Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”

“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”

“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”

“Panthawi imeneyo olungama adzawala ngwee ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.”​—MAT. 13:43.

1. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza mbali zosiyanasiyana ziti za Ufumu?

YESU KHRISTU anagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza mbali zosiyanasiyana za Ufumu. Iye ‘analankhula ndi khamu la anthu m’mafanizo. Ndithudi, sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo.’ (Mat. 13:34) M’mafanizo a kufesa mbewu za Ufumu, Yesu anatsindika za udindo umene munthu amakhala nawo kuti mtima wake ulandire uthenga. Anatsindikanso zimene Yehova amachita kuti mbewuzo zikule mwauzimu. (Maliko 4:3-9, 26-29) Yesu anaperekanso fanizo logwira mtima lokhudza kuwonjezeka kwa anthu amene amamva uthenga wa Ufumu ngakhale kuti izi sizionekera nthawi yomweyo. (Mat. 13:31-33) Iye anasonyezanso kuti si anthu onse amene amalandira uthenga wa Ufumu amene amakhala nzika za Ufumuwo.​—Mat. 13:47-50. *

2. M’fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole, kodi mbewu yabwino ikuimira chiyani?

2 Koma fanizo lina la Yesu limafotokoza kwambiri za kusonkhanitsa anthu amene adzalamulira naye mu Ufumu wake kumwamba. Fanizoli limatchedwa fanizo la tirigu ndi namsongole ndipo lili pa Mateyo chaputala 13. M’fanizo lina Yesu ananena kuti mbewu zofesedwa, zikuimira “mawu a ufumu” koma mu fanizoli iye anati mbewu zabwino zikuimira “ana a ufumu.” (Mat. 13:19, 38) Iwo si nzika za Ufumu koma ndi “ana” kapena kuti olandira cholowa cha Ufumu.​—Aroma 8:14-17, werengani Agalatiya 4:6, 7.

Fanizo la Tirigu ndi Namsongole

3. Fotokozani vuto limene munthu wa m’fanizoli anakumana nalo, nanga anati athana nalo bwanji?

3 Fanizolo limati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake. Koma anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake ndi kudzafesa udzu [kapena kuti namsongole] m’munda wa tiriguwo, ndi kuchoka. Tsopano mmerawo utakula ndi kutulutsa ngala, udzu nawonso unaonekera. Ndiye kunabwera akapolo a mwini munda nati kwa iye, ‘Mbuye, kodi simunafese mbewu zabwino m’munda wanuwu? Nanga udzuwu wachokeranso kuti?’ Iye anati kwa iwo, ‘Munthu wina wodana nane anachita zimenezi.’ Iwo anati kwa iye, ‘Tsopano kodi mukufuna kuti tipite kukam’zula?’ Iye anati, ‘Ayi; kuopera kuti mwina pozula udzu, mungazule pamodzi ndi tirigu. Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola; ndipo m’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani udzu ndi kuumanga m’mitolo kuti ukatenthedwe, ndipo mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.’”​—Mat. 13:24-30.

4. (a) Kodi munthu wa m’fanizoli ndi ndani? (b) Ndi liti pamene Yesu anayamba kufesa mbewu, ndipo kodi anachita zimenezi motani?

4 Kodi munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake ndi ndani? Yesu anayankha funso limeneli pamene ankafotokoza tanthauzo la fanizoli kwa ophunzira ake. Iye anati: “Wofesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu.” (Mat. 13:37) Yesu yemwe ndi “Mwana wa munthu” ankalima munda pa zaka zitatu ndi theka za utumiki wake padziko lapansi. (Mat. 8:20; 25:31; 26:64) Ndiyeno kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E. iye anayamba kufesa mbewu zabwino zomwe ndi “ana a ufumu.” Kufesa kumeneku kunayambika pa nthawi imene Yesu, yemwe ndi woimira Yehova, anayamba kudzoza ophunzira ake ndi mzimu woyera kuti akhale ana a Mulungu. * (Mac. 2:33) Mbewu zabwinozi zinakula n’kukhala tirigu wokhwima bwino. Motero, cholinga cha kufesa mbewu zabwino, chinali chakuti asonkhanitse anthu okwanira kudzakhala olandira cholowa ndiponso mafumu limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake.

5. Mu fanizo la Yesu, kodi mdani akuimira ndani, nanga namsongole akuimira ndani?

5 Kodi mdani akuimira ndani, ndipo namsongole akuimira ndani? Yesu ananena kuti mdaniyo “ndi Mdyerekezi.” Ndipo anati namsongole ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:25, 38, 39) Namsongole amene Yesu ankanena, ndi mtundu wa udzu woipa kwambiri umene ukakhala waung’ono umafanana kwambiri ndi tirigu. Ilitu ndi fanizo labwino kwambiri pofotokoza za anthu amene amanamizira kuti ndi ana a Ufumu koma sabala zipatso zabwino. Akhristu onyenga amenewa, amanamizira kuti ndi otsatira Khristu koma zoona zake n’zakuti iwo ndi mbali ya “mbewu” ya Satana Mdyerekezi.​—Gen. 3:15.

6. Kodi namsongole anaonekera liti, ndipo kodi anthu anagona motani panthawi imeneyo?

6 Kodi anthu ofanana ndi namsongolewa anayamba liti kuonekera? Yesu anati: “Anthu ali m’tulo.” (Mat. 13:25) Kodi zimenezi zinachitika liti? Yankho la funso limeneli tikulipeza m’mawu amene Paulo anauza akulu a ku Efeso. Iye anati: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzalowa pakati panu ndipo siidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati pa inu nomwe padzauka anthu amene adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti akanganule ophunzira aziwatsatira.” (Mac. 20:29, 30) Iye analangizanso akulu amenewa kuti akhale maso mwauzimu. Atumwi amene anali ngati “choletsa” mpatuko atagona mu imfa, Akhristu ambiri anagona mwauzimu. (Werengani 2 Atesalonika 2:3, 6-8.) Apa m’pamene panayambira mpatuko waukulu.

7. Kodi tirigu wina anasintha n’kukhala namsongole? Fotokozani.

7 Yesu sananene kuti tirigu adzasintha n’kukhala namsongole koma anati namsongole anafesedwa m’munda wa tirigu. Choncho fanizoli silikunena za Akhristu oona amene agwa m’choonadi. Koma likunena za zimene Satana wachita n’cholinga chofuna kuipitsa mpingo wachikhristu mwa kulowetsa anthu oipa mumpingomo. Panthawi imene mtumwi Yohane anali wokalamba, mpatuko umenewo n’kuti utayamba kale kuonekera.​—2 Pet. 2:1-3; 1 Yoh. 2:18.

“Zilekeni Zonse Zikulire Pamodzi Mpaka Nthawi Yokolola”

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani zimene mwini munda uja ananena zinali zomveka kwa anthu amene anamva fanizo la Yesu? (b) Pa kukwaniritsidwa kwa fanizoli, kodi tirigu ndi namsongole zinakulira limodzi motani?

8 Akapolo a mwini munda anamuuza za vutoli ndipo anamufunsa kuti: “Tsopano kodi mukufuna kuti tipite kukam’zula?” (Mat. 13:27, 28) N’kutheka kuti akapolowo anadabwa ndi zimene mwini mundayo anawayankha. Iye anawauza kuti aleke tirigu ndi namsongole zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Kwa ophunzira a Yesu, zimene ananena mwini mundazi zinali zomveka. Iwo ankadziwa kuti zimakhala zovuta kwambiri kusiyanitsa tirigu ndi namsongole. Anthu amene anali alimi ankadziwanso kuti mizu ya namsongole imapiringizana ndi ya tirigu. * N’chifukwa chake mwini munda uja anawauza kuti adikire.

9 Mofanana ndi zimenezi, kwa zaka zambiri magulu a Matchalitchi Achikristu chonyenga akhala akuchulukirachulukira. Poyamba m’matchalitchi Akatolika ndi a Orthodox ndipo kenako m’magulu ambirimbiri achipolotesitanti. Koma pa nthawi yomweyi padziko lonse mbewu za tirigu zinafesedwa. M’fanizo limeneli, mwini mundayu anadikira kwanthawi ndithu mpaka nyengo yokolola itafika.

Nyengo Yokolola Imene Anthu Ankaiyembekezera

10, 11. (a) Kodi nthawi yokolola ndi iti? (b) Kodi tirigu wophiphiritsayu akusonkhanitsidwa bwanji munkhokwe ya Yehova?

10 Yesu ananena kuti: “Nthawi yokolola ndi mapeto a dongosolo lino la zinthu, ndipo okololawo ndi angelo.” (Mat. 13:39) M’masiku otsiriza ano a dongosolo lino la zinthu, ntchito yosiyanitsa anthu ikuchitika. Ana a Ufumu akusonkhanitsidwa ndipo akusiyanitsidwa ndi anthu omwe ali ngati namsongole. Pa nkhani imeneyi, mtumwi Petulo ananena kuti: “Ino ndiyo nthawi yoikika yakuti chiweruzo chiyambe, ndipo chiyambira pa nyumba ya Mulungu. Tsopano ngati chiyambira pa ife, ndiye mapeto a anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu adzakhala otani?”​—1 Pet. 4:17.

11 Masiku otsiriza kapena kuti “mapeto a dongosolo lino la zinthu” atangoyamba, chiweruzo chinayamba pa anthu amene ankati ndi Akhristu oona, kuti zidziwike ngati alidi “ana a Ufumu” kapena “ana a woipayo.” Kumayambiriro kwa nyengo yokolola, Babulo wamkulu anagwa ndipo kenako ana a Ufumu anasonkhanitsidwa. (Mat. 13:30) Koma kodi tirigu wophiphiritsayu akusonkhanitsidwa bwanji munkhokwe ya Yehova? Ena mwa anthu amenewa, akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu ndipo amayanjidwa ndiponso kutetezedwa ndi Mulungu. Ena akulandira mphoto yawo kumwamba.

12. Kodi kukolola kuchitika kwa nthawi yaitali bwanji?

12 Kodi chiweruzo chichitika kwa nthawi yaitali bwanji? Mawu akuti “nyengo” amene Yesu anagwiritsa ntchito ponena za kukolola, akusonyeza kuti ndi nthawi yaitali ndithu. (Chiv. 14:15, 16) Kuweruza munthu aliyense amene ali m’gulu la odzozedwa kukupitirirabe nthawi yonse yamapeto. Kudzatha pa nthawi imene odzozedwa onse adzasindikizidwa chizindikiro.​—Chiv. 7:1-4.

13. Kodi namsongole akupunthwitsa anthu m’njira yotani, ndipo amachita zinthu zosamvera malamulo motani?

13 Kodi ndi ndani amene adzachotsedwa mu Ufumu, ndipo amachita zinthu zopunthwitsa komanso zosamvera malamulo motani? (Mat. 13:41) Atsogoleri a Matchalitchi Achikristu amene ali ngati namsongole akhala akusocheretsa anthu kwa zaka zambiri. Iwo achita zimenezi mwa kuphunzitsa anthu mfundo zonyoza Mulungu zomwe zili ngati “zinthu zopunthwitsa.” Zina mwa mfundo zimenezi ndi chiphunzitso chakuti anthu amakaotchedwa kwamuyaya ndiponso chiphunzitso chosamvetsetseka cha Utatu. Atsogoleri azipembedzo ambiri akupereka chitsanzo choipa kwa anthu awo. Iwo akuchita zimenezi mwa kuchita ubwenzi ndi dziko ndiponso mwa khalidwe lawo loipa la chiwerewere. (Yak. 4:4) Chinanso n’chakuti Matchalitchi Achikhristu amalekerera khalidwe lotayirira. (Werengani Yuda 4.) Ngakhale zili choncho, iwo amadzionetsera ngati anthu opembedza. Ana a Ufumu ndi osangalala kwambiri chifukwa chakuti akusiyanitsidwa ndi anthu angati namsongole amenewa ndipo sakutsatira ziphunzitso zabodza zomwe ndi zopunthwitsa.

14. Kodi anthu angati namsongole amalira ndi kukukuta mano motani?

14 Kodi anthu angati namsongole amalira ndi kukukuta mano motani? (Mat. 13:42) “Ana a woipayo” amalira ndi kukukuta mano chifukwa chakuti “ana a ufumu” avumbula ziphunzitso zoipa za anthu angati namsongolewa. Iwo amaliranso chifukwa chakuti anthu awo sakuwachirikiza ndipo sakuwamveranso ngati kale.​—Werengani Yesaya 65:13, 14.

15. Kodi anthu angati namsongolewa adzatenthedwa motani?

15 Kodi anthu angati namsongolewa adzasonkhanitsidwa n’kutenthedwa motani? (Mat. 13:40) Izi zikuimira zimene zidzachitikira namsongoleyu pamapeto. Mfundo yakuti iwo adzaponyedwa m’ng’anjo ya moto ikusonyeza kuti iwo adzawonongedwa kosatha. (Chiv. 20:14; 21:8) Anthu angati namsongole, amene amanamizira kuti ndi Akhristu, adzawonongedwa pa “chisautso chachikulu.”​—Mat. 24:21.

“Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”

16, 17. Kodi Malaki analosera chiyani zokhudza kachisi wa Mulungu wauzimu, ndipo zimenezi zinayamba liti kukwaniritsidwa?

16 Kodi ndi liti pamene anthu omwe ali ngati tirigu “adzawala ngwee ngati dzuwa”? (Mat. 13:43) Ponena za kuyeretsa kachisi wa Mulungu, Malaki analosera kuti: “Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu. Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka; ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.”​—Mal. 3:1-3.

17 Kukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi umenewu kunayamba mu 1918 pamene Yehova ndi Yesu Khristu, yemwe ndi “mthenga wa chipangano,” anayendera kachisi wauzimu. Malaki ananenanso zotsatira za kuyenderaku. Iye anati: “Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Mal. 3:18) Kuwonjezereka kwa ntchito imene Akhristu oona akugwira, kukusonyeza kuti nyengo yokolola inayamba nthawi imeneyi.

18. Kodi Danieli analosera kuti n’chiyani chidzachitika m’masiku athu ano?

18 Mneneri Danieli analosera za masiku athu ano kuti: “Aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi ku nthawi za nthawi.” (Dan. 12:3) Kodi amene akuwalawa ndi ndani? Amenewa si enanso koma Akhristu odzozedwa omwe ndi tirigu weniweni amene Yesu ankanena mu fanizo lake la tirigu ndi namsongole. Khamu lalikulu la anthu okhala ngati nkhosa limene likuwonjezekabe, likuona ‘kuchotsedwa’ kwa anthu okhala ngati namsongole amene amanamizira kuti ndi Akhristu. Akhamu lalikulu amenewa, omwe akuyembekezera kudzakhala nzika za Ufumu, amawalanso m’dziko la mdimali chifukwa chakuti agwirizana ndi otsalira a Isiraeli wauzimu.​—Zek. 8:23; Mat. 5:14-16; Afil. 2:15.

19, 20. Kodi “ana a ufumu” akuyembekezera chiyani ndipo tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Panopa, “ana a ufumu” akuyembekezera mphoto yawo ya ulemerero kumwamba. (Aroma 8:18, 19; 1 Akor. 15:53; Afil. 1:21-24) Mpaka nthawi imeneyo, iwo ayenera kukhalabe okhulupirika, kupitirizabe kuwala kwambiri ndiponso kukhalabe osiyana ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:38; Chiv. 2:10) Ndife osangalala kwambiri kuona zotsatira za ‘kuchotsedwa’ kophiphiritsira kwa namsongole nthawi yathu ino.

20 Khamu lalikulu la anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi kosatha monga nzika za Ufumu likuwonjezeka. Koma kodi pali kugwirizana kotani pakati pa khamu limeneli ndi ana a Ufumu? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mafanizo amenewa onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008 tsamba 12 mpaka 21.

^ ndime 4 M’fanizo limeneli kufesa sikukutanthauza ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira imene imathandiza kuti anthu atsopano akhale Akhristu odzozedwa. Ponena za mbewu zabwino zimene zinafesedwa m’munda Yesu anati: Mbewuzi “ndi ana a ufumu.” Iye sanati “adzakhala” ana a ufumu. Choncho, kufesa kukutanthauza kudzoza ana a Ufumuwo padziko lapansi.

^ ndime 8 Mizu ya namsongole imapiringizana kwambiri ndi mizu ya tirigu moti ngati munthu atayesa kuzula namsongole nthawi yokolola isanafike, akhoza kuwononga tirigu.​—Onani Insight on the Scriptures, Volume 1, tsamba 1178.

Kodi Mukukumbukira?

M’fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole, kodi zinthu izi zikuimira chiyani?

• Mbewu zabwino

• Munthu amene anafesa mbewu

• Kufesa mbewu

• Mdani

• Namsongole

• Nyengo yokolola

• Nkhokwe

• Kulira ndi kukukuta mano

• Ng’anjo ya moto

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Kufesa mbewu zabwino kunayamba pa Pentekosite mu 33 C.E.

[Chithunzi patsamba 23]

Panopa tirigu wophiphiritsira akusonkhanitsidwa munkhokwe ya Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.