Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndife Anthu a Yehova Chifukwa cha Chisomo Chake

Ndife Anthu a Yehova Chifukwa cha Chisomo Chake

Ndife Anthu a Yehova Chifukwa cha Chisomo Chake

“Ndife a Yehova.”​—AROMA 14:8.

1, 2. (a) Kodi ndi mwayi wotani umene tili nawo? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tikambirane?

AISIRAELI anali ndi mwayi waukulu kwambiri pamene Yehova anawauza kuti: “Ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu.” (Eks. 19:5) Masiku ano Akhristu oona alinso ndi mwayi wokhala anthu a Yehova. (1 Pet. 2:9; Chiv. 7:9, 14, 15) Mwayi umenewu ungatithandize kupeza madalitso osatha.

2 Komabe mwayi umenewu umatipatsanso udindo. Motero mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi ineyo ndingakwanitsedi kuchita zonse zimene Yehova amafuna? Ngati nditachimwa, kodi Yehova sadzanditaya? Kodi kukhala munthu wa Yehova sikungandilande ufulu wanga?’ Mafunso amenewa ndi ofunikadi kuwaganizira bwino. Komabe, pali funso lofunika kwambiri limene tiyenera kuliganizira choyamba. Funso lake ndi lakuti: Kodi kukhala munthu wa Yehova kuli ndi phindu lotani?

Kukhala Munthu wa Yehova Kumabweretsa Chimwemwe

3. Kodi Rahabi anapindula bwanji chifukwa chosankha kutumikira Yehova?

3 Kodi anthu amapindula m’njira iliyonse chifukwa chokhala anthu a Yehova? Taganizirani chitsanzo cha Rahabi, mkazi wachiwerewere yemwe ankakhala mumzinda wakale wa Yeriko. N’zachidziwikire kuti makolo ake anam’phunzitsa kulambira milungu yawo yonyansa ya Akanani. Koma atamva za mmene Yehova anathandizira Aisiraeli kugonjetsa adani awo, iye anazindikira kuti Yehova ndiye Mulungu woona. Motero anaika moyo wake pachiswe kuti ateteze anthu a Mulunguwa ndipo potero anaika tsogolo lake lonse m’manja mwawo. Baibulo limati: “Kodi Rahabi mkazi wachiwerewere uja, sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake, powalandira bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njira ina?” (Yak. 2:25) Taganizirani madalitso amene anapeza atakhala m’gulu la anthu oyera a Mulungu, omwe anaphunzira chikondi ndi chilungamo kudzera m’Chilamulo cha Mulungu. N’zosakayikitsa kuti iye anasangalala kwambiri chifukwa chosiya moyo wake wakale. Anakwatiwa ndi Mwisiraeli ndipo mwana amene anabereka, dzina lake Boazi, anam’lera bwino moti anadzakhala munthu woopa Mulungu kwambiri.​—Yos. 6:25; Rute 2:4-12; Mat. 1:5, 6.

4. Kodi Rute anapindula bwanji chifukwa chosankha kutumikira Yehova?

4 Nayenso Rute wa ku Moabu anasankha kutumikira Yehova. N’kutheka kuti adakali kamtsikana ankalambira Kemosi ndi milungu ina ya Amoabu. Koma anadziwa Mulungu woona Yehova, n’kukwatiwa ndi Mwisiraeli amene anasamukira m’dziko lawo. (Werengani Rute 1:1-6.) Kenaka, Rute ananyamuka kupita ku Betelehemu pamodzi ndi apongozi ake, dzina lawo a Naomi. Paulendowu anali limodzi ndi Olipa. Mwamuna wa Olipa ndi wa Rute anali munthu ndi mchimwene wake. Naomi anauza atsikanawo kuti abwerere kwawo. Zinali zovuta kuti iwo akakhazikike ku Isiraeli. Olipa ‘anabwereradi kwa anthu akwawo ndi kwa milungu yake,’ koma Rute sanatero. Chifukwa cha chikhulupiriro chake, iye anafuna kukhala munthu wa Yehova. N’chifukwa chake anauza Naomi kuti: “Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:15, 16) Chifukwa chosankha kutumikira Yehova, Rute anapindula ndi Chilamulo cha Mulungu, chimene chinali ndi mfundo zokomera akazi amasiye, anthu osauka ndiponso anthu opanda minda. Yehova anali naye ndipo iye ankasangalala komanso anali wotetezeka.

5. Kodi ndi madalitso otani amene mukudziwa omwe anthu amene atumikira Yehova mokhulupirika apeza?

5 N’kutheka kuti mukudziwapo anthu ena amene anadzipereka kwa Yehova ndipo akhala akum’tumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri. Afunseni za madalitso amene apeza potumikira Mulungu. Ngakhale kuti pamakhala mavuto ena ndi ena, pali umboni wochuluka wotsimikizira mawu a wamasalmo akuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—Sal. 144:15.

Yehova Safuna Zambiri

6. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kuti sitingakwanitse kuchita zimene Yehova amafuna?

6 Mwina mumakayikira zoti mungakwanitse kuchita zimene Yehova amafuna. Anthu ena amakhala ndi nkhawa akaganizira zotumikira Mulungu, kutsatira malamulo ake ndiponso kulankhula m’dzina lake. Mwachitsanzo, Mose ankaona kuti sangakwanitse kulankhula kwa Aisiraeli ndiponso kwa mfumu ya Iguputo. Koma Yehova ankadziwa zimene Moseyo sakanakwanitsa ndipo ‘anamuphunzitsa zoyenera kuchita.’ (Werengani Eksodo 3:11; 4:1, 10, 13-15.) Mose analandira thandizo limene anamupatsa ndipo izi zinachititsa kuti asangalale chifukwa chodziwa kuti akuchita chifuniro cha Mulungu. Yehova safunanso zambiri kwa ife. Iye amadziwa kuti ndife opanda ungwiro ndipo ndi wokonzeka kutithandiza. (Sal. 103:14) Kutumikira Mulungu monga wotsatira wa Yesu si koopsa koma n’kosangalatsa chifukwa chakuti kumapindulitsa anthu ena ndiponso kumakondweretsa mtima wa Yehova. Yesu anati: “Bwerani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.”​—Mat. 11:28, 29.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova adzatithandiza kuchita zimene amafuna?

7 Ngati tidalira Yehova kuti atipatse mphamvu, iye adzatilimbikitsa. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Yeremiya mwachibadwa analibe luso la kulankhula. N’chifukwa chake pa nthawi imene Yehova anamusankha kuti akhale mneneri wake, Yeremiya anati: “Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithayi kunena pakuti ndili mwana.” Pa nthawi inanso iye anati: “Sindidzanenanso m’dzina lake.” (Yer. 1:6; 20:9) Koma Yehova atamulimbikitsa, Yeremiya analalikira kwa zaka 40 ngakhale kuti anthu ankadana ndi uthenga wake. Yehova ankamulimbikitsa mobwerezabwereza ndi mawu akuti: “Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa.”​—Yer. 1:8, 19; 15:20.

8. Kodi timasonyeza bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

8 Yehova adzatithandiza kuchita zimene amafuna kuti Akhristu azichita masiku ano ngati mmene anathandizira Mose ndi Yeremiya. Chofunika kwambiri n’kumudalira. Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miy. 3:5, 6) Timasonyeza kuti timakhulupirira Yehova mwa kugwiritsa ntchito malangizo amene iye amapereka kudzera m’Mawu ake ndiponso mumpingo. Tikalola kuti Yehova azititsogolera pamoyo wathu, palibe chimene chingatilepheretse kukhala wokhulupirika kwa iye.

Yehova Amasamalira Mtumiki Wake Aliyense

9, 10. Kodi Salmo 91 ndi lonjezo la chitetezo chotani?

9 Anthu ena akamaganizira zodzipereka kwa Yehova, amaopa kuti angadzachimwe n’kuyamba kuonedwa ngati munthu woipa ndipo angadzakanidwe ndi Yehova. Koma chosangalatsa n’chakuti Yehova amatiteteza kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino ndi iye. Tiyeni tione mmene Salmo 91 likufotokozera zimenezi.

10 Salmo limeneli limayamba ndi mawu akuti: “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndim’khulupirira. Pakuti adzakuwonjola ku msampha wa msodzi [“wosaka mbalame,” NW].” (Sal. 91:1-3) Apa Mulungu akulonjeza kuti adzateteza anthu amene amamukonda ndiponso kumudalira. (Werengani Salmo 91:9, 14.) Kodi ndi chitetezo chotani chimene akunena pa lembali? Nthawi zina, Yehova ankateteza atumiki ake akale mwakuthupi n’cholinga choti mzere wobadwira wa Mesiya usasokonezeke. Koma pali anthu ena okhulupirika amene anamangidwa, kuzunzidwa ndiponso kuphedwa mwankhanza pamene Satana ankafuna kuwasokoneza kuti asakhale okhulupirika kwa Mulungu. (Aheb. 11:34-39) Iwo anatha kupirira chifukwa chakuti Yehova anawateteza mwauzimu kuti apitirizebe kum’tumikira ndi mtima wosagawanika. Motero tingati Salmo 91 ndi lonjezo lakuti Mulungu amapereka chitetezo chauzimu.

11. Kodi “ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” ndi chiyani, nanga ndi anthu ati amene Mulungu amawateteza mmenemo?

11 “Ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” imene wamasalmo anatchula ikutanthauza malo ophiphiritsa a chitetezo chauzimu. Anthu amene ali pamalo a Mulungu amenewa, amakhala otetezeka ndipo palibe chilichonse kapena aliyense amene angawononge chikhulupiriro ndiponso chikondi chawo kwa Mulungu. (Sal. 15:1, 2; 121:5) Malowa ndi ngaka kapena kuti obisika chifukwa chakuti anthu osakhulupirira sawadziwa. Pamalo amenewa, Yehova amateteza anthu amene tingati amanena kuti: ‘Inu ndinu Mulungu wanga, amene ndim’khulupirira.’ Tikakhalabe m’malo otetezeka amenewa, sitidzada nkhawa kuti Mulungu adzasiya kutikonda chifukwa chokodwa mumsampha wa Satana yemwe ndi “wosaka mbalame.”

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Mulungu?

12 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Mulungu? Wamasalmo anatchula zinthu monga “mliri woyenda mumdima, . . . [ndi] chiwonongeko chakuthera usana.” (Sal. 91:5, 6) ‘Wosaka mbalameyu’ wakola anthu ambiri powachititsa kukhala ndi mtima wosafuna kuuzidwa zochita. (2 Akor. 11:3) Amakola anthu ena mwa kuwachititsa kukhala adyera, odzikuza ndiponso okondetsa chuma. Amasocheretsanso anthu ena kudzera mu chipembedzo chonyenga, chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka ndiponso mwa kuwachititsa kukonda kwambiri dziko lawo. (Akol. 2:8) Palinso anthu ambiri amene akodwa mumsampha wa chiwerewere. Miliri yosakaza mwauzimu imeneyi yachititsa anthu ambiri kusiya kukonda Mulungu.​—Werengani Salmo 91:7-10; Mat. 24:12.

Zimene Mungachite Kuti Muzikondabe Mulungu

13. Kodi Yehova amatiteteza bwanji ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu?

13 Kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake ku zinthu zimene zingawawononge mwauzimu zimenezi? Wamasalmo ananena kuti: “Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m’njira zako zonse.” (Sal. 91:11) Angelo akumwamba amatitsogolera ndi kutiteteza kuti tizilalikira uthenga wabwino. (Chiv. 14:6) Kuwonjezera pa thandizo la angelo, akulu achikhristu amagwiritsa ntchito kwambiri Malemba pophunzitsa n’cholinga choti atiteteze kuti tisanyengeke ndi malingaliro onama. Iwo amathandizanso munthu aliyense amene akuyesetsa kuthana ndi mtima wokonda zinthu zam’dzikoli. (Tito 1:9; 1 Pet. 5:2) Nayenso, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka chakudya chauzimu chimene chimatiteteza ku chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka. Chakudya chimenechi chimatitetezanso kuti tisakodwe mumsampha wa chiwerewere, kukonda chuma, kufuna kutchuka ndiponso zinthu zoipa zimene timalakalaka kapena zimene ena amatilimbikitsa kuti tichite. (Mat. 24:45) Kodi ndi thandizo liti limene lakutetezani inuyo ku zinthu ngati zimenezi?

14. Kodi tingatani kuti tipindule ndi chitetezo chimene Mulungu amapereka?

14 Kodi tingatani kuti tikhalebe “m’ngaka” ya Mulungu, yomwe ndi malo achitetezo? Anthufe timayesetsa kudziteteza nthawi zonse ku zinthu monga ngozi, achifwamba ndiponso matenda. Mofanana ndi zimenezi tiyeneranso kupitiriza kudziteteza ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu. Motero nthawi zonse tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo amene Yehova amatipatsa kudzera m’mabuku athu, misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu. Tiyeneranso kupempha nzeru kwa akulu mumpingo. Timapindulanso chifukwa cha makhalidwe abwino osiyanasiyana amene Akhristu anzathu amasonyeza. N’zoona kuti kukhala mumpingo kumatithandiza kukhala anzeru.​—Miy. 13:20; werengani 1 Petulo 4:10.

15. N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira kuti Yehova adzakutetezani ku zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi iye?

15 Palibe chifukwa chokayikira kuti Yehova adzatiteteza ku zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi iye. (Aroma 8:38, 39) Iye wateteza mpingo wachikhristu kwa atsogoleri amphamvu andale ndiponso achipembedzo amene cholinga chawo chimakhala, osati kutipha koma kutilekanitsa ndi Mulungu wathu woyera. Lonjezo la Yehova lakuti “palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula” lakwaniritsidwa.​—Yes. 54:17.

Kodi Ndani Amatipatsa Ufulu?

16. N’chifukwa chiyani dzikoli silingatipatse ufulu?

16 Kodi kukhala anthu a Yehova kumatilanda ufulu? Ayi. Kukhala mbali ya dziko n’kumene kumatilanda ufulu. Dzikoli n’lotalikirana kwambiri ndi Yehova ndipo likulamulidwa ndi mulungu wankhanza yemwe wachititsa anthu kukhala akapolo. (Yoh. 14:30) Mwachitsanzo, dongosolo la Satanali limagwiritsa ntchito zachuma kulanda anthu ufulu. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 13:16, 17.) Nawonso uchimo uli ndi mphamvu yogwira anthu ukapolo. (Yoh. 8:34; Aheb. 3:13) Choncho, ngakhale kuti athu osaopa Mulungu amalonjeza kuti munthu amakhala waufulu akamachita zinthu zosemphana ndi zimene Yehova amaphunzitsa, aliyense womvera zimenezi amazindikira pasanapite nthawi yaitali kuti walowa mu ukapolo wa uchimo ndi wa makhalidwe oipa osiyanasiyana.​—Aroma 1:24-32.

17. Kodi Yehova amatipatsa ufulu wotani?

17 Koma tikadzipereka kwa Yehova, iye angathe kutipulumutsa ku chilichonse chimene chingativulaze. Anthufe tili ngati munthu wodwala amene amaika moyo wake m’manja mwa dokotala wodziwa bwino ntchito yake kuti amupange opaleshoni pofuna kumupulumutsa ku matenda ake. Tonsefe tili ndi matenda amene tingathe kufa nawo. Matenda ake ndi uchimo umene tinatengera kwa makolo athu oyambirira. Tingakhale ndi chiyembekezo choti mavuto athu onse obwera chifukwa cha uchimo adzatha ndipo tidzakhala ndi moyo wosatha kokha ngati chifukwa chokhulupirira nsembe ya Khristu, tidzipereka kwa Yehova. (Yoh. 3:36) Timayamba kumukhulupirira kwambiri dokotala tikadziwa bwino mbiri yake. Moteronso, Yehova timayamba kumukhulupirira kwambiri tikamapitiriza kuphunzira za iye. Choncho tiyenera kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu mosamala. Kuchita zimenezi kungatithandize kumukonda kwambiri ndipo sitingaopenso kukhala munthu wake.​—1 Yoh. 4:18.

18. Kodi anthu amene ali a Yehova amadalitsidwa motani?

18 Yehova amapatsa anthu onse ufulu wosankha zochita. Mawu ake amati: “Sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu.” (Deut. 30:19, 20) Iye amafuna kuti anthu azimukonda chifukwa choti asankha okha kumutumikira. Kukhala munthu wa Mulungu chifukwa chomukonda sikungatilande ufulu koma kungatithandize kukhala osangalala kwambiri.

19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ndife anthu a Yehova chifukwa cha chisomo chake basi?

19 Poti ndife anthu ochimwa, siife oyenera kukhala anthu a Mulungu wangwiro. Koma chifukwa cha chisomo cha Mulungu, zimenezi zimatheka. (2 Tim. 1:9) N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Kaya tikhale ndi moyo, tikhalira Yehova, ndipo ngati tifa, tifera Yehova. Chotero kaya tikhala ndi moyo kapena tifa, ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Sitidzadandaula ngakhale pang’ono kuti tinasankha kukhala anthu a Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi timapindula bwanji chifukwa chokhala anthu a Yehova?

• Kodi n’chifukwa chiyani tingakwanitse kuchita zimene Mulungu amafuna?

• Kodi Yehova amateteza bwanji atumiki ake?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 8]

Funsani ena za madalitso amene apeza chifukwa chokhala anthu a Yehova

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi Yehova amatiteteza m’njira zotani?