Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi pa Tsiku la Yehova Padzachitika Zotani?

Kodi pa Tsiku la Yehova Padzachitika Zotani?

Kodi pa Tsiku la Yehova Padzachitika Zotani?

“Tsiku la Yehova lidzafika ngati mbala, . . . ndipo dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.”​—2 PET. 3:10.

1, 2. (a) Kodi dongosolo la zinthu loipali lidzatha bwanji? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

YEHOVA walola kuti dongosolo loipa la Satanali likhalepo chifukwa chakuti anthu amakhulupirira bodza lakuti akhoza kudzilamulira bwinobwino popanda kutsogozedwa ndi iye. (Sal. 2:2, 3) Kodi zinthu zimene zilipo chifukwa chabodza zingakhalepo mpaka kalekale? Ayi ndithu! Komabe sitingayembekezere kuti dziko la Satanali lidzatha lokha. Dzikoli lidzaonongedwa ndi Mulungu pa nthawi yake ndiponso mmene akufunira. Zimene Mulungu adzachitire dziko loipali zidzasonyeza bwinobwino kuti ndi wachilungamo ndiponso wachikondi.​—Sal. 92:7; Miy. 2:21, 22.

2 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Tsiku la Yehova lidzafika ngati mbala, pamene miyamba idzachoka ndi mkokomo waukulu, koma zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi pokhala zitatentha kwambiri, zidzasungunuka, ndipo dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.” (2 Pet. 3:10) Kodi “miyamba” ndi “dziko lapansi” zimene zatchulidwa pa lembali n’chiyani? Nanga kodi “zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi” zimene zidzasungunuke n’chiyani? Ndipo kodi Petulo anatanthauza chiyani pamene anati “dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera”? Kudziwa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kukonzekera zinthu zochititsa mantha zimene zichitike posachedwapa.

Miyamba ndi Dziko Lapansi Zimene Zidzachoka

3. Kodi “miyamba” yotchulidwa pa 2 Petulo 3:10 n’chiyani, ndipo idzachoka bwanji?

3 Mawu akuti “miyamba” akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa m’Baibulo, nthawi zambiri amatanthauza maboma a anthu amene akulamulira. (Yes. 14:13, 14; Chiv. 21:1, 2) Choncho, ‘miyamba imene idzachoka’ ikuimira ulamuliro wa m’dziko losaopa Mulungu. Ndipo mfundo yakuti idzachoka “ndi mkokomo waukulu” ikusonyeza kuti miyamba imeneyi idzatha mofulumira.

4. Kodi “dziko lapansi” n’chiyani ndipo lidzawonongedwa bwanji?

4 “Dziko lapansi” limaimira anthu amene salambira Mulungu. Dziko lotere linaliponso m’masiku a Nowa ndipo Mulungu analiwononga ndi Chigumula. Baibulo limati: “Ndipo mwa mawu amodzimodziwo, miyamba imene ilipo tsopano limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Pet. 3:7) Chigumula chinawononga anthu onse oipa nthawi imodzi, koma chiwonongeko chimene chikubwera chizidzachitika pang’onopang’ono pa “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:14) Poyamba, Mulungu adzachititsa olamulira a ndale a dzikoli kuwononga “Babulo Wamkulu” ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti iye amadana ndi zipembedzo zonyenga zomwe ndi mkazi wachiwerewere. (Chiv. 17:5, 16; 18:8) Ndiyeno pa nthawi ya nkhondo ya Armagedo, imene ndi chimake cha chisautso chachikulu, Yehova adzachotseratu mbali yotsala ya dziko la Satana.​—Chiv. 16:14, 16; 19:19-21.

“Zinthu Zimene Zimapanga Miyamba ndi Dziko Lapansi . . . Zidzasungunuka”

5. Kodi zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi zikuphatikizapo chiyani?

5 Kodi “zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi” zimene “zidzasungunuka” n’chiyani? Zinthu zimene Petulo anatchulazi zikutanthauza zinthu zimene zimachititsa kuti anthu a m’dzikoli azikhala ndi makhalidwe, mtima, zochita ndiponso zolinga zoipa. “Zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi” zimaphatikizapo “mzimu wa dziko” umene “ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (1 Akor. 2:12; werengani Aefeso 2:1-3.) Mzimu, kapena kuti “mpweya” umenewu ukuonekera kwambiri m’dziko la Satanali. Umalimbikitsa anthu kuganiza, kukhala ndi zolinga, kulankhula ndi kuchita zinthu m’njira zimene zimasonyeza maganizo a Satana yemwe ndi wonyada, wotsutsa ndiponso “wolamulira wa mphamvu ya mumpweya.”

6. Kodi mzimu wa dziko umaonekera bwanji?

6 Choncho, mozindikira kapena mosazindikira, anthu amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa dzikoli amalola kuti maganizo awo ndiponso mtima wawo zizitsogoleredwa ndi Satana. Motero, amasonyeza maganizo ndi mtima wa Satanayo. Zimenezi zimachititsa kuti iwo azingochita zofuna zawo mosaganizira zofuna za Mulungu. Amachita zinthu modzikuza ndiponso modzikonda. Iwo amapandukira ulamuliro ndipo amangotsatira “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso.”​—Werengani 1 Yohane 2:15-17. *

7. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kutchinjiriza mtima wathu’?

7 Ndiyetu n’zofunika kwambiri kuti ‘titchinjirize mtima wathu’ mwa kusankha mwanzeru zinthu monga anthu ocheza nawo, zimene timawerenga, zosangalatsa ndiponso zinthu zimene timatsegula pa Intaneti. (Miy. 4:23) Mtumwi Paulo alemba kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinga ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:8) Chenjezo limeneli ndi lofunika kwambiri panopa pamene tsiku la Yehova likuyandikira chifukwa ‘kutentha’ kwake kudzasungunula “zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi” za m’dongosolo la Satanali. Izi zidzasonyeza kuti zinthu zimenezi sizingapulumuke chifukwa cha kutentha kwa mkwiyo wa Mulungu. Zimenezi zikutikumbutsa mawu opezeka pa Malaki 4:1 akuti: “Likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lili n’kudza lidzawayatsa.”

“Dziko Lapansi ndi Ntchito Zake Zidzaonekera Poyera”

8. Kodi dziko lapansi ndi ntchito zake “zidzaonekera poyera” motani?

8 Kodi Petulo ankatanthauza chiyani pamene analemba kuti “dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera”? Petulo ankatanthauza kuti pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzachititsa kuti dziko la Satana lionekere poyera kuti ndi loyenera kuwonongedwa chifukwa chakuti limatsutsana naye komanso limatsutsana ndi Ufumu wake. Lemba la Yesaya 26:21 linalosera za nthawi imeneyi kuti: “Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwawo; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.”

9. (a) Kodi tiyenera kupewa chiyani ndipo chifukwa chiyani? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati ndipo chifukwa chiyani?

9 Pa tsiku la Yehova, zochita za anthu amene amatsatira dzikoli ndi mzimu wake woipa zidzaonekera poyera ndipo adzaphana okhaokha. Zinthu zachiwawa zimene anthu amasangalala nazo, zomwe zafala masiku ano, ziyenera kuti zikukonzekeretsa maganizo a anthu kuti ‘adzagwire yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukire dzanja la mnzake.’ (Zek. 14:13) Ndiyetu n’zofunika kwambiri kuti tizipewa zinthu monga mafilimu, mabuku, masewera a pa kompyuta ndi zilizonse zimene zingatichititse kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amadana nawo monga kunyada ndi kukonda chiwawa. (2 Sam. 22:28; Sal. 11:5) M’malomwake, tiyenera kukhala ndi zipatso za mzimu woyera wa Mulungu chifukwa makhalidwe amenewa sadzapsa ndi kutentha kwa tsiku la Yehova.​—Agal. 5:22, 23.

“Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano”

10, 11. Kodi “miyamba yatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano” n’chiyani?

10 Werengani 2 Petulo 3:13. “Miyamba yatsopano” ndi Ufumu wakumwamba wa Mulungu womwe unakhazikitsidwa mu 1914 pamene “nthawi zoikika za amitundu” zinatha. (Luka 21:24) Boma limeneli ndi lopangidwa ndi Khristu Yesu pamodzi ndi olamulira anzake okwana 144,000, ndipo ambiri mwa anthu amenewa analandira kale mphoto yawo yakumwamba. M’buku la Chivumbulutso anthu osankhidwa amenewa amafotokozedwa kuti ndi “mzinda woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, wokonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake.” (Chiv. 21:1, 2, 22-24) Mu Isiraeli wakale, mzinda wa Yerusalemu unali likulu la ulamuliro wa Isiraeli, choncho Yerusalemu watsopano ndiponso Mkwati wake ndi amene apanga boma la dongosolo latsopano. Mzinda wakumwamba umenewu ‘udzatsika kuchokera kumwamba’ mwa kuyamba kuyendetsa zinthu padziko lapansi.

11 Mawu akuti “dziko lapansi latsopano” akunena za anthu amene adzakhale padziko lapansi omwe adzasonyeze kuti akufunitsitsa kugonjera Ufumu wa Mulungu. Paradaiso wauzimu amene anthu a Mulungu akusangalala naye panopa, adzakhalapobe ‘m’dziko lapansi lokhala anthu likudzalo’ lomwe ndi lokongola ndipo awa adzakhala malo ake oyenerera. (Aheb. 2:5) Kodi tingatani kuti tidzakhale m’dongosolo latsopano la zinthu limenelo?

Konzekerani Tsiku Lalikulu la Yehova

12. N’chifukwa chiyani anthu amene salambira Yehova adzadabwa kwambiri ndi mmene tsiku la Yehova lidzafikire?

12 Paulo ndiponso Petulo analosera kuti tsiku la Yehova lidzabwera mwadzidzidzi “ngati mbala.” (Werengani 1 Atesalonika 5:1, 2.) Ngakhale Akhristu oona amene akudikira tsiku la Yehova adzadabwa ndi mafikidwe a tsikuli. (Mat. 24:44) Nawonso anthu amene salambira Yehova adzadabwa ndipo kuwonjezera pamenepo adzakumana ndi zinthu zina. Paulo analemba kuti: “Pamene [anthu amene salambira Yehova] azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zopweteka za mkazi wapathupi, ndipo sadzapulumuka konse.”​—1 Ates. 5:3.

13. Kodi tingatani kuti tisapusitsidwe ndi mfuu yakuti “Bata ndi mtendere!”?

13 Ziwanda ndi zimene zidzachititse anthu kufuula kuti: “Bata ndi mtendere!” Koma bodza limeneli silidzapusitsa atumiki a Yehova. Paulo analemba kuti: “Simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni mmene lidzachitire kwa mbala. Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala ndi ana a usana.” (1 Ates. 5:4, 5) Choncho tiyeni tikhalebe m’kuwala ndipo titalikirane ndi mdima wa dziko la Satanali. Petulo analemba kuti: “Okondedwa, pokhala odziwiratu zimenezi, chenjerani kuti musasochere pokopeka ndi zolakwa za anthu [aphunzitsi onyenga a mumpingo wachikhristu] ophwanya malamulo, kutinso musagwe polephera kuchirimika kwanu.”​—2 Pet. 3:17.

14, 15. (a) Kodi Yehova amatilemekeza bwanji? (b) Kodi ndi mawu ouziridwa ati amene tiyenera kuwakumbukira nthawi zonse?

14 Onani kuti Yehova sakungotiuza kuti ‘tichenjere.’ Koma mokoma mtima watilemekeza mwa ‘kutidziwitsiratu’ mmene zinthu zidzachitikire mtsogolo.

15 Komabe n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena sakhudzidwa n’komwe ndiponso amakayikira malangizo akuti tiyenera kukhala maso. Iwo amati: ‘Malangizo amenewa takhala tikuwamva kuyambira kalekale.’ Koma anthu amenewa ayenera kudziwa kuti akamanena choncho ndiye kuti akukayikira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yehova ndiponso Mwana wake. Yehova anati: “Uwalindirire.” (Hab. 2:3) Nayenso Yesu anati: “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwera.” (Mat. 24:42) Kuwonjezera pamenepa Petulo analemba kuti: “Lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu. Teroni poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Pet. 3:11, 12) Kapolo wokhulupirika ndiponso Bungwe Lolamulira sadzaona mopepuka malangizo amenewa.

16. Kodi tiyenera kupewa mtima wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

16 “Kapolo woipa” ndi amene amanena kuti Mbuye akuchedwa. (Mat. 24:48) Kapolo woipa ameneyu ali m’gulu la anthu amene afotokozedwa pa 2 Petulo 3:3, 4. Pa lembali, Petulo analemba kuti, “m’masiku otsiriza kudzakhala onyodola” amene ‘potsatira zilakolako zawo’ amanyoza anthu amene amamvera malangizo akuti azikumbukira tsiku la Yehova. M’malo moti aziganizira kwambiri zinthu za Ufumu, anthu onyozawa amangodziganizira okha ndiponso amangoganizira zilakolako zawo. Tiyenera kusamala kuti tisakhale ndi mtima wosamvera ngati umenewu chifukwa ndi woopsa. Koma ‘tiziona kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.’ Tingachite zimenezi mwa kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira ndiponso mwa kupewa kudera nkhawa kwambiri za nthawi imene zinthu zidzachitike chifukwa umenewu ndi udindo wa Yehova Mulungu.​—2 Pet. 3:15; werengani Machitidwe 1:6, 7.

Khulupirirani Mulungu wa Chipulumutso

17. Kodi Akhristu okhulupirika anatani potsatira malangizo a Yesu akuti athawe ku Yerusalemu, ndipo n’chifukwa chiyani?

17 Asilikali a Roma ataukira Yudeya mu 66 C.E., Akhristu okhulupirika anamvera malangizo a Yesu ndipo anathawa nthawi yomweyo. (Luka 21:20-23) Kodi n’chifukwa chiyani iwo achita zinthu mwachangu ndiponso mosazengereza? N’zosakayikitsa kuti chinali chifukwa chakuti ankakumbukira chenjezo la Yesu. Iwo ankadziwa kuti zimene anasankhazi zikhala ndi mavuto ake malinga ndi zimene Khristu anawachenjezeratu. Koma ankadziwanso kuti Yehova sadzasiya anthu ake okhulupirika.​—Sal. 55:22.

18. Kodi mawu a Yesu a pa Luka 21:25-28 amakuchititsani kumva bwanji mukaganizira chisautso chachikulu chimene chikubwera?

18 Nafenso tiyenera kukhulupirira kwambiri Yehova chifukwa ndi iye yekha amene angadzatipulumutse dongosolo la zinthu lilipoli likamadzawonongedwa pa chisautso chachikulu chomwe sichinachitikepo ndi kale lonse. Pa nthawi ina chisautso chachikulu chitayamba, koma Yehova asanapereke chiweruzo ku mbali yotsala ya dzikoli, anthu ‘adzakomoka pochita mantha ndi poyembekezera zimene zidzachitikire dziko lapansi kumene kuli anthu.’ Pamene adani a Mulungu azidzanjenjemera ndi mantha, atumiki a Yehova okhulupirika sadzaopa. Iwo adzasangalala podziwa kuti chipulumutso chawo chayandikira.​—Werengani Luka 21:25-28.

19. Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana chiyani?

19 Anthu amene sali mbali ya dzikoli, ndiponso “zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi” akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Monga taonera, kuti tidzapeze moyo tiyenera kupewa zoipa. Komabe nkhani yotsatira ikusonyeza kuti kungopewa zoipa sikokwanira. Tiyenera kukhalanso ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo ndiponso kuchita zinthu zovomerezeka pamaso pake.​—2 Pet. 3:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya makhalidwe amene mzimu wa dziko umachititsa, onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 323-327.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi zinthu izi zikuimira chiyani?

‘miyamba ndi dziko lapansi’ zimene zilipo

“zinthu zimene zimapanga miyamba ndi dziko lapansi”

‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi ‘mungatchinjirize bwanji mtima wanu,’ nanga mungatani kuti muzisiyana ndi dzikoli?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timaona kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso’?