Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Otanganidwa Koma Osangalala Potumikira Mulungu

Otanganidwa Koma Osangalala Potumikira Mulungu

Otanganidwa Koma Osangalala Potumikira Mulungu

YEHOVA amafuna kuti inuyo muzisangalala. (Sal. 100:2) Koma mofanana ndi atumiki ake ena, inunso muyenera kuti mumakhala wotanganidwa. N’kutheka kuti mutangodzipereka kumene kwa Mulungu, simunkakhala wotanganidwa kwambiri koma panopa ntchito zakuthupi ndiponso maudindo okhudza utumiki amakupanikizani. Nthawi zina mungamadziimbe mlandu chifukwa cholephera kuchita zinthu zina zimene munakonza kuti muchite. Kodi mungatani kuti muzichita zinthu zonse bwinobwino, n’kumapezabe “chimwemwe cha Yehova?”​—Neh. 8:10.

Tikukhala m’masiku ovuta kwambiri ndipo timapanikizika ndi zinthu zambiri, choncho m’pofunika kumachita zinthu mwadongosolo. Pa nkhani imeneyi, malangizo a mtumwi Paulo angatithandize kwambiri. Iye anati: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, podziwombolera nthawi yoyenerera chifukwa masikuwa ndi oipa.”​—Aef. 5:15, 16.

Mogwirizana ndi malangizo amenewa, kodi mungatani kuti muzipeza nthawi yophunzira Baibulo panokha, yosamalira banja, yolalikira, yogwira ntchito ndiponso yochita zinthu zina zofunika?

Kodi mukukumbukira chimwemwe chimene munali nacho mutangodzipereka kumene kwa Mulungu n’kubatizidwa? Chimwemwe chimenechi chinabwera chifukwa cha kudziwa Yehova ndi zolinga zake. N’kutheka kuti zinakutengerani miyezi ndithu mukuphunzira mwakhama kuti mudziwe Yehova ndiponso kuti mupeze chimwemwe. Koma mpake chifukwa kuphunzira koteroko kunathandiza kuti moyo wanu ukhale wabwino.

Kuti mukhale wosangalala, muyenera kupitirizabe kudya mwauzimu. Ngati zimakuvutani kupeza nthawi yowerenga ndi kuphunzira Baibulo, ndi bwino kuonanso zimene mumachita. Ngakhale mutamaphunzira ndi kusinkhasinkha kwa kanthawi kochepa chabe patsiku, zingakuthandizeni kuyandikira Yehova. Ndipo zimenezi zingawonjezere chimwemwe chanu.

Atumiki a Mulungu ambiri angapeze mpata wochitira zinthu zofunika kwambiri mwa kuchepetsa nthawi imene amachita zinthu zosafunika kwenikweni. Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi nthawi yochuluka bwanji imene ndimawerenga magazini kapena nyuzipepala, kuonera TV, kumvetsera nyimbo kapena kuchita zinthu zina zimene ndimakonda?’ Zinthu zimenezi zingakhale zosangalatsa tikamazichita pa nthawi yoyenera. (1 Tim. 4:8) Ngati mukuona kuti kugawa nthawi kumakuvutani, muyenera kusintha mmene mumachitira zinthu.

Adam ndi wokwatira, ali ndi ana atatu ndiponso ndi mkulu. Iye anafotokoza zimene zimamuthandiza ponena kuti: “Ndimayesetsa kukhala moyo wosalira zambiri. Ndimapewa zinthu zimene zingandiwonongere nthawi. N’zoona kuti ndimapeza nthawi yosangalala koma sindilimbana ndi zambiri ayi.”

Kuganizira mozama ubwino wa zimene mukuchitazo kungakuthandizeni kuyambiranso kusangalala n’kumapitirizabe kuona zinthu moyenera. Mwachitsanzo, Mariusz, yemwe ndi mkulu ndipo ali ndi ana atatu, anati: “Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinasiya kudera nkhawa kwambiri za mtsogolo. Nthawi ndi nthawi ndimakumana ndi mavuto, ndipo ambiri mwa mavutowo ndi Yehova yekha amene amawadziwa. Koma chifukwa cha thandizo lake, ndimaona kuti tsogolo langa ndi losangalatsa.”

Monga nkhani ya Mariusz ikusonyezera, kukhala ndi maganizo abwino pakokha sikuthetseratu nkhawa zonse. Komabe kungakuthandizeni kuti musamadandaule kwambiri ndiponso kuti muzidziwa zochita mukakumana ndi mavuto. Baibulo limati: “Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.” (Miy. 15:15) Ganiziraninso za chikondi chimene Mulungu wakusonyezani kale. Kusinkhasinkha zimenezi kungakuthandizeni kuyamba kukonda kwambiri Mulungu ndi kukhala wosangalala kwambiri.​—Mat. 22:37.

Banja limasangalala likamaika patsogolo Yehova ndiponso zolinga zake. Kukhala ndi makhalidwe achikhristu kumachepetsa mikangano ndipo zimenezi zimathandiza kuti anthu m’banja azikhala ogwirizana ndiponso azilankhulana momasuka. Zikatero aliyense m’banjamo amakhala mwamtendere ndiponso banjalo limakhala logwirizana.​—Sal. 133:1

Kuchitira limodzi zinthu zauzimu m’banja, kumathandizanso kuti banjalo lizikhala losangalala. Mariusz anati: “Ndimaona kuti nthawi imene timachitira zinthu limodzi monga banja, ndi yofunika zedi. Mkazi wanga amandithandiza kwambiri. Nthawi zambiri timakhala limodzi kulikonse monga mu utumiki, poyeretsa malo a msonkhano ndiponso ndikamakakamba nkhani kumipingo ina. Zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri.”

Malemba amati Akhristu ayenera kusamalira mabanja awo mwakuthupi. (1 Tim. 5:8) Koma ngati ntchito imakuwonongerani nthawi ndiponso mphamvu, simungamasangalale potumikira Mulungu. Choncho muyenera kupemphera kwa Yehova za nkhaniyi. (Sal. 55:22) Ena aona kuti ayenera kupeza ntchito ina kuti azitha kuika zinthu za Ufumu wa Mulungu patsogolo. Pali ntchito zina zimene zimamuthera munthu nthawi yochuluka ndiponso mphamvu. Mkhristu sayenera kulola ntchito zoterezi kumulepheretsa kusamalira zinthu zauzimu ngakhale itakhala ya ndalama zambiri bwanji.​—Miy. 22:3.

Zingakhale zothandiza kulemba ubwino ndi kuipa kwa ntchito imene mukuiganizira kapena imene mukugwira panopa. N’zoona kuti aliyense amafuna ntchito yakumtima kwake ndiponso yamalipiro abwino. Komabe, kodi ntchito imene mukugwira panopa imakupatsani mpata wosamalira banja lanu mwauzimu? Ganizirani bwino za ntchitoyo ndipo chitani zinthu zimene zingathandize kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ukhale chinthu choyamba pamoyo wanu.

Ngati zimene ntchito imene mukugwira panopa ikukulepheretsani kukula mwauzimu muyenera kusintha ntchitoyo. Akhristu ambiri alolera kusintha zinthu zazikulu pa moyo wawo n’cholinga chakuti azipeza nthawi yochitira zinthu zauzimu. M’bale wina wa ku Poland anati: “Ndinaona kuti sindikanachitiranso mwina koma kusiya ntchito pakampani imene ndinkagwira chifukwa nthawi zambiri ntchitoyo inkachititsa kuti ndizingoyendayenda. Sindinkakhala ndi nthawi yokwanira yosamalira bwinobwino zosowa zanga zauzimu ndiponso zabanja langa.” Panopa iye akugwira ntchito imene simuthera nthawi ndiponso mphamvu zambiri.

Khalani Osangalala mwa Kuthandiza Ena

Yesu ananena kuti “kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Pali njira zambiri zimene Akhristu angasonyezere kupatsa kotereku. Nthawi zambiri kumwetulira, kugwirana chanza, kapena kuyamikira munthu wina moona mtima chifukwa cha ntchito inayake yotumikira Mulungu imene wachita, kumachititsa kuti inuyo ndiponso munthu winayo musangalale.

Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Lankhulani molimbikitsa kwa a mtima wachisoni, thandizani ofooka.” (1 Ates. 5:14) Anthu amtima wachisoni angamaganize kuti paokha sangathe kupirira mavuto amene akukumana nawo. Inuyo mungathe kuthandiza anthu oterewa. Mwachitsanzo, mukaona kuti m’bale wina sakusangalalanso potumikira Yehova, yesetsani kumulimbikitsa. Kuchita zimenezo kungakulimbikitseninso inuyo. Pali mavuto ena oti anthu sangawathetse. Komabe mungasonyeze chifundo chochokera pansi pa mtima n’kulimbikitsa m’bale wanuyo kudalira kwambiri Yehova kuti amuthandize. Anthu ambiri amene amadalira Yehova, sagwiritsidwa mwala.​—Sal. 27:10; Yes. 59:1.

Njira ina imene ingathandize, ndi kupempha munthu amene akuoneka kuti sakusangalala kuti muyendere naye limodzi mu utumiki. Pamene Yesu anatumiza ophunzira okwana 70 kuti akalalikire, anawatumiza “awiriawiri.” (Luka 10:1) Zimenezi zinawathandiza kuti azilimbikitsana. Kodi nanunso mungagwiritse ntchito njira imeneyi kuti muthandize ena kuyambanso kusangalala?

Masiku ano timakumana ndi mavuto ambiri. Komabe, Paulo anatilimbikitsa kuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani!” (Afil. 4:4) Popeza mumakonda Mulungu, mumamumvera ndiponso mumagwirabe mwachangu ntchito imene wakupatsani, moyo wanu ndi watanthauzo. Zimenezi zimakuthandizani kukhala wachimwemwe. Kuwonjezera pamenepo, Yehova amakuthandizani kulimbana ndi mavuto amene mumakumana nawo.​—Aroma 2:6, 7.

Timakhulupirira kuti dziko latsopano limene Yehova walonjeza, latsala pang’ono kufika. Tidzapeza madalitso ambiri m’dziko limeneli ndipo tidzasangalala kwambiri. (Sal. 37:34) Choncho tikhoza kukhalabe osangalala ndipo sitiyenera kuiwala mmene Yehova akutidalitsira panopa. Motero tingathe ‘kutumikira Yehova ndi chikondwerero.’​—Sal. 100:2.

[Chithunzi patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nthawi zina mungafunike kugawa bwino nthawi kuti muzikhalabe osangalala

ZOSANGALATSA

KUSAMALIRA BANJA ndiponso NTCHITO ZAPANYUMBA

NTCHITO

MISONKHANO YA MPINGO

KUPHUNZIRA BAIBULO PANOKHA

UTUMIKI

[Zithunzi patsamba 10]

Kodi mungathandize ena kuyambiranso kusangalala?