Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’

‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’

‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’

NKHOPE ya munthu ili ndi minofu yoposa 30. Ngati mukufuna kumwetulira, ndi minofu 14 imene imakuthandizani kutero. Ndiye mukuganiza bwanji? Mukanakhala kuti mulibe minofu imeneyi, kodi kulankhula kukanakhala kosangalatsa? Ayi. Kwa anthu osamva, minofu imeneyi simangothandiza kuti kukambirana kukhale kosangalatsa. Akamaigwiritsa ntchito limodzi ndi manja ndi thupi polankhula, imakhala njira yothandiza kwambiri pofotokoza maganizo ndi mfundo zawo. Anthu ambiri satha kumvetsa kuti zimatheka bwanji m’chinenero cha manja kufotokoza bwinobwino mfundo, ngakhalenso mfundo zovuta.

Masiku ano, anthu osamva padziko lonse ayamba kuona nkhope yosangalatsa ndiponso yofotokoza bwino kwambiri maganizo kuposa ya munthu aliyense. Iwo mophiphiritsa ayamba kuona “pamaso pa Ambuye,” kapena kuti nkhope ya Yehova. (Maliro 2:19) Sikuti zimenezi zangochitika. Tikutero chifukwa chakuti kuyambira kale, Yehova wasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu osamva. Iye ankawakonda ngakhale m’nthawi ya mtundu wa Isiraeli kalelo. (Lev. 19:14) Masiku ano, chikondi chake pa anthu osamva chikuonekeranso kwambiri. “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Mwa kuphunzira mpaka kudziwa choonadi chonena za Mulungu molondola, tingati anthu osamva ambiri ayamba kuona nkhope yake. Kodi zimenezi zatheka bwanji popeza anthu amenewa samva? Tisanayankhe funso limeneli, tiyeni tione chifukwa chake chinenero cha manja n’chofunika kwambiri kwa anthu amenewa.

Iwo Amamva ndi Maso

Anthu ambiri ali ndi maganizo olakwika okhudza anthu osamva ndiponso chinenero cha manja. Tiyeni tithandizane kumvetsa zinthu zina zokhudza anthu amenewa. Anthu osamva akhoza kuyendetsa galimoto bwinobwino. Anthu amenewa amavutika kwambiri kumvetsa zinthu mwa kungoyang’ana milomo ya munthu amene akulankhula. Chinenero cha manja n’chosiyana kwambiri ndi zilembo za anthu akhungu, ndipo kulankhula chinenerochi sikungoyerekezera kuchita zimene wina akulankhula. Palibe chinenero cha manja chimodzi chimene chingalankhulidwe padziko lonse. Ndiponso ngakhale kwa anthu amene akukhala m’dziko limodzi, chinenerochi chimasiyana malinga ndi dera limene munthu amakhala.

Kodi anthu osamva amatha kuwerenga? Ngakhale kuti ena amatha, ambiri amavutika kuwerenga. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti zilembo zimakhala za zinenero zimene anthu amalankhula. Taganizirani mmene mwana amene amamva amaphunzirira chinenero. Iye akangobadwa, amakhala ndi anthu amene amalankhula chinenero chawo. Posakhalitsa, iye amayamba kulumikiza mawu n’kumapanga ziganizo. Amachita zimenezi mwachibadwa akamamva anthu akulankhula. Choncho ana amene amamva akayamba kuwerenga, amangofunikira kuphunzira kuti zilembo zakuda zikuimira mawu amene iwo akuwadziwa kale.

Ndiye tayerekezerani kuti muli kudziko lachilendo m’chipinda cha magalasi chomwe simukutha kumva chilichonse. Simunamvepo anthu akulankhula chinenero cha kumeneko. Tsiku lililonse anthu amabwera ndi kuyesa kulankhula nanu kudzera pagalasipo. Koma simumva zimene amanena. Mumangoona milomo yawo ikugwedera. Atazindikira kuti simukumva zimene akunena, iwo akukulemberani zomwe akunenazo papepala, kenako ndikukusonyezani kudzera pagalasipo. Akuchita zimenezi chifukwa akuganiza kuti tsopano mutha kumva zimene akunena. Kodi mukuganiza kuti mukhoza kudziwa zimene akunena? Ayi ndithu, simungathe ngakhale pang’ono. Tikutero chifukwa chakuti zilembozo ndi za chinenero chimene simunamvepo. Umutu ndi mmene zinthu zilili ndi anthu ambiri amene samva.

Choncho njira yabwino imene anthu osamva amalankhulirana ndi chinenero cha manja. Munthu amagwiritsa ntchito manja, nkhope ndi thupi lake lonse kuti afotokoze mfundo zinazake. Amapanga zizindikiro motsatira malamulo a chinenero cha manja. Umu ndi mmene anthu amalankhulira m’chinenero cha manja ndipo wina akaona, amamva zimene munthuyo akunena.

Njira iliyonse imene munthu wosamva amayendetsera manja, thupi ndi nkhope yake, imakhala ndi tanthauzo lake. Akamagwiritsa ntchito nkhope yake, sikuti amangofuna kusangalatsa anthu. Zimenezi ndi zofunika kwambiri pa chinenero cha manja. Mwachitsanzo, akamafunsa funso atakweza nsidze, amakhala akufunsa funso longothandiza anthu kuganizira kapena loti angoyankha kuti Eee kapena Ayi. Koma ngati akufunsa funso atatsitsa nsidze, funsolo lingakhale lakuti ndani, chiyani, kuti, liti, chifukwa kapena motani. Nthawi zina, kayendetsedwe ka milomo kamasonyeza kukula kwa chinthu. Kamasonyezanso mphamvu kapena khama limene munthu amakhala nalo pochita zinthu. Njira imene munthu wosamva amagwedezera mutu, mapewa, masaya ndiponso mmene amaphethirira, imathandizira kufotokoza bwinobwino mbali zonse za mfundo imene akunena.

Zimenezi zimathandiza kuti munthu amene akuona amvetse ndiponso asangalale ndi zimene zikunenedwazo. Mwa kugwiritsa ntchito njira imeneyi, anthu osamva amene amadziwa chinenero cha manja sasowa mawu ofotokozera nkhani iliyonse. Amatha kufotokoza ndakatulo kapena mfundo zovuta, nkhani zachikondi kapena zoseketsa, ndiponso zinthu zooneka kapena zosaoneka.

Mabuku a Chinenero cha Manja Akuthandiza Kwambiri

Munthu wosamva akamaphunzitsidwa za Yehova m’chinenero cha manja, tingati amamva uthengawo ndipo ‘amakhulupirira’ Mulungu, yemwe ndi Mwini uthengawo. N’chifukwa chake Mboni za Yehova zikuyesetsa kulalikira kwa anthu osamva padziko lonse ndi kukonza mabuku owathandiza. (Aroma 10:14) Panopa, pali magulu 58 padziko lonse omasulira mabuku m’chinenero cha manja, ndipo mabuku a chinenero cha manja amene ali pa DVD alipo m’zinenero za manja 40. Kodi ntchito yokonza mabuku onsewa ikuthandizadi?

Makolo a Jeremy onse awiri samva. Iye anati: “Ndikukumbukira tsiku lina pamene bambo anali kuchipinda kwa maola ochuluka, akuyesetsa kuwerenga kuti amvetse ndime zochepa za m’nkhani ina ya mu Nsanja ya Olonda. Mwadzidzidzi, anangotuluka n’kuyamba kulankhula ndi manja mosangalala kuti: ‘Ndamva zimene akutanthauza!’ Kenako anandifotokozera tanthauzo la zimene anawerengazo. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 12 zokha. Nditawerenga mwamsanga ndimezo, ndinawauza ndi manja kuti: ‘Bambo, si zimene akutanthauza ayi. Akunena kuti . . . ’ Iwo anatukula mkono, kundiletsa kulankhula ndipo anabwerera kuchipinda kuti akadzipezere okha zimene ndimezo zinali kutanthauza. Anabwerera kuchipinda ali ndi nkhope yokhumudwa kwambiri, ndipo sindiiwala zimenezi. Sindiiwalanso kuti zinali zopatsa chidwi kuwaona akubwerera kuchipinda. Koma panopa chifukwa chakuti ali ndi mabuku a chinenero cha manja pa DVD, amatha kumvetsa mosavuta zimene akuphunzira. Zimandikhudza kwambiri iwo akamafotokoza ndi nkhope yowala mmene amakondera Yehova.”

Taganiziraninso zimene zinachitika ku Chile. Banja lina la Mboni linalankhula ndi mtsikana wina wosamva, dzina lake Jessenia. Mayi ake anawaloleza kuti amuonetse Jessenia DVD ya Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo m’Chinenero cha Manja cha ku Chile. Iwo anati: “Jessenia atayamba kuonera, anayamba kuseka ndipo kenako anayamba kulira. Mayi ake atamufunsa chimene ankalira, iye anati akusangalala kwambiri ndi zimene akuonera. Mayi akewo anazindikira kuti iye akutha kumva zonse zimene zinali pa DVD.”

Kumudzi wina ku Venezuela, kuli mayi wina amene samva. Iye anali ndi mwana mmodzi komanso anali woyembekezera. Iye ndi mwamuna wake, ankaona kuti sangathe kusamalira mwana wina chifukwa anali osauka. Choncho, anali kuganiza zochotsa mimbayo. Mboni za Yehova zinafika pakhomopo, ndipo ngakhale sizinali kudziwa nkhaniyi, zinasonyeza banjalo phunziro 12 m’kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? pavidiyo ya m’Chinenero cha Manja cha ku Venezuela. Phunziro limeneli limafotokoza maganizo a Mulungu pa nkhani ya kuchotsa mimba ndi kupha munthu. Ulendo wina, mkazi uja anauza Mboni zija kuti akuyamikira kwambiri chifukwa chophunzira mutuwo. Iye anati zawathandiza kuti asachotse mimba. Mwaonatu, moyo wa mwana unatetezeka chifukwa cha buku la chinenero cha manja pa DVD.

Lorraine, yemwe ndi mlongo wosamva, anafotokoza kuti: “Kuphunzira Baibulo kunali kovuta kwambiri. Panali mfundo zina zomwe sindinkazimvetsa ndipo chifukwa cha zimenezi, Baibulo ndinkangolidziwa mwa apo ndi apo. Koma choonadi cha m’Baibulo chitayamba kupezeka m’chinenero cha manja, ndinayamba kumvetsa mfundo zomwe poyamba sindinkazimvetsa.” George, amene samva ndipo wakhala Mboni kwa zaka 38, anati: “Kunena zoona, ukamatha kumvetsa zinthu pawekha, zimakuthandiza kudzisungira ulemu ndipo umasiya kudzikayikira. Ndikuona kuti ma DVD a chinenero cha manja andithandiza kwambiri kupita patsogolo mwauzimu.”

“Misonkhano ya M’chinenero Changa”

Kuwonjezera pa mabuku a chinenero cha manja, Mboni za Yehova zakhazikitsa mipingo kumene misonkhano yonse imachitika m’chinenero cha manja. Panopa pali mipingo yoposa 1,100 ya chinenero cha manja padziko lonse. M’mipingo imeneyi, nkhani zimakambidwa m’chinenero cha anthu osamva, ndipo munthu amaphunzira choonadi cha m’Baibulo malinga ndi mmene amaganizira m’chinenero chake. Mfundo za choonadi zimafotokozedwa m’njira yolemekeza chikhalidwe chake ndiponso momuganizira.

Kodi kukhazikitsa mipingo ya chinenero cha manja kwathandiza? Taganizirani za Cyril. Iye anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova mu 1955. Kwa zaka zambiri, iye ankayesetsa kuwerenga mabuku ndiponso sanali kuphonya misonkhano. Masiku ena, kumsonkhanoko kunkakhala omasulira m’chinenero cha manja, koma masiku ena, kunkakhala kulibe. Kukakhala kulibe omasulira, iye ankadalira Mboni zinzake zimene zinkayesetsa kumuthandiza pomulembera zimene zinali kunenedwa kupulatifomu. Mu 1989, iye atakhala Mboni kwa zaka 34, m’pamene mpingo woyamba wa chinenero cha manja unakhazikitsidwa ku New York City, ku United States. Kodi Cyril anamva bwanji kukhala mumpingo umenewo? Iye anati: “Zinali ngati kuti ndatuluka m’dzenje lamdima kupita pamalo owala. Sindinayembekezere kuti kungakhale misonkhano ya m’chinenero changa.”

Kumipingo ya Mboni za Yehova ya chinenero cha manja, anthu osamva amasonkhana kuti aphunzire za Mulungu ndi kumulambira. Kumeneko, anthu a Mulungu amapeza mabwenzi ndi chilimbikitso. M’dzikoli, limene anthu osamva satha kumvana bwinobwino ndi ena ndiponso amasalidwa, mipingo imeneyi ndi malo kumene iwo amacheza ndi kukambirana ndi anthu momasuka. M’mipingo imeneyi, anthu osamva amaphunzira, kupita patsogolo ndi kuyamba kuchita zambiri potumikira Yehova. Mboni zambiri zosamva zikutha kukhala alaliki a nthawi zonse. Zina zasamukira m’mayiko ena kuti zikathandize anthu osamva kuphunzira za Yehova. Abale osamva amaphunzira n’kukhala aphunzitsi aluso, anthu adongosolo ndiponso abusa abwino. Ambiri amayenereranso udindo wosiyanasiyana mumpingo.

Ku United States, kuli mipingo ya chinenero cha manja yoposa 100 ndi timagulu pafupifupi 80. Ku Brazil, kuli mipingo ya chinenerochi pafupifupi 300 ndi timagulu toposa 400. Ku Mexico, mipingo ya chinenerochi iliko pafupifupi 300. Ndipo ku Russia, kuli mipingo ya chinenerochi yoposa 30 ndi timagulu 113. Zimenezi ndi zitsanzo zochepa chabe zosonyeza kuti zinthu zikupita patsogolo m’chinenero cha manja padziko lonse.

Mboni za Yehova zimakhalanso ndi misonkhano yadera ndi yachigawo m’chinenero cha manja. Chaka chatha, misonkhano yachigawo yoposa 120 inachitika padziko lonse m’zinenero za manja. Misonkhano imeneyi imathandiza Mboni zosamva kuona kuti zili m’gulu lapadziko lonse la abale achikhristu amene akulandira chakudya chauzimu pa nthawi yake.

Leonard samva ndipo wakhala wa Mboni za Yehova kwa zaka zoposa 25. Iye anati: “Kuyambira kale, ndakhala ndikudziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona. Ngakhale zili choncho, sindinkamvetsa chifukwa chake iye amalola anthu kuvutika. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zina ndikaganizira za iye, ankandipsetsa mtima. Koma nkhani ina pamsonkhano wachigawo wa chinenero cha manja inandithandiza kumvetsa zifukwa zake. Nkhaniyo itatha, mkazi wanga anandigunyuza ndi kundifunsa kuti: ‘Mwakhutira tsopano?’ Sindikanachitira mwina koma kuvomera ndi mtima wonse. Ndikuthokoza kuti sindinasiye Yehova kwa zaka 25 zonsezi. Ndakhala ndikumukonda kwambiri. Kungoti sindinkamumvetsetsa. Koma ndamumvetsa tsopano.”

Akuthokoza ndi Mtima Wonse

Kodi anthu osamva akamaphunzira za Yehova, amaona chiyani pankhope yake? Amaona chikondi, chifundo, chilungamo, kukhulupirika, kukoma mtima ndi makhalidwe enanso ambiri.

Mboni zonse zosamva padziko lapansi zikuona nkhope ya Yehova ndipo zipitiriza kuiona bwinobwino nkhopeyo. Chifukwa chokonda anthu osamva, ‘Yehova wawalitsa nkhope yake pa iwo.’ (Num. 6:25) Anthu amenewa akuthokoza kwambiri kuti afika pomudziwa Yehova.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Padziko lonse pali mipingo ya chinenero cha manja yoposa 1,100

[Zithunzi patsamba 26]

Nkhope ya Yehova yawawalira kwambiri anthu osamva