Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziwani Zoona Zake za Yesu

Dziwani Zoona Zake za Yesu

Dziwani Zoona Zake za Yesu

KODI MUKUGANIZA KUTI MFUNDO ZOTSATIRAZI N’ZOONA KAPENA BODZA?

Yesu anabadwa pa 25 December.

Anzeru akum’mawa atatu anapita kukaona Yesu atangobadwa kumene.

Yesu analibe achimwene ndi achemwali ake.

Yesu anali Mulungu ndipo anachita kusintha thupi lake n’kudzakhala ngati munthu padziko lapansi pano.

Yesu anali munthu wapadera kwambiri.

ANTHU ambiri anganene kuti mfundo zonse zili pamwambazi n’zoona. Koma ena anganene kuti n’zovuta ndipo n’zosatheka kudziwa kuti zoona zenizeni n’ziti. Ena angaganize kuti zilibe ntchito kudziwa zoona zenizeni pa mfundo zimenezi, chofunika n’kungokhulupirira Yesu basi.

Komabe, Baibulo siligwirizana ndi maganizo amenewa chifukwa limatilimbikitsa “kum’dziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.” (2 Petulo 1:8) Ndipo tingam’dziwe Ambuye Yesu powerenga mabuku a Uthenga Wabwino. Mabuku amenewa amatiuza zoona zake za Yesu, ndipo amatithandiza kusiyanitsa mfundo zoona ndi zabodza zokhudza Yesu. Choncho, tiyeni tione zimene mabuku a Uthenga Wabwino amanena pa mfundo zimene zili pamwambazi.

ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Yesu anabadwa pa 25 December.

ZIMENEZI N’ZABODZA.

M’Baibulo mulibe vesi lililonse limene limatchula mwezi kapena tsiku limene Yesu anabadwa. Ndiyeno kodi zoti Yesu anabadwa pa 25 December zinayamba bwanji? Buku lina linanena kuti anthu ena amene ankadzitcha kuti Akhristu “ankafuna kuti mwambo wokumbukira tsiku limene Yesu anabadwa uzichitika pa tsiku limene ankachita mwambo wina wachikunja umene Aroma ankachita. Mwambowu unkayamba m’nyengo yozizira pomwe tsiku linkakhala lalitali ndipo dzuwa limachedwa kulowa.” Buku lomweli linanenanso kuti miyambo yambiri ya pa Khirisimasi inayamba potengera “miyambo yachikunja yomwe anthu ankachita pokondwerera zaulimi ndiponso dzuwa ndipo inkachitika chapakati pa nyengo yozizira.”​—The Encyclopædia Britannica.

Ndiyeno kodi mukuganiza kuti Yesu angavomereze kuti anthu azikumbukira kubadwa kwake pa 25 December? Ganizirani izi: Tsiku limene Yesu anabadwa silimadziwika. Ndipo m’Baibulo mulibe vesi lililonse limene limanena kuti tizikumbukira tsiku limene iye anabadwa ndipo palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Akhristu oyambirira ankakumbukira tsiku la kubadwa kwa Yesu. Koma Baibulo limatchula tsiku lenileni limene Yesu anafa, ndipo limasonyeza kuti analamula otsatira ake kuti azikumbukira tsiku limeneli. * (Luka 22:19) Apa n’zoonekeratu kuti Yesu ankafuna kuti anthu azikumbukira tsiku limene iye anafa, osati tsiku limene anabadwa.​—Mateyo 20:28.

ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Anzeru akum’mawa atatu anapita kukaona Yesu atangobadwa kumene.

ZIMENEZI N’ZABODZA.

Mwina mwaonapo zithunzi za Yesu ali wakhanda atagona modyera ng’ombe, pambali pake pali anzeru akum’mawa atatu atatenga mphatso. Komabe, zimene amajambula pa zithunzizi si zoona.

N’zoona kuti Yesu ali mwana, anthu ena akum’mawa anapita kukamuona. Koma alendo amenewa anali anthu okhulupirira nyenyezi. (Mateyo 2:1) Kodi iwo anapeza Yesu ali m’khola la ng’ombe? Ayi ndithu. Iwo anam’peza ali m’nyumba. Zoonekeratu kuti iwo anakamuona patatha miyezi ingapo Yesu atabadwa.​—Mateyo 2:9-11.

Nanga kodi alendo akum’mawawo analipo angati? Kodi analipo awiri? atatu? kapena 30? Baibulo silimanena. N’kutheka kuti anthu anayamba kunena kuti analipo atatu chifukwa mphatso zimene anapatsa Yesu zinalipo za mitundu itatu. * (Mateyo 2:11) Ena amanena kuti anthu amene amawatchula kuti anzeru akum’mawawo anali a mafuko osiyana. Koma Baibulo silimanena zimenezi. Buku lina loikira ndemanga pa mabuku a Uthenga Wabwino linanena kuti, bodza limeneli anayambitsa ndi mkulu winawake “wolemba mbiri wa m’zaka za m’ma 700 ndipo zimenezi zinali za m’mutu mwake basi.”

ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Yesu analibe achimwene ndi achemwali ake.

ZIMENEZI N’ZABODZA.

Mabuku a Uthenga Wabwino amasonyeza kuti Yesu anali ndi abale ake. Mwachitsanzo, buku la Uthenga Wabwino wa Luka limanena kuti Yesu anali ‘mwana woyamba wamwamuna’ wa Mariya. Zimenezi zikusonyeza kuti iye anaberekanso ana ena. * (Luka 2:7) Komanso buku la Uthenga Wabwino wa Maliko limanena kuti anthu ankaona kuti Yesu sanali munthu wapadera koma anali wofanana ndi abale ake ena onse. Mwachitsanzo, iwo nthawi ina anafunsa kuti: ‘Kodi iyeyu si m’bale wa Yakobe ndi Yosefe ndi Yudasi ndi Simoni? Ndipo alongo ake si awa omwe tili nawo pompano?’​—Maliko 6:3; Mateyo 12:46; Yohane 7:5.

Ngakhale kuti mabuku a Uthenga Wabwino amanena zimenezi, akatswiri a Baibulo ambiri amalimbikirabe zoti Yesu analibe achimwene ndi achemwali ake. Ena amanena kuti achimwene ndi achemwali amene amanenedwawo anali asuweni ake. * Ndipo ena amati abale ake a Yesu amenewa anali ana amene Yosefe anabereka ndi mayi wina, osati Mariya. Koma taganizirani izi: Ngati Yesu analibe achemwali ndiponso achimwene ake, kodi anthu a ku Nazarete akananena zimene ananena zija? N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewo anaona Mariya ali ndi pakati pa ana amenewa. Choncho, iwo ankadziwa kuti Yesu anali mmodzi mwa ana ambiri a Mariya.

ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Yesu anali Mulungu ndipo anachita kusintha thupi lake n’kudzakhala ngati munthu padziko lapansi pano.

ZIMENEZI N’ZABODZA.

Chikhulupiriro chakuti Mulungu anabwera padziko lapansi kudzakhala Yesu ndi mfundo yaikulu pa chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Yesu ali padziko lapansi pano anthu sankakhulupirira zimenezi, koma maganizo amenewa anachita kuyamba patapita nthawi kuchokera pamene iye anamwalira. Ndiponso buku lina linanena kuti: “M’Chipangano Chatsopano mulibe mawu onena kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi kapena mfundo iliyonse yokhudza chiphunzitso chimenechi . . . Chikhulupirirochi chinafalikira pang’onopang’ono ngakhale kuti panali anthu ena omwe sankagwirizana ndi zimenezi.”​—The Encyclopædia Britannica.

Zipembedzo zikamaphunzitsa kuti Yesu anali Mulungu amene anachita kusintha thupi lake n’kudzakhala ngati munthu pano padziko lapansi, ndiye kuti zikunyoza Yesu. * N’chifukwa chiyani tikunena choncho? Taganizirani chitsanzo ichi: Ogwira ntchito apempha zinazake kwa bwana wawo ndipo iye akuwauza kuti alibe udindo wowapatsa zimene akufuna. Ngatidi zimene akunena bwanayo zili zoona, ndiye kuti akudziwa kuti pali wina amene ali ndi udindo woposa wake. Koma atakhala kuti ali ndi mphamvu zowapatsa zimene apemphazo koma n’kuwauza kuti iye alibe udindo umenewo, ndiye kuti bwanayo ndi wonama.

Ndiyeno kodi Yesu anayankha chiyani ophunzira ake awiri atamupempha malo apamwamba? Iye anawauza kuti: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi kumanzere kwanga, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene Atatewo anawakonzera.” (Mateyo 20:23) Yesu akanakhala kuti ndi Mulungu, bwenzi zimene ananenazi zili zabodza. Koma pozindikira kuti pali Mulungu, yemwe ndi wamphamvu yonse, Yesu anatisiyira chitsanzo cha kudzichepetsa ndipo anasonyeza kuti iye si wofanana ndi Mulungu.

ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Yesu anali munthu wapadera kwambiri.

ZIMENEZI N’ZOONA.

Yesu ananena mosapita m’mbali kuti anali munthu wapadera kwambiri. Iye anati: “Ndine Mwana wa Mulungu.” (Yohane 10:36) N’zoona kuti aliyense angadzitchule kuti ndi Mwana wa Mulungu. Koma ngati zimene Yesu ankanena zoti ndi Mwana wa Mulungu zinali zabodza, kodi anthu akanaganiza kuti iye ndi munthu wotani? Anthu akanaganiza kuti iye sanali munthu wabwino komanso anali wabodza.

Mulungu anapereka umboni wamphamvu kwambiri wosonyeza kuti zimene Yesu ankanena zoti ndi Mwana wa Mulungu zinali zoona. Kawiri konse ananena za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga.” (Mateyo 3:17; 17:5) Tangoganizani: M’Malemba, ndi nthawi zochepa zokha zimene anthu anamva Mulungu akulankhula. Koma panthawi zochepazo, maulendo awiri iye ananena kuti Yesu ndi Mwana wake. Umenewutu ndi umboni waukulu zedi wosonyeza kuti Yesu ankanena zoona kuti anali Mwana wa Mulungu.

Kodi nkhani ino yakuthandizani kudziwa mfundo zina zokhudza Yesu zimene simunkazidziwa? Ngati zili choncho, mungachite bwino kwambiri kufufuza mfundo zina m’mabuku a Uthenga Wabwino. Mungasangalale ndiponso kupeza madalitso ambiri ngati mutachita zimenezi. Ndiponsotu Yesu ananena kuti kuphunzira choonadi cha iye ndiponso Atate wake kudzatithandiza kuti tipeze “moyo wosatha.”​—Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Yesu anafa pa Tsiku la Pasika, kapena kuti pa Nisani 14, malinga ndi kalendala ya Ayuda.​—Mateyo 26:2.

^ ndime 18 Mateyo analemba kuti alendo amenewa “anamasula chuma chawo” ndipo anam’patsa Yesu golide, lubani ndi mule. N’zochititsa chidwi kuti mphatso zamtengo wapatali zimenezi zinafika panthawi yake, popeza zikuoneka kuti makolo a Yesu anali osauka ndiponso chifukwa choti anali atatsala pang’ono kuthawira kudziko lina.​—Mateyo 2:11-15.

^ ndime 21 Ngakhale kuti Yesu anabadwa mozizwitsa, ana ena onse a Mariya anabadwa monga mmene ana ena onse amabadwira ndipo bambo wawo weniweni anali Yosefe.​—Mateyo 1:25.

^ ndime 22 Maganizo amenewa, omwe anayambitsidwa ndi Jerome cha m’ma 383 C.E., ndi otchuka kwambiri kwa anthu amene amakhulupirira kuti Mariya anakhala namwali kwa moyo wake wonse. Patapita nthawi Jerome anazindikira kuti maganizo akewa ndi olakwika. Koma anthu ambiri, makamaka akuluakulu a tchalitchi cha Katolika amakhulupirirabe zimenezi.

^ ndime 26 Kuti mudziwe zambiri za chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, onani kabuku kakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 14]

Mfundo Zina Zimene Mungachite Nazo Chidwi

Kodi Yesu ali padziko lapansi anali munthu wotani? Kodi anali wodzimana zinthu monyanyira, wosakonda kucheza ndi anthu wamba? Ena amaganiza choncho. Mwina n’chifukwa chake amadabwa kudziwa kuti Yesu anachita zinthu zotsatirazi:

• anapita kumalo ena kukasangalala.​—Yohane 2:1-11.

• anayamikira ena.​—Maliko 14:6-9.

• anacheza ndi ana.​—Maliko 10:13, 14.

• analira pagulu.​—Yohane 11:35.

• anamvera ena chisoni.​—Maliko 1:40, 41.