Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Woyeneradi Kulamulira

Yehova Ndiye Woyeneradi Kulamulira

Yehova Ndiye Woyeneradi Kulamulira

“Wam’mwambamwamba alamulira m’ufumu wa anthu.”​—DAN. 4:17.

1, 2. Kodi ulamuliro wa anthu walephera pa zifukwa zina ziti?

ULAMULIRO wa anthu walephera ndipo palibe angatsutse mfundo imeneyi. Chifukwa chachikulu n’chakuti anthu alibe nzeru zowathandiza kulamulira bwinobwino. Kulephera kwa ulamuliro wa anthu kukuonekera kwambiri masiku ano chifukwa olamulira ambiri ndi ‘odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, ndiponso otukumuka chifukwa cha kunyada.’​—2 Tim. 3:2-4.

2 Kalelo makolo athu oyambirira anakana ulamuliro wa Mulungu. Pochita zimenezo, iwo ankaona ngati akhala ndi ufulu wodzilamulira. Koma zoona zake n’zakuti anasankha ulamuliro wa Satana. Tsopano patha zaka 6,000 anthu akudzilamulira motsogoleredwa ndi Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli.” Zimenezi zachititsa mavuto aakulu amene tikukumana nawo masiku ano. (Yoh. 12:31) Ponena za mmene zinthu zilili masiku ano, buku lina linati “kuyesa kukonza zinthu padzikoli kuti zonse ziziyenda bwino n’kungotaya nthawi.” Bukuli linafotokozanso kuti: “Zimenezi n’zosatheka ndipo kuyesa kuchita zimenezi kumangobweretsa mavuto, ulamuliro wankhanza, ngakhalenso nkhondo imene.” Apatu bukuli linanena zoona chifukwa ulamuliro wa anthu ndi wolepheradi.​—The Oxford History of the Twentieth Century

3. Kodi mukuganiza kuti Adamu ndi Hava akanapanda kuchimwa bwenzi Mulungu akulamulira motani?

3 Motero n’zomvetsa chisoni kwambiri kuti makolo athu oyambirira anakana kumvera ulamuliro wa Mulungu. Uwutu ndi ulamuliro wabwino wokhawo kuposa wina uliwonse. N’zoona kuti sitikudziwa bwinobwino dongosolo limene Yehova akanapanga polamulira dziko lapansi, Adamu ndi Hava akanakhalabe okhulupirika kwa iye. Komabe, sitingakayike kuti anthu onse akanavomereza ulamuliro wa Mulungu, bwenzi pali ulamuliro wachikondi ndiponso wosakondera. (Mac. 10:34; 1 Yoh. 4:8) Komanso poganizira nzeru zosaneneka za Yehova, ngati anthu akanakhalabe mu ulamuliro wake, ndiye kuti tikanapewa mavuto onse obwera chifukwa cha ulamuliro wa anthu. Ulamuliro wa Mulungu ‘ukanakwaniritsa chokhumba cha zamoyo zonse.’ (Sal. 145:16) Mwachidule tingoti ukanakhala ulamuliro wopanda vuto ngakhale limodzi. (Deut. 32:4) N’zomvetsa chisoni kuti anthu anakana ulamuliro umenewu.

4. Kodi Satana waloledwa kukhala ndi mphamvu zotani?

4 Komabe, tisaiwale kuti ngakhale Yehova walola anthu kudzilamulira, iye sanasiyirepo wina aliyense ufulu wake wolamulira zinthu zonse zimene analenga. Ngakhale mfumu yamphamvu ya Babulo inafika povomereza kuti “Wam’mwambamwamba alamulira m’ufumu wa anthu” ndipo palibe wom’posa. (Dan. 4:17) Pamapeto pake, Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zimene Yehova akufuna. (Mat. 6:10) N’zoona kuti kwa kanthawi kochepa, Yehova walola Satana kukhala “mulungu wa dongosolo lino la zinthu” pofuna kuti nkhani zimene wotsutsayu anayambitsa zithetsedwe mwa njira yoti aliyense akhutire nazo. (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19) Komabe, Mulungu sanam’lole Satana kukhala ndi mphamvu zochita chilichonse chimene akufuna. (2 Mbiri 20:6; yerekezerani ndi Yobu 1:11, 12; 2:3-6.) Ndipotu kuyambira kale, pakhala anthu omvera Mulungu ngakhale kuti dzikoli likulamulidwa ndi mdani wamkulu wa Mulungu.

Ulamuliro wa Mulungu kwa Aisiraeli

5. Kodi Aisiraeli anamulonjeza chiyani Mulungu?

5 Kuyambira nthawi ya Abele mpaka nthawi imene mtundu wa Isiraeli unayamba, panali anthu ambiri okhulupirika amene ankalambira Yehova ndi kumvera malamulo ake. (Aheb. 11:4-22) M’nthawi ya Mose, Yehova anachita pangano ndi mbadwa za Yakobo ndipo anthu amenewa anakhala mtundu wa Isiraeli. M’chaka cha 1513 B.C.E., Aisiraeli analonjeza kuti iwo ndiponso ana awo azimvera Yehova monga Wolamulira wawo. Iwo anati: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.”​—Eks. 19:8.

6, 7. Kodi Mulungu ankawalamulira bwanji Aisiraeli?

6 Yehova anali ndi cholinga posankha Aisiraeli kukhala anthu ake. (Werengani Deuteronomo 7:7, 8.) Sikuti Yehova anachita zimenezi chifukwa chongofuna kupindulitsa mtundu wa Isiraeliwo. Nkhani imeneyi kwenikweni inkakhudza dzina la Mulungu ndi ulamuliro wake. Zimenezitu n’zimene zinali zofunika kwambiri. Aisiraeli anafunika kuchitira umboni mfundo yoti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. (Yes. 43:10; 44:6-8) N’chifukwa chake Yehova anauza mtunduwo kuti: “Ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pawokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.”​—Deut. 14:2.

7 Mulungu ankawalamulira Aisiraeli moganizira kuti ndi anthu opanda ungwiro. Komabe malamulo amene anawapatsa anali angwiro ndipo ankasonyeza makhalidwe abwino a Mulungu. Malamulo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose anasonyeza bwinobwino kuti Mulungu ndi woyera, amakonda chilungamo, ali ndi mtima wokhululuka ndiponso ndi woleza mtima. Kenako m’nthawi ya Yoswa, mtunduwu unkamvera malamulo a Yehova. Izi zinachititsa kuti ukhale pamtendere ndiponso kuti Yehova aziudalitsa mwauzimu. (Yos. 24:21, 22, 31) Panthawi imeneyo, zinaonekeratu kuti ulamuliro wa Yehova ndiye wabwino.

Ulamuliro wa Anthu Unabwera ndi Mavuto Ake

8, 9. Kodi Aisiraeli anapempha chiyani kwa Mulungu, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

8 Komabe patapita nthawi, Aisiraeli anayamba kupandukira ulamuliro wa Mulungu ndipo zikatero iye ankasiya kuwateteza. Ndiyeno kudzera mwa mneneri Samueli, Aisiraeli anauza Mulungu kuti akufuna munthu woti akhale mfumu yawo. Yehova anamuuza Samueli kuti awapatse mfumuyo koma anamuuzanso kuti: “Sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yawo.” (1 Sam. 8:7) Ngakhale kuti Yehova analola kuti Aisiraeli akhale ndi mfumu imene ankafunayo, iye anawachenjeza kuti zimenezi zinali ndi mavuto ake.​—Werengani 1 Samueli 8:9-18.

9 Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti zimene Yehova anachenjezazi zinali zoona. Aisiraeli ankavutika kwambiri chifukwa cholamulidwa ndi anthu makamaka olamulirawo akakhala osakhulupirika. Tikaganizira chitsanzo cha Aisiraeli chimenechi, timamvetsa chifukwa chake maboma a anthu alephera kuthetsa mavuto. N’zoona kuti atsogoleri ena amapempha Mulungu kuti awadalitse n’cholinga chakuti abweretse bata ndi mtendere. Komabe kodi Mulungu angadalitse bwanji anthu amene sagonjera ulamuliro wake?​—Sal. 2:10-12.

Mtundu Watsopano Wolamulidwa ndi Mulungu

10. N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha anthu ena kuti alowe m’malo mwa mtundu wa Isiraeli?

10 Mtundu wa Isiraeli unasonyeza kuti sunkafuna kutumikira Yehova mokhulupirika. Kenako mtunduwu unakana Mesiya amene Mulungu anamusankha ndipo Yehova anausiya n’kukonza zoti pakhale gulu lina la anthu loti likhale mtundu watsopano. Motero m’chaka cha 33 C.E., mpingo wachikhristu wa odzozedwa a Yehova unayambika. Mpingo umenewu ndi umene unali mtundu watsopano wolamulidwa ndi Yehova. Paulo anati mtundu umenewu ndi “Isiraeli wa Mulungu.”​—Agal. 6:16.

11, 12. Fotokozani kufanana ndiponso kusiyana pakati pa oyang’anira a Isiraeli ndi a “Isiraeli wa Mulungu.”

11 Pali zinthu zina zomwe ndi zosiyana ndiponso zina zomwe ndi zofanana pakati pa mtundu woyamba wa Isiraeli wakale ndi ‘Isiraeli watsopano wa Mulungu.’ Mwachitsanzo, Isiraeli wakale ankakhala ndi mfumu ndipo anthu akachimwa ankapereka nsembe za nyama. Izi sizichitika mumpingo wachikhristu. Koma mofanana ndi Isiraeli wakale, mumpingo wachikhristu mumakhala akulu. (Eks. 19:3-8) Ntchito ya akulu amenewa si kulamulira nkhosa. M’malomwake amaweta mpingo ndipo amatsogolera ntchito zachikhristu mwakhama. Iwo amasamalira mwachikondi ndiponso kulemekeza munthu aliyense mumpingo.​—2 Akor. 1:24; 1 Pet. 5:2, 3.

12 Kuganizira mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi Aisiraeli, kumathandiza “Isiraeli wa Mulungu” ndiponso a “nkhosa zina” kuti aziyamikira Yehova ndiponso mmene amalamulirira. (Yoh. 10:16) Mwachitsanzo, zimene zinachitika pakati pa Aisiraeli zimasonyeza kuti mafumu ankachititsa anthu kuchita zinthu zabwino kapena zoipa. Mfundo imeneyi imathandiza oyang’anira mumpingo wachikhristu kuzindikira kuti, ngakhale kuti iwo si olamulira ngati mafumu akale, ayenera kuyesetsa kupereka chitsanzo chabwino nthawi zonse.​—Aheb. 13:7.

Kodi Yehova Akulamulira Bwanji Masiku Ano?

13. Kodi ndi chinthu chofunika kwambiri chiti chimene chinachitika mu 1914?

13 Masiku ano Akhristu amalalikira padziko lonse kuti ulamuliro wa anthu watsala pang’ono kutha. Mu 1914, Yehova anakhazikitsa Ufumu wake kumwamba ndipo anasankha Yesu Khristu kukhala Mfumu ya Ufumuwo. Pa nthawi imeneyi iye anapatsa Yesu mphamvu kuti apite “kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake.” (Chiv. 6:2) Ndipo anauza Mfumu yatsopanoyi kuti: “Chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Sal. 110:2) N’zomvetsa chisoni kuti mitundu ya anthu ikupitirizabe kukana ulamuliro wa Yehova. Iwo akungochitabe zinthu ngati “kulibe Mulungu.”​—Sal. 14:1.

14, 15. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu umatilamulira bwanji masiku ano, ndipo tiyenera kudzifunsa mafunso ati pa nkhani imeneyi? (b) Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zimene zikusonyeza kuti ulamuliro wa Mulungu ndi wapamwamba kwambiri?

14 M’gulu la ‘Isiraeli wa Mulunguli,’ muli Akhristu odzozedwa ochepa amene atsala ndipo monga abale a Khristu iwo akupitirizabe kuchita zinthu monga “akazembe m’malo mwa Khristu.” (2 Akor. 5:20) Iwo ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene amasamalira ndiponso kupereka chakudya chauzimu kwa odzozedwa komanso kwa khamu lalikulu. Panopa anthu a khamu lalikululi akuwonjezereka ndipo alipo mamiliyoni ambiri. Chiyembekezo chawo n’chodzakhala padziko lapansi kosatha. (Mat. 24:45-47; Chiv. 7:9-15) Akhristu oona akusangalala mwauzimu ndipo uwu ndi umboni wakuti Yehova akudalitsa dongosolo limeneli.

15 Aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikukwaniritsa udindo wanga mumpingo wachikhristu? Kodi ndikuchirikiza ulamuliro wa Yehova m’njira yoyenera? Kodi ndimanyadira kukhala nzika ya Ufumu wa Yehova umene ukulamulira? Kodi ndimafunitsitsa kuuza ena za Ufumu wa Mulungu mmene ndingathere?’ Monga gulu, timamvera ndi mtima wonse malangizo a Bungwe Lolamulira amene timalandira kudzera mwa akulu mumpingo. Tikamatero timasonyeza kuti tikulola kulamulidwa ndi Mulungu. (Werengani Aheberi 13:17.) Kumvera kumeneku kumathandiza kuti pakhale mgwirizano pakati pa Akhristu ndipo izi ndi zosowa kwambiri m’dzikoli limene anthu sagwirizana. Kumachititsanso kuti pakhale mtendere ndi chilungamo. Izi zimalemekeza Yehova ndipo zimasonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino koposa.

Ulamuliro wa Yehova Udzapambana

16. Pa nkhani ya ulamuliro, kodi aliyense ayenera kusankha chiyani masiku ano?

16 Nthawi yatsala pang’ono yoti nkhani zonse zimene zinayambitsidwa m’munda wa Edeni zithetsedwe. Motero ino ndi nthawi yoti aliyense asankhe kaya kulamulidwa ndi Yehova kapena anthu. Ifeyo tili ndi mwayi wothandiza anthu odzichepetsa kusankha mwanzeru. Posachedwapa, pa Armagedo, ulamuliro wa Yehova udzalowa m’malo mwa maboma a anthu otsogoleredwa ndi Satana. (Dan. 2:44; Chiv. 16:16) Ulamuliro wa anthu udzatha ndipo Ufumu wa Mulungu udzalamulira padziko lonse lapansi. Apa m’pamene zidzatsimikizirike kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.​—Werengani Chivumbulutso 21:3-5.

17. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingathandize anthu odzichepetsa kusankha bwino pa nkhani ya ulamuliro?

17 Anthu amene sanasankhebe kulamulidwa ndi Yehova ayenera kupemphera ndiponso kuganizira bwinobwino zinthu zabwino zimene ulamuliro wa Mulungu udzachitire anthu. Ulamuliro wa anthu walephera kuthetsa upandu ndi uchigawenga, koma ulamuliro wa Mulungu udzachotsa oipa onse padziko lapansi. (Sal. 37:1, 2, 9) Ulamuliro wa anthu wabweretsa nkhondo zoopsa, koma ulamuliro wa Mulungu ‘udzaletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’ (Sal. 46:9) Ndiponso ulamuliro wa Mulungu udzachititsa kuti anthu ndi nyama akhale pamtendere ngati mmene zinalili poyamba. (Yes. 11:6-9) Mu ulamuliro wa Mulungu simudzakhala njala ndi umphawi monga mmene zakhalira mu ulamuliro wa anthu. (Yes. 65:21) Ngakhale atsogoleri ofunadi kusintha zinthu alephera kuthetsa matenda ndi imfa. Koma mu ulamuliro wa Mulungu okalamba ndi odwala adzakhalanso ndi mphamvu ngati anyamata. (Yobu 33:25; Yes. 35:5, 6) Dziko lapansi lidzakhala paradaiso ndipo anthu amene anamwalira adzaukitsidwa.​—Luka 23:43; Mac. 24:15.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira kuti ulamuliro wa Mulungu ndiye wabwino koposa?

18 Zoonadi, ulamuliro wa Mulungu udzathetsa mavuto onse amene Satana anayambitsa pamene anachititsa makolo athu oyamba kupandukira Mlengi wawo. Ndipo taganizirani izi, Satana wabweretsa mavuto kwa zaka 6,000 koma chochititsa chidwi n’chakuti, Mulungu adzagwiritsa ntchito Khristu kuthetsa mavuto onsewa kwa zaka 1,000 zokha. Umenewutu ndi umboni wosatsutsika wakuti ulamuliro wa Mulungu sungafanane ndi ulamuliro wina uliwonse. Popeza ndife Mboni za Mulungu wathu, timavomereza kuti iye azitilamulira. Motero tiyeni tsiku lililonse tizisonyeza kuti ndife atumiki a Yehova komanso nzika za Ufumu wake ndipo tizinyadira kuti ndife Mboni zake. Tiyeni tizigwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene tingapeze kuuza aliyense amene angatimvetsere, kuti ulamuliro wa Yehova ndiwo wabwino koposa.

Pa Nkhani ya Ulamuliro wa Mulungu, Fotokozani Zimene Mwaphunzira pa Malemba Awa:

Deuteronomo 7:7, 8.

1 Samueli 8:9-18.

Aheberi 13:17.

Chivumbulutso 21:3-5.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 29]

Yehova wakhala akulamulira nthawi zonse

[Chithunzi patsamba 31]

Kugonjera ulamuliro wa Yehova kumachititsa kuti tizigwirizana padziko lonse