Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Maganizo a Khristu

Khalani ndi Maganizo a Khristu

Khalani ndi Maganizo a Khristu

‘Khalani ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.’​—AROMA 15:5.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kutengera maganizo a Khristu?

YESU KHRISTU anati: “Bwerani kwa ine . . . Phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu.” (Mat. 11:28, 29) Mawu okhazika mtima pansi amenewa, amasonyeza kuti Yesu anali ndi mtima wachikondi kwambiri. Palibe munthu aliyense amene angakhale chitsanzo chabwino ngati Yesu. Ngakhale kuti anali Mwana wamphamvu wa Mulungu, Yesu anali wokoma mtima ndiponso woganizira anthu, makamaka ovutika.

2. Kodi tikambirana makhalidwe ati amene Yesu anali nawo?

2 M’nkhani ino, ndiponso ziwiri zotsatira, tikambirana mmene tingakhalire ndi “maganizo a Khristu” ndi mmene tingamawasonyezere pa moyo wathu. (1 Akor. 2:16) Tikambirana makamaka makhalidwe a Yesu asanu awa: Kufatsa ndi kudzichepetsa, kukoma mtima, kumvera Mulungu, kulimba mtima ndiponso chikondi chake chosalephera.

Phunzirani kwa Khristu Kukhala Ofatsa

3. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji ophunzira ake kukhala odzichepetsa? (b) Kodi Yesu anatani ophunzira ake atafooka?

3 Yesu, yemwe ndi Mwana wangwiro wa Mulungu, analolera kubwera padziko lapansi kudzatumikira anthu opanda ungwiro komanso ochimwa. Ena mwa anthu amenewa anali oti adzamupha. Ngakhale zinali choncho, Yesu sanasiye kukhala wosangalala ndiponso kudziletsa. (1 Pet. 2:21-23) ‘Kuyang’anitsitsa’ chitsanzo cha Yesu kungatithandize ifenso kukhalabe osangalala ndiponso odziletsa pamene anthu ena, chifukwa chopanda ungwiro, achita zinthu zotikhumudwitsa. (Aheb. 12:2) Yesu anauza ophunzira ake kuti alowe pansi pa goli lake limodzi naye ndi kuphunzira kwa iye. (Mat. 11:29) Kodi iwo akanaphunzira chiyani kwa iye? Chinthu chimodzi chimene akanaphunzira n’chakuti Yesu anali wofatsa ndipo ankaleza mtima ndi ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu. Usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi, Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Ilitu linali phunziro losaiwalika pa nkhani ya ‘kudzichepetsa.’ (Werengani Yohane 13:14-17.) Pa nthawi ina Petulo, Yakobe ndi Yohane atalephera ‘kukhala maso,’ Yesu anamvetsa ndi kuwachitira chifundo chifukwa choganizira za kufooka kwawo. Iye anati: “Simoni, zoona ukugona? . . . Amuna inu, khalanitu maso ndi kupemphera, kuti musalowe m’mayesero. Inde, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”​—Maliko 14:32-38.

4, 5. Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji pamene ena achita zinthu zokhumudwitsa?

4 Kodi ife timatani ngati wokhulupirira mnzathu ali wokonda kupikisana, wokwiya msanga kapena wochedwa kutsatira uphungu wa akulu kapena wa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Mat. 24:45-47) Anthu m’dziko la Satanali akatilakwira timamvetsa ndipo timatha kuwakhululukira. Koma zimakhala zovuta kwambiri ngati amene watilakwirayo ali m’bale kapena mlongo. Ngati timafulumira kukwiya ndi zimene ena achita, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizisonyeza kwambiri “maganizo a Khristu”?’ Tisaiwale kuti Yesu sankakhumudwa ndi ophunzira ake ngakhale pamene iwo anasonyeza kufooka mwauzimu.

5 Taganizirani za mtumwi Petulo. Yesu atamuuza kuti atsike m’ngalawa n’kuyenda pamadzi kupita kumene Yesuyo anali, Petulo anayenda kamtunda ndithu. Koma kenako ataona mphepo ya mkuntho, iye anayamba kumira. Kodi Yesu anakwiya n’kunena kuti “Eya, ukhaule kuti utengerepo phunziro”? Ayi sanatero. “Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake nam’gwira dzanja, ndi kumuuza kuti: ‘Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?’” (Mat. 14:28-31) Ngati zingachitike kuti chikhulupiriro cha m’bale wathu chikuoneka ngati chikufooka, kodi tingam’gwire dzanja ndi kum’thandiza kuti chikhulupiriro chake chilimbe? Izitu n’zimene tikuphunzira pa kufatsa kumene Yesu anasonyeza pothandiza Petulo.

6. Kodi Yesu anawaphunzitsa chiyani atumwi ake pa nkhani yofuna malo aulemu?

6 Petulo analinso m’gulu la atumwi amene ankakanganakangana pa nkhani yoti wamkulu ndani. Yakobe ndi Yohane ankafuna kuti mu Ufumu wa Yesu wina adzakhale kudzanja lamanja la Yesu, wina kulamanzere. Petulo ndi atumwi ena atamva zimenezi anakwiya kwambiri. Yesu ankadziwa kuti iwo anatengera khalidwe limeneli kwa anthu a m’dziko limene anakulira. Choncho anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira amitundu amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho pakati panu; koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu, ndipo amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wanu.” Kenako Yesu anatchula chitsanzo cha zimene iye anachita. Iye anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”​—Mat. 20:20-28.

7. Kodi aliyense wa ife angatani kuti athandize kuti mumpingo mukhale mgwirizano?

7 Kuganizira za kudzichepetsa kwa Yesu kungatithandize ‘kukhala ngati wamng’ono’ pakati pa abale athu. (Luka 9:46-48) Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tizigwirizana. Yehova, mofanana ndi atate wa banja lalikulu, amafuna kuti ana ake “akhale pamodzi” mogwirizana. (Sal. 133:1) Yesu anapemphera kwa Atate wake kuti Akhristu onse oona akhale ogwirizana, kuti dziko lidziwe kuti Atate anamutuma iye, ndi kuti Atateyo anawakonda iwo mmene anamukondera iye. (Yoh. 17:23) Motero, kugwirizana kwathu kumathandiza anthu kudziwa kuti ndife otsatira a Khristu. Koma kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuona zolakwa za anzathu ngati mmene Khristu anachitira. Yesu ankakhululukira anthu ndipo anaphunzitsa kuti ifenso tingakhululukidwe kokha ngati timakhululukira anthu ena.​—Werengani Mateyo 6:14, 15.

8. Kodi tingaphunzire chiyani kwa anthu amene akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali?

8 Tingaphunzirenso zambiri mwa kutsanzira chikhulupiriro cha anthu amene akhala akutsanzira Khristu kwa zaka zambiri. Mofanana ndi Yesu, anthu amenewa amamvetsa zolakwa za anthu ena. Iwo aphunzira kuti kusonyeza chifundo ngati mmene Khristu ankachitira, kumathandiza kuti munthu azitha “kunyamula zofooka za osalimba” ndiponso kumalimbikitsa umodzi. Kuwonjezera pamenepo, amadziwanso kuti zimenezi zimathandiza mpingo wonse kukhala ndi maganizo a Khristu. Iwo amafuna kuti Akhristu anzawo akhalenso ndi maganizo ngati omwewa, ndi kulimbikitsa umodzi. Izi n’zimenenso Paulo ankafunira Akhristu a ku Roma. Iye anawalembera kuti: “Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu kuti athe kupirira, achititse nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo, kuti nonse pamodzi, ndi pakamwa pamodzi, mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.” (Aroma 15:1, 5, 6) Zoonadi, kulambira kwathu mogwirizana kumalemekeza Yehova.

9. N’chifukwa chiyani timafunika mzimu woyera kuti titengere chitsanzo cha Yesu?

9 Yesu anasonyeza kuti kukhala “wodzichepetsa” ndi kufatsa, komwe ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu, n’kogwirizana. Choncho kuphatikiza pa kuphunzira chitsanzo cha Yesu, timafunikanso mzimu woyera wa Yehova kuti tithe kutengera bwinobwino chitsanzo cha Yesu. Tiyenera kupempha mzimu woyera wa Mulungu ndiponso kuyesetsa kukhala ndi zipatso za mzimuwo zomwe ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Choncho tikamatsatira khalidwe la Yesu la kudzichepetsa ndi kufatsa, timasangalatsa Atate wathu wa kumwamba, Yehova.

Yesu Ankakomera Mtima Anthu

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wokoma mtima?

10 Kukoma mtima nakonso ndi chipatso cha mzimu woyera. Nthawi zonse Yesu ankakomera mtima anthu. Anthu onse amene anafunafuna Yesu ndi mtima wonse, anaona kuti iye ‘anawalandira bwino.’ (Werengani Luka 9:11.) Kodi tingaphunzire chiyani pa kukoma mtima kumene Yesu ankasonyeza? Munthu wokoma mtima amakhala wochezeka, wofatsa, wachifundo ndiponso wachisomo. Umu ndi mmene Yesu analili. Iye ankamvera anthu chisoni “chifukwa anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.”​—Mat. 9:35, 36.

11, 12. (a) Fotokozani nkhani yosonyeza kuti Yesu ankachitira chifundo anthu. (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani imeneyi?

11 Sikuti Yesu ankangomvera anthu chisoni, iye ankachitapo kanthu kuti awathandize. Taganizirani chitsanzo ichi. Mayi wina anazunzika ndi matenda otaya magazi kwa zaka 12. Mayiyu ankadziwa kuti anali wodetsedwa malinga ndi Chilamulo cha Mose. Iye sakanatha kuchita zilizonse zokhudza kulambira limodzi ndi anthu ena ndipo aliyense wokhudzana naye akanakhalanso wodetsedwa. (Lev. 15:25-27) Komabe khalidwe la Yesu ndiponso zimene ankachitira anthu, zinachititsa mayiyu kukhulupirira kuti Yesu angathe kumuchiritsa, ndipo amuchiritsadi. Mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” Iye analimba mtima n’kuchitadi zimenezo ndipo nthawi yomweyo anazindikira kuti wachira.

12 Yesu anazindikira kuti munthu wina wam’khudza ndipo anayamba kuyang’anayang’ana kuti adziwe amene wamukhudzayo. Mayiyu ayenera kuti anachita mantha kwambiri poganiza kuti adzudzulidwa chifukwa choti waswa Chilamulo. Iye anagwada pansi uku akunjenjemera n’kufotokoza zonse zimene anachita. Kodi Yesu anamukalipira mayi wodwalayu amene anavutika kwambiri? Ayi ndithu. Iye mokoma mtima anati: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.” (Maliko 5:25-34) Mtima wa mayiyu, uyenera kuti unakhala m’malo atamva mawu okoma mtima amenewa.

13. (a) Kodi maganizo a Yesu ankasiyana bwanji ndi a Afarisi? (b) Kodi Yesu ankawaona bwanji ana?

13 Mosiyana ndi Afarisi ouma mtima, Khristu sankagwiritsa ntchito udindo wake mowalemetsa anthu. (Mat. 23:4) Iye mokoma mtima ndiponso moleza mtima, ankaphunzitsa ena njira za Yehova. Yesu ankawakonda ndiponso kuwakomera mtima otsatira ake nthawi zonse. Iye anali bwenzi lawo lapamtima. (Miy. 17:17; Yoh. 15:11-15) Ngakhale ana ankamasuka akakhala ndi Yesu ndipo Yesunso ankamasuka nawo. Iye sankakhala wotanganidwa kwambiri moti n’kulephera kupeza nthawi yocheza ndi ana. Tsiku lina ophunzira ake anasonyeza mtima wodzikonda umene atsogoleri achipembedzo ambiri anali nawo pa nthawiyo. Ophunzirawo analetsa anthu kubweretsa ana awo kwa Yesu kuti awaike manja. Yesu sanasangalale ndi zimene ophunzira ake anachitazi. Iye anawauza kuti: “Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine; musawaletse iyayi, pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa onga amenewa.” Ndiyeno pogwiritsa ntchito anawo, Yesu anawaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa konse mu ufumuwo.”​—Maliko 10:13-15.

14. Kodi ana amapindula motani akamasonyezedwa chikondi?

14 Kodi mukuganiza kuti anawa atakula ankamva bwanji akakumbukira kuti ali ana, Yesu Khristu ‘anawatenga m’manja mwake ndi kuwadalitsa’? (Maliko 10:16) Masiku anonso, ana amene amasonyezedwa chikondi ndi akulu ndiponso anthu ena, akadzakula azidzasangalala akakumbukira zimenezi. Chofunika kwambiri n’chakuti ana amene amasonyezedwa chikondi choterechi mumpingo, amaphunzira kuyambira ali aang’ono kuti anthu a Yehova amatsogozedwa ndi mzimu woyera.

Sonyezani Kukoma Mtima M’dziko Lankhanzali

15. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ndi mzimu wosakomerana mtima womwe wafala masiku ano?

15 Anthu ambiri masiku ano amaona kuti alibe nthawi yoti azikomera anthu ena mtima. Motero, tsiku lililonse anthu a Yehova akakhala kusukulu, kuntchito, paulendo ndiponso mu utumiki, amavutika ndi mzimu wa dzikoli. Tingakhumudwe ndi mzimu wosakomerana mtima womwe wafala, koma sitiyenera kudabwa nawo. Yehova anauzira Paulo kutichenjeza kuti “masiku otsiriza” ovuta ano, Akhristu oona azikumana ndi anthu “odzikonda, . . . opanda chikondi chachibadwa.”​—2 Tim. 3:1-3.

16. Kodi tingatani kuti tilimbikitse khalidwe lokomerana mtima mumpingo ngati Khristu?

16 Komabe mumpingo wachikhristu mumachitika zosiyana kwambiri ndi zimene zikuchitika m’dziko lankhanzali. Aliyense akamatsanzira Yesu, amathandiza kuti mpingo uzikhala malo osangalatsa kukhalamo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Choyamba, tiyenera kudziwa kuti anthu ambiri mumpingo akukumana ndi vuto la matenda kapenanso mavuto ena, ndipo amafunika kuwathandiza ndi kuwalimbikitsa. “M’masiku otsiriza” ano, mavuto amenewa akuwonjezereka kwambiri, komabe si achilendo. M’nthawi za m’Baibulo, Akhristu ankakumananso ndi mavuto otere. Pa nthawiyo Akhristu ankafunika kuthandizidwa, ndipo ndi mmene zililinso masiku ano. Mwachitsanzo, Paulo analimbikitsa Akhristu ‘kulankhula molimbikitsa kwa a mtima wachisoni, kuthandiza ofooka ndi kukhala oleza mtima kwa onse.’ (1 Ates. 5:14) Izi zimafuna kuti tizikomera ena mtima ngati Khristu.

17, 18. Kodi tingakhale okoma mtima ngati Yesu m’njira ziti?

17 Akhristu ali ndi udindo ‘wolandira bwino abale awo’ ndi kuwachitira zinthu ngati mmene Yesu akanachitira. Ayeneranso kusonyeza chikondi chenicheni kwa anthu amene adziwana nawo kwa nthawi yaitali ndiponso amene n’koyamba kukumana nawo. (3 Yoh. 5-8) Yesu sankadikira kuti anthu amupemphe koma ankayesetsa kupeza mpata wosonyezera kukoma mtima. Nafenso tiyenera kuchita zimenezi n’kumatsitsimula anzathu nthawi zonse.​—Yes. 32:2; Mat. 11:28-30.

18 Ife tonse tingasonyeze kukoma mtima mwa kuchita zinthu zosonyeza kuti timaganizira abale athu. Ganizirani njira zimene mungawathandizire ndipo yesetsani kuwathandiza. Paulo akutilimbikitsa kuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake.” Iye akunenanso kuti: “Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Izi zikusonyeza kuti tiyenera kutsanzira Khristu, kuchitira anthu ena zinthu mwachikondi ndi mokoma mtima ndiponso kuphunzira kusonyeza “chikondi chopanda chinyengo.” (2 Akor. 6:6) Pofotokoza chikondi chofanana ndi cha Khristu chimenechi, Paulo anati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza.” (1 Akor. 13:4) Sitiyenera kusungira abale ndi alongo athu chakukhosi koma tiyenera kutsatira malangizo akuti: “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.”​—Aef. 4:32.

19. Kodi tikamakhala okoma mtima ngati Khristu timapeza madalitso otani?

19 Tikamayesetsa nthawi zonse kukhala okoma mtima ngati Khristu, timapeza madalitso ochuluka. Mzimu wa Yehova umagwira bwino ntchito pampingo ndipo izi zimathandiza kuti aliyense mumpingomo azisonyeza zipatso za mzimu. Kuwonjezera pamenepa, tikamatsanzira zimene Yesu ankachita pa moyo wake ndiponso kuthandiza ena kuti azimutsanziranso, Mulungu amakondwera ndi kulambira kwathu kogwirizana ndiponso kosangalatsa. Motero tiyeni tiziyesetsa nthawi zonse kukhala ofatsa ndi okoma mtima ngati Yesu pochita zinthu ndi anthu ena.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa”?

• Kodi Yesu anasonyeza kuti anali wokoma mtima m’njira zotani?

• M’dziko lopanda ungwiroli, kodi tingasonyeze kuti ndife ofatsa ndi okoma mtima ngati Khristu m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi chikhulupiriro cha m’bale wina chikafooka ngati cha Petulo, timam’gwira dzanja?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mungathandize bwanji kuti mpingo ukhale malo osangalatsa amene anthu amasonyezana kukoma mtima