Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sonyezani Kuti Ndinu Wotsatira Weniweni wa Khristu

Sonyezani Kuti Ndinu Wotsatira Weniweni wa Khristu

Sonyezani Kuti Ndinu Wotsatira Weniweni wa Khristu

“Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.”​—MAT. 7:17.

1, 2. Kodi anthu amene amatsatiradi Khristu akusiyana bwanji ndi Akhristu onyenga, makamaka m’masiku otsiriza ano?

YESU ananena kuti chimene chidzasiyanitse anthu amene amanamizira kuti amamutumikira ndi otsatira ake enieni, ndi zipatso zawo. Zipatso zimenezi ndi ziphunzitso ndiponso zochita zawo. (Mat. 7:15-17, 20) Zochita za munthu zimachokera mumtima ndi m’maganizo mwake malinga ndi zimene munthuyo amalola kuti zilowe mumtima mwakemo. (Mat. 15:18, 19) Anthu amene aphunzitsidwa mabodza, amabala “zipatso zopanda pake” koma amene aphunzitsidwa choonadi amabala “zipatso zabwino.”

2 Mitundu iwiri ya zipatsozi ikuoneka kwambiri m’masiku otsiriza ano. (Werengani Danieli 12:3, 10.) Akhristu onyenga sadziwa Mulungu molondola ndipo amanamizira kuti ndi odzipereka kwa Mulungu. Koma anthu amene amadziwa bwino Mulungu amamulambira “ndi mzimu ndi choonadi.” (Yoh. 4:24; 2 Tim. 3:1-5) Amayesetsa kusonyeza makhalidwe ngati a Khristu. Koma kodi inuyo panokha mumachita zimenezi? Mukamaganizira mfundo zisanu zotsatirazi zodziwikitsa Akhristu oona, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndimachita ndiponso zimene ndimaphunzitsa ena zimagwirizana ndi Mawu a Mulungu? Kodi zimene ndimachita zingakope anthu amene akufunafuna choonadi?’

Muzitsatira Mawu a Mulungu pa Moyo Wanu

3. Kodi Yehova amasangalala ndi chiyani, ndipo zimenezi zimakhudza bwanji Akhristu oona?

3 Yesu ananena kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wa kumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba.” (Mat. 7:21) Mulungu amasangalala ngati munthu akuchitadi zimene Mkhristu amayenera kuchita osati kungonena kuti ndine Mkhristu. Akhristu oona amachita zimenezi pa nkhani za ndalama, ntchito, zosangalatsa ndiponso pa zinthu zina zonse. Zimenezi zimakhudzanso mmene amaonera miyambo ndiponso zikondwerero zakudziko, ukwati komanso ubwenzi wawo ndi anthu osiyanasiyana. Koma Akhristu onyenga amatengera zochita za dzikoli zimene zikuipiraipira m’masiku otsiriza ano.​—Sal. 92:7.

4, 5. Kodi mawu a Yehova opezeka pa Malaki 3:18 tingawagwiritse ntchito bwanji pa moyo wathu?

4 N’chifukwa chake mneneri Malaki analemba kuti: “Mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Mal. 3:18) Ganizirani mawu amenewa ndi kudzifunsa kuti: ‘Kodi zochita zanga zimafanana ndi anthu a m’dzikoli, kapena ndimasiyana nawo kwambiri? Kodi nthawi zonse ndimayesetsa kuchita zinthu zoti ndizifanana ndi anzanga kuntchito kapena kusukulu, kapena ndimalimba mtima kutsatira mfundo za m’Baibulo mwinanso kuuza ena zimene ndimakhulupirira?’ (Werengani 1 Petulo 3:16.) Cholinga chathu si kudzionetsera kuti ndife olungama, komabe tiyenera kukhala osiyana kwambiri ndi anthu amene sakonda Yehova ndiponso samutumikira.

5 Ngati mukuona kuti mukufunika kusintha, pempherani kwa Mulungu za nkhaniyo. Ndipo ngati mutamachita khama kuphunzira Baibulo, kupemphera, ndiponso kupezeka pamisonkhano, iye angakuthandizeni kusintha. Mukamayesetsa kutsatira Mawu a Mulungu pamoyo wanu, mumabala “zipatso zabwino” zambiri monga, “chipatso cha milomo yathu, inde, milomo imene imalengeza dzina [la Mulungu] poyera.”​—Aheb. 13:15.

Muzilalikira Ufumu wa Mulungu

6, 7. Pa nkhani ya uthenga wa Ufumu, kodi Akhristu enieni amasiyana bwanji ndi Akhristu onyenga?

6 Yesu anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, chifukwa ndizo anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Kodi n’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu unali nkhani yaikulu pa utumiki wa Yesu? Yesu ankadziwa kuti iye monga Mfumu ya Ufumu umenewo, limodzi ndi abale ake oukitsidwa ndiponso odzozedwa ndi mzimu, adzachotsa zimene zimayambitsa mavuto onse a anthu zomwe ndi uchimo ndiponso Mdyerekezi. (Aroma 5:12; Chiv. 20:10) N’chifukwa chake iye anauza otsatira ake kuti azilalikira Ufumuwo mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Mat. 24:14) Anthu amene amangonena kuti ndi otsatira a Khristu sagwira ntchito imeneyi ndipo zoona zake n’zakuti sangaikwanitse. Chifukwa chiyani tikutero? Tingotchulapo zifukwa zitatu. Chifukwa choyamba n’chakuti, sangathe kulalikira zinthu zimene iwowo sakuzidziwa. Chachiwiri, ambiri sangakwanitse kulalikira uthenga wa Ufumu, chifukwa ntchito imeneyi imafuna kuti munthu akhale wodzichepetsa kuti azitha kupirira akamanyozedwa ndiponso kulimba mtima akamatsutsidwa. (Mat. 24:9; 1 Pet. 2:23) Ndipo chifukwa chachitatu n’chakuti, Akhristu onyenga alibe mzimu wa Mulungu.​—Yoh. 14:16, 17.

7 Koma otsatira enieni a Khristu amadziwa bwino Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene udzachite. Chinanso, amaika zinthu za Ufumu umenewu patsogolo m’moyo wawo ndipo amalalikira Ufumuwo padziko lonse mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova. (Zek. 4:6) Kodi mumagwira nawo ntchito imeneyi nthawi zonse? Kodi mukuyesetsa kupita patsogolo pa nkhani ya kulalikira Ufumu, mwina powonjezera nthawi imene mumakhala mu utumiki kapena pokulitsa luso lanu? Ena akulitsa luso lawo mu utumiki mwa kuyesetsa kugwiritsa ntchito bwino Baibulo. Mtumwi Paulo yemwe ankakonda kukambirana Malemba ndi anthu, analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”​—Aheb. 4:12; Mac. 17:2, 3.

8, 9. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza ubwino wogwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki? (b) Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito kwambiri Mawu a Mulungu mu utumiki?

8 M’bale wina akulalikira khomo ndi khomo, anapeza bambo wina wa Katolika ndipo anamuwerengera lemba la Danieli 2:44 n’kumufotokozera mmene Ufumu wa Mulungu udzabweretsere bata ndi mtendere. Bamboyo anati: “Ndikuyamikira kwambiri chifukwa mwatsegula Baibulo n’kundisonyeza zimene lemba limeneli limanena m’malo mongondiuza pakamwa.” M’bale winanso atakumana ndi mayi wa tchalitchi cha Greek Orthodox, anamuwerengera lemba ndipo mayiyo anafunsa mafunso angapo osonyeza kuti anali ndi chidwi. M’baleyo ndi mkazi wake anamuyankhanso pogwiritsa ntchito Baibulo. Kenako mayiyo anafunsa kuti: “Kodi mukudziwa chimene chinachititsa kuti ndilole kulankhula nanu? N’chifukwa chakuti munabwera ndi Baibulo ndipo munkandiwerengera kuchokera m’Baibulomo.”

9 N’zoona kuti mabuku athu ndi ofunika kwambiri ndipo tiyenera kugawira anthu mabukuwa mu utumiki. Komabe Baibulo ndilo buku lathu lofunika kwambiri. Choncho ngati mulibe chizolowezi chogwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki, khalani ndi cholinga chochita zimenezi. Mukhoza kusankha malemba angapo odziwika bwino amene amafotokoza Ufumu wa Mulungu ndiponso mmene udzathetsere mavuto osiyanasiyana amene amadetsa nkhawa anthu a m’dera lanu. Ndiyeno mungakonzekere kuti muziwerenga malemba amenewo mukamalalikira khomo ndi khomo.

Muzinyadira Mwayi Wodziwika ndi Dzina la Mulungu

10, 11. Pa nkhani yogwiritsa ntchito dzina la Mulungu, kodi Yesu amasiyana bwanji ndi anthu amene amangonena kuti amamutsatira?

10 Yehova anati: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndipo Ine ndine Mulungu.” (Yes. 43:12) Yesu Khristu, yemwe ali Mboni yaikulu koposa, ankaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kudziwika ndi dzina la Mulungu ndiponso kuuza ena za dzinalo. (Werengani Eksodo 3:15; Yohane 17:6; Aheberi 2:12.) Yesu analalikira dzina la Atate wake ndipo chifukwa cha zimenezi, ankatchedwa ‘Mboni Yokhulupirika.’​—Chiv. 1:5; Mat. 6:9.

11 Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amanamizira kuti amaimira Mulungu ndiponso Mwana wake, amadana kwambiri ndi dzina la Mulungu moti afika polichotsa m’Mabaibulo awo. Posonyeza mzimu womwewo, posachedwapa mabishopu a Katolika analamulidwa kuti polambira “asamagwiritse ntchito dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo zinayi zomwe ndi YHWH, ndipo asamalitchulenso.” * Umenewutu ndi maganizo olakwika kwambiri.

12. Kodi atumiki a Yehova anayamba bwanji kudziwika kwambiri ndi dzina lake mu m’chaka cha 1931?

12 Mofanana ndi Khristu ndiponso “mtambo wa mboni” waukulu umene unakhalako Yesu asanabwere, Akhristu enieni amanyadira kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. (Aheb. 12:1) Ndipotu m’chaka cha 1931, atumiki a Mulungu anayamba kudziwika kwambiri ndi dzina la Yehova pamene anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. (Werengani Yesaya 43:10-12.) Choncho otsatira oona a Khristu anakhala “anthu otchedwa ndi dzina [la Mulungu]” m’njira yapadera kwambiri imeneyi.​—Mac. 15:14, 17.

13. Kodi tingatani kuti zochita zathu zizigwirizana ndi dzina limene Mulungu wathu watipatsa?

13 Kodi aliyense payekha angatani kuti azichita zinthu zogwirizana ndi dzina lapaderali? Njira imodzi ndiyo kuchitira umboni za Mulungu mokhulupirika. Paulo analemba kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka. Komabe, kodi adzaitana bwanji munthu amene sakhulupirira mwa iye? Ndipo adzakhulupirira bwanji mwa munthu amene sanamve za iye? Ndipo adzamva bwanji za iye popanda wina kulalikira? Ndipo adzalalikira bwanji ngati sanatumidwe?” (Aroma 10:13-15) Chinanso tiyenera kuthandiza anthu mwaulemu kudziwa ziphunzitso zonama zimene zimaipitsa dzina la Mlengi wathu monga chiphunzitso chakuti Mulungu amawotcha anthu kumoto. Ziphunzitso zoterezi zimachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu wathu, yemwe ndi wachikondi, ndi wankhanza ngati Mdyerekezi.​—Yer. 7:31; 1 Yoh. 4:8; yerekezerani ndi Maliko 9:17-27.

14. Kodi anthu ambiri akadziwa dzina la Mulungu amatani?

14 Kodi mumanyadira kudziwika ndi dzina la Atate wanu wakumwamba? Kodi mumathandiza ena kudziwa dzina loyera limeneli? Mayi wina wa ku Paris, m’dziko la France, anamva kuti Mboni za Yehova zimadziwa dzina la Mulungu. Choncho iye anafunsa mlongo wina amene anakumana naye, kuti amusonyeze dzina la Mulungu m’Baibulo lake. Atawerenga naye lemba la Salmo 83:18, mayiyo anakhudzidwa kwambiri. Iye anayamba kuphunzira Baibulo moti panopa akutumikira Mulungu mokhulupirika m’dziko lina. Mayi wina wa Katolika ataona dzina la Mulungu m’Baibulo kwa nthawi yoyamba, analira ndi chisangalalo. Iye tsopano wakhala akuchita upainiya wokhazikika kwa zaka zambiri. Posachedwapa, mayi wina wa ku Jamaica analiranso chifukwa chokhudzidwa mtima, Mboni za Yehova zitamusonyeza dzina la Mulungu m’Baibulo lake. Choncho muzinyadira kuti mumadziwika ndi dzina la Mulungu ndipo mofanana ndi Yesu, muziuza ena za dzina lapamwamba kwambiri limeneli.

“Musamakonde Dziko”

15, 16. Kodi Akhristu oona ayenera kuliona bwanji dzikoli, ndipo kodi tingadzifunse mafunso ati?

15 Baibulo limati: “Musamakonde dziko kapena za m’dziko. Ngati wina akonda dziko, sakonda Atate.” (1 Yoh. 2:15) Dzikoli komanso mzimu wake wokonda zinthu zakuthupi limatsutsana kwambiri ndi Yehova ndiponso mzimu woyera. Motero otsatira oona a Khristu sikuti amangopewa kukhala mbali ya dzikoli. Iwo amadana nalo kuchokera pansi pa mtima, chifukwa amadziwa mfundo imene Yakobe analemba yakuti “kuchita ubwenzi ndi dziko ndiko udani ndi Mulungu.”​—Yak. 4:4.

16 N’zoona kuti kutsatira mawu a Yakobe amenewa n’kovuta kwambiri chifukwa m’dzikoli timakumana ndi mayesero ambirimbiri. (2 Tim. 4:10) N’chifukwa chake Yesu anapempherera otsatira ake kuti: “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yoh. 17:15, 16) Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kusakhala mbali ya dziko? Kodi anthu amadziwa kuti sindichita nawo zikondwerero ndi miyambo yotsutsana ndi Malemba? Nanga bwanji zikondwerero ndi miyambo zimene zimasonyeza mzimu wa dzikoli, ngakhale kuti si zochokera ku chipembedzo chonyenga?’​—2 Akor. 6:17; 1 Pet. 4:3, 4.

17. Kodi n’chiyani chingachititse kuti anthu ofuna kudziwa choonadi abwere kwa Yehova?

17 Inde, tikamatsatira mfundo za m’Baibulo dzikoli silingatikonde, komabe zimenezi zingachititse chidwi anthu ofuna kudziwa choonadi. Anthu amenewa akazindikira kuti zonse zimene timakhulupirira n’zochokera m’Malemba, ndipo timayesetsa kuzitsatira pa zochita zathu zonse, mophiphiritsa angathe kuuza Akhristu odzozedwa kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zek. 8:23.

Muzisonyeza Chikondi Chenicheni Ngati Khristu

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova ndiponso mnansi wathu?

18 Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” Iye anatinso: “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 22:37, 39) Chikondi chimenechi (chomwe pa Chigiriki chimatchedwa kuti a·gaʹpe), ndi chikondi chimene munthu amachisonyeza chifukwa chodziwa kuti ndi udindo wake kutero, ndiponso chifukwa chotsatira mfundo za makhalidwe abwino. Chimachokeradi mumtima, ndipo chimakhudza mmene munthu akumvera. (1 Pet. 1:22) Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amalankhula ndiponso kuchita zinthu moganizira ena, ndipo amakhala alibiretu mtima wodzikonda.​—Werengani 1 Akorinto 13:4-7.

19, 20. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti chikondi chimene Akhristu amasonyezana ndi champhamvu kwambiri?

19 Popeza chikondi ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, chimathandiza Akhristu oona kukwaniritsa zinthu zimene ena sangathe. Zinthu zimenezi ndi monga kukonda anthu mosaganizira mtundu, chikhalidwe kapena ndale. (Werengani Yohane 13:34, 35; Agal. 5:22) Anthu onga nkhosa amakhudzidwa kwambiri akaona chikondi choterechi. Mwachitsanzo, mnyamata wina m’dziko la Israel, atapita koyamba kumisonkhano ya Mboni za Yehova, anadabwa kuona Ayuda ndi Aluya akulambira Yehova limodzi. Izi zinachititsa kuti ayambe kupezeka pamisonkhano nthawi zonse komanso kuphunzira Baibulo. Kodi inuyo mumasonyeza chikondi choterechi kwa abale anu? Ndipo kodi mumayesetsa kulandira mwansangala atsopano onse amene amabwera ku Nyumba ya Ufumu mosaganizira dziko limene achokera, khungu lawo ndiponso kuti ndi olemera kapena osauka?

20 Poti ndife Akhristu oona, timayesetsa kusonyeza chikondi kwa anthu onse. Ku El Salvador, mlongo wina wachitsikana ankaphunzira Baibulo ndi mayi wa zaka 87 yemwe anali Mkatolika ndipo anali wolimbikira kwambiri kutchalitchi kwawo. Tsiku lina, mayiyu anadwala mwakayakaya ndipo anagonekedwa m’chipatala. Atatulutsidwa m’chipatala, alongo ankapita kukamuona ndiponso kumupatsa chakudya. Izi zinachitika kwa mwezi wathunthu. Koma palibe ngakhale munthu mmodzi wakutchalitchi kwawo amene anapita kukamuona. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anataya mafano ake onse, kutsanzika kutchalitchi chake ndipo anayambiranso kuphunzira Baibulo. Chikondi chimene Akhristu amasonyeza n’champhamvu kwambiri. Chimakhudza mtima kwambiri kuposa mmene mawu okha amachitira.

21. Kodi tingatani kuti tikhale ndi tsogolo labwino?

21 Posachedwapa Yesu adzakana anthu amene amanamizira kuti amam’tumikira. Iye adzawauza kuti: “Sindinakudziweni konse chiyambire! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.” (Mat. 7:23) Motero tiyeni tiziyesetsa kubala zipatso zimene zingalemekeze Atate ndi Mwana. Yesu ananena kuti: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” (Mat. 7:24) Inde, tikakhala otsatira enieni a Khristu, Yehova amasangalala nafe ndipo timakhala ndi tsogolo labwino ngati nyumba yomangidwa pathanthwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mabuku ena a Akatolika a m’Chingelezi kuphatikizapo Baibulo la The Jerusalem Bible, amalemba kuti “Yahweh” pa malo pamene pali zilembo zoimira dzina la Mulungu.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chiyani chimasiyanitsa otsatira oona a Khristu ndi Akhristu onyenga?

• Tchulani “zipatso “ zimene zimadziwikitsa Akhristu oona.

• Kodi ndi zinthu ziti zimene mukufuna kuchita pa nkhani yobala zipatso zachikhristu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi mumakonda kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki?

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi anthu amadziwa kuti simuchita nawo zikondwerero ndi miyambo yotsutsana ndi Malemba?