo wanu komanso mnzanu wapamtima.

[Chithunzi patsamba 20]

Kodi mkazi wanu ndi mnzanu wapamtima?

[Chithunzi patsamba 20]

‘Pitirizani kukonda mkazi wanu’