Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi alembi omwe ankatsutsa zimene Yesu ankaphunzitsa anali ndani?

Pa utumiki wake, Yesu ankakumana ndi alembi ku Yerusalemu, m’matauni ang’onoang’ono ndi m’midzi. M’madera a kunja kwa Yerusalemu komanso a kunja kwa dziko la Palesitina komwe kunali Ayuda, anthu amenewa anali odziwa Chilamulo ndipo ankagwira ntchito m’boma, mwina yolemba makalata kapena yoweruza milandu.​—Maliko 2:6; 9:14; Luka 5:17-21.

Ku Yerusalemu, alembi ankagwira ntchito mogwirizana kwambiri ndi boma la Ayuda. (Mateyo 16:21) Buku lina limati ntchito ya alembi kumeneku inali “yothandiza ansembe pankhani yoweruza milandu, ndiponso kulimbikitsa miyambo ndi malamulo achiyuda komanso kuthandiza ntchito za Bungwe Lalikulu la Ayuda.” (The Anchor Bible Dictionary) Popeza kuti alembiwa anali aphunzitsi otchuka a Chilamulo, ena mwa iwo anali m’Bungwe Lalikulu la Ayuda kapena kuti m’khoti lalikulu la Ayuda. Iwo ankagwira ntchito limodzi ndi ansembe aakulu ndiponso Afarisi.

Zikuoneka kuti nthawi zambiri alembi ankakonda kutsutsa zimene Yesu ankaphunzitsa. Komabe, ena sankamutsutsa. Mwachitsanzo, mlembi wina anauza Yesu kuti: “Ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” Ndipo panthawi ina Yesu anauza mlembi wina kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.”​—Mateyo 8:19; Maliko 12:28-34.

Kodi kudzozedwa kunkatanthauza chiyani?

Kale ku Middle East, munthu ankadzozedwa mafuta m’mutu posonyeza kuti ndi wofunika kwambiri komanso posonyeza kuti walandiridwa bwino. Nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mafuta a maolivi osakaniza ndi zinthu zina zonunkhiritsa. Ndiponso Aheberi ankadzoza kapena kuthira mafuta pamutu pa munthu amene wasankhidwa paudindo winawake wapadera. Mwachitsanzo, Aroni anadzozedwa atasankhidwa kukhala mkulu wa ansembe. (Levitiko 8:12) Komanso ponena za mfumu Davide, Baibulo limati: “Samueli anatenga nyanga ya mafuta, nam’dzoza . . . ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli.”​—1 Samueli 16:13.

M’Chiheberi, mawu omwe amawagwiritsa ntchito ponena za kudzoza kotereku ndi ma·shachʹ, ndipo mawu akuti ma·shiʹach kapena kuti Mesiya anachokera ku mawu amenewa. Ndipo m’Chigiriki, mawu omwe amagwiritsidwa ntchito ponena za kudzoza kotereku ndi khriʹo, ndipo mawu akuti khri·stosʹ kapena kuti Khristu anachokera ku mawu amenewa. Choncho, Aroni ngakhalenso Davide angatchedwe kuti mesiya kapena kuti wodzozedwa. Nayenso Mose amatchedwa khristu, kapena kuti wodzozedwa, chifukwa chakuti anachita kusankhidwa ndi Mulungu kukhala womuimira.​—Aheberi 11:24-26.

Yesu wa ku Nazarete anachita kusankhidwa ndi Mulungu kuti akhale paudindo waukulu kwambiri. M’malo modzozedwa ndi mafuta enieni, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Mateyo 3:16) Choncho, n’zosadabwitsa kuti Yesu amatchedwa Mesiya ndiponso Khristu chifukwa ndi Wodzozedwa amene anasankhidwa ndi Yehova.​—Luka 4:18.