Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mdindo Wokhulupirika ndi Bungwe Lake Lolamulira

Mdindo Wokhulupirika ndi Bungwe Lake Lolamulira

Mdindo Wokhulupirika ndi Bungwe Lake Lolamulira

“Ndani kwenikweni ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yake?”​—LUKA 12:42.

1, 2. Tchulani funso lofunika limene Yesu anafunsa pamene amanena chizindikiro cha masiku otsiriza.

PAMENE ankafotokoza za chizindikiro cha masiku otsiriza, Yesu anafunsa kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuyang’anira antchito ake a pakhomo, kuwapatsa chakudya chawo panthawi yoyenera?” Kenako Yesu ananena kuti kapolo ameneyu adzapatsidwa udindo woyang’anira zinthu zonse za Mbuye wake monga mphoto ya kukhulupirika kwake.​—Mat. 24:45-47.

2 Aka sikanali koyamba kuti Yesu afunse funso limeneli. Iye anali atafunsapo funso lomweli miyezi ingapo m’mbuyomo pa nthawi ya madyerero amisasa. (Werengani Luka 12:42-44.) Pa nthawiyo, iye sanatchule mawu oti kapolo koma anati “mdindo.” Ndipo m’malo mwa mawu oti “zinthu zake,” iye anagwiritsa ntchito mawu oti “gulu la atumiki ake.” Mawu akuti mdindo amatanthauza munthu amene amayang’anira nyumba ndi antchito a munthu wina. Koma nayenso amakhala wantchito. Ndiyeno kodi kapolo kapena kuti mdindo ameneyu ndi ndani, nanga amapereka bwanji ‘chakudya pa nthawi yoyenera’? Ndi bwino kuti tonsefe tizizindikira njira imene Yehova amagwiritsa ntchito popereka chakudya chauzimu.

3. (a) Kodi akatswiri ena ofotokoza za Chikhristu amati mawu a Yesu akuti “kapolo” amanena za ndani? (b) Kodi “kapolo” kapena kuti “mdindo” ndi ndani, nanga “gulu la atumiki ake” kapena kuti “zinthu zake” zikuimira ndani?

3 Akatswiri ena ofotokoza za Chikhristu amati pamenepa Yesu amanena za anthu amene ali ndi udindo m’matchalitchi. Koma mu fanizoli Yesu, yemwe ndi “mbuye,” sananene kuti padzakhala akapolo ambirimbiri m’zipembedzo zosiyanasiyana zachikhristu. M’malomwake, iye ananena momveka bwino kuti padzakhala “mdindo” kapena kuti “kapolo” mmodzi yekha amene adzamuika kuyang’anira zinthu zake zonse. Choncho, monga magazini ya Nsanja ya Olonda yakhala ikufotokozera, n’zosakaikitsa ngakhale pang’ono kuti mdindo ameneyu akuimira “kagulu ka nkhosa” komwe ndi gulu lonse la Akhristu odzozedwa. Malinga ndi zimene Luka analemba, Yesu ananena za kapoloyu atangonena kumene za Akhristu amenewa. (Luka 12:32) Mawu akuti “gulu la atumiki ake” kapena kuti “zinthu zake,” amanena za gulu la Akhristu odzozedwa lomweli koma amasonyeza udindo umene aliyense payekha ali nawo. Ndiyeno funso lofunika kuliganizira ndi lakuti, kodi munthu aliyense wa m’gululi amagwira nawo ntchito yopereka chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyenera kuona bwino zimene Malemba amanena.

Mtumiki wa Yehova Wakale

4. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito mawu ati ponena za mtundu wa Isiraeli wakale, ndipo kodi ndi zinthu ziti zokhudza mtunduwu zimene tiyenera kukumbukira?

4 Yehova anatchula anthu ake a mtundu wa Isiraeli kuti mtumiki. Iye anati: ‘Inu ndinu mboni zanga ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.’ (Yes. 43:10) Aisiraeli onse anali m’gulu la mtumiki ameneyu. Komabe tiyenera kukumbukira kuti ansembe ndi Alevi okha ndi amene anali ndi udindo wophunzitsa mtunduwo.​—2 Mbiri 35:3; Mal. 2:7.

5. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, kodi zinthu zinasintha bwanji?

5 Kodi mtundu wa Isiraeli unali kapolo amene Yesu ankanena? Ayi. Tikutero chifukwa cha mawu amene Yesu anauza Ayuda a m’nthawi yake. Iye anati: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) N’zoonekeratu kuti zinthu zinali kudzasintha. Ndipo Yehova anasinthadi zinthu n’kuyamba kugwiritsa ntchito mtundu watsopano. Komabe pa nkhani ya malangizo auzimu, ntchito ya kapolo amene Yesu ananena imachitika mofanana ndi mmene ankachitira “mtumiki” wa Mulungu m’nthawi ya Isiraeli wakale.

Kapolo Wokhulupirika Anadziwika

6. Tchulani mtundu watsopano umene unayamba pa Pentekosite 33 C.E., ndipo ndani amene anali m’gululi?

6 Mtundu watsopano kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu” wapangidwa ndi Isiraeli wauzimu. (Agal. 6:16; Aroma 2:28, 29; 9:6) Mtunduwu unayamba ndi anthu amene analandira mzimu wa Mulungu pa Pentekosite mu 33 C.E. Kuyambira nthawi imeneyi Akhristu odzozedwa onse anapanga mtundu umenewu ndipo iwo anali m’gulu la kapolo woikidwa ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mbuye. Aliyense amene anali mu mtundu umenewu anapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Ndiyeno kodi munthu aliyense wa m’gululi ankagwira nawo ntchito yopereka chakudya chauzimu pa nthawi yake? Tiyeni tione mmene Malemba amayankhira funsoli.

7. Kodi poyamba ntchito yaikulu ya atumwi inali yotani, ndipo kenako iwo anapatsidwanso ntchito yotani?

7 Yesu atasankha atumwi ake 12, ntchito yaikulu imene anawapatsa inali kulalikira uthenga wabwino. (Werengani Maliko 3:13-15.) Ntchito imeneyi inali yogwirizana ndi tanthauzo la mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti mtumwi. Mawuwo amatanthauza “kutuma.” Komabe patapita nthawi, komanso mpingo wachikhristu utatsala pang’ono kuyamba, udindo waukulu wa atumwi unali ‘kuyang’anira.’​—Mac. 1:20-26.

8, 9. (a) Kodi ntchito yaikulu ya atumwi 12 inali yotani? (b) Kodi kenako ndi anthu ati amene bungwe lolamulira linavomereza kuti apatsidwe maudindo ena?

8 Kodi n’chiyani chimene atumwi 12 ankaona kuti n’chofunika kwambiri? Kuti tidziwe, tiyeni tione zimene zinachitika pambuyo pa Pentekoste. Panali kusagwirizana pa nkhani ya kagawidwe ka chakudya kwa akazi amasiye. Motero atumwi 12 anasonkhanitsa ophunzira n’kunena kuti: “N’kosayenera kuti ife tisiye mawu a Mulungu n’kuyamba kumakagawa chakudya.” (Werengani Machitidwe 6:1-6.) Kenako atumwi anasankha abale ena oyenerera kuti achite “ntchito yofunikayi” n’cholinga choti atumwiwo aike maganizo awo onse pa “utumiki wokhudza mawu a Mulungu.” Dongosolo limeneli linabweretsa madalitso a Yehova chifukwa “mawu a Mulungu anapitirira kufalikira ponseponse. Chiwerengero cha ophunzira chinali kuwonjezeka mowirikiza kwambiri mu Yerusalemu.” (Mac. 6:7) Motero, udindo wopereka chakudya chauzimu unali wa atumwi.​—Mac. 2:42.

9 Patapita nthawi, ena anapatsidwa maudindo akuluakulu. Motsogoleredwa ndi mzimu woyera, mpingo wa ku Antiokeya unatumiza Paulo ndi Baranaba kuti akagwire ntchito ya umishonale. Iwo ankatchedwanso atumwi ngakhale kuti sanali m’gulu la atumwi 12 oyambirira. (Mac. 13:1-3; 14:14; Agal. 1:19) Pambuyo pake, bungwe lolamulira la ku Yerusalemu linawavomereza kuti akhale atumwi. (Agal. 2:7-10) Pasanapite nthawi yaitali, Paulo anayamba kugwira nawo ntchito yopereka chakudya chauzimu. Ndipo iye analemba kalata yake yoyamba youziridwa.

10. M’nthawi ya atumwi, kodi Akhristu odzozedwa onse ankagwira ntchito yokonza chakudya chauzimu? Fotokozani.

10 Kodi Akhristu odzozedwa onse ankayang’anira ntchito yolalikira komanso kupereka chakudya chauzimu? Ayi ndithu. Mtumwi Paulo anati: “Sikuti onse angakhale atumwi, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aneneri, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aphunzitsi, angatero ngati? Si onse amachita ntchito zamphamvu, ndi onse ngati?” (1 Akor. 12:29) Ngakhale kuti Akhristu odzozedwa onse ankagwira ntchito yolalikira, ndi amuna 8 okha amene anagwiritsidwa ntchito polemba mabuku 27 a Malemba Achigiriki Achikristu.

Kapolo Wokhulupirika Masiku Ano

11. Kodi kapolo wapatsidwa udindo woyang’anira “zinthu” ziti?

11 Mawu a Yesu opezeka pa Mateyo 24:45 anasonyeza kuti gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lidzakhalapobe padzikoli mpaka nthawi ya mapeto. Lemba la Chivumbulutso 12:17 limati anthu amenewa ndi “otsala” a mbewu ya mkazi. Iwo monga gulu apatsidwa udindo woyang’anira zinthu zonse za Khristu padziko lapansi. “Zinthu” zonse za Mbuye zimene gululi lauzidwa kuti liyang’anire zikuphatikizapo anthu onse amene amagonjera Ufumu komanso zinthu zonse zimene zimathandiza kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino itheke.

12, 13. Kodi Mkhristu amadziwa bwanji kuti ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba?

12 Kodi Mkhristu amadziwa bwanji kuti ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba ndipo ali m’gulu la otsala a Isiraeli wauzimu? Tingapeze yankho m’mawu amene mtumwi Paulo anauza anzake omwe analinso ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Iye anati: “Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewa ndiwo ana a Mulungu. Popeza simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene tifuula nawo kuti: “Abba, Atate!” Pakuti mzimuwo uchitira umboni pamodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu. Chotero, ngati tili ana, tilinso olowa ufumu: olowa ufumu a Mulungu, komanso olowa ufumu anzake a Khristu, malinga ngati tivutika naye limodzi kotero kuti tikalandire ulemerero limodzi naye.”​—Aroma 8:14-17.

13 Choncho mwachidule tingati anthuwa amadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo amalandira “chiitano cha kumwamba.” (Aheb. 3:1) Mulungu ndi amene amaitana anthu amenewa aliyense payekha. Izi zikachitika, iwo amadziwa kuti ndi ana a Mulungu popanda kukayika kapena kuchita mantha. (Werengani 1 Yohane 2:20, 21.) Motero, munthu sasankha yekha kuti akhale ndi chiyembekezo chimenechi, koma Yehova ndi amene amamuika chisindikizo kapena kuti kumudzoza ndi mzimu woyera.​—2 Akor. 1:21, 22; 1 Pet. 1:3, 4.

Kukhala ndi Maganizo Oyenera

14. Kodi odzozedwa ayenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya chiyembekezo chawo?

14 Kodi Akhristu odzozedwawa ayenera kukhala ndi maganizo otani pamene akuyembekezera kupita kumwamba? Iwo ayenera kukumbukira kuti angoitanidwa, sikuti apita kale kumwambako. Ayenera kukhala okhulupirika mpaka imfa kuti akalandire mphoto yawo. Ayeneranso kukhala odzichepetsa ndiponso kukhala ndi maganizo amene Paulo anali nawo. Iye anati: “Abale, ine sindidziyesa wopata kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi, poiwala zinthu za kumbuyo ndi kukalamira za kutsogolo, ndikuyesetsa mpaka ndikapate mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.” (Afil. 3:13, 14) Odzozedwa amene atsala padzikoli ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti ‘ayende moyenera chiitano chimene anaitanidwa nacho modzichepetsa kotheratu,’ komanso “mwa mantha ndi kunjenjemera.”​—Aef. 4:1, 2; Afil. 2:12; 1 Ates. 2:12.

15. Kodi Akhristu ena ayenera kuwaona bwanji anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso, nanga anthu odzozedwawo ayenera kukhala ndi maganizo otani?

15 Nanga kodi Akhristu ena ayenera kukhala ndi maganizo otani ngati munthu wina wayamba kudya zizindikiro pa tsiku la Chikumbutso, n’kumanena kuti wadzozedwa? Iwo sayenera kuweruza munthuyo. Imeneyi ndi nkhani ya pakati pa iyeyo ndi Yehova. (Aroma 14:12) Koma dziwani kuti Akhristu amene adzozedwadi safuna ulemu wapadera. Iwo sakhala ndi maganizo oti kudzozedwako kumawathandiza kudziwa zinthu zina zapadera zimene a “khamu lalikulu” ena okhwima mwauzimu sazidziwa. (Chiv. 7:9) Saganizanso kuti kudzozedwako pakokha kumawapangitsa kukhala ndi mzimu woyera wambiri kuposa a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Iwo safuna kuti azilemekezedwa kwambiri komanso sakhala ndi maganizo akuti amaposa akulu mumpingo chifukwa choti amadya zizindikiro.

16-18. (a) Kodi odzozedwa onse amagwira nawo ntchito yopereka mfundo za choonadi zatsopano? Perekani chitsanzo. (b) N’chifukwa chiyani Bungwe Lolamulira silifunika kufunsa maganizo kwa aliyense amene amati ndi wodzozedwa?

16 Kodi odzozedwa onse padziko lapansi amalumikizana n’kumakambirana kaye asanatulutse mfundo zatsopano zachoonadi? Ayi. N’zoona kuti gulu limeneli lili ndi udindo wopereka chakudya chauzimu. Komabe sikuti onse ali ndi maudindo kapena ntchito zofanana. (Werengani 1 Akorinto 12:14-18.) Monga taonera kale, m’nthawi ya atumwi odzozedwa onse ankagwira nawo ntchito yolalikira. Koma ndi ochepa okha amene analemba nawo mabuku a Baibulo ndiponso amene ankayang’anira mpingo wachikhristu.

17 Mwachitsanzo, nthawi zina Malemba amanena kuti “mpingo” umasamalira nkhani zina zachiweruzo. (Mat. 18:17) Koma zoona zake n’zakuti ndi akulu okha amene amasamalira nkhanizo moimira mpingo. Akulu safunsa kaye anthu onse mumpingomo kuti anene maganizo awo asanaweruze nkhani inayake. Iwo amagwira ntchito yawo ndipo amaimira mpingo wonse.

18 Masiku anonso ndi kagulu kochepa chabe ka Akhristu odzozedwa kamene kamagwira ntchito moimira gulu lonse la kapolo. Kagulu kameneka ndiko Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Abale odzozedwa amenewa, amayang’anira ntchito ya Ufumu ndiponso yopereka chakudya chauzimu. Mofanana ndi nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulira likafuna kusankha zochita siliyamba lafunsa anthu onse a m’gulu la kapolo. (Werengani Machitidwe 16:4, 5.) Komabe Akhristu odzozedwa onse amagwira nawo mwakhama ntchito yofunika kwambiri yokolola yomwe ikuchitika masiku ano. Akhristu onse odzozedwa ali m’gulu limodzi la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” koma aliyense ali ndi ntchito yake.​—1 Akor. 12:19-26.

19, 20. Kodi a khamu lalikulu ayenera kuona motani “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi bungwe lake lolamulira?

19 Khamu lalikulu la anthu amene adzakhale kosatha padzikoli likuwonjezereka. Ndiyeno kodi iwo ayenera kumva bwanji ndi mfundo zimene takambiranazi? Podziwa kuti iwo ndi mbali ya zinthu za Mfumu, amagwira ntchito mosangalala komanso mogwirizana ndi Bungwe Lolamulira limene limaimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” A khamu lalikulu amayamikira chakudya chauzimu chimene chikuperekedwa motsatira malangizo a Bungwe Lolamulira. Komabe ngakhale kuti a khamu lalikulu amalemekeza gulu la kapolo, iwo ayenera kusamala kuti asamapereke ulemu wosayenerera kwa anthu amene amanena kuti ndi odzozedwa. Mkhristu wodzozedwadi ndi mzimu wa Mulungu safuna ulemu woterowo.​—Mac. 10:25, 26; 14:14, 15.

20 Tonsefe tili m’gulu la “zinthu” za ambuye. Kaya ndife otsalira a odzozedwa kaya ndife a khamu lalikulu, tiyenera kutsimikiza mtima kuchita zinthu mogwirizana ndi mdindo wokhulupirika ndi bungwe lake lolamulira. Motero aliyense ayenera ‘kukhalabe maso’ n’kukhalabe wokhulupirika mpaka mapeto.​—Mat. 24:13, 42.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi ndani, nanga zinthu zake zonse zikuimira ndani?

• Kodi munthu amadziwa bwanji kuti ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba?

• Kodi udindo wokonza chakudya chauzimu ndi wa ndani kwenikweni?

• Kodi munthu wodzozedwa ayenera kukhala ndi maganizo otani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Masiku ano Bungwe Lolamulira limaimira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ndi mmenenso zinalili m’nthawi ya atumwi