Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Ana Anu Kulimbana ndi Mavuto Awo

Thandizani Ana Anu Kulimbana ndi Mavuto Awo

Thandizani Ana Anu Kulimbana ndi Mavuto Awo

ACHINYAMATA amakumana ndi mavuto ambirimbiri. Iwo amakhudzidwa kwambiri ndi mzimu wa dziko loipa la Satanali ndipo amalimbananso ndi “zilakolako za unyamata.” (2 Tim. 2:22; 1 Yoh. 5:19) Chinanso n’chakuti iwo akamayesetsa ‘kukumbukira mlengi wawo,’ amanyozedwa kapenanso kuzunzidwa ndi anthu amene amatsutsa zikhulupiriro zawo. (Mlal. 12:1) M’bale wina dzina lake Vincent, anafotokoza zimene zinkamuchitikira ali mnyamata. Iye anati: “Nthawi zonse anzanga ankandivutitsa kapena kundiyamba dala kuti timenyane. Iwo ankachita zonsezi chifukwa chakuti ndine Mboni. Nthawi zambiri zinkafika poipa kwambiri moti sindinkafunanso kupita kusukulu.” *

Kuwonjezera pa mavuto amene amakumana nawo m’dzikoli, achinyamata amakhalanso ndi vuto lofuna kutsanzira anzawo. Mtsikana wina wa zaka 16 dzina lake Cathleen anati: “Ukamachita zinthu zosiyana ndi anzako umakumana ndi zovuta zambiri.” Mnyamata wina, dzina lake Alan anati: “Anzanga akusukulu ankakonda kundiitana kuti tipite kukacheza kwinakwake Loweruka kapena Lamlungu. Kunena zoona, ndinkalakalaka nditapita.” Achinyamata angathenso kutengeka mosavuta ndi makhalidwe oipa a anzawo chifukwa chofunitsitsa kuchita nawo masewera osiyanasiyana. Mtsikana wina dzina lake Tanya anati: “Ndimakonda kwambiri masewera. Aphunzitsi ambiri kusukulu ankandilimbikitsa kuti ndilowe nawo m’matimu a masewera osiyanasiyana. Sizinali zophweka kukana.”

Kodi mungathandize bwanji ana anu kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana amene amakumana nawo? Yehova analamula makolo kuti azipereka malangizo kwa ana awo. (Miy. 22:6; Aef. 6:4) Makolo oopa Mulungu amakhala ndi cholinga chothandiza ana awo kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumvera Yehova. (Miy. 6:20-23) Ana akakhala ndi mtima umenewu, angathe kulimbana ndi ziyeso zosiyanasiyana ngakhale atakhala kwaokha.

Makolo amafunika kupeza zinthu zofunika pabanja, kulera ana komanso kusamalira zinthu zakumpingo, ndipo si zophweka kuchita zimenezi nthawi imodzi. Ena amachita zimenezi akulera okha ana kapena akutsutsidwa ndi mwamuna kapena mkazi wawo wosakhulupirira. Komabe Yehova amafuna kuti makolo azipeza nthawi yophunzitsa ndi kuthandiza ana awo. Ndiyeno popeza kuti ana anu amayesedwa kapena kuzunzidwa tsiku lililonse, kodi mungatani kuti muwathandize kukhala olimba kwambiri?

Athandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Yehova

Chofunika kwambiri n’chakuti muyenera kuthandiza ana anu kudziwa kuti Yehova ndi weniweni. Muyenera kuwathandiza ‘kuona Wosaonekayo.’ (Aheb. 11:27) Vincent amene tamutchula poyamba uja, amakumbukira kuti makolo ake anamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iye anati: “Anandiphunzitsa kufunika kopemphera. Ndimakumbukira kuti kuyambira ndili mwana ndinkapemphera kwa Yehova tsiku lililonse ndisanakagone. Ndinkadziwa kuti Yehova ndi weniweni.” Kodi mumapemphera pamodzi ndi ana anu? Mungachite bwino kumvetsera zimene ana anu amanena kwa Yehova m’mapemphero awo. Kodi amangobwereza mawu enaake amene anawaloweza kapena amafotokoza zinthu zosonyeza kuti amakonda Yehova ndiponso kum’dziwa bwino? Mungathe kudziwa kuti anawo akupita patsogolo mwauzimu mukamamvetsera mapemphero awo.

Njira ina imene ingathandize achinyamata kuti ayambe kukonda Yehova kwambiri ndiyo kuchita khama kuwerenga Mawu a Mulungu paokha. Cathleen, amene tam’tchula poyamba uja, anati: “Ndinawerenga Baibulo lonse ndidakali wamng’ono ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri. Zinachititsa kuti ndisamakayike kuti Yehova ali nane ngakhale anthu atamanditsutsa.” Kodi ana anu ali ndi pulogalamu yawo yowerenga Baibulo?​—Sal. 1:1-3; 77:12.

N’zoona kuti ana amasiyanasiyana. Ena amamvera makolo mosavuta koma ena satero. Komanso ana amapita patsogolo mogwirizana ndi zaka zawo. Komabe popanda inuyo kuwalangiza, n’zovuta kuti iwo aziona kuti Yehova ndi weniweni. Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo mawu a Mulungu mwakhama kuti anawo asamaiwale Yehova kulikonse kumene apita. (Deut. 6:6-9) Ana anu azikhulupirira kuti Yehova amawakonda iwowo paokha.

Zimene Mungachite Kuti Muzilankhulana Momasuka

Njira ina yofunika imene mungathandizire ana anu ndiyo kulankhula nawo. Komabe kuti muzilankhula momasuka ndi ana anu pamafunika zambiri. Pamafunika kuwafunsa mafunso ndi kumvetsera mayankho awo moleza mtima, ngakhale mutakhala kuti simukugwirizana ndi mayankhowo. Anne, mayi wa ana awiri aamuna, anati: “Ndimawafunsa mafunso osiyanasiyana kuti ndifike pomvetsa bwinobwino zimene akuganiza ndiponso mavuto amene akukumana nawo.” Kodi ana anu amaona kuti mumamvetsera zimene akukuuzani? Tanya, amene tam’tchula kale uja, anati: “Makolo anga ankamvetsera mosamala ndikamalankhula ndipo ankakumbukira zimene takhala tikukambirana. Ankadziwa mayina a anzanga kusukulu. Ankandifunsa za anzangawo ndiponso za zinthu zina zimene tinakambiranapo.” Inde, kuti muzilankhulana momasuka m’pofunika kumvetserana komanso kukumbukira zimene mwakambirana.

Mabanja ambiri aona kuti amakhala ndi mpata wolankhulana momasuka panthawi ya chakudya. Vincent anati: “M’banja mwathu tinkakonda kwambiri kudyera pamodzi. Panthawi ya chakudya tonse tinkayenera kudyera pamodzi ngati n’zotheka. Sitinkaloledwa kuonera TV, kumvetsera wailesi, kapena kuwerenga panthawi ya chakudya. Popeza nthawi zambiri tinkangocheza basi, tsiku lililonse ndinkakhala ndi mpata wokhala mwabata ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisamaganizire kwambiri mavuto amene ndimakumana nawo kusukulu.” Iye ananenanso kuti: “Kulankhulana ndi makolo anga panthawi ya chakudya kunandithandizanso kukhala womasuka pokambirana nawo nkhani zina zikuluzikulu.”

Dzifunseni kuti, ‘Kodi banja lathu limadyera pamodzi kangati pa mlungu?’ N’kutheka kuti ngati mutasintha zina ndi zina pa mbali imeneyi mungayambe kulankhulana ndi ana anu momasuka komanso m’njira yopindulitsa.

Kuyesera Kumathandiza Kwambiri

Kukhala ndi tsiku la Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse kumathandizanso kuti anthu m’banja azilankhulana momasuka komanso kuti achinyamata asamagonje akakumana ndi mavuto enaake. Alan amene tam’tchula poyamba uja anati: “Makolo anga ankayesetsa kudziwa maganizo athu pa nthawi ya phunziro la banja. Iwo ankasankha nkhani zimene zikugwirizana ndi mavuto amene tinkakumana nawo.” Mayi a Alan anati: “Panthawi ya phunziro la banja tinkayeserera zinthu zina. Zimenezi zinkathandiza ana athu kuti azitha kufotokoza molimba mtima zimene amakhulupirira ndiponso kupereka umboni wakuti zimene amakhulupirirazo n’zoona. Izi zinawathandiza kuti azikhala olimba mtima akakumana ndi mavuto.”

Anzawo akamawauza kuti achite zinthu zoipa, anawo ayenera kukana n’kuchokapo. Koma nthawi zina kuchita zimenezi si kokwanira. Iwo ayenera kufotokozera anzawo zifukwa zimene sakuchitira zinthu zinazake. Ayenera kudziwanso zoyenera kuchita anzawo akamawanyoza chifukwa cha zimene amakhulupirira. N’zovuta kuti alimbe mtima kutsatira mfundo za choonadi ngati sangathe kuuza ena zifukwa zomveka zokhudza chikhulupiriro chawo. Komabe kuti alimbe mtima m’pofunika kuti muziyeserera zimenezi kunyumba.

 Bokosi limene lili pa tsamba 18 likutchula zinthu zina zimene mungayeserere pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Kuti anawo ziwafikedi pamtima, muyenera kukhala ngati munthu woti akutsutsa mayankho a ana anuwo. Kuwonjezera pa zimenezi, mungakambirane zimene mukuphunzirapo pa zitsanzo za anthu a m’Baibulo. Kuphunzitsa ana kunyumba m’njira imeneyi kungawathandize kuti alimbane ndi mavuto amene amakumana nawo kusukulu kapena kwina kulikonse.

Kodi Panyumba Panu Pali Mtendere?

Kodi ana anu amasangalala kubwerera kunyumba akaweruka kusukulu? Ngati panyumba panu pali mtendere, ana anu azitha kulimbana bwinobwino ndi mavuto amene amakumana nawo tsiku ndi tsiku. Mlongo wina amene panopa akutumikira pa Beteli anati: “Ndili mwana, chomwe chinali chofunika kwambiri chinali kudziwa kuti ndine wotetezeka kunyumba kwathu. Ndinkadziwa kuti kaya ndikumane ndi zotani kusukulu, mtima wanga ukhala m’malo ndikafika kunyumba.” Ndiye kodi zinthu zili bwanji panyumba panu? Kodi mumangokhalira ‘kupsetsana mtima, kukangana’ ndiponso kusamvana? Kapena m’banja mwanu muli ‘chikondi, chimwemwe ndi mtendere’? (Agal. 5:19-23) Ngati m’banja mwanu mulibe mtendere, kodi mukuchitapo chiyani kuti ana anu aziona kuti panyumba panu pali mtendere?

Njira ina imene ingathandize kuti ana anu azilimbana ndi mavuto amene amakumana nawo ndiyo kuyesetsa kupeza njira zoti ana anuwo azicheza ndi anthu olongosoka. Mwachitsanzo, kodi mungathe kuitana abale ndi alongo okonda zinthu zauzimu a mumpingo mwanu panthawi imene banja lanu likuchita zinthu zosangalatsa? Mwinanso mungakonze kachakudya kenakake n’kuitana woyang’anira dera kapena anthu ena amene akuchita utumiki wa nthawi zonse. Kodi mukudziwa amishonale kapena atumiki a pa Beteli amene angamacheze ndi ana anu, kulemberana nawo makalata, kuimbirana mafoni kapena kutumizirana mauthenga pa kompyuta? Kucheza ndi anthu otere kungathandize kuti ana anu akhale olongosoka ndiponso kuti akhale ndi zolinga zauzimu. Taganizirani mmene Paulo anamuthandizira Timoteyo. (2 Tim. 1:13; 3:10) Chifukwa chocheza ndi Paulo, Timoteyo anayamba kukonda kwambiri zinthu zauzimu.​—1 Akor. 4:17.

Muziyamikira Ana Anu

Yehova amasangalala akaona achinyamata akuchita zabwino ngakhale kuti akukumana ndi mayesero osiyanasiyana m’dziko la Satanali. (Sal. 147:11; Miy. 27:11) N’zodziwikiratu kuti inunso mumasangalala mukaona ana anu akusankha kuchita zinthu zoyenera. (Miy. 10:1) Ana anu azidziwa kuti mumasangalala ndi zimene iwo akuchita ndipo muziwayamikira pafupipafupi. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo. Pamene Yesu anabatizidwa, Yehova anati: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.” (Maliko 1:11) Mawu a Atate wake amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Yesu kuthana ndi mavuto amene anakumana nawo. Nanunso muzichita zinthu zoti ana anu azidziwa kuti mumawakonda ndipo mumayamikira zimene akuchita.

Ngakhale mutayesetsa bwanji kuteteza ana anu, dziwani kuti ana anuwo azizunzidwabe ndiponso kunyozedwa. Komabe, pali zinthu zambiri zimene mungachite kuti muwathandize. Kodi mungachite chiyani? Athandizeni kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Muziyesetsa kulankhulana momasuka. Pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja, muzikambirana zinthu zothandiza anawo ndipo muziyesetsa kuti panyumba panu pazikhala mtendere. Izi zidzathandiza kuti ana anu azithana bwinobwino ndi mavuto osiyanasiyana amene amakumana nawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena m’nkhani ino tawasintha.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 18]

 NDI BWINO KUYESERERA

M’munsimu talemba zinthu zina zimene ana amakumana nazo. Mwina mungamayeserere zinthu zimenezi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja.

▸ Aphunzitsi akuuza mwana wanu wamkazi kuti alowe timu ya sukulu.

▸ Mwana wanu wamwamuna akupatsidwa ndudu pochokera kusukulu.

▸ Anyamata ena akuopseza mwana wanu wamwamuna kuti adzamumenya akadzangomuonanso akulalikira.

▸ Mwana wanu wamkazi akulalikira khomo ndi khomo ndipo atafika pa khomo lina, mnzake wa kusukulu akutuluka.

▸ Mphunzitsi akuuza mwana wanu wamkazi kuti afotokoze m’kalasi chifukwa chake sachitira sawatcha mbendera.

▸ Mnyamata wina amanyoza mwana wanu wamwamuna nthawi zonse chifukwa choti ndi wa Mboni.

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi ana anu ali ndi pulogalamu yawo yowerenga Baibulo?

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi banja lanu likamachita zinthu zosangalatsa, mumaitana anthu ena okonda zinthu zauzimu?