Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Saopanso Kutha kwa Dziko

Saopanso Kutha kwa Dziko

Saopanso Kutha kwa Dziko

CHAKUMAPETO kwa zaka za m’ma 1970, Gary ndi mkazi wake Karen, ankakhulupirira kwambiri kuti dziko latsala pang’ono kutha. Choncho anachoka mumzinda ndi kusamukira kudera lina kumene kunalibe anthu ambiri, kuti azikapanga okha china chilichonse chimene angafunikire pa moyo wawo. Anachita zimenezi n’cholinga choti adzapulumuke dziko likadzatha.

Kuti adziwe maluso owathandiza kupanga zinthu pa okha, anagula mabuku, anachita nawo maphunziro osiyanasiyana komanso anafunsa nzeru kwa anthu ambiri. Ndiponso iwo anadzala mitengo 50 yazipatso zosachedwa kucha ndipo analimanso dimba. Anasonkhanitsa mbewu ndi zipangizo zosiyanasiyana zogwirira ntchito. Anaphunziranso kukonza chakudya chimene akolola kuti chikhale nthawi yaitali chisanawole. Mnzawo wina anawaphunzitsa kupha nyama ndi kuiwamba kuti isawonongeke. Karen anaphunziranso mmene angapezere zomera ndiponso mizu m’nkhalango zimene angadzadye chakudya chitatheratu. Nayenso Gary anaphunzira kupanga mafuta oyatsira moto pogwiritsa ntchito chimanga. Iye anaphunziranso kukhoma uvuni wachitsulo ndiponso kumanga nyumba yosadalira magetsi kapena madzi ogula.

Karen ananena kuti: “Chifukwa cha zoipa zimene zinkachitika m’dziko panthawiyo, ndinkangoona ngati zinthu zonse padziko lapansi zatsala pang’ono kuwonongeka.” Gary anafotokoza kuti: “Mofanana ndi achinyamata ena, ndinalowa m’magulu a anthu ofuna kuthetsa tsankho, nkhondo ya ku Vietnam komanso katangale. Koma mwamsanga ndinazindikira kuti sitingathetse mavutowo. Ndinkangoona ngati anthu atsala pang’ono kudziwononga okha.”

Gary ananena kuti: “Usiku wina ndinalibe chochita, choncho ndinayamba kuwerenga Baibulo. Ndinawerenga kuyambira Mateyo mpaka Chivumbulutso. Tsiku lotsatira, ndinayambanso kuliwerenga pang’onopang’ono ndipo ndinamaliza patatha masiku anayi. Tsiku lachisanu, ndinauza Karen kuti: ‘Ano ndi masiku otsiriza. Mulungu watsala pang’ono kuwononga anthu oipa kuti ayeretse dziko lapansi. Choncho tifunika kufunafuna anthu amene adzapulumuke.’” Kenako, Gary ndi Karen anayamba kusinthasintha zipembedzo pofunafuna anthu amene akukonzekera kuti adzapulumuke.

Pasanapite nthawi, kunabwera wa Mboni za Yehova ndi kuyamba kuphunzira nawo Baibulo. Karen ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri chifukwa wa Mboniyo anandithandiza kumvetsa bwino Baibulo. Ndinkafunitsitsa nditadziwa zoona zokhudza nthawi ya mapeto ndipo anandithandizadi kudziwa zoona zenizeni. Anandithandizanso kudziwa kuti Mulungu watikonzera zabwino m’tsogolo. Koma chofunika kwambiri ndi chakuti ndinayamba kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wanga wakumwamba, amene ndi Mlengi ndiponso Mulungu wa chilengedwe chonse.”

Gary ananena kuti: “Ndinayamba kukhala moyo wosangalala. Nditangoyamba kuphunzira Baibulo sindinafune kusiya. Ndinawerenga ulosi wosiyanasiyana m’Baibulo wokhudza mapeto ndipo ndinafufuza n’kuona kuti unali kukwaniritsidwa. Chifukwa cha zimenezi, ndinayamba kukhulupirira kuti posachedwapa Mulungu athetsa mavuto onse. Ndinaonanso kuti munthu aliyense ayenera kukonzekera moyo wabwino umene Mulungu akufuna kuti tidzakhale nawo, osati kukonzekera kutha kwa dziko.” Gary ndi Karen anayamba kukhulupirira kuti kutsogolo kuli zabwino. M’malo momada nkhawa ndi kutha kwa dziko, anayamba kukhulupirira kuti Mulungu adzathetsa mavuto a anthu ndipo adzakonza dziko lapansi kuti likhale paradaiso.

Papita zaka 25 Gary ndi Karen ataphunzira Baibulo. Kodi masiku ano akuchita chiyani? Karen ananena kuti: “Ndikupitirizabe kulimbitsa chikondi ndi chikhulupiriro changa pa Yehova Mulungu ndipo ndikuyesetsa kuthandiza ena kuti nawonso ayambe kukonda ndi kukhulupirira Mulungu. Ine ndi Gary timathandizana polimbitsa banja lathu ndiponso timapembedza Mulungu mogwirizana. Timayesetsa kuchita zinthu mwadongosolo ndiponso timakhala ndi moyo wosafuna zambiri. Timachita zimenezi n’cholinga choti tithandize anthu ena.”

Gary ananenanso kuti: “Kawirikawiri ndimapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere kudzathetsa mavuto amene anthu ambiri amakumana nawo. Nthawi zonse pamene ndikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu ena, ndimapemphera kuti ndithe kuthandiza ngakhale munthu mmodzi yekha kuti akhale ndi chiyembekezo cha zinthu zimene Baibulo limalonjeza. Kwa zaka zoposa 25 tsopano, Yehova wandichitira chifundo ndipo wakhala akuyankha pemphero limeneli. Ine ndi Karen timakhulupirira kuti posachedwapa Yehova asintha kwambiri zinthu padziko lapansi, koma sitiopanso kuti dziko lidzatha.”​—Mateyo 6:9, 10; 2 Petulo 3:11, 12.

[Chithunzi patsamba 9]

Masiku ano Gary ndi Karen akuthandiza ena kuti akhale ndi chiyembekezo cha zimene Baibulo limalonjeza