Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Uthenga wa Yesu Khristu Umakukhudzani Bwanji?

Kodi Uthenga wa Yesu Khristu Umakukhudzani Bwanji?

Kodi Uthenga wa Yesu Khristu Umakukhudzani Bwanji?

“Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka.”​—YOHANE 10:10.

YESU KHRISTU anabwera padziko lapansi kudzapereka, osati kudzalandira. Kudzera mu utumiki wake, Yesu anapatsa anthu mphatso yamtengo wapatali. Iye analalikira uthenga umene unathandiza anthu kudziwa choonadi ponena za Mulungu ndi chifuniro chake. Mofanana ndi Akhristu oona, anthu amene amamvetsera uthenga umenewu amakhala mosangalala panopa. * Koma mfundo yofunika kwambiri pa uthenga umene Yesu analalikira inali yokhudza mphatso yamtengo wapatali koposa mphatso zonse. Mphatso imeneyi ndi moyo wangwiro umene anapereka kuti atiwombole. Kuti tidzakhale ndi moyo wosatha tiyenera kukhulupirira uthenga wokhudza mphatso imeneyi.

Zimene Mulungu ndi Khristu anapereka Yesu ankadziwa kuti adani ake adzamupha mwankhanza kwambiri. (Mateyo 20:17-19) Komabe, iye ananena mawu odziwika kwambiri amene ali pa Yohane 3:16. Mawu ake ndi akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” Yesu ananenanso kuti anabwera “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) N’chifukwa chiyani pa lembali Yesu ananena kuti adzapereka moyo wake m’malo monena kuti moyo wake udzachotsedwa?

Popeza Mulungu amakonda kwambiri anthu, anakonza njira yoti awapulumutse ku uchimo ndi mavuto amene amabwera chifukwa cha uchimo monga kupanda ungwiro ndiponso imfa. Mulungu anachita zimenezi potumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake nsembe. Yesu anachita zimenezi mwa kufuna kwake, ndipo anapereka moyo wake wangwiro kuti tipulumuke. Zimene anachitazi, zimatchedwa kuti dipo, ndipo ndi mphatso yamtengo wapatali yoposa zonse zimene Mulungu anapatsa anthu. * Mphatso imeneyi ingatithandize kupeza moyo wosatha.

Zimene muyenera kuchita Kodi n’zotheka kuti mphatso ya dipo ikhale yanuyanu? Zili kwa inu kuilandira kapena ayi. Mwachitsanzo: Tiyerekeze kuti munthu wina akukupatsani mphatso. Mphatsoyo sikhala yanu mpaka mutailandira. N’chimodzimodzinso ndi dipo. Yehova akukupatsani mphatso ya dipo, koma ingakhale yanu ngati mutailandira. Kodi mungatani kuti muilandire?

Yesu ananena kuti anthu amene ‘amakhulupirira iye’ ndi amene adzalandire moyo wosatha. Chikhulupiriro chimaoneka mwa zinthu zimene timachita pa moyo wathu. (Yakobe 2:26) Kukhulupirira Yesu kumatanthauza kuchita zinthu motsatira mfundo zimene iye ankaphunzitsa ndiponso kuchita zimene ankachita. Kuti muthe kuchita zimenezi, muyenera kudziwa bwino Yesu ndiponso Atate ake. Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Zaka zoposa 2,000 zapitazo, Yesu Khristu analalikira uthenga umene wakhudza mitima ya anthu ambiri padziko lonse lapansi. Kodi mukufuna kudziwa zambiri za uthenga umenewu ndiponso zimene inuyo ndi abale anu mungachite kuti uthenga umenewu ukuthandizeni panopa mpaka muyaya? Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani.

Nkhani zotsatirazi zikuthandizani kudziwa zambiri za Yesu Khristu, yemwe ndi munthu amene analalikira uthenga umene ungathandize kuti moyo wanu ukhale wabwino mpaka muyaya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Si anthu onse amene amanena kuti ndi Akhristu amene alidi Akhristu enieni. Akhristu enieni ndi amene amatsatira mfundo zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza chifuniro cha Mulungu.​—Mateyo 7:21-23.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene malemba amanena pankhani ya dipo, onani mutu 5, wakuti “Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse,” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.