Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wokumbutsa Chikale

Ulendo Wokumbutsa Chikale

Kalata Yochokera ku America

Ulendo Wokumbutsa Chikale

TAYEREKEZERANI kuti muli paulendo wokaona mmene makolo anu akale ankakhalira. Ulendowo ungakhale wosangalatsa kwambiri ndipo ifeyo tinayenda ulendo woterowo kuchokera ku Switzerland kupita ku America. Anthu ambiri amaganiza kuti dera lililonse ku America ndi lotukuka kwambiri, koma sizili choncho chifukwa ulendo wathuwu unatikumbutsa mmene makolo athu ankakhalira zaka 200 zapitazo. Tadikirani tikuuzeni mmene tinayendera.

Tinaitanidwa kukacheza kwa miyezi itatu m’dera la Indiana ku America chifukwa choti timalankhula chinenero cha ku Switzerland chosakanikirana ndi Chijeremani. Cholinga chathu chinali choti tikalalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu a mtundu wa Amishi omwe amalankhulanso chinenerochi. M’dera la Indiana muli anthu ambiri a mtunduwu.

Anthu amenewa ndi mbadwa za Anabapatisiti, omwe ndi gulu lachipembedzo lomwe linayamba m’zaka za m’ma 1600. Dzina lawo lakuti Amishi, linachokera ku dzina la mtsogoleri wawo Jacob Amman, yemwe anali wa ku Switzerland. Chifukwa chophunzira Baibulo panthawi imeneyo, anthu oopa Mulungu amenewa anazindikira kuti kubatiza ana akhanda ndiponso kulowa usilikali zinali zosayenera. Zimenezi zinachititsa kuti boma liyambe kuwazunza moti ena anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Anthuwa anapitirizabe kuzunzidwa ndipo zimenezi zinachititsa kuti ena mwa iwo athawire kumadera ena a ku Switzerland komweko ndiponso ku France. Pomafika chapakati pa zaka za m’ma 1800, anthu ambiri anali atathawira ku America ndipo anapitiriza chikhalidwe ndiponso chinenero chawo.

Titapita kukaona anthu achifundo amenewa, anadabwa kwambiri kutiona tikulankhula chinenero chawo. Tamvani mmene tinachezera nawo.

Iwo anatifunsa m’chinenero chawo kuti: “Zikutheka bwanji kuti mukutha kulankhula chinenero chathu?”

Tinayankha kuti: “N’chifukwa choti kwathu ndi ku Switzerland.”

Anthuwo anadabwa n’kunena kuti: “Komatu inu si Amishi.”

Anthu ambiri anatilandira bwino kwambiri ndipo tinazindikira kuti anthu amenewa amakhala moyo wofanana ndi wa anthu akale kwambiri. Mwachitsanzo, nyumba zawo zilibe magetsi, koma amagwiritsa ntchito nyale; iwo alibe magalimoto koma amakwera ngolo. Komanso iwo alibe madzi a m’mipope m’malomwake amatunga madzi pachitsime ndiponso alibe mawailesi oti azimvera nyimbo koma amangoyimba pakamwa.

Koma chimene chinatichititsa chidwi kwambiri n’chakuti anthuwa ndi odzichepetsa. Anthu ambiri a mtundu wa Amishi amakonda kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kukambirana nkhani ndi anthu ena. Zimenezi zinatipatsa mwayi wokambirana nawo chifukwa chake Mulungu analenga anthu ndiponso dziko lapansi.

Pasanapite nthawi, anthu onse m’deralo anamva zoti kwabwera alendo ochokera ku Switzerland. Anthu ambiri anatipempha kuti tikachezere abale awo ndipo tinaterodi. Tinasangalala kwambiri atatipemphanso kuti tikacheze pasukulu ina ya ana a mtundu wa Amishi.

Titafika pasukuluyo, tinagogoda pakhomo la kalasi ina. Posakhalitsa, mphunzitsi anatitsegulira n’kutiuza kuti tonse anayi tilowe m’kalasimo, momwe munali ana okwana 38, omwe ankatiyembekezera mwachidwi. Ana onse apasukuluyo anawasonkhanitsa m’kalasi imodzi ndipo anali a zaka zoyambira 7 mpaka 15. Atsikana anali atavala yunifolomu ya buluu ndi zipewa zoyera, ndipo anyamata anavala mathalauza akuda ndi malaya abuluu. Denga la kalasiyo linali m’mwamba kwambiri. M’kati mwa kalasiyo munali mwa buluu ndipo kutsogolo kunali bolodi. Chapafupi ndi bolodiyo panali mapu a dziko lapansi ndipo chapakona panali mbaula yaukulu ya chitsulo.

Anawo ankatiyang’anitsitsa mwachidwi kwambiri pamene timakhala pamipando kutsogolo kwa kalasiyo. Kenako, mphunzitsi anayamba kuitana anawo, kalasi iliyonse payokha, kuti aone ngati analemba homuweki. Tinachita chidwi kwambiri pamene mphunzitsi ankafunsa anawo mafunso okhudza mapiri a ku Switzerland otchedwa Alps. Mabuku omwe ankagwiritsa ntchito anali akale kwambiri ndipo mphunzitsiyo anatifunsa ngati panopo dziko la Switzerland likuoneka mofanana ndi mmene analifotokozera m’mabukuwo. Ena mwa mafunso amene anatifunsa anali akuti, ‘Kodi anthu amadyetsabe ng’ombe m’mapiri a Alps panthawi ya chilimwe? Kodi mapiriwo amakutidwabe ndi chipale chofewa m’nthawi yozizira?’ Mphunzitsiyo anasangalala kwambiri titamuonetsa zithunzi za mapiri okutidwa ndi chipale chofewa. Zithunzizi zinali zooneka bwino kwambiri poyerekezera ndi zomwe zinali m’mabuku omwe iye amagwiritsa ntchito.

Kenako, mkazi wa mphunzitsiyo, yemwe analinso mphunzitsi, anatifunsa funso limene anthu ambiri anatifunsanso. Iye anati: “Kodi mumatha kuimba mingoli?” Tinamuyankha kuti sititha. Komabe, popeza timadziwa kuti anthu a mtundu wa Amishi amayimba bwino mingoli, tinawapempha kuti atiimbire nyimbo. Iwo anavomera ndipo tinamvetsera mwachidwi pamene anthu onse okwana 40 anaimba nyimbo mogwirizana. Kenako, aphunzitsiwo anauza ana asukuluwo kuti apite panja akapume.

Ndiyeno mkazi wa mphunzitsiyo anatipempha kuti timuimbire nyimbo ina iliyonse. Tinavomera popeza timadziwa kuyimba nyimbo zambiri za zachikhalidwe chathu. Ana a sukulu aja atangomva kuti tikuimba nyimbo, onse anathamanga kudzalowa m’kalasimo n’kutizungulira. Tinapitiriza kuimba nyimbozo ndi mtima wonse titaima kutsogolo kwa kalasiyo.

Kenako, banja lina la Amishi, la anthu 12, linatiitana kuti tikadye chakudya chamasana kunyumba kwawo. Titafika, tinapeza kuti patebulo panadzaza ndi zakudya zosiyanasiyana monga mbatata yopota, nyama ya nkhumba, chimanga, buledi, tchizi, ndiwo zamasamba ndiponso tinan’tina monga makeke. Tisanayambe kudya, aliyense anapemphera payekha chamumtima. Tikudya, tinkakambirana za ku Switzerland, kumene kunachokera makolo awo ndiponso anthuwa anatiuza mmene ulimi wawo ukuyendera. Panthawiyi ana ankangonong’onezana n’kumaseka. Anthuwa akamaliza kudya, amapempheranso ndipo chimenechi chimakhala chizindikiro choti ana akhoza kuchoka patebulo, osati kupita kosewera, koma kuti achotse mbale n’kukazitsuka. Ana onse amapatsidwa ntchito zawo, ena kuchotsa mbale, ena kutunga madzi otsukira mbalezo n’kuwatenthetsa ndipo ena kutsuka mbalezo.

Pamene anawo ankatsuka mbalezo, makolo awo anatiuza kuti tipite kuchipinda chochezera. Panalibe mipando ya sofa, koma tinakhala pamipando ya ndalema. Posakhalitsa, iwo anatulutsa Baibulo lakale kwambiri la Chijeremani m’kabati ndipo tinayamba kukambirana nkhani zauzimu. Zimenezi n’zimene mabanja a Amishi amachita akalandira alendo. Tinakambirana mafunso ambiri monga akuti: ‘N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu analenga anthu ndiponso dziko lapansi? Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati ofatsa adzalandira dziko lapansi? Kodi Mulungu amazunzadi anthu oipa powaotcha kumoto? Kodi ndani masiku ano amene akutsatira lamulo la Yesu loti uthenga wabwino ulalikidwe kulikonse kumene kuli anthu?’ Tinasangalala kwambiri kukambirana mafunso amenewa ndi enanso ambiri ndi anthu okonda zinthu zauzimu amenewa pogwiritsa ntchito Baibulo lawo.

Panopa timasangalala kwambiri tikakumbukira ulendo wokumbutsa chikale umenewu. Paulendowu, tinaona zinthu zambiri zosangalatsa. Tikukhulupirira kuti ulendo umenewu ndiponso zimene tinakambirana ndi anthu a mtundu wa Amishi n’chinenero chawo, zinathandiza kuti anthu ambiri atilandire mwansangala komanso kuti adziwe choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.