Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mpando Wachifumu Wako Udzakhazikika”

“Mpando Wachifumu Wako Udzakhazikika”

Yandikirani Mulungu

“Mpando Wachifumu Wako Udzakhazikika”

2 SAMUELI 7:1-16

KUYAMBIRA kale, olamulira akhala akuchoka pa maudindo awo. Ena amachoka nthawi yawo yolamulira ikatha, koma ena amachita kuchotsedwa. Nanga bwanji Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, kodi chilipo chimene chingamulepheretse kulamulira monga Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu? Yankho tingalipeze m’mawu amene Yehova anauza Mfumu Davide ya a Isiraeli, monga zilili pa 2 Samueli chaputala 7.

Kumayambiriro kwa chaputala chimenechi, timawerenga kuti Davide anakwiya chifukwa chakuti iye monga mfumu, ankakhala m’nyumba yokongola, pamene likasa la Mulungu linkakhala muhema. * Pamenepa Davide anasonyeza kuti ankafunitsitsa kumanga nyumba yabwino, kapena kuti kachisi wa Yehova. (Vesi 2) Komabe Mulungu ananena kuti Davide si amene amange nyumbayo. Koma kudzera mwa mneneri Natani, Yehova anauza Davide kuti mwana wake ndi amene adzamange kachisiyo.​—Vesi 4, 5, 12, 13.

Komabe, Yehova anasangalala kwambiri ndi mtima umene Davide anasonyeza ndipo anamulonjeza kuti adzasankha wina m’banja lake kuti adzalamulire mpaka kalekale. Mulungu anapangana ndi Davide zimenezi chifukwa choti Davide anali wodzipereka pom’tumikira ndiponso Mulungu ankafuna kukwaniritsa ulosi winawake wa m’Baibulo. Mneneri Natani ndi amene anapereka uthenga umenewu kwa Davide. Iye anati: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.” (Vesi 16) Kodi Mfumu yamuyaya imene ikutchulidwa m’pangano limeneli ndi ndani?​—Salmo 89:20, 29, 34-36.

Yesu wa ku Nazarete anali mwana wa Davide. Polengeza za kubadwa kwa Yesu, mngelo wina anati: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwa muyaya, mwakuti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32, 33) Choncho zimene Yehova anapangana ndi Davide zinakwaniritsidwa mwa Yesu Khristu. Panopo iye akulamulira, osati chifukwa chosankhidwa ndi anthu, koma chifukwa cha zimene Mulungu analonjeza kuti iye adzalamulira mpaka kalekale. Zimenezi zikutikumbutsa mfundo yakuti zimene Mulungu amalonjeza, nthawi zonse zimachitikadi.​—Yesaya 55:10, 11.

Pankhani ya pa 2 Samueli chaputala 7 tikuphunzirapo mfundo ziwiri zofunika. Choyamba, nkhaniyi ikutiphunzitsa mfundo yakuti, palibe chimene chingalepheretse Yesu Khristu kulamulira. Chifukwa cha zimenezi tisamakayike kuti Ufumu wake udzagwira ntchito yake, yomwe ndi kukwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lapansi lino monga mmene zilili kumwamba.​—Mateyo 6:9, 10.

Chachiwiri, nkhaniyi imatiphunzitsa mfundo yolimbikitsa yokhudza Yehova. Kumbukirani kuti Yehova anaona zimene zinali mumtima wa Davide ndiponso anasangalala ndi zimene Davide ankafuna kuchita. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amaona zimene zili mumtima mwathu ndipo amasangalala tikamamutumikira modzipereka. Nthawi zina, zinthu zimene zimatichitikira osati mwakufuna kwathu, monga kudwaladwala, kapena kukalamba, zingatilepheretse kuchita zonse zimene timafuna titachita potumikira Mulungu. Ngati zimenezi zikukuchitikirani, musamadandaule. Chifukwa Yehova amaona ngakhale za mumtima wa munthu amene akufuna kutumikira modzipereka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Likasa la chipangano linali bokosi lopatulika limene linapangidwa potsatira zimene Yehova ananena. Likasali linali umboni wakuti Yehova akutsogolera Aisiraeli.​—Eksodo 25:22.