Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi mwana wamwamuna woyamba kubadwa anali ndi mwayi wapadera komanso udindo wotani?

Kuyambira kale mtundu wa Isiraeli usanakhazikitsidwe, atumiki a Mulungu ankapereka mwayi wapadera kwa ana awo aamuna oyamba kubadwa. Bambo akamwalira, mwana woyamba ankatenga udindo wotsogolera banjalo. Iye ankasamalira banjalo ndiponso kulamulira anthu onse amene ankakhala pakhomopo. Mwana woyambayo ankatsogoleranso banja lonselo polambira Mulungu. Iye ankalandira mbali yaikulu kwambiri ya cholowa chimene ana onse aamuna a m’banjalo ankalandira. Mwana woyambayo ankalandira zinthu zochuluka kuwirikiza kawiri kuyerekezera ndi zimene ena onse ankalandira.

M’nthawi imeneyo, mwana wamwamuna woyamba kubadwa ankatha kutaya mwayi umenewu. Mwachitsanzo, Esau anagulitsa ukulu wake kwa mng’ono wake. (Genesis 25:30-34) Yakobo analanda ukulu kwa mwana wake woyamba Rubeni n’kumupatsa Yosefe. Rubeni analandidwa mwayi wapaderawu chifukwa cha khalidwe lake loipa. (1 Mbiri 5:1) Komabe, Chilamulo cha Mose sichinkalola kuti mwamuna wamitala alande udindowu kwa mwana wa mkazi woyamba n’kuupereka kwa mwana wa mkazi wina amene ankamukonda kwambiri. Mwachibadwa, mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa anali ndi mwayi wapadera ndipo bamboyo ankafunika kutsatira dongosolo limeneli.​—Deuteronomo 21:15-17.

N’chifukwa chiyani alembi ndi Afarisi ankavala “timapukusi tokhala ndi malemba”?

Yesu anadzudzula alembi ndi Afarisi, omwe ankakonda kumutsutsa, chifukwa iwo ankakulitsa “timapukusi tokhala ndi malemba timene [ankavala] monga zithumwa.” (Mateyo 23:2, 5) Alembi ndi Afarisi komanso anthu owatsatira ankamangirira timapukusi tachikopa pamphumi pawo. Timapukusiti tinkakhala takuda komanso tamakona anayi ngati kabokosi. Timapukusi tina ankatimangirira pamkono wawo wakumanzere pafupi ndi kukhwapa, moyandikana ndi mtima. M’timabokosi timeneti ankasungamo mavesi ena a m’Malemba. Mwambo wovala timapukusi timeneti unayamba poganiza kuti n’zimene Mulungu ankatanthauza pamene anauza Aisiraeli kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; . . . ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu.” (Deuteronomo 6:6-8) Nthawi yeniyeni imene anthu anayamba mwambo wovala timapukusiti sikudziwika, koma akatswiri ambiri amati mwambowu unayamba m’zaka za m’ma 200 kapena 100 B.C.E.

Yesu anadzudzula anthu ovala timapukusiti pa zifukwa ziwiri. Choyamba, alembi ndi Afarisi ankavala mapukusi aakulu kwambiri n’cholinga choti ena aziwaona kuti ndi olungama kwambiri. Chachiwiri, anthuwa ankaona timapukusiti ngati zithumwa zoti zingathe kuwateteza. M’Chigiriki, timapukusiti timatchedwa phylakterion (filakiteliyoni). Malinga ndi mmene amagwiritsidwira ntchito m’mabuku ena omwe si a m’Baibulo, mawuwa amamasuliridwanso kuti “mudzi wa asilikali,” “mpanda wolimba kwambiri,” kapenanso “chodzitetezera.”