Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?

Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?

Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?

Yosimbidwa ndi Ruth Danner

Mayi anga ankakonda kunena moseka kuti chaka cha 1933 chinali chaka cha tsoka, chifukwa ndi chaka chimene Hitler anayamba kulamulira, chimene Papa anachitchula kuti Chaka Choyera, komanso chimene ineyo ndinabadwa.

MAKOLO anga ankakhala m’tauni ya Yutz, ku Lorraine, chomwe ndi chigawo chakale cha ku France kufupi ndi malire a dziko la Germany. M’chaka cha 1921, mayi anga, omwe anali Mkatolika wolimbikira kwambiri anakwatirana ndi bambo anga, omwe anali Mpolotesitanti. Mkulu wanga, Helen, anabadwa mu 1922 ndipo makolo anga anakam’batizitsa m’tchalitchi cha Katolika ali khanda.

Tsiku lina mu 1925, bambo analandira buku la Zeze wa Mulungu la m’Chijeremani. Atawerenga bukulo sanakayike kuti apeza choonadi. Iwo analembera kalata ofalitsa bukulo ndipo anawathandiza kupezana ndi a Mboni za Yehova. Nthawi yomweyo, bambo anayamba kulalikira choonadi chimene anachipezacho. Mayi sanasangalale nazo zimenezi. Ankakonda kunena kuti: “Ine sindingakuletseni kuchita chilichonse chimene mukufuna, komano zomacheza ndi a Mboni ndiye ayi.” Iwo ankalankhula zimenezi ndi mawu okopa mu Chijeremani. Ngakhale zinali choncho, bambo anali atasankha kale zochita, moti mu 1927 anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

Zitatero, agogo anga akuchikazi anayamba kuuza mayi anga kuti athetse banjalo. Ponena za bambo, tsiku lina kumwambo wa Misa wansembe anachenjeza anthu kuti: “Musamale naye Danner chifukwa ndi mneneri wonyenga.” Atabwera kutchalitchiko, agogo anawagenda bambo anga ndi mphika wa maluwa. Iwo anaponya mphikawu ali m’chipinda chapamwamba ndipo unafikira paphewa moti pang’onong’ono ukanafikira pamutu. Zimenezi zinapangitsa mayi kuyamba kuganiza kuti: ‘Chipembedzo chimenechi si chabwino ayi chifukwa chikupangitsa munthu kufuna kupha mnzake.’ Motero, iwo anayamba kuwerenga mabuku a Mboni za Yehova. Pasanapite nthawi, anazindikira kuti apeza choonadi ndipo anabatizidwa m’chaka cha 1929.

Makolo anga anayesetsa kundithandiza ine ndi mkulu wanga kuti timudziwe bwino Yehova. Ankatiwerengera nkhani za m’Baibulo n’kumatiuza kuti tifotokoze chifukwa chimene anthu otchulidwa m’nkhanizo anachitira zimene tawerengazo. Pa nthawi imeneyi bambo analolera kuti asamagwire ntchito usiku ngakhale kuti izi zinachititsa kuti tisauke. Iwo anachita zimenezi kuti azipeza nthawi yopita kumisonkhano, kukalalikira ndiponso kuphunzira ndi ana awofe.

Zizindikiro Zosonyeza Kuti Zinthu Zivuta

Makolo anga ankakonda kuchereza oyang’anira madera ndi anthu otumikira pa Beteli ochokera ku Switzerland ndi France. Anthu amenewa ankatiuza mavuto amene abale athu ankakumana nawo ku Germany, m’dera limene linali kufupi ndi kwathu. Achipani cha Nazi ankatsekera Mboni za Yehova kundende zozunzirako anthu ndipo ankawalanda ana awo.

Ine ndi mkulu wanga Helen tinali okonzeka kukumana ndi mavuto. Makolo athu anatiphunzitsa kuloweza malemba amene angatithandize. Iwo ankanena kuti: “Mukathedwa nzeru muzikumbukira lemba la Miyambo 3:5, 6. Mukakumana ndi mayesero kusukulu muzikumbukira lemba la 1 Akorinto 10:13. Ngati atakusiyanitsani ndi makolo anufe, muzikumbukira lemba la Miyambo 18:10.” Ndinaloweza Salmo 23 ndi 91 ndipo sindinkakayika kuti Yehova azinditeteza nthawi zonse.

Mu 1940, boma la Germany linalanda dera la Alsace-Lorraine ndipo linkafuna kuti munthu aliyense wamkulu alowe chipani chawo cha Nazi. Bambo atakana, apolisi anawaopseza kuti awatsekera m’ndende. Mayi anakana kusoka mayunifolomu a asilikali motero apolisi anawaopsezanso kuti awatsekera m’ndende.

Zinali zovuta kuti ndizipita kusukulu panthawi imeneyi. Tsiku lililonse tisanayambe kuphunzira tinkafunika kupempherera Hitler. Tinkafunikanso kunena kuti, “Hitler ndi mpulumutsi wathu” komanso kuyimba nyimbo yafuko titakweza dzanja lamanja. M’malo mongondiletsa kulambira Hitler, makolo anga anandithandiza kuti chikumbumtima changa chizinditsogolera kuchita zinthu zoyenera. Choncho ndekha ndinasankha kuti ndisamanene nawo mawu akuti “Hitler ndi mpulumutsi wathu.” Aphunzitsi ankandimenya ndipo ankanena kuti andichotsa sukulu. Ndili ndi zaka 7, tsiku lina anandiimika pamaso pa aphunzitsi athu onse 12. Iwo anandikakamiza kuchita sawatcha ya Hitler. Komabe ndi thandizo la Yehova ndinalimba mtima ndipo sindinalole.

Mphunzitsi wina anayamba kundinyengerera. Iye anandiuza kuti ndine mwana wabwino ndipo amandikonda kwambiri moti sangasangalale kuti ndichotsedwe sukulu. Iye anati: “Usachite kuvutika kutambasula dzanja lako, ungolikweza pang’ono basi. Ndipo usachite kunena mawu oti ‘Hitler ndi mpulumutsi wathu,’ ungogwedeza milomo yako n’kuyerekeza ngati wanena.”

Nditawauza mayi zimene aphunzitsi ankachitazi, anandikumbutsa nkhani ya m’Baibulo ya Aheberi atatu achinyamata amene anauzidwa kuti alambire fano limene linaimikidwa ndi mfumu ya ku Babulo. Ndiyeno anandifunsa kuti: “Kodi iwo anauzidwa kuti atani?” Ndinayankha kuti: “Anauzidwa kuti aligwadire.” Kenako mayiwo anati: “Ndiyeno pa nthawi imene iwo ankafunika kuti alambire fanolo, akanati awerame n’kumamanga zingwe za nsapato zawo akanachita bwino? Ndiyeno pa nkhaniyi sankha wekha, zimene ukuona kuti n’zolondola.” Mofanana ndi Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, inenso ndinasankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova yekha basi.​—Dan. 3:1, 13-18

Kangapo konse, aphunzitsi anandichotsa sukulu ndipo anandiuza kuti andisiyanitsa ndi makolo anga. Ndinali ndi nkhawa zedi koma makolo anga ankandilimbikitsa nthawi zonse. Ndikamapita ku sukulu amayi ankapemphera nane. Iwo ankapempha Yehova kuti anditeteze. Ndinkadziwa kuti Yehova andithandiza kuti ndikhalebe wolimba ndiponso kuti ndisasiye choonadi. (2 Akor. 4:7) Bambo ankandiuza kuti zinthu zikavuta kwambiri kusukulu ndisamaope kupita kunyumba. Iwo ankati: “Ife timakukonda kwambiri ndipo ndiwe mwana wathu zivute zitani. Nkhani yagona pakati pa iwe ndi Yehova.” Mawu amenewo ankandilimbikitsa kuti ndizifunabe kukhala wokhulupirika.​—Yobu 27:5.

Nthawi zambiri apolisi ankabwera kunyumba kwathu kudzafufuza ngati tili ndi mabuku a Mboni ndiponso kudzafunsa mafunso makolo anga. Ankawatenga amayi mwina kwa maola angapo. Iwo ankapitanso kuntchito kwa bambo ndi kwa mkulu wanga kukawatenga. Ndikamachokera kusukulu, sindinkadziwa ngati mayi ndikawapeze ali kunyumba. Nthawi zambiri, amayi amene tinkakhala nawo pafupi ankandiuza kuti: “Mayi ako atengedwa.” Ndikamva zimenezo ndinkabisala m’nyumba n’kumadzifunsa kuti, ‘Pano si akuwazunza amenewo? Kaya ndidzawaonanso kaya?’

Kuthamangitsidwa M’dziko

Pa January 28, 1943, apolisi anatidzutsa cha m’ma 3:30 m’mawa. Anatiuza kuti satithamangitsa m’dzikolo ngati makolo anga, mkulu wanga ndi ineyo tilowe m’chipani cha Nazi. Anatipatsa maola atatu kuti tikonzekere. Amayi anali atakonzeka kale ndipo anali atalongedza kale zovala komanso Baibulo m’zikwama zathu. Choncho tinagwiritsa ntchito nthawi imeneyi kupemphera komanso kulimbikitsana. Bambo anatikumbutsa kuti palibe chimene chingathe “kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu.”​—Aroma 8:35-39.

Monga ananenera, apolisi aja anabweranso. Ndimakumbukirabe zimene zinachitika tikunyamuka. Mlongo wina wachikulire dzina lake Anglade, anaima poteropo potsanzikana nafe, uku misozi ikulengeza m’maso mwake. Apolisiwo anatitengera kusiteshoni ya sitima yotchedwa Metz. Patatha masiku atatu, tinafika kundende ya Kochlowice yomwe inali mbali ya ndende ya Auschwitz m’dziko la Poland. Titakhala miyezi iwiri kumeneko, anatisamutsira kundende ya Gliwice, yomwe poyamba inali malo okhala masisitere. Achipani cha Nazi anatiuza kuti tikasainira chikalata chonena kuti tasiya chikhulupiriro chathu, atitulutsa ndipo atibwezera katundu wathu. Bambo ndi mayi anakana ndipo asilikaliwo anati: “Muiwale zoti mudzatuluka muno.”

M’mwezi wa June anatitumiza ku Swietochlowice. Kumeneku ndinayamba kudwala mutu womwe umandivutabe mpaka pano. Komanso mu zala zanga munatuluka tizilonda ndipo dokotala wina anandichotsa zikhadabo moti ndinamva kupweteka kwambiri chifukwa anachita izi popanda mankhwala oletsa ululu. Mwamwayi, anandipatsa ntchito yomakagula zakudya za asilikali kunyumba ina yophikira buledi. Kumeneko, mayi wina ankandipatsa chakudya.

Pa nthawiyi, banja lathu ankalisiyanitsa ndi akaidi ena. Mu October 1943, anatitumiza kundende ya Ząbkowice. Tinkagona m’mabedi osanjikizana m’chipinda chinachake, limodzi ndi anthu ena 60, omwe anali amuna, akazi ndi ana. Asilikali ankachita kuonetsetsa kuti chakudya chimene ankatipatsa chikhale choti munthu wabwinobwino sangadye.

Ngakhale kuti tinkakumana ndi mavuto onsewa, sitinataye mtima. Tinali titawerenga m’magazini a Nsanja ya Olonda kuti nkhondo ikadzatha padzakhala ntchito yaikulu yolalikira. Choncho tinkamvetsa chifukwa chake tikuvutika ndiponso tinkadziwa kuti mavuto athu ndi akanthawi.

Titamva kuti asilikali a mayiko amene ankamenyana ndi boma la Germany akuyandikira tinadziwa kuti a Nazi akugonja. Chakumayambiriro kwa 1945, asilikali a Nazi anaganiza zothawa pandende yathu. Motero, pa February 19, anatiuza kuti tiyende nawo ulendo wapansi wa makilomita 240. Patatha milungu inayi, tinafika ku Steinfels m’dziko la Germany. Kumeneku, asilikali anatilowetsa mumgodi ndipo anzathu ambiri anaganiza kuti tifera momwemo. Koma tsiku lomwelo, adani awo anafika, ndipo asilikaliwo anathawa n’kutisiya. Apa m’pamene tinapulumukira.

Kukwaniritsa Zolinga Zanga

Patatha zaka pafupifupi ziwiri ndi theka, pa May 5, 1945, tinafika kwathu ku Yutz tili bii, komanso zovala zathu zinali nsabwe zokhazokha. Zovala zimenezi tinali titazivala kwa miyezi itatu osasintha, choncho tinangoziwotcha zovalazo. Ndimakumbukira mayi anga akutiuza kuti: “Lero ndi tsiku losaiwalika pamoyo wanu. Ngakhale kuti tilibe chilichonse, ndiponso tavala zovala zobwereka, tonsefe tabwerako tili okhulupirika, sitinagonje.”

Tili ku Switzerland, panatha miyezi itatu kuti thupi langa libwerere mwakale ndipo kenako ndinayambiranso sukulu. Pa nthawiyi, sindinkaopanso kuchotsedwa sukulu. Tinkatha kukumana ndi abale athu auzimu ndiponso tinkalalikira poyera. Pa August 28, 1947, ndili ndi zaka 13, bambo anga anandibatiza mumtsinje wa Moselle. Ndinali nditadzipereka kale kwa Yehova zaka zingapo m’mbuyomo ndipo ichi chinali chizindikiro cha kudzipereka kumeneko. Ndinkafuna kuyamba upainiya nthawi yomweyo koma bambo anga anandiuza kuti ndiphunzire kaye ntchito ina. Choncho ndinaphunzira ntchito yosoka zovala. Mu 1951, ndili ndi zaka 17, ndinavomerezedwa kukhala mpainiya ndipo ananditumiza m’dera la Thionville.

Chaka chomwecho ndinapita kumsonkhano wa ku Paris ndipo ndinalemba kalata yofunsira utumiki waumishonale. Ndinali wamng’ono, koma m’bale Nathan Knorr anandiuza kuti asunga kaye kalatayo. Mu June 1952, ndinalandira kalata yondiitana kuti ndikalowe nawo kalasi ya 21 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo ku South Lansing, m’boma la New York, ku United States.

Zochitika Tili Kusukulu ya Gileadi Komanso Titachokako

Ndinali wosangalala kwambiri kupita kusukulu ya Gileadi ngakhale kuti sukuluyi inali m’Chingelezi. Koma vuto langa lalikulu linali lakuti mwachibadwa ndimavutika kulankhula pagulu, ngakhale m’chinenero changa. Komabe, alangizi a sukuluyi ankandithandiza mwachikondi. Chifukwa choti ndinali wamanyazi, m’bale wina ankandinena moseka kuti ndinkamwetulira mwa Teokalase.

Pa July 19, 1953, tinachita mwambo womaliza maphunziro a Gileadi ku Yankee Stadium, ku New York. Ineyo ndi Ida Candusso anatitumiza ku Paris. Pambuyo pake Ida anadzakwatiwa ndi m’bale Seignobos. Kulalikira kwa anthu olemera a ku Paris kunali kovuta kwambiri, komabe ndinkatha kuphunzira Baibulo ndi anthu ambiri odzichepetsa. Ida atakwatiwa, anachoka mu 1956 n’kupita ku Africa koma ine ndinatsalabe ku Paris.

Mu 1960, ndinakwatiwa ndi m’bale Vichy, yemwe ankatumikira pa Beteli ndipo anatitumiza kuti tikachite upainiya wapadera ku Chaumont. Patatha zaka zisanu, ndinayamba kudwala chifuwa cha TB ndipo ndinasiya kuchita upainiya. Izi zinandikhumudwitsa kwambiri chifukwa kuyambira ndili wamng’ono cholinga changa chinali kuchita utumiki wa nthawi zonse ndipo ndinalibe maganizo osiya. Patapita nthawi, mwamuna wanga anandisiya n’kukakwatira mkazi wina. Abale ndi alongo anga anandithandiza kwambiri pa zaka zovuta zimenezi. Ndipo Yehova anapitirizabe kundisenzera katundu wanga.​—Sal. 68:19.

Panopa ndikukhala ku Louvier, m’chigawo cha Normandy pafupi ndi ofesi ya nthambi ya France. Ngakhale kuti ndine wodwaladwala, ndimasangalala kuona kuti Yehova wakhala akundithandiza pa moyo wanga. Makolo anga anandilera bwino ndipo izi zimandithandiza kuti ndizikhala munthu wosakonda kudandauladandaula. Iwo anandiphunzitsa kuti Yehova alikodi, angathe kukhala bwenzi langa lapamtima, ndingathe kulankhula naye ndipo angathe kuyankha mapemphero anga. Moti ndimadzifunsa kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?”​—Sal. 116:12.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Ndimasangalala kuona kuti Yehova wakhala akundithandiza pa moyo wanga”

[Chithunzi patsamba 5]

Ndili ndi zaka 6, nditatenga chikwama chomwe munali chovala chodzitetezera ku mpweya woipa

[Chithunzi patsamba 5]

Ndili pantchito yapadera yolalikira limodzi ndi apainiya ndi amishonale ku Luxembourg. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 16

[Chithunzi patsamba 5]

Ndili ndi bambo ndi mayi pamsonkhano wachigawo mu 1953