Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhala Oona Mtima Nthawi Zonse?

Kodi Muyenera Kukhala Oona Mtima Nthawi Zonse?

Kodi Muyenera Kukhala Oona Mtima Nthawi Zonse?

MUNTHU aliyense amachita zinthu moona mtima nthawi zina; ndipo mwina ambiri amatero nthawi zambiri. Koma kodi ndi anthu angati amene mukuwadziwa omwe amayesetsa kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse?

Masiku ano anthu ambiri sakonda kuchita zinthu moona mtima. Komabe, ambiri amadziwa mmene Mulungu amaonera nkhaniyi. Mwachitsanzo, anthu ambiri amadziwa lamulo lakuti “usabe,” lomwe ndi limodzi mwa Malamulo Khumi. (Eksodo 20:15) Koma anthu ambiri amaganiza kuti nthawi zina kuba kapena kuchita zinthu zina mosaona mtima si kulakwa. Tiyeni tione zitsanzo zitatu za kuba kumene nthawi zambiri anthu amaona kuti si kulakwa.

Kodi Kuba Chifukwa cha Umphawi Si Kulakwa?

Wandale wina wotchuka wa ku Rome ananena kuti: “Vuto lalikulu lomwe limachititsa anthu kuphwanya malamulo ndilo umphawi.” Munthu wosauka angaganize kuti palibe vuto ngati ataba. Anthu omuona angathenso kumumvetsa. Koma kodi Yesu ankaona bwanji nkhani imeneyi? N’zoona kuti Yesu ankamvera chisoni anthu ovutika. Baibulo limati: “Anawamvera chisoni.” (Mateyo 9:36) Komabe, iye sankagwirizana ngakhale pang’ono ndi maganizo oti nthawi zina kuba si kulakwa. Ndiyeno kodi munthu wosauka ayenera kutani?

Mulungu amakonda kwambiri anthu amene amayesetsa kumumvera, ndipo amawadalitsa akamachita khama kuti apeze zimene akufunikira. (Salmo 37:25) Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova sadzachititsa munthu wolungama kukhala ndi njala, koma zolakalaka za anthu oipa adzazikankhira kumbali.” (Miyambo 10:3, NW) Kodi munthu wosauka ayenera kudalira lonjezo limeneli?

Victorine ndi mayi wosauka amene sakayikira lonjezoli. Iye amakumana ndi mavuto ambiri chifukwa ndi wamasiye ndipo ali ndi ana asanu amene amapita kusukulu. Iye amakhala m’dziko losauka choncho salandira chithandizo chokwanira kuchokera ku boma. Chifukwa cha zimene amachita tsiku lililonse, m’posavuta kuti abe atafuna. Komabe, Victorine salola kuti agonjere mayeserowa. M’malomwake iye amayesetsa kukhala woona mtima ndipo amakhetsa thukuta lake kuti apeze chakudya pochita bizinezi. N’chifukwa chiyani amayesetsa kukhala woona mtima?

Iye anati: “Choyamba, ndimakhulupirira kuti Mulungu ndi woona mtima ndipo angapitirize kundidalitsa ngati nditatengera chitsanzo chake. Chachiwiri, ndimadziwa kuti ana anga angaphunzire kukhala oona mtima akamaona ineyo ndikuchita zomwezo.”

Kodi Victorine wapindula nazo zimenezi? Iye anati: “Timatha kupeza chakudya, zovala, komanso tili ndi pokhala. Komabe nthawi zina zinthu zikativuta, mwina wina akadwala mwadzidzidzi, timapempha thandizo kwa anzathu ena. Nthawi zonse timapeza zimene timafunikira. Zimenezi zimatheka chifukwa choti anzanga amadziwa kuti ndimawauza mavuto anga moona mtima ndipo sindimakokomeza vuto langa kuti ndipeze podyera.

“Ana anganso akuphunzira kukhala oona mtima. Mnzanga wina atabwera kunyumba kwanga anadabwa kuona kuti ndasiya ndalama zasiliva patebulo poti ana angathe kuba. Iye sanakhulupirire nditamuuza kuti ana anga sangabe. Ndiye anafuna kuti awayese anawo ine ndisakudziwa. Motero anaika ndalama zambiri pamalo oti anawo azione mosavuta. Atabwera mawa lake, anadabwa kwambiri kupeza kuti ndalama zija zidakali pomwepo. Kukhala ndi ana oona mtima ndi chinthu chosangalatsa kwambiri kuposa kukhala ndi katundu wambiri.”

“Aliyense Amaba”

Anthu amakonda kuba kuntchito kwawo. Chifukwa cha zimenezi, ambiri amayendera maganizo akuti, “Aliyense amaba, ndiye ine ndilekerenji?” Koma mosiyana ndi maganizo amenewa, Baibulo limati: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” (Eksodo 23:2) Victoire amatsatira malangizo amenewa. Ndiye kodi zimenezi zamuthandiza?

Iye ali ndi zaka 19 anayamba kugwira ntchito pa fakitale ina yoyenga mafuta kuchokera ku mbewu za kanjedza. Atangoyamba ntchitoyi iye anazindikira kuti amayi okwana 40 amene ankagwira nawo ntchito ankaba mbewu za kanjedza kuntchitoko pozibisa m’mabasiketi awo. Kumapeto a mlungu uliwonse iwo ankagulitsa mbewuzo ndipo ankatha kupeza ndalama zofanana ndi malipiro a masiku atatu kapena anayi. Victoire anati: “Aliyense ankachita zimenezi. Iwo anandinyengerera kuti ndiziba nawo koma ndinakana ndipo ndinawauza kuti ndimayesetsa kukhala woona mtima nthawi zonse. Nditawauza zimenezi anayamba kundinyoza n’kumati ndine wogona.

“Tsiku lina tikuweruka abwana anthu anatulukira mwadzidzidzi. Iwo anayamba kusecha m’mabasiketi athu ndipo anapeza mbewu za kanjedza m’basiketi ya wina aliyense kupatulapo yanga yokha. Onse amene anagwidwa anauzidwa kuti awachotsa ntchito kapena agwira ntchito kwa milungu iwiri popanda kulandira malipiro. Pa milungu iwiri imeneyi iwo anadziwa kuti si ndine wogona ayi.”

“Sapatsa Pamanja”

Kodi mumamva bwanji mukatola chinachake chamtengo wapatali chimene wina wataya? Anthu ambiri akangotola chinthu chotere amayamba kuganiza kuti ndi chawo basi ndipo saganizira zobweza chinthucho kwa mwini wake. Iwo amakhala ndi maganizo akuti “sapatsa pamanja.” Ena angaone kuti palibe vuto kuchita zimenezi chifukwa mwiniwakeyo amakhala atasayina kale kuti chinthu chakecho chatayika. Enanso amati sangadzilembe ntchito yofufuza mwini wa chinthu chimene atola chifukwa si udindo wawo.

Koma kodi Mulungu amaona bwanji nkhani imeneyi? Lemba la Deuteronomo 22:1-3 limasonyeza kuti Mwisiraeli amene watola chinachake sikuti ankangofunikira kuchisunga basi, koma ankayenera kuchisunga ‘kufikira mwiniwakeyo atafika kudzachifufuza ndipo azim’bwezera.’ (NW) Nthawi imeneyo munthu akatola chinthu chinachake n’kusawadziwitsa anthu ena, ankaimbidwa mlandu wakuba. (Eksodo 22:9) Kodi masiku ano kubweza zimene tatola n’kofunika? Christine ali ndi umboni wotsimikizira kuti zimenezi n’zofunika.

Christine amayang’anira sukulu ina yomwe si yaboma. Tsiku lina mwezi utatha, analandira malipiro ake. Iye anaika ndalama zake zonse zija m’chikwama chake, monga mmene amachitira anthu ambiri kumaiko a kumadzulo kwa Africa. Kenako iye anakwera njinga yamoto yamatola kuti ikamusiye kumsonkhano. Atafika kumeneko anatsegula chikwama chija kuti atenge ndalama zasiliva zoti alipire wanjinga uja. Akutsegula chikwamacho mpukutu wa ndalama uja unagwera pansi koma iye sanadziwe chifukwa kunali mdima.

Patangodutsa kanthawi kochepa, mnyamata wina wa zaka 19, dzina lake Blaise, anadutsa pamalopa. Mnyamatayu anangobwera kudzacheza kumaloku. Iye anali atapangana ndi mnzake wina kuti adzakumane kumsonkhano kumene Christine anapita. Blaise anaona ndalama zija ndipo anazitola n’kuzisunga m’thumba mwake. Msonkhanowo utatha, iye anamuuza mnzake uja kuti watola zinazake kunja kwa nyumba imene ankachitira msonkhanoyo ndipo aliyense amene wataya chinachake amuimbire foni ndi kufotokoza zimene wataya.

Christine atafika kunyumba kwake, anasokonezeka maganizo atapeza kuti malipiro ake aja atayika. Patapita mlungu umodzi iye anamuuza mnzake wina, dzina lake Josephine, za nkhaniyi. Josephine anamuuza kuti mlendo wina amene anabwera kumsonkhano kuja ananena kuti watola zinazake. Choncho, Christine anaimbira foni Blaise ndipo anamufotokozera ndalama zimene anataya. Iye anasangalala kwambiri Blaise atadzam’bwezera ndalama zake zonse. Kodi Blaise anapeza phindu lanji? Iye anali atasunga ndalamazi kwa mlungu umodzi, ndipo anati, “Nditabweza ndalamazo ndinasangalala kwambiri kusiyana ndi mmene ndinkangozisunga.”

N’chifukwa Chiyani Amayesetsa Kukhala Oona Mtima Nthawi Zonse?

Victorine, Victoire, ndi Blaise amakhala kosiyana ndipo sadziwana. Komabe onsewa ndi ofanana pa chinthu chimodzi. Iwo ndi Mboni za Yehova, ndipo amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kukhala oona mtima. Iwo akuyembekezera dziko latsopano limene Mulungu analonjeza. “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” Anthu onse amene adzakhalepo panthawi imeneyi adzakhala achilungamo ndiponso oona mtima.​—2 Petulo 3:13.

Victorine amaona kuti n’zokayikitsa kuti panopo zinthu zingayambe kumuyendera bwino n’kumapeza ndalama zambiri, koma amadziwa kuti zonse zidzamuyendera bwino kwambiri Mulungu akadzasintha zinthu padzikoli. Komabe, iye ali ndi chuma chauzimu, chomwe munthu sangachipeze ndi ndalama. Ana ake ndi oona mtima ndiponso ndi akhalidwe labwino. Lamlungu lililonse iwo amasangalala kwambiri akamauza anthu ena zinthu zabwino zimene Mulungu amachita ndi kuwafotokozera lonjezo lake lakuti iye adzasamalira “onse akuitanira kwa Iye m’choonadi” ndipo adzateteza “onse akukondana naye.”​—Salmo 145:7, 18, 20.

Patapita nthawi, Victoire anasiya ntchito pa fakitale yoyenga mafuta ija. Anayamba bizinesi yake yogulitsa ufa wachinangwa pamsika. Iye anapeza makasitomala ambiri chifukwa cha kuona mtima kwake. Moti posakhalitsa anachepetsa nthawi imene ankakhala kumsika n’kuyamba kuthera nthawi yake yambiri pouza ena za chiyembekezo chodzakhala m’dziko lopanda khalidwe losaona mtima. Kenako anakwatiwa ndipo panopo akuchita utumiki wa nthawi zonse pamodzi ndi mwamuna wake.

Kumene Christine anataya ndalama zake kuja kunali ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Blaise sankadziwa anthu ambiri amene anabwera ku Nyumba ya Ufumuyo koma ankadziwa kuti iwo anali abale ndi alongo ake achikhristu omwe amayesetsa kukhala oona mtima nthawi zonse.

Kodi mukudziwa anthu angati amene amayesetsa kukhala oona mtima nthawi zonse? Tangoganizirani mmene zingakhalire mutamakhala ndi anthu 50, 100, kapena 200 amene amayesetsa kukhala oona mtima nthawi zonse. Umu ndi mmene zimakhalira mukapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Mungachite bwino kudzapitako nthawi ina kuti mukadzionere nokha.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Kukhala ndi ana oona mtima ndi chinthu chosangalatsa kwambiri kuposa kukhala ndi katundu wambiri.”​—VICTORINE

[Bokosi patsamba 14]

Kodi Lemba la Miyambo 6:30 Limaloleza Kuba?

Lemba la Miyambo 6:30 limati: “Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala.” Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti kuba uli ndi njala sikulakwa? Ayi. Mawu a m’mavesi oyandikana ndi vesili akusonyeza kuti Mulungu amaonabe kuti wakubayo ndi woyenera kuimbidwa mlandu. Vesi 31 limati: “Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.” (Miyambo 6:31) Munthu amene waba chifukwa cha njala angamveredwe chisoni kusiyana ndi amene waba chifukwa cha dyera kapena ndi cholinga chofuna kuvutitsa ena. Komabe wakuba chifukwa cha njalayo amaimbidwabe mlandu ndipo amafunikira ‘kubweza’ zimene anabazo. Anthu amene akufunitsitsa kuti Mulungu aziwakonda sayenera kuba ngakhale zinthu zitavuta chotani.