Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zokhudza Moyo wa Banja

Zokhudza Moyo wa Banja

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zokhudza Moyo wa Banja

Kodi anthu okwatirana aziliona motani banja lawo kuti azikhala mosangalala?

Ukwati ndi wopatulika. Yesu atafunsidwa ngati zinali zololeka kuti anthu okwatirana azisudzulana, iye anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi ndi kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. . . . Aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo, kupatulapo ngati am’sudzula chifukwa cha dama.” (Mateyo 19:4-6, 9) Anthu okwatirana akamatsatira malangizo amenewa ndiponso akakhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake, banja lawo limakhala losangalala.

N’chifukwa chiyani kukonda Mulungu kumathandiza kuti banja likhale losangalala?

Yesu ananena kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba.” Nanga kodi lachiwiri kwa lamulo lalikulu kwambirili ndi liti? Yesu anati: “Uzikonda mnansi wako [kuphatikizapo anthu a m’banja mwanu] mmene umadzikondera wekha.” (Mateyo 22:37-39) Choncho, kuti banja lathu lizikhala mosangalala tiyenera kukonda kwambiri Mulungu chifukwa zimenezi zingatithandize kuti tizikondanso anthu ena.

Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti aliyense azisangalatsa mnzake?

Mwamuna akamatsatira chitsanzo cha Yesu, amasangalatsa mkazi wake. Yesu ankakonda kwambiri mpingo, womwe uli ngati mkazi wake. (Aefeso 5:25) Yesu anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira.” (Mateyo 20:28) Iye ankalimbikitsa anthu amene ankawayang’anira, osati kumangowalamula kapena kuwachitira nkhanza. (Mateyo 11:28) Choncho, amuna ayenera kuchita udindo wawo mokoma mtima, zomwe zingapindulitse onse m’banjamo.

Akazi nawonso ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu. Baibulo limati: “Mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” Ndipo limanenanso kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akorinto 11:3) Yesu sankaona kuti anyozeka akamagonjera Mulungu. Iye ankalemekeza kwambiri Atate wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:29) Mkazi amene amagonjera mwamuna wake chifukwa chokonda ndiponso kulemekeza Mulungu, banja lake limasangalala.

Kodi makolo angaphunzire chiyani pa zimene Yesu ankachitira ana?

Yesu ankacheza ndi ana ndipo ankakonda kumva maganizo awo komanso ankazindikira mmene anawo akumvera. Baibulo limati: “Yesu anaitana anawo, nati: ‘Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine.’” (Luka 18:15, 16) Nthawi ina anthu anadzudzula anyamata ena omwe ankatamanda Yesu. Koma Yesu anayamikira anyamatawo ndipo anauza anthu omwe ankawadzudzulawo kuti: “Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa tiana ndi makanda oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”​—Mateyo 21:15, 16.

Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yesu?

Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana kuti azikonda zinthu zauzimu. Panthawi ina ali ndi zaka 12, anapezeka “m’kachisi, atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.” Ndiyeno kodi chinachitika n’chiyani? Baibulo limapitiriza kuti: “Onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri chifukwa cha kumvetsa zinthu kwake ndi mayankho ake.” (Luka 2:42, 46, 47) Komabe, Yesu sankadzikuza chifukwa choti anali ndi nzeru. Koma zinam’pangitsa kuti azilemekeza kwambiri makolo ake. Baibulo limati: “Anapitiriza kuwamvera.”​—Luka 2:51.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 14 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.