Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Paubwenzi ndi Mulungu Ngakhale Zinthu Zitasintha

Khalanibe Paubwenzi ndi Mulungu Ngakhale Zinthu Zitasintha

Khalanibe Paubwenzi ndi Mulungu Ngakhale Zinthu Zitasintha

KODI zinthu zina zasintha pa moyo wanu? Kodi zikukuvutani kuvomereza kusintha kumeneku? Ambiri a ife takumanapo ndi zoterezi kapena tidzakumana nazo nthawi ina. Zimene zinachitikiradi anthu ena akale, zingatithandize kudziwa makhalidwe amene angatithandize zinthu zikasintha.

Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zosiyanasiyana zimene zinam’chitikira Davide. Pa nthawi imene Samueli anam’dzoza kuti adzakhale mfumu, iye anali kamnyamata komanso kam’busa wamba. Adakali kamnyamata anadzipereka kuti amenyane ndi Mfilisti wina dzina lake Goliati, yemwe anali chimphona. (1 Sam. 17:26-32, 42) Kenako, Davide anaitanidwa kuti azikakhala ku nyumba ya Mfumu Sauli, ndipo anasankhidwa kukhala mkulu wa asilikali. Davide sankaganiza n’komwe kuti zimenezi zingamuchitikire komanso sankadziwa kuti mtsogolo akumana ndi zotani?

Koma kenako ubwenzi wa Davide ndi Sauli unasokonezeka kwambiri. (1 Sam. 18:8, 9; 19:9, 10) Kuti apulumutse moyo wake, Davide ankakhala moyo wothawathawa kwa zaka zambiri. Ngakhale pamene anali mfumu ya Isiraeli, zinthu zinasinthanso kwambiri pa moyo wake makamaka pamene anachita chigololo kenako n’kupha munthu pofuna kubisa tchimo lakelo. Chifukwa cha machimo akewa, iye anakumana ndi mavuto ambiri m’banja lake. Mwachitsanzo, mwana wake, Abisalomu anamuukira. (2 Sam. 12:10-12; 15:1-14) Koma Davide atalapa tchimo lake la chigololo ndiponso lopha munthu, Yehova anam’khululukira ndipo anakhala nayenso paubwenzi.

Inunso zinthu zingasinthe pa moyo wanu. Zinthu monga matenda, mavuto a zachuma kapena a m’banja, ndiponso zochita zathu, zingachititse kuti moyo wathu usinthe. Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kuti tizitha kupirira mavuto ngati amenewa?

Mmene Kudzichepetsa Kumatithandizira

Munthu wodzichepetsa amakhala ndi mtima wogonjera. Kudzichepetsa kungatithandize kuti tizidziona moyenera ndiponso kuti tiziona anthu ena moyenera. Tikamazindikira makhalidwe a ena ndiponso zinthu zimene akuchita bwino, tidzayamikira kwambiri umunthu wawo ndiponso zimene amachita. N’chimodzimodzi ifenso, kudzichepetsa kudzatithandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zina zatichitikira ndiponso kudziwa zimene tingachite.

Chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi ndi Jonatani, mwana wa Sauli. Zinthu zinasintha pa moyo wake. Pamene Samueli anauza Sauli kuti Yehova adzachotsa ufumu wake, sananene kuti Jonatani ndi amene adzakhale mfumu. Ndipo panalibe zimene Jonatani akanachita kuti zimenezi zisachitike. (1 Sam. 15:28; 16:1, 12, 13) Mulungu anasonyeza kuti Davide ndi amene adzakhale mfumu osati Jonatani. Kusakhulupirika kwa Sauli kunakhudza Jonatani. Iye sakanalowa ufumu wa bambo ake ngakhale kuti si amene anachititsa kuti bambo akewo akhale wosakhulupirika. (1 Sam. 20:30, 31) Kodi Jonatani anamva bwanji zinthu zitatere? Kodi anasunga chakukhosi chifukwa choti sanakhale mfumu, n’kuchitira nsanje Davide? Ayi, sanatero. Ngakhale kuti anali wamkulu poyerekeza ndi Davide ndiponso ankadziwa zinthu zambiri, Jonatani anakhalabe wokhulupirika ndipo analimbikitsa Davide. (1 Sam. 23:16-18) Kudzichepetsa kunam’thandiza kudziwa kuti Davide ndi amene Mulungu wam’dalitsa, ndipo ‘sanadziganizire koposa mmene anayenera kudziganizira.’ (Aroma 12:3) Jonatani anamvetsa zimene Yehova ankafuna kuti iye achite ndipo anavomereza maganizo a Yehova pankhaniyi.

N’zoona kuti nthawi zambiri kusintha kwa zinthu kumakhala ndi mavuto ake. Jonatani ankachita zinthu ndi anthu awiri amene ankadziwana nawo bwino kwambiri. Wina anali mnzake, Davide, yemwe anasankhidwa ndi Yehova kuti adzakhale mfumu. Ndipo wina anali bambo ake, Sauli, amene anali atakanidwa ndi Yehova koma ankalamulirabe. Zimenezi ziyenera kuti zinachititsa Jonatani kuvutika maganizo chifukwa ankayesetsa kuti akhalebe paubwenzi ndi Yehova. Zinthu zikasintha pa moyo zingatidetse nkhawa ndiponso kutichititsa mantha. Koma tikamayesetsa kuona zinthu mmene Yehova akuzionera, tidzapitiriza kum’tumikira mokhulupirika ngakhale tikukumana ndi mavuto.

Tifunika Kudziwa Zimene Sitingathe Kuchita

Munthu wodzichepetsa amadziwa kuti pali zina zimene sangathe kuchita. Komabe, nthawi zina zingakhale zovuta kuti munthu wodzichepetsa adziwe zimenezi.

Davide ankadziwa zimene sangathe kuchita. Ngakhale kuti Yehova anali atamusankha kuti adzakhale mfumu, panapita zaka zambiri asanayambe kulamulira. Baibulo silinena kuti Yehova anafotokozera Davide chifukwa chake panapita nthawi yaitali chonchi. Ngakhale kuti zimenezi zinali zokhumudwitsa, Davide sanasokonezeke ndi zimenezi. Iye ankadziwa zimene sangathe kuchita, ndipo ankadziwanso kuti Yehova, yemwe analola kuti zimenezi zichitike, ndi amene ankayendetsa zonse. Motero, Davide sanaphe Sauli pofuna kupulumutsa moyo wake ndipo analetsanso Abisai kuti asaphe Sauli.​—1 Sam. 26:6-9.

Nthawi zina, mumpingo mungachitike nkhani imene sitikuimvetsa kapena imene malinga ndi kuona kwathu sinasamaliridwe bwino. Popeza timadziwa zimene sitingathe kuchita, timazindikira kuti Yesu ndi Mutu wa mpingo ndipo akugwiritsa ntchito akulu kuti azititsogolera. Kuti tikhalebe paubwenzi ndi Yehova tiyenera kudalira iye pamene akutsogolera mpingo wake kudzera mwa Yesu Khristu ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta.​—Miy. 11:2.

Kufatsa Kumatithandiza Kuti Tiziona Zinthu Moyenera

Kufatsa kumaphatikizapo kusakwiya msanga ndipo kumatithandiza kupirira mavuto moleza mtima.Timachita zimenezi popanda kupsa mtima, kukwiya kapena kufuna kubwezera. Koma kukhala munthu wofatsa n’kovuta kwambiri. N’zochititsa chidwi kuti lemba lina m’Baibulo limauza ‘ofatsa onse a m’dziko’ kuti ‘afune chifatso.’ (Zef. 2:3) Kufatsa n’kogwirizana ndi kudzichepetsa ndiponso kudziwa zimene sitingathe kuchita. Koma n’kogwirizananso ndi makhalidwe ena monga ubwino ndi chifundo. Munthu wofatsa amakula mwauzimu chifukwa amakhala wophunzitsika ndiponso amatsatira malangizo.

Kodi kufatsa kungatithandize bwanji zinthu zikasintha pa moyo wathu? Mwina mwaonapo kuti anthu ambiri amaona kusintha kwa zinthu pa moyo ngati chinthu choipa. Koma zoona n’zakuti, kusintha kwa zinthu kungatipatse mwayi woti Yehova atiphunzitse zinthu zina. Chitsanzo pa nkhani imeneyi ndi zimene zinachitikira Mose.

Pamene Mose anali ndi zaka 40, n’kuti ali kale ndi makhalidwe abwino kwambiri. Iye ankadera nkhawa kwambiri anthu a Mulungu ndipo ankasonyeza mzimu wodzimana. (Aheb. 11:24-26) Komabe, Yehova asanam’patse udindo wotsogolera Aisiraeli kutuluka mu Iguputo, zinthu zinasintha pa moyo wake ndipo zimenezi zinathandiza kuti akhale wofatsa kwambiri. Iye anathawa ku Iguputo n’kukakhala ku Midiyani kwa zaka 40. Ali kumeneku ankagwira ntchito yaubusa, ndipo sanalinso munthu wotchuka. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Kusintha kumeneku kunam’chititsa kukhala munthu wabwino kuposa kale. (Num. 12:3) Iye anaphunzira kuika zinthu zauzimu patsogolo, osati zofuna zake.

Kuti timvetse kuti Mose anali wofatsa, tiyeni tione zimene anachita Yehova atamuuza kuti akufuna kuwononga mtundu wosamvera n’kupangitsa mbadwa za Moseyo kukhala mtundu wamphamvu. (Num. 14:11-20) Mose anachonderera Mulungu kuti asawononge mtunduwo. Zimene iye ananena zikusonyeza kuti ankadera nkhawa kwambiri dzina la Mulungu ndiponso moyo wa abale ake, osati zofuna zake. Udindo umene Mose anali nawo ngati mtsogoleri ndiponso mkhalapakati wa mtunduwo, unkafunikadi munthu wofatsa. Ngakhale kuti Miriamu ndi Aroni ankatsutsa Mose, Baibulo limati iye anali “wofatsa woposa anthu onse.” (Num. 12:1-3, 9-15) Zikuoneka kuti chifukwa choti Mose anali wofatsa, iye anapirira ndipo sanakwiye ndi zimenezi. Kodi mukuganiza kuti chikanachitika n’chiyani akanakhala kuti Mose sanali wofatsa?

Pa nthawi inanso, amuna ena analandira mzimu wa Yehova n’kuyamba kunenera. Yoswa yemwe anali mtumiki wa Mose, anaona kuti Aisiraeliwa sakuchita bwino. Koma chifukwa choti Mose anali wofatsa, iye ankaona zinthu mmene Yehova ankazionera ndipo sanade nkhawa kuti alandidwa udindo. (Num. 11:26-29) Kodi Mose akanakhala kuti sanali wofatsa, akanavomereza kusintha kumene Yehova anachitaku?

Kufatsa kunathandiza Mose kuti agwiritse ntchito bwino udindo waukulu umene Mulungu anam’patsa. Yehova anapempha Mose kupita ku Phiri la Horebe kuti akalankhule naye m’malo mwa Aisiraeli. Mulungu analankhula naye kudzera mwa mngelo ndipo anamusankha kuti akhale mkhalapakati wa chipangano. Pamene zinthu zinasintha choncho, kufatsa kunathandiza Mose kuvomereza udindo waukulu umenewu ndipo anakhalabe paubwenzi ndi Mulungu.

Nanga bwanji ifeyo? Kufatsa n’kofunika kwambiri kuti tikule mwauzimu. Anthu onse amene apatsidwa udindo ndiponso mwayi wotumikira anthu a Mulungu, afunika kukhala ofatsa. Zinthu zikasintha pa moyo wathu, khalidweli, lingatithandize kuti tisakhale odzikuza ndiponso kuti tikhale ndi maganizo oyenera zinthu zina zikatichitikira. Kodi mumatani zinthu zikasintha pa moyo wanu? Kodi mumavomereza kusinthako? Kodi mumauona kuti ndi mwayi woti mukulitse makhalidwe abwino? Umenewu ungakhale mwayi wathu wapadera kwambiri woti tiphunzire kukhala wofatsa.

Zinthu zipitirizabe kusintha pa moyo wathu. Nthawi zina, n’zovuta kumvetsa chifukwa chake zinthu zina zachitika. Kusadziwa zinthu zonse ndiponso kupanikizika maganizo kungachititse kuti tivutike kuona zinthu mmene Yehova akuzionera. Komabe, makhalidwe monga kudzichepetsa, kudziwa zomwe sitingathe kuchita ndiponso kufatsa angatithandize kuvomereza kusintha kulikonse. Zimenezi zingatithandize kukhalabe paubwenzi ndi Mulungu.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tizidziona moyenera

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kufatsa n’kofunika kwambiri kuti tikule mwauzimu

[Chithunzi patsamba 5]

Mavuto amene Mose anakumana nawo anam’thandiza kuti akhale wofatsa kwambiri