Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Khristu Anaphunzitsa za Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi?

Kodi Khristu Anaphunzitsa za Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi?

Kodi Khristu Anaphunzitsa za Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi?

“[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.”​—CHIV. 21:4.

1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Ayuda ambiri a m’nthawi ya Yesu anali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi?

MNYAMATA wina wachuma ndiponso wotchuka anathamangira Yesu, ndipo anagwada pamaso pake n’kumufunsa kuti: “Mphunzitsi wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” (Maliko 10:17) Mnyamatayu anali kufunsa za zimene angachite kuti adzapeze moyo wosatha. Koma kodi iye ankafuna kudzakhala ndi moyo wosatha kuti? Monga tinakambirana m’nkhani yapita, zaka mazana ambiri izi zisanachitike, Mulungu anapereka kwa Ayuda chiyembekezo cha kuuka kwa akufa ndiponso cha moyo wosatha padziko lapansi. Ayuda ambiri a m’nthawi ya Yesu anali ndi chiyembekezo chimenechi.

2 Zikuoneka kuti Marita, bwenzi la Yesu, ankaganiza za kuuka kwa akufa padziko lapansi pamene ananena zokhudza mlongo wake amene anali atamwalira kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” (Yoh. 11:24) N’zoona kuti Asaduki pa nthawiyo sankakhulupirira kuti akufa adzauka. (Maliko 12:18) Komabe, George Foot Moore analemba m’buku lake kuti: “Zolemba . . . za m’zaka zapakati pa [200 ndi 1 B.C.E.] zimasonyeza kuti anthu ankakhulupirira kuti pa nthawi inayake m’tsogolo, anthu amene anamwalira m’mibadwo ya m’mbuyo adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.” (Judaism in the First Centuries of the Christian Era) Choncho munthu wachuma amene anafunsa Yesu uja ankafuna kupeza moyo wosatha padziko lapansi.

3. Kodi m’nkhani ino tikambirana mafunso ati?

3 Masiku ano, zipembedzo zambiri ndiponso akatswiri a Baibulo ambiri amanena kuti Khristu sanaphunzitse za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi. Anthu ambiri amayembekezera kuti akamwalira, adzapita kudziko la mizimu. Choncho akamawerenga Malemba Achigiriki Achikristu n’kupeza mawu akuti “moyo wosatha,” ambiri amaganiza kuti mawuwa amanena za moyo wakumwamba. Koma kodi zimenezi n’zoona? Kodi Yesu anatanthauza chiyani pamene analankhula za moyo wosatha? Kodi ophunzira ake ankakhulupirira chiyani? Kodi Malemba Achigiriki Achikristu amaphunzitsa za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi?

Moyo Wosatha “Panthawi ya Kukonzanso Zinthu”

4. Kodi n’chiyani chidzachitika “panthawi ya kukonzanso zinthu”?

4 Baibulo limaphunzitsa kuti Akhristu odzozedwa adzaukitsidwa kupita kumwamba ndipo adzalamulira dziko lapansi. (Luka 12:32; Chiv. 5:9, 10; 14:1-3) Koma sikuti nthawi iliyonse imene Yesu ankalankhula za moyo wosatha, ankaganiza za gulu lokhalo. Taganizirani zimene iye anauza ophunzira ake ataona kuti mnyamata wachuma uja wachoka ali wachisoni pokana zoti asiye chuma chake chonse ndi kukhala wotsatira wa Khristu. (Werengani Mateyo 19:28, 29.) Yesu anauza atumwi ake kuti iwo adzakhala m’gulu la olamulira monga mafumu ndi kuweruza “mafuko 12 a Isiraeli,” kutanthauza anthu onse amene sali m’gulu lokalamulira kumwambali. (1 Akor. 6:2) Ananenanso kuti “aliyense” amene amamutsatira adzapeza mphoto. Anthu amenewanso “adzapeza moyo wosatha,” ndipo zonsezi zidzachitika “panthawi ya kukonzanso zinthu.”

5. Kodi mawu akuti “panthawi ya kukonzanso zinthu” amatanthauza chiyani?

5 Kodi Yesu anatanthauza chiyani ponena kuti “nthawi ya kukonzanso zinthu”? Mawu amenewa anamasuliridwa kuti “dziko latsopano” mu Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono. Baibulo lina linamasulira kuti, “nthawi imene zinthu zonse zidzapangidwa kukhala zatsopano.” (The Jerusalem Bible) Popeza kuti Yesu anatchula mawu amenewa popanda kufotokozera, ayenera kuti ankanena za chiyembekezo chimene Ayuda anali nacho kwa zaka mazana ambiri. Chiyembekezocho chinali chakuti kudzakhala kukonzanso zinthu padziko lapansi, kuti zikhale ngati mmene zinalili m’munda wa Edene, Adamu ndi Hava asanachimwe. Kukonzanso zinthu kumeneku kudzakwaniritsa lonjezo la Mulungu lakuti ‘adzalenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.’​—Yes. 65:17.

6. Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi likutiphunzitsa chiyani za chiyembekezo cha moyo wosatha?

6 Yesu analankhulanso za moyo wosatha pofotokoza za mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Mat. 24:1-3) Iye anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake, pamenepo adzakhala pa mpando wake wachifumu waulemerero. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye, ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.” Anthu amene adzaweruzidwa kuti ndi oipa “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama kumoyo wosatha.” Anthu “olungama” amene adzalandira moyo wosatha ndi amene mokhulupirika amathandiza “abale” a Khristu odzozedwa ndi mzimu. (Mat. 25:31-34, 40, 41, 45, 46) Popeza kuti odzozedwa amasankhidwa kuti akalamulire mu Ufumu wakumwamba, anthu “olungama” ayenera kukhala nzika zapadziko lapansi za Ufumuwo. Baibulo linalosera kuti Mfumu yosankhidwa ndi Yehova idzakhala ndi nzika za Ufumu wake kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi. (Sal. 72:8) Nzika zimenezi zidzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.

Kodi Uthenga Wabwino wa Yohane Umati Chiyani?

7, 8. Kodi Yesu anatchula chiyembekezo chiti ndi chiti polankhula ndi Nikodemo?

7 Malinga ndi mabuku a Uthenga Wabwino a Mateyo, Maliko ndi Luka, Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “moyo wosatha” pa zochitika zimene tanena zija. Uthenga Wabwino wa Yohane umatchula mawu a Yesu onena za moyo wosatha ka 17. Tiyeni tikambirane malemba ena amene mawu amenewa amapezekapo, kuti tione zimene Yesu ananena zokhudza chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi.

8 Malinga ndi zimene Yohane analemba, Yesu analankhula koyamba za moyo wosatha kwa Mfarisi, dzina lake Nikodemo. Yesu anauza Nikodemo kuti: “Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu.” Anthu amene adzalowa mu Ufumu wakumwamba ayenera “kubadwanso.” (Yoh. 3:3-5) Koma Yesu sanalekere pomwepo. Iye ananenanso za chiyembekezo chimene anthu onse padziko lapansi angakhale nacho. (Werengani Yohane 3:16.) Choncho Yesu ananena za chiyembekezo cha moyo wosatha kumwamba cha otsatira ake odzozedwa ndiponso cha moyo wosatha padziko lapansi cha anthu ena onse.

9. Kodi Yesu anauza mayi wachisamariya za chiyembekezo chiti?

9 Atachoka ku Yerusalemu komwe analankhula ndi Nikodemo, Yesu analowera chakumpoto ku Galileya. Paulendo wakewu, anakumana ndi mayi wina pafupi ndi mzinda wotchedwa Sukari, pachitsime cha Yakobo ku Samariya. Yesu anamuuza mayiyo kuti: “Amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu mpang’ono pomwe, ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otumphuka mwa iye opatsa moyo wosatha.” (Yoh. 4:5, 6, 14) Madzi amenewa amaimira zinthu zimene Mulungu wapereka pofuna kuthandiza anthu onse kupeza moyo wosatha. Anthu amenewa akuphatikizapo amene adzakhale padziko lapansi. Buku la Chivumbulutso, limafotokoza kuti Mulungu akunena kuti: “Aliyense wakumva ludzu, ndidzam’patsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.” (Chiv. 21:5, 6; 22:17) Motero moyo wosatha umene Yesu anauza mayi wachisamariya uja, ndi wa odzozedwa odzalowa Ufumu, ndiponso wa anthu okhulupirira amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi.

10. Atachiritsa munthu padziwe la Betesida, kodi Yesu ananena zotani zokhudza moyo wosatha kwa atsogoleri a chipembedzo omwe ankamutsutsa?

10 Chaka chotsatira, Yesu anapitanso ku Yerusalemu. Ali kumeneko, anachiritsa munthu wina padziwe lotchedwa Betesida. Yesu anauza Ayuda omwe ankamutsutsa chifukwa cha zimene anachitazi kuti: “Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.” Atawauza kuti Atate “wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana,” Yesu anati: “Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira iye amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha.” Kenako ananenanso kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Mwana wa munthu] ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo, amene anachita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” (Yoh. 5:1-9, 19, 22, 24-29) Pamenepa, Yesu ankauza Ayuda omwe anali kumutsutsawo kuti iye anasankhidwa ndi Mulungu kuti akwaniritse chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi chimene Ayudawo anali nacho ndipo adzachita zimenezi mwa kuukitsa akufa.

11. Kodi tikudziwa bwanji kuti mawu a Yesu a pa Yohane 6:48-51 amanenanso za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi?

11 Yesu ali ku Galileya, anthu ambiri omwe ankafuna chakudya chimene iye anawapatsa mozizwitsa, anayamba kumutsatira. Ndipo iye anawauza za mtundu wina wa chakudya chomwe ndi “chakudya chopatsa moyo.” (Werengani Yohane 6:40, 48-51.) Yesu anati: “Chakudya chimene ndidzapereka . . . ndicho mnofu wangawu.” Iye anapereka moyo wake m’malo mwa anthu amene adzalamulire naye mu Ufumu kumwamba, komanso “kuti dzikoli lipeze moyo.” Mawu akuti “dzikoli” akutanthauza anthu otheka kuwawombola. “Ngati wina adyako chakudya chimenechi,” kutanthauza kukhulupirira mphamvu yowombola ya nsembe ya Yesu, adzakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Ndithudi, mawu a Yesu ofotokoza za ‘moyo wosatha’ amanenanso za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi mu ulamuliro wa Mesiya chimene Ayuda anali nacho kwa nthawi yaitali.

12. Kodi Yesu ankanena za chiyembekezo chiti pamene anauza anthu amene ankamutsutsa kuti ‘adzapatsa nkhosa zake moyo wosatha’?

12 Kenako pa Chikondwerero cha Kupatula Kachisi ku Yerusalemu, Yesu anauza anthu amene ankamutsutsa kuti: “Koma inu simukhulupirira, chifukwa sindinu nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, ine ndimazidziwa, izonso zimanditsatira. Ndimazipatsa moyo wosatha.” (Yoh. 10:26-28) Kodi pamenepa Yesu ankanena za moyo wakumwamba wokha kapena ankanenanso za moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi? Yesu anali atangolimbikitsa kumene otsatira ake ndi mawu akuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) Komabe ali pachikondwerero chomwechi, Yesu ananenanso kuti: “Nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa.” (Yoh. 10:16) Choncho mawu amene Yesu anauza anthu amene ankamutsutsa aja, amanena za chiyembekezo cha moyo wakumwamba cha “kagulu ka nkhosa” ndiponso chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi cha anthu mamiliyoni ambiri a “nkhosa zina.”

Chiyembekezo Chimene Sichinafunikire Kuchifotokoza

13. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati: “Iwe udzakhala nane m’Paradaiso”?

13 Akumva ululu pamtengo wozunzikirapo, Yesu anapereka umboni wosatsutsika wa chiyembekezo cha anthu. Munthu wochita zoipa amene anapachikidwa pambali pake anati: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Ndipo Yesu anamulonjeza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala nane m’Paradaiso.” (Luka 23:42, 43) Popeza munthu ameneyu anali Myuda, sanafunikire kufotokozeredwa za Paradaiso. Iye ankadziwa za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi latsopano.

14. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti chiyembekezo chopita kumwamba chinali chovuta kwa atumwi kuti achimvetse? (b) Kodi ndi liti pamene otsatira a Yesu anayamba kumvetsa za chiyembekezo chopita kumwamba?

14 Koma zimene Yesu ananena zokhudza chiyembekezo cha kumwamba n’zimene zinafunikira kuzifotokoza. Iye atauza ophunzira ake kuti akupita kumwamba kukawakonzera malo, ophunzirawo sanamvetse zimene ankatanthauza. (Werengani Yohane 14:2-5.) Kenako iye anawauza kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma simungathe kuzimvetsa zonsezo pakali pano. Koma iyeyo akadzafika, mzimu wa choonadi, adzakutsogolerani m’choonadi chonse.” (Yoh. 16:12, 13) Pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., otsatira a Yesu atadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu kuti adzakhale mafumu m’tsogolo, m’pamene anazindikira kuti adzakalamulira kumwamba. (1 Akor. 15:49; Akol. 1:5; 1 Pet. 1:3, 4) Chiyembekezo chokalandira moyo kumwamba chinali mfundo yatsopano, ndipo chinakhala nkhani yaikulu ya m’makalata ouziridwa a Malemba Achigiriki Achikristu. Koma kodi makalata amenewa amatsimikiziranso za chiyembekezo cha anthu cha moyo wosatha padziko lapansi?

Kodi Makalata Ouziridwa Amati Chiyani?

15, 16. Kodi mawu a m’kalata youziridwa yopita kwa Aheberi ndiponso mawu a Petulo amasonyeza motani za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi?

15 M’kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anatchula okhulupirira anzake kuti “abale athu oyera, otenga mbali m’chiitano cha kumwamba.” Koma ananenanso kuti Mulungu anaika “dziko lapansi lokhala anthu likudzalo” pansi pa Yesu. (Aheb. 2:3, 5; 3:1) Motero “dziko lapansi lokhala anthu likudzalo” likuimira dongosolo la zinthu lam’tsogolo la padziko lapansi mu ulamuliro wa Yesu Khristu. Pa nthawi imeneyo Yesu adzakwaniritsa lonjezo la Mulungu lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Sal. 37:29.

16 Mtumwi Petulo anauziridwanso kulemba zokhudza tsogolo la anthu. Iye analemba kuti: “Miyamba imene ilipo tsopano limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Pet. 3:7) Kodi n’chiyani chidzalowe m’malo mwa miyamba imene ilipo tsopano, yomwe ndi maboma omwe alipowa? Nanga n’chiyani chomwe chidzalowe m’malo mwa anthu oipa? (Werengani 2 Petulo 3:13.) Mabomawa adzalowedwa m’malo ndi “miyamba yatsopano,” yomwe ndi Ufumu wa Mesiya wa Mulungu. Ndipo anthu oipa adzalowedwa m’malo ndi “dziko lapansi latsopano,” lomwe ndi gulu la anthu olungama omwe amalambira Mulungu woona.

17. Kodi chiyembekezo cha anthu chafotokozedwa motani pa lemba la Chivumbulutso 21:1-4?

17 Buku lomaliza la m’Baibulo ndi lochititsa chidwi kwambiri chifukwa lili ndi masomphenya osonyeza anthu atakhalanso angwiro. (Werengani Chivumbulutso 21:1-4.) Anthu onse okhulupirira akhala akuyembekezera zimenezi kuyambira kale kwambiri pamene anthu anataya ungwiro m’munda wa Edene. Anthu olungama adzakhala m’Paradaiso kosatha ndipo sadzakalambanso. Chiyembekezo chimenechi n’chozikidwa pa Malemba Achihebri ndiponso Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo chikulimbitsabe chikhulupiriro cha atumiki a Yehova mpaka pano.​—Chiv. 22:1, 2.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Yesu anatanthauza chiyani ponena kuti “nthawi ya kukonzanso zinthu”?

• Kodi Yesu anamuuza Nikodemo zokhudza chiyani?

• Kodi Yesu anamulonjeza chiyani munthu wochita zoipa amene anapachikidwa pambali pake?

• Kodi mawu a m’kalata youziridwa yopita kwa Aheberi ndiponso mawu a Petulo amatsimikizira bwanji za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Anthu onga nkhosa adzalandira moyo wosatha padziko lapansi

[Zithunzi patsamba 10]

Yesu anauza anthu za moyo wosatha