Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zotheka Kumvetsa Baibulo?

Kodi N’zotheka Kumvetsa Baibulo?

Kodi N’zotheka Kumvetsa Baibulo?

“Lamlungu lililonse, banja lathu linkawerenga Baibulo chifukwa tinkakhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu. Koma ineyo sindinkasangalala nazo kwenikweni chifukwa zambiri zomwe tinkawerengazo sindinkazimvetsa.”​—Anatero Steven, wa ku Britain.

“Ndinayamba kuwerenga Baibulo ndili ndi zaka 17, koma patapita nthawi ndinasiya chifukwa sindinkalimvetsa.”​—Anatero mayi wina wa ku Spain, dzina lake Valvanera.

“Ndinawerengapo Baibulo lonse mpaka kulimaliza chifuwa ndinkaona kuti monga Mkatolika, ndifunika kuliwerenga. Zinanditengera zaka zitatu kuti ndilimalize, koma palibe chimene ndinkamva.”​—Anatero mayi wina wa ku Australia, dzina lake Jo-Anne.

BAIBULO ndi buku lotchuka kwambiri padziko lonse, ndipo likuyenda malonda kwambiri kuposa mabuku ena onse. Anthu ambiri masiku ano ali ndi Baibulo ndipo likupezeka m’zinenero zambiri komanso lafalitsidwa m’zinthu zochuluka monga matepi, ma CD ndi ma DVD. Komabe, ambiri mwa anthu amene ali ndi Baibulo salimvetsa. Kodi inunso zimakuvutani kulimvetsa?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Timvetse Mawu Ake?

Baibulo limati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Mawuwa akusonyeza kuti Yehova Mulungu ndi amene analemba Baibulo. Komano kodi iye amafuna kuti timvetse Mawu ake? Kapena kodi anasankha anthu ochepa okha, monga atsogoleri a zipembedzo ndiponso akatswiri a maphunziro a Baibulo kuti ndi amene afunika kulimvetsa?

Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tione mavesi otsatirawa:

“Lamulo ili ndikuuzani lerolino, silikulakani kulizindikira, kapena silikhala kutali.”​—Deuteronomo 30:11.

“Potsegulira mawu anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.”​—Salmo 119:130.

“Nthawi yomweyo [Yesu] anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera ndi kunena kuti: ‘Atate ndikutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana.’”​—Luka 10:21.

Mavesiwa akusonyezeratu kuti Mulungu amafuna kuti tonse tizimvetsa Mawu ake. Komabe, anthu ambiri amene amafunitsitsa kuti adziwe bwino Baibulo zimawavuta kulimvetsa. Kodi chingawathandize n’chiyani? Nkhani zotsatirazi zikusonyeza mfundo zitatu zimene angatsatire kuti azimvetsa Baibulo.