Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Gulu Limodzi, Mbusa Mmodzi

Gulu Limodzi, Mbusa Mmodzi

Gulu Limodzi, Mbusa Mmodzi

“Inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.”​—MAT. 19:28.

1. Kodi mbadwa za Abrahamu zinali paubwenzi wotani ndi Yehova, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti iye ankasamalanso anthu amitundu ina?

YEHOVA anasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mbadwa za Abrahamu chifukwa chakuti ankakonda Abrahamuyo. Kwa zaka zoposa 1,500 iye ankaona kuti mtundu wa Isiraeli, womwe unali mbadwa za Abrahamu, unali anthu ake apadera, mtundu wa “iye yekha.” (Werengani Deuteronomo 7:6.) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sankasamala n’komwe anthu amitundu ina? Ayi, chifukwa pa zaka zonsezi, anthu amene sanali Aisiraeli koma ankafuna kulambira Yehova, ankaloledwa kukhala m’gulu la anthu omwe anali mtundu wapaderawa. Anthu otembenukira ku Chiyuda amenewa, ankaonedwa kuti ndi mbali ya mtunduwu. Choncho, Aisiraeli anafunika kuwaona anthu amenewa monga abale awo. (Lev. 19:33, 34) Ndipo anthu amenewa ankafunika kumvera malamulo onse a Yehova.​—Lev. 24:22.

2. Kodi ndi mawu odabwitsa ati amene Yesu anena, ndipo kodi zimenezi zikubweretsa mafunso ati?

2 Komabe, zimene Yesu anauza Ayuda a m’nthawi yake zinali zodabwitsa. Iye anati: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) Kodi ndani anali kudzakhala mtundu wa tsopano umenewu, nanga zimenezi zikutikhudza bwanji masiku ano?

Mtundu Watsopano

3, 4. (a) Kodi mtumwi Petulo anaufotokoza bwanji mtundu watsopano? (b) Kodi ndani amene ali mumtundu watsopanowu?

3 Mtumwi Petulo anafotokoza bwino za mtundu watsopanowu. Iye analembera Akhristu anzake kuti: “Inu ndinu ‘fuko losankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze zabwino zopambana’ za amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9) Ulosi umasonyeza kuti Ayuda amene anavomereza zakuti Yesu ndi Mesiya, anali oyambirira kukhala mu mtundu watsopanowu. (Dan. 9:27a; Mat. 10:6) Kenako malinga ndi zimene Petulo ananena, anthu omwe sanali Aisiraeli anakhalanso m’gulu limeneli. Iye anati: “Pakuti kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.”​—1 Pet. 2:10.

4 Kodi pamenepa Petulo ankanena za ndani? Iye anayamba kalata yake ndi mawu akuti: “[Mulungu] anatibala mwatsopano kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu. Anatibala kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka ndi chosadetsedwa ndi chosasuluka. Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.” (1 Pet. 1:3, 4) Choncho, Akhristu odzozedwa amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, ndi amene ali mumtundu watsopanowu. Iwo ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Yohane anaona m’masomphenya kuti anthu 144,000 ndi amene amapanga Isiraeli wauzimu. Iwo “anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyamba zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa,” kuti akhale “ansembe” ndiponso kuti ‘adzalamulire monga mafumu limodzi ndi Yesu zaka 1,000.’​—Chiv. 5:10; 7:4; 14:1, 4; 20:6; Yak. 1:18.

Kodi Mtundu wa Isiraeli Umangoimira Akhristu Odzozedwa Okha?

5. (a) Kodi mawu akuti “Isiraeli wa Mulungu” amanena za ndani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu akuti “Isiraeli” sanena za odzozedwa okha?

5 N’zoonekeratu kuti mawu akuti “Isiraeli wa Mulungu” amene ali pa Agalatiya 6:16, amanena za Akhristu odzozedwa onse. Koma kodi Yehova amagwiritsanso ntchito mawu akuti Isiraeli, pofotokoza za anthu ena kuwonjezera pa Akhristu odzozedwa? Yankho la funso limeneli tingalipeze m’mawu amene Yesu anauza atumwi ake okhulupirika. Iye anati: “Ndikuchita nanu chipangano, mmene Atate wanga wachitira chipangano cha ufumu ndi ine, kuti mukadye ndi kumwa patebulo langa mu ufumu wanga, ndipo mukakhala m’mipando yachifumu kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.” (Luka 22:28-30) Zimenezi zidzachitika “panthawi ya kukonzanso zinthu” mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000.​—Werengani Mateyo 19:28.

6, 7. Kodi pa lemba la Mateyo 19:28 ndi Luka 22:30, mawu akuti “mafuko 12 a Isiraeli” akunena za ndani?

6 Anthu a 144,000 adzatumikira kumwamba monga mafumu, ansembe ndi oweruza mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. (Chiv. 20:4) Kodi iwo adzaweruza ndiponso kulamulira ndani? Malinga ndi Mateyo 19:28 ndiponso Luka 22:30, iwo adzaweruza “mafuko 12 a Isiraeli.” Kodi pa malemba amenewa “mafuko 12 a Isiraeli” akuimira ndani? Akuimira anthu onse amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala pa dziko lapansi. Anthu amenewa amakhulupirira nsembe ya Yesu koma sali m’gulu la ansembe achifumu. (Fuko la Levi silinkawerengedwa pa mndandanda wa mafuko 12 a Isiraeli wa kuthupi.) Pa malemba amenewa, mafuko 12 a Isiraeli akuimira anthu amene adzapindule mwauzimu ndi ntchito ya anthu 144,000 amene adzakhale ansembe. Ngakhale kuti anthu amenewa si ansembe, Mulungu amawaona kuti ndi anthu ake ndipo amawakonda. N’chifukwa chake amayerekezedwa ndi Aisiraeli omwe anali anthu ake.

7 Mpake kuti m’masomphenya, mtumwi Yohane ataona anthu 144,000 omwe ndi Isiraeli wauzimu atasindikizidwa chizindikiro chomaliza chisautso chachikulu chisanayambe, anaonanso “khamu lalikulu” losawerengeka “lochokera m’dziko lililonse.” (Chiv. 7:9) Khamu limeneli lidzapulumuka chisautso chachikulu ndipo lidzakhala mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000. Lidzakhalanso limodzi ndi anthu mabiliyoni ambiri amene adzaukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29; Chiv. 20:13) Anthu amene adzapulumuke chisautso chachikulu ndiponso omwe adzaukitsidwe, ndi amene adzapange “mafuko 12 a Isiraeli.” Anthu amenewa adzaweruzidwa ndi Yesu ndiponso anthu 144,000 amene adzalamulire naye.​—Mac. 17:31; 24:15; Chiv. 20:12.

8. N’chifukwa chiyani tingati zimene zinkachitika pa Tsiku la Chitetezo zinkaimira ubwenzi umene uli pakati pa a 144,000 ndi anthu ena onse?

8 Ubwenzi umene uli pakati pa a 144,000 ndi anthu ena onse unachitiridwa chithunzi ndi zimene zinkachitika pa Tsiku la Chitetezo. (Lev. 16:6-10) Choyamba, mkulu wa nsembe ankapereka ng’ombe monga nsembe yauchimo ‘yodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.’ Motero, nsembe ya Yesu choyamba ndi ya mbumba yake, omwe ndi ansembe aang’ono amene adzalamulire naye kumwamba. Pa Tsiku la Chitetezo, ankaperekanso mbuzi ziwiri chifukwa cha machimo a Aisiraeli ena omwe sanali ansembe. Choncho, fuko la ansembe limaimira a 144,000 ndipo Aisiraeli ena onse akuimira anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti mawu akuti “mafuko 12 a Isiraeli” pa Mateyo 19:28 akuimira anthu ena onse amene amakhulupirira nsembe ya Yesu, osati ansembe aang’ono a Yesu odzozedwa ndi mzimu. *

9. M’masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi, kodi ansembe ankaimira ndani, nanga mafuko a Aisiraeli omwe sanali ansembe ankaimira ndani?

9 Tiyeni tionenso chitsanzo china. Mneneri Ezekieli anaona m’masomphenya kachisi wa Yehova. (Ezekieli machaputala 40 mpaka 48) M’masomphenya amenewo ansembe ankagwira ntchito m’kachisi. Iwo ankalandira malangizo a Yehova komanso kulangiza anthu. (Ezek. 44:23-31) Anthu a mafuko osiyanasiyana ankabwera kudzalambira komanso kudzapereka nsembe. (Ezek. 45:16, 17) M’masomphenya amenewa, ansembe akuimira odzozedwa ndipo Aisiraeli omwe sanali ansembe akuimira anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Masomphenyawa akusonyeza mgwirizano umene ulipo pakati pa magulu awiriwa ndipo ansembe ndi amene amatsogolera pa kulambira koona.

10, 11. (a) Kodi tikuona kukwaniritsidwa kotani kwa mawu a Yesu? (b) Kodi ndi funso liti limene tingafunse lokhudza nkhosa zina?

10 Yesu ananena za “nkhosa zina” zomwe sizili ‘m’khola’ la “kagulu ka nkhosa” ka Akhristu odzozedwa. (Yoh. 10:16; Luka 12:32) Iye anati: “Zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi, m’busa mmodzi.” N’zolimbikitsa kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwa mawu amenewa. Magulu awiri aphatikizidwa. Kagulu ka odzozedwa kagwirizana ndi khamu lalikulu la nkhosa zina. (Werengani Zekariya 8:23.) A nkhosa zina satumikira m’bwalo la mkati la kachisi wauzimu, koma amatumikira m’bwalo la kunja kwa kachisiyu.

11 Popeza nthawi zina Yehova amagwiritsa ntchito anthu omwe sanali m’gulu la ansembe mu Isiraeli wakale akamanena za nkhosa zina, kodi ndiye kuti a nkhosa zina nawonso ayenera kudya zizindikiro pa Chikumbutso? Tiyeni tione yankho la funso limeneli.

Pangano Latsopano

12. Kodi Yehova analosera njira yatsopano iti?

12 Yehova analosera kuti adzagwiritsa ntchito njira yatsopano pochita zinthu ndi anthu ake. Iye anati: “Ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja. . . . Ndidzaika chilamulo changa m’kati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga.” (Yer. 31:31-33) Kudzera m’pangano limeneli, lonjezo limene Yehova anauza Abulahamu linali kudzakwaniritsidwa m’njira yochititsa chidwi.​—Werengani Genesis 22:18.

13, 14. (a) Ndani ali m’pangano latsopano? (b) Kodi ndani amene amapindula ndi panganoli ndipo kodi ‘amagwira bwanji zolimba’ panganoli?

13 Yesu anatchula za pangano limeneli usiku woti afa mawa lake. Iye anati: “Chikho ichi chikutanthauza chipangano chatsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.” (Luka 22:20; 1 Akor. 11:25) Kodi Akhristu onse ali m’pangano limeneli? Ayi. Anthu ena monga atumwi amene anamwa za m’chikho usiku umenewu, ndi amene ali m’pangano latsopanoli. * Yesu anachita nawo pangano lina lakuti adzalamulira naye mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30) Iwo adzakhala mafumu anzake a Yesu.​—Luka 22:15.

14 Nanga bwanji za anthu amene adzakhale padziko lapansi monga nzika za Ufumu wake? Iwo amapindula ndi pangano latsopanoli. (Agal. 3:8, 9) Ngakhale kuti sadya zizindikirozi, iwo ‘amagwira zolimba’ chipanganochi mwa kumvera zimene chimanena. Izi n’zimene mneneri Yesaya analosera kuti: “Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti am’tumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa; nawonso ndidzanka nawo ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.” Kenako Yehova ananena kuti: “Pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.”​—Yes. 56:6, 7.

Kodi Ndani Ayenera Kudya Zizindikiro?

15, 16. (a) Kodi mtumwi Paulo anati anthu amene ali m’pangano latsopano adzalandira madalitso otani? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi sayenera kudya nawo zizindikiro za pa Chikumbutso?

15 Baibulo limati anthu amene ali m’pangano latsopano, ndi “olimba mtima ponena za njira yolowera m’malo oyera.” (Werengani Aheberi 10:15-20.) Iwo ndi amene ‘adzalandire ufumu umene sungagwedezeke.’ (Aheb. 12:28) Motero, ndi anthu okha amene adzakhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Yesu Khristu kumwamba amene ayenera kumwa ‘za m’chikho’ chimene chimaimira pangano latsopano. Anthu amene ali m’pangano latsopanoli ndi amene atomeredwa ndi Mwanawankhosa. (2 Akor. 11:2; Chiv. 21:2, 9) Anthu ena onse amene amapezeka pa Chikumbutso chomwe chimachitika chaka ndi chaka, amangoonerera mwaulemu ndipo sadya nawo zizindikiro.

16 Paulo akutithandizanso kumvetsa mfundo yakuti anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, sayenera kudya nawo zizindikiro za pa Chikumbutso. Iye anauza Akhristu odzozedwa kuti: “Pakuti nthawi zonse pamene mudya mkate umenewu ndi kumwa za m’chikho chimenechi, mulengezabe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.” (1 Akor. 11:26) Kodi ndi liti pamene Ambuye “adzafike”? Izi zidzachitika akamadzatenga wodzozedwa womaliza kuti akakhale kumwamba m’gulu la odzozedwa omwe ali ngati mkwatibwi. (Yoh. 14:2) Choncho, mwambo wa Chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye womwe umachitika chaka ndi chaka, udzakhala ndi malire ake. “Otsala” a mbewu ya mkazi amene adakali padziko lapansi azidyabe zizindikiro mpaka onse a m’gulu limeneli akalandire mphoto yawo kumwamba. (Chiv. 12:17) Zikanakhala kuti anthu amene adzakhale ndi moyo kosatha padziko lapansi amadya zizindikiro, ndiye kuti mwambo wa Chikumbutso ukanapitirirabe mpaka kalekale.

‘Iwo Adzakhala Anthu Anga’

17, 18. Kodi ulosi wopezeka pa lemba la Ezekieli 37:26, 27 wakwaniritsidwa bwanji?

17 Yehova analosera kuti anthu ake adzakhala ogwirizana. Iye anati: “Ndipo ndidzapangana nawo pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nawo, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pawo kosatha. Kachisi wanganso adzakhala nawo, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga.”​—Ezek. 37:26, 27.

18 Anthu onse a Mulungu angapindule ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli lomwe ndi pangano la mtendere. Apatu Yehova walonjeza mtendere motsimikiza kwa atumiki ake onse omvera. Iwo amasonyeza zipatso za mzimu wa Yehova pamoyo wawo. Kachisi wa Yehova, yemwe akuimira kulambira koyera, ali pakati pawo. Iwo akhaladi anthu ake chifukwa asiya kulambira mafano kwa mtundu uliwonse ndipo amalambira Yehova Mulungu yekha.

19, 20. Kodi ndani amene alinso m’gulu la anthu amene Yehova amawatcha “anthu anga,” nanga pangano latsopano likutheketsa zinthu ziti?

19 N’zosangalatsa kwambiri nthawi yathu ino kuona umboni wakuti magulu awiriwa ndi ogwirizana. Ngakhale kuti anthu a m’khamu lalikulu lomwe likuwonjezeka sayembekeza kudzapita kumwamba, iwo amasangalala kutumikira limodzi ndi anthu amene ali ndi chiyembekezochi. Iwo agwirizana ndi Isiraeli wa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, nawonso ali m’gulu la anthu amene Yehova amawatcha kuti “anthu anga.” Ulosi uwu ukukwaniritsidwa pa anthu amenewa: “Amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako.”​—Zek. 2:11; 8:21; werengani Yesaya 65:22; Chivumbulutso 21:3, 4.

20 Yehova wachititsa kuti zonsezi zitheke kudzera m’pangano la tsopano. Alendo auzimu mamiliyoni ambiri ali m’gulu la anthu amene Yehova akuwaona kuti ndi mtundu wake. (Mika 4:1-5) Iwo akufunitsitsa kupitirizabe kugwira zolimba pangano limeneli mwa kulandira madalitso ake ndiponso kumvera mfundo za m’panganolo. (Yes. 56:6, 7) Akamachita zimenezi, iwo limodzi ndi Isiraeli wa Mulungu amadalitsidwa ndi mtendere wosatha. Choncho, yesetsani kuti mupeze madalitso amenewa panopa ndiponso mpaka kalekale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 N’chimodzimodzinso ndi mawu akuti “mpingo.” Mawuwa kwenikweni amatanthauza odzozedwa. (Aheb. 12:23) Komabe mawu omwewa amatanthauzanso Akhristu onse, kaya ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padziko lapansi.​—Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 2007 masamba  21 mpaka 23.

^ ndime 13 Yesu sali m’panganoli koma ndi Mkhalapakati wake. Choncho iye sanadye nawo zizindikirozi.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi “mafuko 12 a Isiraeli” amene adzaweruzidwe ndi a 144,000, ndi ndani?

• Kodi pangano latsopano limagwirizanitsa bwanji odzozedwa ndi a nkhosa zina?

• Kodi Akhristu onse ayenera kudya zizindikiro pa Chikumbutso?

• Ponena za masiku athu ano, kodi ndi m’gwirizano uti umene unaloseredwa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Anthu ambiri akutumikira limodzi ndi Isiraeli wa Mulungu

1950 | 373,430

1970 | 1,483,430

1990 | 4,017,213

2009 | 7,313,173