Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amakonda Anthu Ofatsa

Yehova Amakonda Anthu Ofatsa

Yandikirani Mulungu

Yehova Amakonda Anthu Ofatsa

Numeri 12:1-15

ANTHU amene zikuwayendera bwino m’dzikoli, kawirikawiri amakhala onyada, ansanje ndiponso odzikuza. Koma kodi makhalidwe amenewa amatithandiza kuti tiyandikire kwa Yehova Mulungu? Ayi, chifukwa Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira akhale ofatsa. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha nkhani ya pa Numeri chaputala 12. Nkhaniyi inachitikira m’chipululu cha Sinai, Aisiraeli atatulutsidwa m’dziko la Iguputo.

Miriamu ndi Aroni, anayamba ‘kutsutsana’ ndi Mose, yemwe anali m’bale wawo wamng’ono. (Vesi 1) M’malo mongolankhula ndi Mose, iwo anayamba kutsutsana naye, mwinanso ankadandaula kwa anthu ambirimbiri pamsasapo. Zikuoneka kuti Miriamu ndi amene ankatsogolera zimenezi chifukwa ndi yemwe watchulidwa koyamba m’nkhaniyi. Chifukwa choyamba chimene iwo ankadandaulira, chinali chakuti Mose anakwatira mkazi wachikusi. Mwina Miriamu ankachita nsanje kuti mkaziyo, yemwe sanali wachiisiraeli, azipatsidwa ulemu kwambiri kuposa iye.

Panali chifukwa chinanso chimene iwo ankadandaulira. Miriamu ndi Aroni ankakonda kunena kuti: “Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga?” (Vesi 2) Mwina cholinga chawo podandaula chinali kufuna udindo ndiponso kutchuka.

Mose sanayankhe chilichonse koma zikuoneka kuti anapirira. Zimenezi zikutsimikizira mfundo ya m’Baibulo yakuti iye anali munthu “wofatsa woposa anthu onse” padziko lapansi. * (Vesi 3) Mose sanafunikire kuwafotokozera chifukwa chake Yehova ankamugwiritsa ntchito. Yehova anamva zimene anthuwo ankanena ndipo anawayankha m’malo mwa Mose.

Yehova anaona kuti anthuwo sakudandaula Mose, koma akudandaula Iye chifukwa ndi amene anasankha Mose. Podzudzula anthu odandaulawo, Mulungu anawakumbutsa kuti iye anali paubwenzi wapadera ndi Mose. Iye anati: “Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa.” Kenako, Yehova anafunsa Miriamu ndi Aroni kuti: “Munalekeranji kuwopa kutsutsana naye . . . Mose?” (Vesi 8) Chifukwa chotsutsana ndi Mose, anthuwo anapalamula mlandu wotsutsana ndi Mulungu. Ndipo anayenera kulangidwa chifukwa cha kupanda ulemu kwawo.

Miriamu, yemwe akuoneka kuti ndi amene ankatsogolera potsutsana ndi Mose, analangidwa ndi khate. Nthawi yomweyo Aroni anachonderera Mose kuti apempherere Miriamu. Tangoganizani: Kuti Miriamu akhalenso bwino zinadalira kuti Mose, yemwe ankamunyoza uja amuthandize. Modzichepetsa, Mose anachita zimene anapemphedwazo. Apano, Mose anayankhula koyamba m’nkhaniyi popempherera mchemwali wakeyo. Miriamu anachira, komabe anachita manyazi kwambiri chifukwa anachotsedwa pamsasapo n’kuikidwa kwayekha kwa masiku 7.

Nkhaniyi ikutithandiza kudziwa makhalidwe amene Yehova amakonda ndiponso amene amadana nawo. Choncho, ngati tikufuna kuyandikira kwa Mulungu, tiyesetse kuchotseratu khalidwe lililonse limene tingakhale nalo losonyeza kuti ndife onyada, ansanje ndiponso odzikuza. Yehova amakonda anthu ofatsa. Ndipo iye akulonjeza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11; Yakobe 4:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kufatsa ndi khalidwe lofunika kwambiri limene limathandiza munthu kupirira ndiponso kuleza mtima, popanda kusunga chakukhosi, akamachitiridwa zinthu mopanda chilungamo.