Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

PONENA za Mulungu, Baibulo limati: “Iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” Ndiponso Mulungu amatitsimikizira kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Yakobe 1:17; Malaki 3:6) Yehova Mulungu ndi wosiyana kwambiri ndi anthu ambiri omwe amakhala ovuta maganizo ndipo zimakhala zovuta kuwakhulupirira chifukwa choti amasinthasintha maganizo awo.

Komabe, anthu ena omwe amawerenga Baibulo amafuna atadziwa ngati Mulungu wasintha maganizo ake. Mwachitsanzo, kale Yehova Mulungu ankapereka kwa Akhristu mphatso yochitira zozizwitsa, koma masiku ano sapereka. Kale Mulungu ankalola anthu kukwatira mitala, koma masiku ano salola zimenezi. Komanso m’Chilamulo cha Mose, Yehova ankafuna kuti anthu azisunga sabata, koma masiku ano zimenezo zinatha. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Mulungu wasintha maganizo ake?

Choyamba, tiyenera kudziwa kuti Mulungu sasintha mfundo zake zachikondi ndiponso zachilungamo. Chinanso n’chakuti iye sanasinthe “chifuniro [chake] cha nthawi za nthawi,” chakuti anthu onse adzapeze madalitso osatha mu Ufumu wake. (Aefeso 3:11) Komabe, mofanana ndi mmene inuyo mungasinthire ngati munthu wina amakukhumudwitsani kawirikawiri, nayenso Yehova amasintha mogwirizana ndi mmene zinthu zilili.

Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amasinthanso malangizo amene amapereka kwa anthu ake mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pamoyo wawo komanso zimene anthuwo akufunikira. Ndipo zimenezi n’zosadabwitsa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene munthu wodziwa bwino ntchito yotsogolera alendo angachite ngati atazindikira kuti kutsogolo kwa njira imene akuyenda kuli zoopsa. Iye akhoza kuuza anthu amene akuwatsogolerawo kuti adutse njira ina n’cholinga choti asakumane ndi zoopsazo. Koma zimenezo sizikutanthauza kuti munthu amene akutsogolera ulendowo wasintha kumene anthuwo akupita. Tiyeni tione mwatsatanetsatane mfundo zitatu tazitchula poyamba zija, zimene anthu ena sazimvetsa bwino.

N’chifukwa Chiyani Mphatso Yochitira Zozizwitsa Inatha?

N’chifukwa chiyani Mulungu ankapereka mphamvu zochita zozizwitsa kwa Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi? Mwina mukudziwa kuti panthawi imene Aisiraeli anali mtundu wa Mulungu wosankhika, iye nthawi zambiri ankawachitira zozizwitsa posonyeza kuti akuwayanja. Mulungu anasonyeza mphamvu zake zodabwitsa pogwiritsa ntchito Mose kuti atsogolere mtundu wa Isiraeli paulendo wawo wodutsa m’chipululu, kuchoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti mobwerezabwereza, Aisiraeli ankalephera kukhulupirira Yehova. Ndipo kenako Yehova atakana mtundu wa Isiraeli n’kukhazikitsa mpingo wachikhristu, iye anapereka mphatso yochitira zozizwitsa kwa atumwi ndiponso anthu ena. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo ndi Yohane anachiritsa munthu yemwe anali wolumala chibadwire. Nayenso Paulo anaukitsa munthu wakufa. (Machitidwe 3:2-8; 20:9-11) Zozizwitsa zimene iwo ankachita zinathandiza kuti Chikhristu chifalikire m’mayiko ambiri. Nangano n’chifukwa chiyani mphatso yochitira zozizwitsa inatha?

Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo pofotokoza chifukwa chake. Iye anati: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Makolo amalangiza mwana wamng’ono mosiyana ndi mmene amalangizira mwana wamkulu. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anasintha mmene ankachitira zinthu ndi mpingo wachikhristu, mpingowo utakula, zomwe zinatanthauza kuti sunalinso ngati “kamwana.” Mtumwi Paulo ananena kuti mphatso yochitira zozizwitsa monga kulankhula malilime kapena kulosera ‘zidzatha.’​—1 Akorinto 13:8.

N’chifukwa Chiyani Anthu Ankaloledwa Kukwatira Mitala?

Yesu anasonyeza kuti Mulungu anakhazikitsa mfundo yokhudza ukwati pamene anauza Adamu ndi Hava kuti: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?” (Mateyo 19:5) Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti anthu awiri akakwatirana, afunika kukhalira limodzi kwa moyo wawo wonse. Komabe, panthawi imene Mulungu anakhazikitsa mtundu wa Aisiraeli ndi kuupatsa Chilamulo, anthu anali atayamba kale kukwatira mitala. Choncho, ngakhale kuti Mulungu si amene anayambitsa kapena kulimbikitsa mitala, iye anapereka malamulo okhudza nkhani imeneyi. Koma mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, Mawu a Mulungu analetsa mosapita m’mbali kuti anthu asamachite mitala.​—1 Timoteyo 3:2.

Yehova Mulungu amalola kuti zinthu zina zizichitika mpaka panthawi imene iye waona kuti ndi yoyenera kukonza zinthuzo. (Aroma 9:22-24) Yesu anasonyeza kuti Yehova analolera kwa kanthawi kuti maukwati osayenera azichitika chifukwa cha ‘kuuma mtima’ kwa Aisiraeliwo.​—Mateyo 19:8; Miyambo 4:18.

N’chifukwa Chiyani Kusunga Sabata N’kosafunika Masiku Ano?

Mulungu atapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, anawalamula kuti azisunga sabata mlungu ulionse. Kenako iye anaika lamuloli kukhala mbali ya Chilamulo. (Eksodo 16:22-30; 20:8-10) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu anapereka moyo wake nsembe ndipo “anathetsa . . . Chilamulo chokhala ndi malamulo operekedwa monga malangizo,” ndiponso ‘anafafaniza chikalata cholemba pa manja.’ (Aefeso 2:15; Akolose 2:14) Lamulo lokhudza sabata ndi limene ‘linathetsedwa’ ndiponso ‘kufafanizidwa.’ Zimenezi zili choncho chifukwa Baibulo limanena kuti: “Munthu asakuweruzeni ponena za kudya ndi kumwa kapena chikondwerero chinachake, kapena kusunga tsiku la mwezi watsopano, kapena sabata.” (Akolose 2:16) Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu anapereka Chilamulo cha Mose komanso lamulo loti anthu azisunga sabata?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilamulo chakhala namkungwi wotitsogolera kwa Khristu.” Kenako iye ananenanso kuti: “Popeza chikhulupirirocho tsopano chafika, sitilinso pansi pa namkungwi.” (Agalatiya 3:24, 25) Mulungu sanasinthe maganizo ake, koma kwa kanthawi kochepa anagwiritsa ntchito lamulo loti anthu azisunga sabata, ngati njira yophunzitsira anthuwo kuti azipeza nthawi yoganizira mozama pa zinthu zauzimu. Ngakhale kuti lamuloli linali la kanthawi kochepa chabe, linkachitira chithunzi nthawi imene anthu adzapume ku mavuto awo, mwauzimu ndiponso mwakuthupi.​—Aheberi 4:10; Chivumbulutso 21:1-4.

Mulungu Wodalirika Ndiponso Wachikondi

Zitsanzo za m’Baibulo taonazi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu anapereka malangizo osiyanasiyana panthawi zosiyanasiyananso. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti iye anasintha maganizo ake. M’malomwake, ankachita zinthu mogwirizana ndi m’mene zinalili panthawiyo n’cholinga choti athandize anthu ake. Yehova sanasinthe chifukwa ndi mmenenso amachitira zinthu masiku ano.

Popeza kuti Yehova sasintha mfundo zake, sizingativute kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti timusangalatse. Komanso sitingakayike kuti chilichonse chimene walonjeza chidzachitika. Yehova anati: “Ndidzachita zofuna zanga zonse . . . ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.”​—Yesaya 46:10, 11.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Mulungu sasintha mfundo zake zachikondi ndiponso zachilungamo

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti mphatso yochitira zozizwitsa ‘idzatha’

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Anthu awiri akakwatirana, amafunika kukhalira limodzi kwa moyo wawo wonse