Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Mulungu?

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Mulungu?

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Mulungu?

“Amene akuwadziwa bwino Atate ndi Mwana yekha. Koma Mwanayo amafuna kuuza anthu ena za Atatewo, kuti nawonso amudziwe.”​—LUKA 10:22, CONTEMPORARY ENGLISH VERSION.

MWANA woyamba kubadwa wa Mulungu ali kumwamba, anakhala zaka zambiri paubwenzi wabwino ndi Atate wake. (Akolose 1:15) Choncho, Mwana ameneyu ankadziwa bwino maganizo, makhalidwe ndiponso mmene Atate wake amamvera mumtima mwawo. Mwana ameneyu atabwera padziko lapansi, ankatchedwa Yesu ndipo anali wofunitsitsa kuphunzitsa anthu zoona za Atate wake. Tingaphunzire zambiri za Mulungu powerenga zimene Mwana ameneyu ananena.

Dzina la Mulungu Yesu ankaona kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova n’lofunika kwambiri. Mwana wokondedwa ameneyu ankafuna kuti anthu ena adziwe dzina la Atate ake ndi kumaligwiritsa ntchito. Dzina la Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, Yesu anapemphera kwa Yehova kuti: “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo.” (Yohane 17:26) N’zosadabwitsa kuti Yesu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu ndiponso ankauza ena dzinali chifukwa anthu amene Yesu ankawalalikira sakanatha kumvetsa zoona zokhudza Yehova popanda kudziwa dzinali ndiponso tanthauzo lake. *

Mulungu ndi wachikondi kwambiri Yesu nthawi ina anapemphera kwa Mulungu kuti: “Atate, . . . munandikonda musanayale maziko a dziko.” (Yohane 17:24) Popeza Yesu ali kumwamba ankakondedwa kwambiri ndi Mulungu, iyenso ali padziko lapansi anayesetsa kusonyeza chikondi chimenechi m’njira zosiyanasiyana.

Yesu anasonyeza kuti chikondi cha Yehova n’chachikulu kwambiri. Iye anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mawu achigiriki amene awamasulira kuti “dziko” palembali sakutanthauza “dziko lapansi,” kapena kuti nthaka, koma akutanthauza anthu onse. Mulungu amakonda kwambiri anthu moti anapereka Mwana wake wapadera kuti anthu okhulupirika amasulidwe ku uchimo ndi imfa ndiponso kuti akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Sitingathe mpang’ono pomwe kudziwa bwino kukula kwa chikondi chimenechi.​—Aroma 8:38, 39.

Yesu anatchula mfundo ina yapadera kwambiri yakuti: Yehova amakonda kwambiri mtumiki wake aliyense payekha. Yesu anaphunzitsa kuti Yehova ali ngati m’busa amene amaona nkhosa iliyonse kuti ndi yofunika ndiponso yosiyana ndi zinzake. (Mateyo 18:12-14) Yesu ananenanso kuti palibe mpheta ngakhale imodzi imene imagwa pansi popanda Yehova kudziwa. Ndipo ananenanso kuti: “Tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.” (Mateyo 10:29-31) Ngati Yehova amadziwa mpheta ina ikasowa, kuli bwanji atumiki ake okhulupirika? Iye amadziwa mtumiki wake aliyense payekha. Ngati Yehova amawerenga tsitsi lililonse la m’mutu mwathu, ndiye kuti palibe chilichonse chokhudza moyo wathu chimene angalephere kudziwa, kaya tikusowa chinachake kapena takumana ndi mavuto enaake.

Atate wakumwamba Monga taonera m’nkhani yapita ija, Yesu ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. N’chifukwa chake, Mwana wokondedwa ameneyu ankakonda kunena za Yehova ndiponso kumutchula kuti “Atate.” Ndipotu, m’mawu a Yesu oyamba kulembedwa, iye anatchula Yehova kuti “Atate wanga.” Yesu ananena mawuwa m’kachisi ali ndi zaka 12 zokha. (Luka 2:49) M’mabuku a Uthenga Wabwino mawu akuti “Atate” amapezeka pafupifupi maulendo 190. Yesu anatchulanso Yehova nthawi zingapo kuti “Atate wanu,” “Atate wathu,” ndiponso “Atate wanga.” (Mateyo 5:16; 6:9; 7:21) Popeza Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito mawu amenewa, zimenezi zikusonyeza kuti n’zotheka kwa anthu ochimwa ndiponso opanda ungwiro kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

Wachifundo ndiponso wofunitsitsa kutikhululukira Yesu ankadziwa kuti anthu opanda ungwirofe timafunika kuti Yehova azitichitira chifundo kwambiri. M’fanizo lake la mwana wolowerera, iye anayerekeza Yehova ndi bambo wachifundo ndiponso wokhululuka amene analandira ndi manja awiri mwana wake atalapa n’kubwerera panyumba. (Luka 15:11-32) Mawu a Yesu amenewa akutitsimikizira kuti Yehova amafufuza kuti aone ngati munthu amene wachimwa ali ndi mtima wolapa n’cholinga chakuti amuchitire chifundo. Yehova amafunitsitsa kukhululukira munthu wochimwa amene walapa. Yesu anafotokoza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, kumwamba kudzakhalanso chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa kuposa cha anthu 99 olungama osafunika kulapa.” (Luka 15:7) Ndithudi, palibe amene sangafune kukhala paubwenzi ndi Mulungu wachifundo chonchi.

Wakumva mapemphero Yesu asanabwere padziko lapansi pano, anaona yekha kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero” ndiponso kuti amasangalala kumva mapemphero a atumiki ake okhulupirika. (Salmo 65:2) Choncho panthawi ya utumiki wake, iye ankaphunzitsa anthu mmene ayenera kupempherera ndiponso zimene ayenera kupempha. Iye anauza otsatira ake kuti: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” Ndipo analimbikitsa omvera ake kupemphera kuti chifuno cha Mulungu “chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” Ifenso tsiku lililonse tingapemphere kuti atipatse chakudya cha tsikulo, atikhululukire machimo ndiponso kuti atithandize kupewa kuchimwa. (Mateyo 6:5-13) Yesu anaphunzitsa kuti Yehova amayankha mwachikondi mapemphero a atumiki ake omwe amam’pempha mochokera pansi pa mtima komanso mwachikhulupiriro.​—Mateyo 7:7-11.

Kunena zoona, Yesu ankaphunzitsa choonadi ponena za Yehova. Koma panalinso chinthu china chimene Yesu ankakonda kuuza ena chomwe ndi njira imene Yehova adzagwiritsa ntchito posintha zinthu padziko lapansi kuti akwaniritse chifuno chake chokhudza dzikoli ndiponso anthu. Ndipotu, imeneyi ndi imene inali mfundo yaikulu ya uthenga umene Yesu ankalalikira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Dzina lakuti Yehova limapezeka pafupifupi maulendo 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. Dzinali limatanthauza kuti “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eksodo 3:14) Mulungu angathe kukhala chilichonse chimene iye wafuna n’cholinga chakuti akwaniritse cholinga chake. Choncho, dzina limeneli limasonyeza kuti Mulungu nthawi zonse amachita zofuna zake ndiponso kuti chilichonse chimene amalonjeza chimachitika.