Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Ufumu wa Mulungu?

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Ufumu wa Mulungu?

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Ufumu wa Mulungu?

“Anachoka nayendayenda mu mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi, akulalikira . . . uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.”​—LUKA 8:1.

TONSE timakonda kulankhula zinthu zimene timaziona kuti n’zofunika komanso zosangalatsa. Monga mmene Yesu ananenera “pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Mateyo 12:34) Tikaona zimene Yesu ankakonda kunena mu utumiki wake, titha kumvetsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene unali wofunika kwambiri kwa iye.

Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Ufumu ndi boma lolamuliridwa ndi mfumu. Choncho, Ufumu wa Mulungu ndi boma limene Mulungu wakhazikitsa. Yesu ankakonda kukamba za Ufumu wa Mulungu ndipo mfundo yaikulu ya uthenga wake inali yokhudza Ufumuwo. M’mabuku anayi a Uthenga Wabwino, timapeza mawu onena za Ufumu umenewu maulendo oposa 110. Koma Yesu sankangophunzitsa ndi pakamwa chabe. Zochita zake zinkaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene udzachite.

Kodi Mfumu yake ndani? Mfumu ya Ufumu wa Mulungu inachita kusankhidwa ndi Mulungu osati anthu. Zimene Yesu ankaphunzitsa zimasonyeza kuti iye ndi amene anasankhidwa ndi Mulungu kukhala Mfumu ya Ufumu umenewu.

Yesu ankadziwa kuti maulosi a m’Baibulo anali ataneneratu kuti Mesiya wolonjezedwa adzalamulira mu Ufumu womwe sudzatha. (2 Samueli 7:12-14; Danieli 7:13, 14; Mateyo 26:63, 64) Kumbukirani kuti Yesu ananena poyera kuti iye ndi Mesiya wolonjezedwayo. Ponena zimenezi, iye ankavomereza mfundo yakuti analidi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. (Yohane 4:25, 26) N’chifukwa chake Yesu ananena nthawi zingapo kuti “ufumu wanga.”​—Yohane 18:36.

Yesu anaphunzitsanso kuti anthu ena adzalamulira naye mu Ufumu umenewu. (Luka 22:28-30) Iye anatchula anthu amenewa kuti ndi “kagulu ka nkhosa” chifukwa alipo ochepa. Ponena za anthu amenewa, Yesu anati: “Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti anthu amene adzakhala ndi mwayi wolamulira limodzi ndi Khristu amenewa ndi okwana 144,000.​—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1.

Kodi Ufumu wa Mulungu uli kuti? Yesu anauza wolamulira wachiroma wina, dzina lake Pontiyo Pilato kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Ufumu wa Mulungu womwe wolamulira wake ndi Khristu sudzalamulira pogwiritsa ntchito mabungwe a anthu. Yesu ananena maulendo ambirimbiri kuti Ufumu wa Mulungu ndi “ufumu wa kumwamba.” * (Mateyo 4:17; 5:3, 10, 19, 20) Choncho, Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba.

Ali padziko lapansi, Yesu ankadziwa kuti adzabwerera kumwamba ‘kukakonza malo’ a anthu amene akalamulire naye limodzi.​—Yohane 14:2, 3.

Kodi Ufumuwo udzachita chiyani? Yesu anauza otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:9, 10) Choncho, chifuniro cha Mulungu chikuchitika kumwamba. Ndipo Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuti akwaniritse cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga dziko lapansili. Ufumuwo udzasintha zinthu kwambiri padzikoli kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzabweretsa chiyani padziko lapansili? Yesu anaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu udzachotseratu zoipa zonse powononga anthu amene amachita zoipazo. (Mateyo 25:31-34, 46) Zimenezi zikusonyeza kuti zoipa zonse zidzatheratu. Yesu ananenanso kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu “ofatsa,” olungama, achifundo, “oyera mtima” komanso okonda mtendere.​—Mateyo 5:5-9.

Kodi anthu okhulupirika amenewa adzakhala m’dziko loipali? Ayi ndithu. Yesu analonjeza kuti dziko lapansi lidzasintha kwambiri mu Ufumu wa Mulungu. Munthu wina amene anaphedwa limodzi ndi Yesu ananena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Poyankha, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala nane m’Paradaiso.” (Luka 23:42, 43) Ndithudi, Ufumu wa Mulungu udzasintha kwambiri dzikoli kuti likhale paradaiso ngati mmene unalili munda wa Edene.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzachitiranso chiyani anthu? Yesu analonjeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite komanso anasonyeza zimene Ufumuwo udzachite. Iye anachiritsa mozizwitsa anthu ambiri posonyeza zimene adzachite padziko lonse m’tsogolo muno pomwe azidzalamulira mu Ufumu wa Mulungu. Buku la Uthenga Wabwino wa Mateyo limanena za Yesu kuti: “Anayendayenda m’Galileya yense, kuphunzitsa m’masunagoge mwawo ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”​—Mateyo 4:23.

Yesu anachiritsa matenda osiyanasiyana. Mwachitsanzo, iye ‘anatsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu.’ (Yohane 9:1-7, 32, 33) Komanso anachiritsa munthu wina amene ankadwala matenda oopsa kwambiri a khate pongomukhudza mwachifundo. (Maliko 1:40-42) Pamene anthu ena anabweretsa “munthu wogontha komanso wovutika kulankhula,” iye anamuchiritsa posonyeza kuti angathe kuchiritsa ‘ogontha ndi osalankhula.’​—Maliko 7:31-37.

Mfumu ya Ufumu wa Mulungu inaukitsa ngakhale akufa. M’Baibulo muli nthawi zitatu zimene Yesu anaukitsa akufa. Iye anaukitsa mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mayi wina wa masiye, mtsikana wina wazaka 12 komanso Lazaro, yemwe anali mnzake wapamtima.​—Luka 7:11-15; 8:41-55; Yohane 11:38-44.

Pofotokoza zinthu zosangalatsa zimene anthu omwe adzakhale mu Ufumu wa Mulungu akuyembekezera, Yesu analosera kudzera mwa mtumwi Yohane kuti: “Taonani! chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Inde, Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 1:1; 21:3, 4) Tangoganizani mmene moyo udzakhalire m’dzikoli. Anthu sazidzalira chifukwa cha chisoni, kupweteka komanso imfa. Nthawi imeneyo pemphero lakuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi monga kumwamba, lidzakwaniritsidwa.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti? Yesu anaphunzitsa kuti ulamuliro wake udzayamba munthawi yapadera yomwe anaitchula kuti nthawi ya “kukhalapo” kwake. Iye anapereka ulosi womveka bwino wosonyeza chiyambi cha nthawi ya kukhalapo kwake monga mfumu. Iye ananena kuti panthawi imeneyi padziko lapansi padzachitika zoipa zambiri monga nkhondo, njala, zivomezi, milili ndiponso kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo. (Mateyo 24:3, 7-12; Luka 21:10, 11) Zimene Yesu analoserazi komanso zinthu zina zambiri zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914. Chimenechi ndi chaka chimene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba. Choncho, panopa Yesu akulamulira ngati Mfumu. Posachedwapa Ufumu ubwera ndipo uchititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. *

Kodi kubwera kwa Ufumu wa Mulungu kudzakukhudzani bwanji inuyo panokha? Yankho la funso limeneli lidalira pa zimene mungachite mutamva uthenga wa Yesu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mawu akuti “ufumu wa kumwamba” amapezeka nthawi 30 m’buku la Uthenga Wabwino wa Mateyo.

^ ndime 17 Kuti mumvetsetse chifukwa chake timanena kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi, onani mutu 9 wakuti “Kodi Tili ‘M’masiku Otsiriza’?” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.