Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mesiya Ndiye Njira ya Mulungu Yopulumutsira Anthu

Mesiya Ndiye Njira ya Mulungu Yopulumutsira Anthu

Mesiya Ndiye Njira ya Mulungu Yopulumutsira Anthu

“Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”​—1 AKOR. 15:22.

1, 2. (a) Kodi Andireya ndi Filipo anatani atakumana ndi Yesu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti panopa tili ndi umboni wochuluka wakuti Yesu ndiye Mesiya kuposa umboni umene Akhristu oyambirira anali nawo?

ANDIREYA anatsimikizira kuti Yesu wa ku Nazarete anali Wodzozedwa wa Mulungu. Kenako anakauza m’bale wake Petulo kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” Filipo atakhulupirira zimene anauzidwa anapita kukafuna mnzake Natanayeli, ndipo anamuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri, ife tam’peza, iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.”​—Yoh. 1:40, 41, 45.

2 Kodi ndinu wotsimikiza ndi mtima wonse kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa, “Mtumiki Wamkulu wa chipulumutso” wa Yehova? (Aheb. 2:10) Poyerekezera ndi otsatira oyambirira a Yesu, ifeyo masiku ano tili ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu ndiye Mesiya. Kuyambira pa nkhani ya kubadwa kwa Yesu mpaka kuukitsidwa kwake, Mawu a Mulungu amapereka umboni wokwanira wakuti iye ndi Khristu. (Werengani Yohane 20:30, 31.) Baibulo limasonyezanso kuti Yesu adzapitiriza kukwaniritsa udindo wake monga Mesiya ali kumwamba. (1 Akor. 15:22; Yoh. 6:40) Malinga ndi zimene mwaphunzira m’Baibulo, inunso masiku ano munganene kuti ‘mwapeza Mesiya.’ Koma choyamba ganizirani zimene zinachititsa ophunzira oyambirirawo kuti afike ponena kuti anali atapeza Mesiya.

“Chinsinsi Chopatulika” Chokhudza Mesiya Chinaululidwa Pang’onopang’ono

3, 4. (a) Kodi n’chiyani chikanathandiza ophunzira oyambirira a Yesu ‘kupeza Mesiya’? (b) N’chifukwa chiyani mukuona kuti Yesu yekha ndi amene akanakwaniritsa maulosi onse onena za Mesiya?

3 Kodi otsatira a Yesu oyambirira akanadziwa bwanji kuti iye analidi Mesiya? Kudzera mwa aneneri, Yehova anaulula pang’onopang’ono zizindikiro zosonyeza Mesiya amene anali kudzabwerayo. Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo anayerekezera zimenezi ndi kulumikiza zidutswa za chiboliboli. Tiyerekeze kuti anthu ambiri amene sanayambe alankhulanapo, aliyense akubweretsa chidutswa chimodzi m’chipinda chinachake. Ngati atalumikiza zidutswazo n’kupezeka kuti apanga chiboliboli chooneka bwino, mukhoza kudziwiratu kuti pali wina amene anaduladula chibolibolicho n’kupereka zidutswa zakezo kwa anthuwo. Mofanana ndi chidutswa chilichonse cha chibolibolicho, ulosi uliwonse wonena za Mesiya umafotokoza mbali yofunika yokhudza Mesiyayo.

4 Kodi n’zotheka kuti munthu mmodzi yekha angakwaniritse mwangozi maulosi onse onena za Mesiya? Wofufuza wina ananena kuti sizikanatheka kuti munthu mmodzi akwaniritse mwangozi maulosi onse onena za Mesiya. Iye ananena kuti “ndi Yesu yekha m’mbiri yonse amene anatha kukwaniritsa zimenezi.”

5, 6. (a) Kodi Satana adzaweruzidwa bwanji? (b) Kodi Mulungu anaulula bwanji pang’onopang’ono mzere wobadwira wa “mbewu” yolonjezedwa?

5 Zimene maulosi onena za Mesiya amafotokoza, ndi “chinsinsi chopatulika,” chomwe ndi chofunika kwambiri m’chilengedwe chonse. (Akol. 1:26, 27; Gen. 3:15) Zina mwa mfundo za chinsinsi chimenechi ndi zokhudza kuweruzidwa kwa Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “njoka yakale,” amene anachititsa kuti anthu akhale ochimwa ndiponso kuti azifa. (Chiv. 12:9) Kodi chiweruzo chimenechi chidzaperekedwa bwanji? Yehova analosera kuti “mbewu” ya “mkazi” idzaphwanya mutu wa Satana. “Mbewu” yoloseredwa imeneyi idzaphwanya mutu wa njoka, kuchotseratu Satanayu amene anayambitsa kupanduka, matenda ndi imfa. Komabe, zimenezi zisanachitike, Mulungu adzalola Satana kuvulaza chitende cha “mbewu” ya mkazi.

6 Yehova anaulula pang’onopang’ono yemwe adzakhale “mbewu” yolonjezedwa. Mulungu analumbira kwa Abulahamu kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Gen. 22:18) Mose analosera kuti ameneyu adzakhala “mneneri” woposa Mose. (Deut. 18:18, 19) Mulungu anatsimikizira Davide kuti Mesiya adzakhala mbadwa yake ndiponso kuti adzalowa ufumu wa Davide kosatha. Kenako, aneneri anatsimikiziranso zimenezi.​—2 Sam. 7:12, 16; Yer. 23:5, 6.

Umboni Wakuti Yesu Ndiye Mesiya

7. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anachokera kwa “mkazi” wa Mulungu?

7 Mulungu anatumiza Mwana wake, woyamba wa chilengedwe chonse, kuti adzakhale “mbewu” yolonjezedwa. Mwanayo anachokera m’gulu la kumwamba la zolengedwa zauzimu lomwe lili ngati mkazi wa Mulungu. Kuti zimenezi zitheke, panafunika kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu asiye zonse zokhudza moyo wake wakumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwiro padziko lapansi. (Afil. 2:5-7; Yoh. 1:14) Mariya anakhala ndi pakati kudzera mwa mzimu woyera, ndipo izi zinatsimikizira kuti wodzabadwayo “adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”​—Luka 1:35.

8. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi wonena za Mesiya pamene anabatizidwa?

8 Maulosi onena za Mesiya anasonyeza kumene Yesu adzaonekere ndiponso nthawi yake. Yesu anabadwira ku Betelehemu malinga ndi mmene ulosi unanenera. (Mika 5:2) M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Ayuda ankayembekezera zambiri. Chifukwa chakuti ankayembekezera kubwera kwa Mesiya, ena anafunsa za Yohane Mbatizi kuti: “Kodi Khristu uja si ameneyu?” Koma Yohane anayankha kuti: “Wina wamphamvu kuposa ine akubwera.” (Luka 3:15, 16) Chakumapeto kwa chaka cha 29 C.E., Yesu anapita kwa Yohane kuti akabatizidwe ali ndi zaka 30. Mwakutero iye anaonekera monga Mesiya panthawi yake. (Dan. 9:25) Ndipo kenako anayamba utumiki wake womwe unali wosaiwalika ndipo ananena kuti: “Nthawi yoikika yakwaniritsidwa, ndipo ufumu wa Mulungu wayandikira.”​—Maliko 1:14, 15.

9. Ngakhale kuti ophunzira a Yesu sankadziwa mfundo zonse, kodi iwo ankakhulupirira chiyani ndi mtima wonse?

9 Koma anthu anafunikira kusintha maganizo awo pa zimene ankayembekezera. Ngakhale kuti anthu amene anamulandira Yesu monga mfumu anachita bwino, iwo sanamvetse panthawiyo kuti ulamuliro wake udzakhala m’tsogolo ndipo adzalamulira kuchokera kumwamba. (Yoh. 12:12-16; 16:12, 13; Mac. 2:32-36) Yesu atafunsa kuti: “Inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha mosakayika kuti: “Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mat. 16:13-16) Petulo ananenanso mawu ngati amenewa pa nthawi imene anthu ena anakhumudwa chifukwa cha mfundo imene Yesu anaphunzitsa.​—Werengani Yohane 6:68, 69.

Tiyenera Kumvera Mesiya

10. N’chifukwa chiyani Yehova anatsindika kufunika komvera Mwana wake?

10 Pamene Mwana wa Mulungu wobadwa yekha anali kumwamba, anali mngelo wamphamvu. Ndipo atabwera padziko lapansi anadzakhala “nthumwi ya Atate” wake. (Yoh. 16:27, 28) Iye anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.” (Yoh. 7:16) Potsimikiza kuti Yesu ndi Mesiya, Yehova analamula kuti: “Mumvereni iye.” (Luka 9:35) Ndithudi tiyenera kumvera Wosankhidwa ameneyu ndipo zimenezi zimafuna chikhulupiriro ndi ntchito zabwino. Zinthu ziwirizi n’zofunika kuti tikondweretse Mulungu ndiponso kuti tidzapeze moyo wosatha.​—Yoh. 3:16, 35, 36.

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani Ayuda a m’nthawi ya Yesu anakana zakuti iye ndi Mesiya? (b) Kodi ndani anakhulupirira Yesu?

11 Ngakhale kuti panali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu ndi Mesiya, Ayuda ambiri m’nthawi imeneyo anamukana. Iwo anamukana chifukwa chakuti anali ndi maganizo olakwika ponena za Mesiya. Ankaganiza kuti Mesiya adzakhala mtsogoleri wa ndale amene adzawapulumutse ku ulamuliro wopondereza wa Aroma. (Werengani Yohane 12:34.) Chifukwa cha zimenezi, iwo sanavomereze kuti Yesu ndi Mesiya ngakhale kuti anakwaniritsa ulosi wakuti Mesiya adzanyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, adzakhala wachisoni, adzamva zowawa ndipo kenako adzaphedwa. (Yes. 53:3, 5) Ngakhale ophunzira okhulupirika ena a Yesu, anakhumudwa chifukwa chakuti sanawapulumutse ku ulamuliro wa Aroma. Koma iwo anakhalabe okhulupirika ndipo kenako anathandizidwa kumvetsa bwino mfundo zokhudza Mesiya.​—Luka 24:21.

12 Chifukwa china chimene chinachititsa kuti anthu ena akane zakuti Yesu ndi Mesiya, ndi ziphunzitso zake zimene iwo ankaona kuti ndi zovuta kuzitsatira. Mwachitsanzo Yesu anaphunzitsa kuti, kuti munthu alowe mu Ufumu ayenera ‘kudzikana yekha,’ ‘kudya’ thupi ndi magazi ake, “kubadwanso” ndiponso ‘kusakhala mbali ya dziko.’ (Maliko 8:34; Yoh. 3:3; 6:53; 17:14, 16) Anthu odzikuza, olemera ndiponso achinyengo ankaona kuti zinthu zimenezi n’zovuta kuzitsatira. Komabe, Ayuda odzichepetsa anazindikira kuti Yesu ndi Mesiya monga mmene anachitira Asamariya ena omwe ananena kuti: ‘Ndithu munthu uyu ndi mpulumutsi wa dziko.’​—Yoh. 4:25, 26, 41, 42; 7:31.

13. Kodi Yesu anavulazidwa bwanji chitende?

13 Yesu analosera kuti iye adzaweruzidwa ndi ansembe aakulu kenako kupachikidwa ndi Akunja koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa. (Mat. 20:17-19) Atauza Bungwe Lalikulu la Ayuda kuti iye ndi “Khristu Mwana wa Mulungu,” anaweruzidwa kuti wanyoza Mulungu. (Mat. 26:63-66) Pilato anaona kuti Yesu “sanachite kanthu koyenera kumuphera” koma popeza Ayuda anamunamiziranso kuti ndi woukira boma, Pilato “anam’pereka m’manja mwawo kuti chifuniro chawo chichitike.” (Luka 23:13-15, 25) Motero iwo ‘anam’kana’ ndipo anagwirizana zopha “Mtumiki Wamkulu wa moyo,” ngakhale kuti panali umboni wonse wakuti iye anatumidwa ndi Mulungu. (Mac. 3:13-15) Mogwirizana ndi ulosi, Mesiya ‘analikhidwa’ kapena kuti kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo pa Tsiku la Pasika mu 33 C.E. (Dan. 9:26, 27; Mac. 2:22, 23) Mwa kufa imfa yowawa chonchi, iye anavulazidwa “chitende” mogwirizana ndi ulosi wa pa Genesis 3:15.

Chifukwa Chake Mesiya Anafunika Kufa

14, 15. (a) Kodi Yehova analolera kuti Yesu afe pa zifukwa ziwiri ziti? (b) Kodi Yesu anatani ataukitsidwa?

14 Yehova analola kuti Yesu afe pa zifukwa zikuluzikulu ziwiri. Chifukwa choyamba n’chakuti kukhulupirika kwa Yesu mpaka imfa kunakwaniritsa mbali yofunika ya “chinsinsi chopatulika.” Iye anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa ndipo zimenezi zinasonyeza kuti ngakhale atayesedwa kwambiri ndi Satana, munthu wangwiro akhoza kukhalabe ‘wodzipereka kwa Mulungu’ ndi kukhalabe kumbali ya Ulamuliro Wake. (1 Tim. 3:16) Chifukwa chachiwiri n’chakuti mogwirizana ndi mawu a Yesu, ‘Mwana wa munthu anabwera kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’ (Mat. 20:28) “Dipo lolinganiza” limeneli linaperekedwa chifukwa cha uchimo umene mbadwa za Adamu zinatengera kwa makolo awo. Ndipo linachititsa kuti anthu onse amene amakhulupirira Yesu monga njira ya Mulungu yopulumutsira anthu, adzakhale ndi moyo kosatha.​—1 Tim. 2:5, 6.

15 Atakhala m’manda masiku atatu, Khristu anaukitsidwa ndipo anakhala akuonekera kwa ophunzira ake kwa masiku 40. Iye anawatsimikizira kuti anali moyo ndipo anawapatsa malangizo enanso. (Mac. 1:3-5) Kenako anapita kumwamba kukapereka kwa Yehova mtengo wa nsembe yofunika kwambiri ndiponso kukayembekezera nthawi ya kukhalapo kwake monga Mfumu yomwe ndi Mesiya. Koma pa nthawi yoyembekezerayo anali ndi zambiri zoti achite.

Kutsiriza Udindo Wake Monga Mesiya

16, 17. Fotokozani udindo wa Yesu monga Mesiya atapita kumwamba.

16 Kuchokera nthawi imene anaukitsidwa, Yesu wakhala akutsogolera mokhulupirika ntchito zonse za mpingo wachikhristu umene akuulamulira monga Mfumu. (Akol. 1:13) Pa nthawi yoyenera, iye anadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Maulosi a m’Baibulo ndiponso zochitika padziko lapansi zimatsimikizira kuti kukhalapo kwake monga Mfumu kunayamba mu 1914, ndipo nthawi imeneyi inalinso chiyambi cha “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 24:3; Chiv. 11:15) Zimenezi zitangochitika, iye anatsogolera gulu la angelo oyera pogwetsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba.​—Chiv. 12:7-10.

17 Ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa imene Yesu anayamba mu 29 C.E. yatsala pang’ono kutha. Posachedwapa adzaweruza anthu onse amoyo. Kenako iye adzauza anthu onga nkhosa, amene amakhulupirira kuti iye ndiye njira ya Yehova yopulumutsira anthu, kuti ‘adzalowe ufumu umene anakonzera iwo kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.’ (Mat. 25:31-34, 41) Anthu amene amakana zoti Yesu ndi Mfumu, adzawonongedwa pa nthawi imene adzatsogolere magulu ankhondo akumwamba kuti achotse kuipa konse. Ndiyeno Yesu adzamanga Satana limodzi ndi ziwanda zake n’kuwaponya ‘kuphompho’.​—Chiv. 19:11-14; 20:1-3.

18, 19. Kodi Yesu akukwaniritsa chiyani pa udindo wake monga Mesiya, ndipo kodi zotsatira zake ndi zotani kwa anthu omvera?

18 Mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000, Yesu adzakwaniritsa udindo wake wonse monga “Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.” (Yes. 9:6, 7) Anthu onse, kuphatikizapo akufa amene adzawaukitse, adzakhala angwiro chifukwa cha Ulamuliro wake. (Yoh. 5:26-29) Mesiya adzatsogolera anthu odzipereka ku “akasupe a madzi a moyo” ndipo adzathandiza anthu omvera kukhala pamtendere ndi Yehova. (Werengani Chivumbulutso 7:16, 17.) Chiyeso chomaliza chikadzatha, opanduka onse kuphatikizapo Satana ndi ziwanda zake “adzaponyedwa m’nyanja ya moto” ndipo kumeneku kudzakhala kuphwanyiratu mutu wa “njoka.”​—Chiv. 20:10.

19 Yesu akukwaniritsa udindo wake monga Mesiya m’njira yochititsa chidwi kwambiri. M’paradaiso padziko lapansi, anthu opulumutsidwa adzakhala kosatha mosangalala ndiponso adzakhala ndi thanzi labwino. Nthawi imeneyo, dzina loyera la Yehova lidzachotsedwa chitonzo chonse ndipo ulamuliro wake udzatsimikiziridwa kuti ndiwo woyenera m’chilengedwe chonse. Anthu onse amene amamvera Wodzozedwa wa Mulungu akuyembekezera madalitso ochuluka.

Kodi Mwam’peza Mesiya?

20, 21. N’chifukwa chiyani muyenera kuuza ena za Mesiya?

20 Kuyambira mu 1914, takhala tili mu nyengo yomwe m’Chigiriki amati pa·rou·siʹa (parusiya) kapena kuti kukhalapo kwa Khristu. Ngakhale kuti kukhalapo kwake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu n’kosaoneka, umboni wake ukuoneka chifukwa cha kukwaniritsidwa kwa maulosi. (Chiv. 6:2-8) Ngakhale zili choncho, anthu ambiri masiku ano amanyalanyaza umboni wa kukhalapo kwa Mesiya ngati mmene ankachitira Ayuda m’nthawi ya Yesu. Iwonso akufuna mesiya wa ndale kapena winawake amene angawathandize kudzera mwa atsogoleri a ndale. Koma inu munazindikira kuti Yesu akulamulira panopa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kodi simunasangalale mutadziwa zimenezi? Mofanana ndi ophunzira a Yesu oyambirira, inunso munanena kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.”

21 Kodi mukamauza ena choonadi masiku ano, mumafotokoza udindo wa Yesu monga Mesiya? Kuchita zimenezi, kudzakuthandizani kuyamikira kwambiri zimene iye wakuchitirani, zimene akuchita panopa ndiponso zimene adzachita m’tsogolo. Mosakayikira inunso mumauza achibale anu komanso anzanu za Mesiya ngati mmene Andireya ndi Filipo anachitira. Bwanji osawafikiranso mwachangu n’kuwasonyeza kuti Yesu Khristu ndi Mesiya wolonjezedwa ndiponso njira ya Mulungu yopulumutsira anthu?

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi ophunzira a Yesu oyambirira akanadziwa bwanji kuti iye ndi Mesiya?

• Kodi Yesu anafa pa zifukwa ziwiri zofunika kwambiri ziti?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu adzachita pokwaniritsa udindo wake monga Mesiya?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi anthu m’nthawi ya Yesu akanadziwa bwanji kuti iye ndiye Mesiya wolonjezedwa?

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi mukamauza ena choonadi, mumafotokoza udindo wa Yesu monga Mesiya?