Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuchita Zimenezi N’kusaonadi Mtima?

Kodi Kuchita Zimenezi N’kusaonadi Mtima?

Kodi Kuchita Zimenezi N’kusaonadi Mtima?

“Mungonama pang’ono pa lipoti lanu la ngozi imene mwachita ndipo zonse zikhala bwino.”

“Akuluakulu a boma otolera msonkho si ofunika kuwauza zonse.”

“Choipa n’kugwidwatu basi.”

“Palibe chifukwa choperekera ndalama pa zinthu zomwe munthu ukhoza kuzipeza mwaulere.”

MWINA munamvapo anthu akunena mawu ngati amenewa mutawafunsa kuti akupatseni malangizo pa nkhani zimene zingafune kuti muperekepo ndalama. Zikuoneka kuti anthu ena savutika kupeza “njira zothetsera mavuto.” Komabe tingachite bwino kudzifunsa kuti, Kodi titatsatira njira zimenezo kukhaladi kuona mtima?

Masiku ano chinyengo chili ponseponse. Anthu ambiri amaona kuti kunama, katangale ndi kuba si kulakwa. Iwo amaona kuti kuchita zimenezi ndi njira yabwino yozembera chilango ndiponso yowathandiza kuti apeze ndalama zambiri kapena kuti zinthu ziyambe kuwayendera bwino. Anthu ambiri olemekezeka ndi omwe amakonda kuchita zachinyengo kwambiri. Mwachitsanzo, nkhani zakatangale m’dziko lina ku Ulaya, zinawonjezereka ndi 85 peresenti mu 2005 ndi 2006. Chiwerengero chimenechi sichinaphatikizepo nkhani zing’onozing’ono zakatangale zimene ena amaona kuti ndi “timachimo ting’onoting’ono.” Mwina n’chifukwa chake m’dziko limenelo makampani ambiri komanso akuluakulu andale anakhudzidwa ndi milandu yogwiritsa ntchito madipuloma achinyengo kuti zinthu ziwayendere bwino.

Komabe, ngakhale kuti m’dzikoli anthu ndi osaona mtima, pali anthu ena amene amafuna kuchita zinthu moona mtima. Mwina inuyo ndi mmodzi wa anthu amenewa, ndipo chifukwa chokonda kwambiri Mulungu mumafuna kuchita zinthu zoyenera. (1 Yohane 5:3) Muyenera kuti mungagwirizane ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Chifukwa cha zimenezi, tikukupemphani kuganizira zochitika zina zimene zingapangitse kuti “kuchita zinthu zonse moona mtima” kukhale kovuta. Tikambirananso mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize pa nkhani zimenezi.

Ndani Ayenera Kulipira Ndalama Pakachitika Ngozi?

Mtsikana winawake dzina lake Lisa * anachititsa ngozi. Galimoto yake inawomba galimoto ina. Pa ngoziyi palibe amene anavulala koma magalimoto onsewo anawonongeka. Malinga ndi malamulo a m’dziko lawo, achinyamata amalipira ndalama zambiri za inshuwalansi ya galimoto zawo. Ndipo akachita ngozi inshuwalansiyo imawonjezereka. Koma panthawi ya ngoziyi Lisa anali ndi msuweni wake Gregor, yemwe ndi wamkulu poyerekeza ndi iye. Choncho mnzawo wina anawauza kuti pa lipoti la ngoziyo aname kuti amene amayendetsa galimotoyo ndi Gregor. Anamuuza zimenezi kuti Lisa asalipire ndalama zambiri za inshuwalansi. Njira imeneyi inaoneka ngati yanzeru. Kodi pamenepa Lisa akanatani?

Kuti makampani a inshuwalansi alipirire anthu amene achita ngozi, amawonjezera mtengo wa ndalama za inshuwalansi. Choncho ngati Lisa akanatsatira maganizo a mnzakeyo ndiye kuti akanachititsa kuti anthu ena omwe amalipira ndalama za inshuwalansi kukampani ya msuweni wakeyo alipire ndalama zambiri zimene Lisa amafunika kulipira. Kuchita zimenezi kukanakhala kunama komanso kubera anthu ena. Zimenezi ndi zofanananso ndi kulemba zabodza pa lipoti lokhudza ngozi imene munthu wachita pofuna kuti kampani ya inshuwalansi imupatse ndalama zambiri.

Ndi zoona kuti anthu angapewe kuchita zachinyengo poopa kuti awalipiritsa ndalama zambiri akagwidwa. Koma chifukwa chachikulu chokhalira oona mtima chimapezeka m’Mawu a Mulungu. Limodzi mwa Malamulo Khumi limati: “Usabe.” (Eksodo 20:15) Mtumwi Paulo anakumbutsa Akhristu za lamulo limeneli pamene analemba kuti: “Wakubayo asabenso.” (Aefeso 4:28) Mukamatsatira Mawu a Mulungu pa nkhani ya inshuwalansi, mumapewa kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Komanso mumasonyeza kuti mumakonda ndiponso mumalemekeza lamulo la Mulungu komanso anzanu.​—Salmo 119:97.

“Zinthu za Kaisara kwa Kaisara”

Taganizirani za bambo wina dzina lake Peter, yemwe ndi wabizinesi. Nthawi ina atagula katundu woti azigwiritsa ntchito pa kampani yake, akauntanti wake anamuuza kuti aname kuti wagula makompyuta okwera mtengo kwambiri pofuna kuti boma lisawalipiritse ndalama zambiri zamsonkho. Iye anamuuza zimenezi chifukwa ankaona kuti boma silingakayikire kuti kampani ngati yawoyo ingaguledi makompyutawo ndipo silingafufuze kuti lidziwe ngati anaguladi katunduyo. Ngati akanakhoma msonkho wochepa, Peter sakanawononga ndalama zambiri. Kodi pamenepa akanatani? Kodi n’chiyani chikanamuthandiza kuti achite zinthu mwanzeru?

Mtumwi Paulo anauza Akhristu mu nthawi yake kuti: “Munthu aliyense azimvera olamulira aakulu . . . Perekani kwa onse zimene amafuna, kwa amene amafuna msonkho, perekani msonkho; kwa amene amafuna ndalama ya chiphaso, perekani ndalama ya chiphaso.” (Aroma 13:1, 7) Anthu amene amafuna kuti Mulungu aziwakonda amakhoma msonkho umene boma limafuna. Komabe ngati malamulo a m’dziko lanu amachotsera msonkho anthu ena kapena mabizinesi ena, sikulakwa kupempha kuti akuchotsereni ngati inuyo muli woyenerera.

Taganizirani nkhani inanso yokhudza kukhoma msonkho. David analembedwa ntchito ngati kalipentala pakampani ina. Koma anzake ndiponso anthu ena amamupempha kuti awapangire makabati ndi mipando. Iye amagwira ntchitoyo akaweruka kuntchito yake yolembedwa. Iwo amamuuza kuti amulipira ndalama zambiri kuposa zimene amalandira kuntchito kwake ndipo amamuuzanso kuti asawalembere lisiti. Zimenezi zingachititse kuti pasakhale umboni wantchito imene wagwira ndipo Davide sangakhome msonkho uliwonse. Anthu ambiri sangakane zimenezi. Koma chifukwa choti David amafunitsitsa kusangalatsa Mulungu, kodi anayenera kutani pa nkhaniyi?

Ngakhale kuti munthu sangagwidwe atachita zimenezi, iye amakhala akuzemba kukhoma msonkho umene ayenera kukhoma ku boma. Yesu anatilamula kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mateyo 22:17-21) Yesu ananena zimenezi pofuna kukonza maganizo a omvera ake pa nkhani ya msonkho. Akuluakulu a boma amene Yesu anawatchula kuti Kaisara ankaona kuti ali ndi ufulu wolandira ndalama zamsonkho. Choncho, otsatira Khristu amaona kuti ayenera kukhoma misonkho yonse malinga ndi zimene Malemba amanena.

Kubera Mayeso

Mtsikana wina wakusekondale dzina lake Marta ankakonzekera kulemba mayeso. Popeza ankadziwa kuti akakhoza bwino angadzathe kupeza ntchito yabwino, analimbikira kwambiri kuwerenga. Nawonso anzake ena a m’kalasi yake anakonzekera koma mosiyana ndi mmene iye anakonzekerera. Anzakewo anakonzekera kuti adzabere mayeso pogwiritsa ntchito zipangizo ngati mafoni a m’manja ndi zipangizo zina za magetsi. Kodi Marta anayenera kubera mayeso kuti adzakhoze kwambiri popeza zimaoneka ngati aliyense anali kubera?

Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto kubera mayeso chifukwa choti anthu ambiri amaberanso. Iwo amaganiza kuti “choipa n’kugwidwatu basi.” Komabe Akhristu oona amadziwa kuti maganizo amenewa ndi olakwika. Ngakhale kuti aphunzitsi anu sangaone kuti mukubera, pali winawake amene amaona. Yehova Mulungu amadziwa zonse zimene tikuchita ndipo adzatiweruza chifukwa cha zochita zathu. Paulo analemba kuti: “Palibe cholengedwa chobisika pamaso pake. Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (Aheberi 4:13) Kudziwa kuti Mulungu amationa n’cholinga choti tizichita zoyenera, zimatilimbikitsa kuti tizichita zinthu moona mtima polemba mayeso.

Kodi Inuyo Mungatani?

Lisa, Gregor, Peter, David, ndi Marta anaona kuti kuona mtima ndi nkhani yaikulu. Choncho anasankha kuti achite zinthu moona mtima kuti akhale ndi chikumbumtima choyera komanso kuti akhale okhulupirika. Nanga inuyo, kodi mungatani ngati zimenezi zitakuchitikirani?

Mwina anzanu akusukulu ndiponso omwe mumakhala nawo pafupi angaone kuti kunama kapena kuba sikulakwa. Iwo angafike pomakusekani n’cholinga choti muzichita nawo zimene iwo amachita. Kodi chingakuthandizeni n’chiyani kuti muchite zinthu mwanzeru ngakhale kuti ena akukukakamizani kuchita zinthu mosaona mtima?

Kumbukirani kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kumathandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino komanso kuti Mulungu azitikonda kwambiri. Mfumu Davide inalemba kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. . . . Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka ku nthawi zonse.” (Salmo 15:1-5) Kukhala ndi chikumbumtima choyera komanso ubwenzi wabwino ndi Mulungu wathu wakumwamba ndi kofunika kwambiri kuposa zinthu zimene tingapeze mosaona mtima.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Tasintha mayina ena.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Wakubayo asabenso.”

Kulemekeza malamulo a Mulungu komanso kukonda anthu ena kumatilimbikitsa kuchita zinthu moona mtima pa nkhani yolipira inshuwalansi

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Perekani kwa onse zimene amafuna, kwa amene amafuna msonkho, perekani msonkho.”

Kuti Mulungu azitikonda, timakhoma msonkho umene boma limafuna

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Zinthu zonse . . . ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.”

Ngakhale kuti mwina aphunzitsi athu sangatigwire tikubera mayeso, timafuna kukhala oona mtima kwa Mulungu

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 14]

Kuba “Kwachinsinsi”

Tiyerekezere kuti mnzanu wagula pulogalamu yatsopano yapakompyuta ndipo nanunso mukufuna mutakhala nayo yanu. Iye wakuuzani kuti akupatsani pulogalamuyo kuti mukopere n’cholinga choti musawononge ndalama pogula ina. Kodi kuchita zimenezi n’kusaona mtima?

Munthu akagula pulogalamu yapakompyuta amavomera kutsatira malamulo a kampani imene inakonza pulogalamuyo. Mwina malamulowo angalole munthu kugwiritsa ntchito pulogalamuyo pakompyuta imodzi yokha basi. Choncho, kukopera pulogalamu imene munthu wina anagula n’kuphwanya malamulo a kampani imene inakonza pulogalamuyo ndipo ndi mlandu. (Aroma 13:4) Komanso kukopera pulogalamu mwanjira imeneyi ndi kuba, chifukwa zimaphwanya ufulu wa kampani yokonza pulogalamuyo wolandira ndalama zimene imayenera kulandira.​—Aefeso 4:28.

Koma ena anganene kuti: ‘Palibe amene akundiona.’ Ndi zoona kuti mwina ena sangaone zimene tachita, koma tiyenera kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Tonse timafuna kuti tikagwira ntchito tilipiridwe ndalama zokwanira ndiponso timafuna kuti ena alemekeze zinthu zathu. Choncho, nafenso tiyenera kuchita zinthu moganizira ena. Tiyenera kupewa kuba “mwachinsinsi” zinthu zimene ena apanga. *​—Eksodo 22:7-9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 40 Zinthu zimenezi ndi zimene ena angathe kukopera monga nyimbo, mabuku kapena mapulogalamu apakompyuta, kaya zikhale zochita kupulinta kapena zosungidwa pakompyuta. Zikuphatikizanso zizindikiro zimene kampani imaika pa pulogalamuyo, laisensi, zinsinsi zochitira malonda ndi malamulo okhudza kufalitsa pulogalamuyo.