Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Akutani?

Kodi Mulungu Akutani?

Kodi Mulungu Akutani?

“Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?” *​—SALMO 10:1.

TIKANGOONA mitu ya nkhani za m’manyuzipepala sitikayikira zoti tikukhala “m’nyengo za nsautso.” Ndipo ifeyo tikakumana ndi mavuto, mwina kuberedwa, kuchita ngozi, kapena munthu wina amene timamukonda akamwalira, tingadzifunse kuti, Kodi Mulungu sakuona zimenezi? Kodi sakukhudzidwa nazo? Kodi alikodi kumwambako?

Komabe n’kutheka kuti chifukwa chokhala ndi maganizo olakwika timayembekezera kuti Mulungu atichitira zinthu zinazake. Tiyerekezere chonchi: Taganizirani kuti pali mwana amene wakwiya chifukwa choti bambo ake apita kuntchito. Mwanayo akufuna kuti bambo akewo abwere kuti aziwaona. Iye akuona ngati kuti iwo amuthawa. Tsiku lonse iye akungokhalira kufunsa kuti, “Kodi bambo ali kuti?”

Tingathe kuona kuti mwanayo akuganiza molakwika chifukwatu bambo akewo akugwira ntchito kuti apeze ndalama zothandizira banja lonselo. N’kutheka kuti nafenso tikakumana ndi mavuto n’kumafunsa kuti, “Kodi Mulungu ali kuti?” timakhala tili ndi maganizo olakwika.

Mwachitsanzo, ena amafuna kuti ntchito yaikulu ya Mulungu izikhala kupha nthawi yomweyo aliyense amene wachita zoipa. Ena amaona kuti Mulungu ali ngati Father Christmas, amene ntchito yake yaikulu ndi kupereka mphatso. Motero amaona kuti ntchito yaikulu ya Mulungu ndi kupereka mphatso monga mwamuna kapena mkazi womanga naye banja, mwayi wa ntchito, kapenanso wopeza mphoto pampikisano.

Maganizo awiri onsewa ndi olakwika chifukwa amachititsa anthu ena kuona kuti Mulungu akuchedwa kuweruza anthu oipa ndipo amachititsanso ena kuona kuti Mulungu sakuwapatsa zimene apempha chifukwa choti iye sakhudzidwa ndi mavuto awo kapena samadziwa zimene iwo akufunikira. Komatu zonsezi si zoona ngakhale pang’ono. Zoona zake n’zakuti Yehova Mulungu akuchita zonse zimene zili zoyenera kuti asamalire anthu onse, ngakhale kuti amachita zimenezi mosiyana ndi mmene anthu ambiri amafunira.

Ndiyeno kodi Mulungu akutani kwenikweni? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyenera kukumbukira zimene zinachitika Mulungu atangolenga anthu. Panthawiyo ubwenzi wa anthu ndi Mulungu unasokonekera kwambiri. Komabe ubwenziwu sunawonongeke moti n’kulephereka kuubwezeretsa.

Mavuto Amene Uchimo Unabweretsa

Tayerekezerani kuti munthu ali ndi nyumba imene yakhala yopasuka kwa zaka zambiri. Denga lake linaphotchoka, zitseko zinaguluka ndipo anthu anaiwononga kunja konse. Poyamba, nyumbayi inali yosamalidwa bwino komanso yokongola. Poganizira mmene nyumbayo yawonongekera, ntchito yoikonzanso ingakhale yaikulu ndipo ingatenge nthawi yaitali.

Ndiye taganizirani mmene zinthu zinasokonezekera zaka 6,000 zapitazo pamene Satana ananyenga Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu. Izi zisanachitike, anthu awiri oyambirirawa anali athanzi ndipo akanatha kukhala ndi moyo wosatha pamodzi ndi ana awo. (Genesis 1:28) Koma atachimwa, Adamu ndi Hava anawononga tsogolo la ana awo onse.

Zimene anachitazi zinabweretsa mavuto aakulu kwambiri. Baibulo limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo.’ (Aroma 5:12) Uchimo sunabweretse imfa yokha koma unawononganso ubwenzi wathu ndi Mlengi. Unawononganso thanzi lathu, nzeru zathu, komanso maganizo athu. Chifukwa cha zimenezi anthufe tili ngati nyumba yomwe yawonongedwa. Yobu, yemwe anali munthu wolungama, ananena zimenezi mwachidule. Iye anati moyo wa munthu ndi wa “masiku owerengeka, nakhuta mavuto.”​—Yobu 14:1.

Koma kodi Adamu ndi Hava atachimwa Mulungu ananyanyala anthu onse? Ayi sanatero. Ndipotu mpaka pano Atate wathu wakumwamba akuchita zinthu zosiyanasiyana pofuna kuthandiza anthu onse. Kuti mumvetse zimene Mulungu akukuchitirani, tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene munthu amene akufuna kukonzanso nyumba yake amachita. Ndipo tikambirananso zimene Mulungu wachita kale panopo pofuna kutikonzera tsogolo labwino.

1 Munthu akaona mmene nyumba yake yawonongekera, angasankhe kuikonzanso kapena kungoigwetsa.

Adamu ndi Hava atangochimwa m’munda wa Edene, Yehova Mulungu ananena kuti ali ndi cholinga chobwezeretsa moyo wangwiro kwa anthu. Poweruza mngelo amene anachititsa kuti makolo athuwo achimwe, Mulungu anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.”​—Genesis 3:15.

Apa Yehova analonjeza kuti adzawononga Satana, yemwe anachititsa kuti Adamu ndi Hava achite zosamvera. (Aroma 16:20; Chivumbulutso 12:9) Kuwonjezera pamenepo, Yehova analosera kuti kudzabwera “mbewu” imene idzawombole anthu ku uchimo. * (1 Yohane 3:8) Malonjezo amenewa akutsimikizira mfundo yofunika yakuti: Mulungu ali ndi cholinga chokonzanso zinthu zimene zinawonongeka, osati kuwononga zonse zimene analenga. Koma panafunika nthawi yaitali kuti achite zimenezi.

2 Katswiri wojambula mapulani a nyumba amalemba bwinobwino pulani yonse imene ingafunike pokonzanso nyumbayo.

Yehova Mulungu anapereka malamulo kwa ana a Isiraeli ndipo anawapatsa pulani ya kachisi woti azigwiritsa ntchito polambira. Baibulo limati: “Zinthu zimenezo ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera.” (Akolose 2:17) Zili ngati pulani chifukwa zinkapereka chithunzi cha zinthu zazikulu zimene zinali mtsogolo.

Mwachitsanzo, Aisiraeli ankapereka nsembe zanyama kuti Mulungu awakhululukire machimo awo. (Levitiko 17:11) Nsembe zimenezi zinkaimira nsembe yaikulu imene inadzaperekedwa patatha zaka zambiri. Nsembe imeneyi ndi imene inali yofunikira kuti anthu awomboledwe. * Kamangidwe ka chihema komanso kachisi amene Aisiraeli ankalambirirapo kankaimira zinthu zimene Mesiya adzachite, kungoyambira pa kupereka moyo wake nsembe mpaka kubwerera kumwamba.​—Onani  tchati patsamba 7.

3 Amapeza mmisiri womanga nyumba amene angathe kutsatira zimene zalembedwa papulani ija.

Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa amene anayenera kusonyeza tanthauzo lenileni la nsembe zimene Aisiraeli ankapereka ndipo anayenera kutero popereka moyo wake kuti apulumutse anthu. N’chifukwa chake Yohane M’batizi anamutcha Yesu kuti “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yohane 1:29) Yesu anavomera ndi mtima wonse kuchita zimenezi. Iye anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.”​—Yohane 6:38.

Mulungu ankafuna kuti Yesu ‘adzapereke moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri’ komanso kuti iye adzachite pangano la Ufumu ndi otsatira ake. (Mateyo 20:28; Luka 22:29, 30) Ufumu umenewo ndi umene Mulungu adzagwiritse ntchito pokwaniritsa zonse zimene akufuna kuchitira anthu. Uthenga wokhudza Ufumu wa Mulungu umatchedwa “uthenga wabwino” chifukwa umafotokoza kuti Mulungu wakhazikitsa boma kumwamba loti liziyendetsa zinthu padzikoli.​—Mateyo 24:14; Danieli 2:44. *

Ntchito Yokonzanso Zinthu Ikupitirirabe

Yesu asanabwerere kumwamba, analamulira otsatira ake kuti: “Mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera . . . Ndipo dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.”​—Mateyo 28:19, 20.

Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito yokonzanso zinthu sinathere pa imfa ya Yesu chifukwa inayenera kupitirirabe mpaka “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” kapena kuti nthawi imene Ufumu wa Mulungu uyenera kuyamba kulamulira padziko lapansi. Nthawi yake ndi inoyo. Tikudziwa zimenezi chifukwa zimene Yesu analosera kuti zidzachitika m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu” zikuchitika panopo. *​—Mateyo 24:3-14; Luka 21:7-11; 2 Timoteyo 3:1-5.

Masiku ano, m’mayiko 236, Mboni za Yehova zimamvera lamulo la Yesu lokhudza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndipotu cholinga cha magazini imene mukuwerengayi ndicho kukuthandizani kudziwa bwino za Ufumu umenewu ndiponso zimene udzachite. Patsamba 2 la magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda, pamakhala mawu akuti: “Magazini ino . . . imakhazika pansi mitima ya anthu onse ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu, umene ndi boma lenileni la kumwamba, posachedwapa udzachotsa zoipa zonse ndi kusandutsa dziko lapansi paradaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khristu amene anatifera kuti tipeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.”

N’zoona kuti pakali pano tizimvabe za uchigawenga, masoka achilengedwe, kapenanso inuyo panokha mungathe kukumana ndi mavuto enaake. Komabe kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kukhulupirira kuti Mulungu sanatinyanyale anthufe. Ndipo sangachite zimenezo chifukwa Baibulo limati “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndipotu adzakwaniritsadi lonjezo lake lakuti adzakonzanso zinthu zimene zinawonongeka chifukwa cha kuchimwa kwa makolo athu.​—Yesaya 55:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Yehova ndi dzina la Mulungu limene limatchulidwa m’Baibulo.

^ ndime 16 Kuti mumvetse lemba la Genesis 3:15, onani mutu 19, m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 22 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu, onani mutu 8 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

[Tchati/​Chithunzi patsamba 7]

 (Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

“Chithunzi cha Malo Enieniwo”​—Zimene Chihema Chinkaimira

GUWA LA NSEMBE

Kufunitsitsa kwa Mulungu kulandira nsembe ya Yesu.​—AHEBERI 13:10-12.

MKULU WA ANSEMBE

Yesu.​—AHEBERI 9:11.

1 Pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe ankapereka nsembe yophimba machimo a anthu onse.​—LEVITIKO 16:15, 29-31.

1 Pa Nisani 14, mu 33 C.E., Yesu anapereka moyo wake nsembe yotiwombola.​—AHEBERI 10:5-10; 1 YOHANE 2:1, 2.

MALO OYERA

Kubadwanso ndi mzimu kwa Yesu ali padziko lapansi.​—MATEYO 3:16, 17; AROMA 8:14-17; AHEBERI 5:4-6.

NSALU YOTCHINGA

Thupi la Yesu lanyama linali chotchinga chimene chinasiyanitsa moyo wake wapadziko lapansi ndi wakumwamba.​—1 AKORINTO 15:44, 50; AHEBERI 6:19, 20; 10:19, 20.

2 Mkulu wa ansembe ankadutsa nsalu yotchinga imene inali pakati pa Malo Oyera ndi Malo Oyera Kopambana.

2 Ataukitsidwa, Yesu anakhala ngati wadutsa nsalu yotchinga. Anachita zimenezi popita kumwamba kuti “akaonekere pamaso pa Mulungu mwiniyo kaamba ka ife.”​—AHEBERI 9:24-28.

MALO OYERA KOPAMBANA

Kumwamba.​—AHEBERI 9:24.

3 Akalowa m’Malo Oyera Kopambana, mkulu wa ansembe ankadontheza ena mwa magazi ansembeyo kutsogolo kwa likasa la chipangano.​—LEVITIKO 16:12-14.

3 Popereka kwa Mulungu moyo wake wangwiro umene anaupereka nsembe ali padziko, Yesu anapereka njira yeniyeni yophimbira machimo athu.​—AHEBERI 9:12, 24; 1 PETULO 3:21, 22.