Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila kwa Yeehova?

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila kwa Yeehova?

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila kwa Yeehova?

“Usiku mngelo wa Mulungu wanga, amene ndikum’citlla utumiki wopatulika, anaima pafupi nane.”MAC. 27:23.

1. Kodi anthu amene akukabatizika amakhala atacita kale ciani, motelo tingafunse mafunso ati?

 “PAMAZIKO a nsembe ya Yesu Khristu, kodi mwalapa macimo anu na kudzipatulila kwa Yehova kuti mucite cifunilo cake?” Ili ni limodzi mwa mafunso aŵili omwe anthu amene akukabatizika amayankha pamapeto pa nkhani ya ubatizo. N’cifukwa ciani Akhristu ayenela kudzipatulila kwa Yehova? Kodi kudzipatulila kwa Mulungu kumatithandiza motani? N’cifukwa ciani n’zosatheka kulambila Mulungu movomelezeka popanda kudzipatulila kwa iye? Kuti timvetse mayankho a mafunso amenewa, coyamba tiyeni tione tanthauzo la kudzipatulila.

2.Kodi kudzipatulila kwa Yehova kumatanthauza ciani?

2 Kodi kudzipatulila kwa Mulungu kumatanthauza ciani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione coyamba zimene mtumwi Paulo ananena pofotokoza ubale wake na Mulungu. Polankhula na gulu la anthu amene anali nawo limodzi m’sitima imene inakumana na mkuntho, iye anati, Yehova ni “Mulungu wanga” [“Mulungu amene ndili wake,” Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu]. (Ŵelengani Machitidwe 27:22-24.) Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu onse ni anthu a Yehova. Koma dziko lonse “lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Akhristu amakhala a Yehova, pamene adzipatulila moyenelela m’pemphelo. Kudzipatulila kumeneku, ni lumbilo limene Mkhristu amalipanga yekha ndipo kenako amabatizika m’madzi.

3. Kodi ubatizo wa Yesu unaimila ciani ndipo kodi otsatila ake amam’tsanzila bwanji?

3 Yesu anatipatsa citsanzo posankha yekha kucita cifunilo ca Mulungu. Iye anabadwa ali wodzipatulila kale kwa Mulungu cifukwa anabadwila mu mtundu wa Isiraeli womwe unali wodzipatulila kwa Mulungu malinga na Cilamulo. Komabe mwa kubatizika, Yesu anafuna kucitanso zinthu zina zowonjezela pamenepo. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti iye anati: “Taonani! Ndabwela . . . kudzacita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.” (Aheb. 10:7; Luka 3:21) Motelo, ubatizo wa Yesu unaimila kuti iye waonekela kwa Mulungu Atate wake kuti acite cifunilo Cake. Otsatila ake amam’tsanzila pocitanso cimodzi-modzi. Komabe kwa iwo, ubatizo wa m’madzi umasonyeza kwa anthu kuti anadzipatulila okha kwa Mulungu m’pemphelo.

Mmene Kudzipatulila Kumatithandizila

4. Kodi ubwenzi wa Davide na Yonatani umatiphunzitsa ciani pa nkhani ya kufunika kwa pangano?

4 Kudzipatulila kwa Mulungu si nkhani yamasewela ayi. Limeneli si lonjezo wamba. Koma kodi kudzipatulila kumatithandiza motani? Tiyeni tiyelekezele zimenezi na zimene zimacititsa kuti anthu akhale na ubwenzi wolimba. Kuti munthu ukhale na mnzako wa ponda apa m’pondepo, pamafunika kuti nawenso uzicitapo kanthu. Paubwenzi wotelo mumakhulupililana kwambili ndipo mumakhala okonzeka kuthandizana m’njila zosiyana-siyana. M’Baibo muli zitsanzo za mabwenzi amene anali kugwilizana kwambili. Mwacitsanzo, Davide na Yonatani anafika pocita pangano la ubwenzi wawo. (Ŵelengani 1 Samueli 17:57; 18:1 3.) Ngakhale kuti zotelezi sizicitikacitika, munthu ukamadziŵa kuti mnzakoyo angasunge malonjezo amene mungapangane, ubwenzi wanu umakhala wolimba.—Miy. 17:17; 18:24.

5. Kodi kapolo anali kutani kuti azikhalabe na mbuye wake wabwino mpaka kale-kale?

5 Cilamulo cimene Mulungu anapeleka kwa Aisiraeli cinafotokozanso njila ina imene pangano linali kuthandizila anthu. Ngati kapolo amene mbuye wake anali wabwino akufuna kuti azikhalabe naye, anali kutha kucita pangano na mbuye wakeyo kuti adzam’gwilila nchito mpaka kale-kale. Cilamuloci cinati: “Mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweluza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am’boole khutu lake ndi lisungulu; ndipo iye azim’gwilila nchito masiku onse.”—Eks. 21:5, 6.

6,7. (a)Kodi mapangano amathandiza bwanji anthu? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza ciani pa nkhani ya ubwenzi wathu na Yehova?

6 Okwatilana amafunika kuti azikhulupilika kwambili ku malonjezo amene anapanga. Pangano la mu ukwati silili ngati pangano la bizinesi, cifukwa nkhani yaikulu imakhala pa munthuyo. Anthu aŵili amene amakhala limodzi popanda pangano la ukwati, ubwenzi wawo sukhala wolimba ndipo ana awo sakhala otetezeka. Koma amene anakwatilana ndipo amakhulupilika m’banja, amakhala na zifukwa za m’Malemba zowacititsa kuti aziyesetsa kuthetsa mavuto awo mwacikondi.—Mat. 19:5, 6; 1 Akor. 13:7, 8; Aheb. 13:4.

7 M’nthawi za m’Baibo anthu anali kucita mapangano pankhani za malonda kapena polembana nchito ndipo zimenezi zinali zothandiza. (Mat. 20:1, 2, 8) Kucita zimenezi n’kothandizanso masiku ano. Mwacitsanzo, zimakhala bwino kulembelana pangano tisanayambe kupanga bizinesi na munthu wina kapena tisanayambe nchito pakampani. Ndiyeno ngati pangano limathandiza pa ubwenzi, ukwati, ndiponso pa nchito, kuli bwanji na ubwenzi wanu na Yehova? Tsopano tiyeni tione mmene anthu anapindulila cifukwa codzipatulila kwa Yehova Mulungu komanso mmene kudzipatulila kumeneku kumasiyanilana kwambili na malonjezo ena.

Aisiraeli Anapindula Cifukwa Codzipatulila kwa Mulungu

8. Kodi kudzipatulila kwa Aisiraeli kunali na tanthauzo lotani?

8 Mtundu wa Isiraeli wonse unadzipatulila kwa Yehova pamene unalumbila kwa ye. Yehova anasonkhanitsa mtunduwo pafupi na Phili la Sinai ndipo anati: “Ngati mudzamvela mawu anga ndithu, ndi kusunga cipangano canga, ndidzakuyesani cuma canga capadela koposa mitundu yonse ya anthu.” Anthuwo anavomeleza kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita.” (Eks. 19:4-8) Kudzipatulila kwa Aisiraeli kunali na tanthauzo lina lalikulu kuposa lonjezo loti adzakhala okhulupilika kwa iye. Kunatanthauza kuti iwo anali anthu a Yehova ndipo Yehovayo anali kuwaona kuti ni ‘cuma cake capadela.’

9. Kodi Aisiraeli anapindula motani cifukwa codzipatulila kwa Mulungu?

9 Aisiraeli anapindula cifukwa cokhala anthu a Yehova. Iye anali wokhulupilika kwa iwo ndipo anali kuwasamalila ngati mmene kholo limasamalila mwana wake. Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabele, kuti iye sangacitile cifundo mwana wom’bala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine siningaiwale iwe.” (Yes. 49:15) Yehova anali kuwalangiza kudzela m’Cilamulo, kuwalimbikitsa pogwilitsa nchito aneneli, na kuwateteza pogwilitsa nchito angelo. Wamasalmo wina analemba kuti: “Aonetsa mawu ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweluzo ake kwa Israyeli. Sanatelo nawo anthu a mtundu wina.” (Sal. 147:19, 20; Ŵelengani Salmo 34:7, 19; 48:14.) Yehova amasamalilanso anthu amene amadzipatulila kwa iye masiku ano ngati mmene anali kucitila na mtundu wake kalelo.

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kudzipatulila kwa Mulungu?

10,11. Kodi anthufe timabadwila m’banja la Mulungu? Fotokozani.

10 Anthu ena akamaganizila za kudzipatulila kwa Mulungu ndiponso kubatizika amadzifunsa kuti, ‘Kodi sindingathe kumalambila Mulungu popanda kudzipatulila kwa iye?’ Zimenezi n’zosatheka. Kuti timvetse cifukwa cake, tiyeni tiganizile mmene Mulungu amationela palipano. Tisaiwale kuti chimo la Adamu linacititsa kuti tonse tibadwile kunja kwa banja la Mulungu. (Aroma 3:23; 5:12) Conco, kudzipatulila n’kofunika kwambili kuti Mulungu atilandile m’banja lake la zolengedwa za kumwamba na dziko lapansi. Tiyeni tione cifukwa cake tikutelo.

11 Palibe bambo aliyense amene angabeleke mwana wangwilo monga mmene Mulungu anafunila paciyambi. (1 Tim. 6:19) Sitibadwa tili ana a Mulungu cifukwa coti kucimwa kwa anthu oyambilila kunacititsa kuti anthu onse asakhalenso ana a Mulungu, yemwe ni Tate wacikondi ndiponso Mlengi. (Yelekezelani na Deuteronomo 32:5.) Kuyambila nthawi imeneyo, anthu onse akhala ali kunja kwa banja la Yehova la zolengedwa za kumwamba na dziko lapansi, ndipo ni otalikilana na Mulungu.

12. (a)Kodi anthu opanda ungwilo ayenela kutani kuti akhale m’banja la Mulungu? (b) Kodi ni zinthu ziti zimene tiyenela kucita tisanabatizike?

12 Komabe, tingathe kupempha Mulungu patokha kuti tikhale m’banja la atumiki ake. a Kodi zimenezi zingatheke bwanji popeza ndife anthu ocimwa? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzela mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Tikamabatizika, timapempha Mulungu kuti atipatse cikumbumtima cabwino kuti tikhale ovomelezeka kwa iye. (1 Pet. 3:21) Koma pali zinthu zina zimene tiyenela kucita tisanabatizike. Tiyenela kudziŵa Mulungu, kuyamba kum’khulupilila, kulapa macimo athu ndiponso kusintha njila zathu. (Yoh. 17:3; Mac. 3:19; Aheb. 11:6) Palinso cinthu cina cimene tiyenela kucita tisanalandilidwe m’banja la Mulungu. Kodi cinthu cake n’ciani?

13. N’cifukwa ciani m’pomveka kuti munthu amene akufuna kulandilidwa m’banja la atumiki a Mulungu ayenela coyamba kulonjeza kuti akudzipatulila kwa iye?

13 Kuti munthu ayandikile kwa Mulungu n’kulandilidwa m’banja la atumiki ake, ayenela kucita pangano na Yehova. Kuti timvetse mfundoyi, tayelekezani kuti bambo wina wacifundo akufuna kutenga mwana wamasiye kuti azimulela m’banja lake. Bamboyo ni waulemu wake ndipo amadziŵika kuti ni munthu wabwino. Komabe asanamutenge, bamboyo akufuna kuti mwanayo alonjeze cinthu cimodzi. Bamboyo akuti: “Nisanakutenge nikufuna ulonjeze kuti uzinikonda na kunimvela ngati bambo ako.” M’pomveka kuti bamboyo sangalole kutenga mwanayo ngati salonjeza zimenezi. N’cimodzi-modzinso na Yehova. Iye amalola anthu kuti akhale m’banja lake ngati anthuwo akulonjeza na mtima wonse kuti akudzipatulila kwa iye. Baibo imati: “Pelekani matupi anu kwa iye: nsembe ya moyo, odzipeleka ndi oyenela kulandilidwa ndi iye.”—Aroma 12:1, The New English Bible.

Kudzipatulila Kumasonyeza Cikondi Ndiponso Cikhulupililo

14. N’cifukwa ciani kudzipatulila kwa Mulungu kumasonyeza cikondi?

14 Tikadzipatulila kwa Mulungu, timasonyeza kuti timam’konda kwambili. Lonjezo limeneli, limafananako na lonjezo la ukwati. Mwamuna wacikhristu amasonyeza kuti amakonda mkazi wake mwa kulonjeza kuti adzakhala wokhulupilika kwa iye zivute zitani. N’zoona kuti munthu amene wadzipeleka mwa njila imeneyi mtima wake umakhala pa mnzakeyo osati pa malonjezowo ayi. Komabe mwamuna wacikhristu amadziŵa kuti n’zosatheka kukhala na mkazi wakeyo popanda malumbilo a ukwati. Nafenso sitingakhale m’banja la Yehova popanda kulonjeza kuti tikudzipatulila kwa iye. Conco timadzipatulila kwa Mulungu cifukwa cakuti timafunitsitsa kukhala anthu ake ndipo tatsimikiza kukhala okhulupilika kwa iye zivute zitani. Timacita zimenezi ngakhale kuti ndife opanda ungwilo.—Mat. 22:37.

15. N’cifukwa ciani tingati kudzipatulila kwa Mulungu kumasonyeza cikhulupililo?

15 Tikadzipatulila kwa Mulungu timasonyeza kuti timamukhulupilila. N’cifukwa ciani tikutelo? Kukhulupiila Yehova kumaticititsa kukhulupilila kuti kukhala pa ubwenzi na Mulungu n’kofunika kwambili kwa ife. (Sal. 73:28) Timadziŵa kuti kuyenda na Mulungu pakati pa “m’badwo wopotoka maganizo na wokhota-khota” si cinthu capafupi. Koma timakhulupilila lonjezo la Mulungu lakuti atithandiza tikamayesetsa kucita zimenezi. (Afil. 2:15; 4:13) Timadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, koma timakhulupilila kuti ngati titalakwitsa cinacake, Yehova angaticitile cifundo. (Ŵelengani Salmo 103:13, 14; Aroma 7:21-25.) Timakhulupilila kuti Yehova adzatidalitsa cifukwa cokhala na mtima wofunitsitsa kumutumikila zivute zitani.—Yobu 27:5.

Kudzipatulila kwa Mulungu Kumabweletsa Cimwemwe

16,17. N’cifukwa ciani kudzipeleka kwa Yehova kumabweletsa cimwemwe?

16 Yesu anafotokoza mfundo ya coonadi yakuti: “Kupatsa kumabweletsa cisangalalo coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) N’cifukwa cake kudzipatulila kwa Yehova kumabweletsa cimwemwe popeza kuti timapeleka moyo wathu wonse kwa iye. Yesu anapeza cimwemwe coculuka mu utumiki wake wapadziko lapansi cifukwa cakuti anali wopatsa. Nthawi zina anali kulephela kupuma, kudya ndiponso kucita zinthu zina momasuka, n’colinga cakuti athandize ena kupeza njila yakumoyo. (Yoh. 4:34) Yesu anali kusangalala kucita zinthu zokondweletsa mtima wa Atate wake. Iye anati: “Ndimacita zinthu zom’kondweletsa nthawi zonse.”—Yoh. 8:29; Miy. 27:11.

17 Motelo, mawu amene Yesu anauza ophunzila ake, ni othandiza kuti anthu akhale na moyo wabwino. Iye anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatila adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Kucita zimenezi kumatithandiza kukhala paubwenzi na Yehova. Kodi pali munthu winanso amene angatisamalile mwacikondi kuposa Yehova?

18. N’cifukwa ciani kudzipatulila kwa Yehova n’kumacita cifunilo cake kumaticititsa kukhala acimwemwe kwambili kuposa kudzipatulila ku cinacake kapena kwa munthu wina aliyense?

18 Kudzipatulila kwa Yehova, n’kumacita cifunilo cake, kumabweletsa cimwemwe. Cimwemwe cimeneci cimaposa cimene timapeza tikadzipatulila kucita cinthu cina ciliconse kapena tikadzipatulila kwa munthu aliyense. Mwacitsanzo, anthu ambili amadzipeleka kwambili kuti apeze cuma, komabe sakhala osangalala ndipo sakhutila na zimene akucitazo. Koma anthu amene amadzipatulila kwa Yehova, amapeza cimwemwe cosatha. (Mat. 6:24) Iwo amakhala osangalala cifukwa codziŵa kuti ni mwayi kukhala “anchito anzake a Mulungu.” Koma iwo amadzipatulila kwa Mulungu osati ku nchitoyo. (1 Akor. 3:9) Ndipo palibe amene amayamikila kwambili kudzipatulila kwawo koposa Yehova. Ndipotu ngakhale iwo atakalamba,Yehova adzacititsa kuti akhalenso anyamata n’colinga cakuti asangalale na cikondi cake kwamuyaya.—Yobu 33:25; ŵelengani Aheberi 6:10.

19. Kodi anthu amene adzipatulila kwa Yehova amakhala na mwayi wotani?

19 Mukapatulila moyo wanu kwa Yehova, mumakhala naye paubwenzi wa ponda apa m’pondepo. Baibo imati: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8; Sal. 25:14) M’nkhani yotsatila, tiona cifukwa cake sitiyenela kukayikila kuti ni cinthu canzelu kusankha kukhala anthu a Yehova.

[Mau apansi]

a “Nkhosa zina” za Yesu zidzakhala ana a Mulungu pamapeto pa zaka 1,000. Komabe, cifukwa coti iwowa anadzipatulila kwa Mulungu, angathe kuchula Mulungu kuti “Atate” ndipo amaonedwa kuti ali m’banja la olambila Yehova.—Yoh. 10:16; Yes. 64:8; Mat. 6:9; Chiv. 20:5.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kudzipatulila kwa Mulungu kumatanthauza ciani?

• Kodi timapindula bwanji tikadzipatulila kwa Mulungu?

• N’cifukwa ciani Akhristu ayenela kudzipatulila kwa Yehova?

[Mafunso Ophunzilila]

[Cithunzi]

Kucita zinthu mogwilizana na kudzipatulila kwathu, kumabweletsa cimwemwe cosatha