Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri

Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri

Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri

“Umboni wosatsutsika wosonyeza kuti munthu wina wa ku Kaperenao anali wanzeru kwambiri, ndi uthenga womwe ankalalikira chifukwa ukupitirizabe kukhudza mitima ya anthu ambiri.” *Anatero munthu wina wolemba mabuku dzina lake GREGG EASTERBROOK.

MAWU ali ndi mphamvu ndipo mawu anzeru komanso osankhidwa bwino angathandize anthu kukhala ndi chiyembekezo komanso angawasinthe mitima. Palibe munthu amene analalikira uthenga wa wamphamvu kwambiri kuposa wa Yesu Khristu. Munthu wina amene anamvetsera Yesu akulalikira uthenga umene masiku ano umatchedwa ulaliki wa paphiri, analemba kuti: “Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.”​—Mateyo 7:28.

Mpaka pano, uthenga umene Yesu anaphunzitsa ndi wodziwika kwa anthu ambiri padziko lonse. Taonani chitsanzo cha mfundo zina zothandiza zimene iye anaphunzitsa.

“Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Mateyo 6:24.

“Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”​—Mateyo 7:12.

“Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”​—Mateyo 22:21.

“Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Komabe uthenga wa Yesu sikuti unangokhala wosaiwalika, koma uli ndi mphamvu chifukwa umathandiza anthu kudziwa choonadi chonena za Mulungu, uli ndi mfundo zothandiza anthu kukhala ndi moyo wabwino ndipo umawathandiza kudziwa Ufumu wa Mulungu womwe udzathetse mavuto onse a anthu. Tikamakambirana za uthenga wa Yesu m’nkhani zotsatirazi, tiona chifukwa chake uthenga wake ukupitirizabe kukhudza mitima ya anthu ambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Kaperenao unali mzinda wa ku Galileya, kwawo kwa Yesu.​—Maliko 2:1.