Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Paulo potchula mawu akuti “chionetsero cha kupambana” ankanena za chiyani?

Paulo analemba kuti: “Mulungu . . . amatitsogolera poguba pamodzi ndi Khristu pa chionetsero cha kupambana. Kudzera mwa ife, Mulungu akupangitsa fungo labwino la kum’dziwa iye kumveka ponseponse! Pakuti pamaso pa Mulungu ndife fungo la Khristu lonunkhira bwino kwa anthu amene akupulumuka ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongekawo ndife fungo lochokera ku imfa kupita ku imfa, kwa amene akupulumuka ndife fungo lochokera ku moyo kupita ku moyo.”​—2 Akorinto 2:14-16.

Pamenepa, mtumwi Paulo anali kunena za chikondwerero chimene Aroma ankachita pofuna kulemekeza mkulu wa asilikali amene wagonjetsa adani a Boma. Iwo anali kuchita chikondwerero chimenechi akuyenda mumsewu. Pa zochitika zimenezi, Aromawo anali kuonetsa anthu zimene afunkha komanso akaidi ogwidwa kunkhondo. Iwo anali kutenga ng’ombe n’kupita nazo kumalo operekera nsembe, kwinaku akukondwera ndi kutamanda mkulu wa asilikaliyo ndi gulu lake lankhondo. Pa mapeto pake anali kupereka nsembe ng’ombe zija ndipo n’kutheka kuti ambiri mwa akaidiwo anali kuwapha.

Buku lina limanena kuti pamene Paulo ananena za “fungo la Khristu lonunkhira bwino” lotanthauza moyo kwa anthu ena komanso imfa kwa ena, “ayenera kuti ankayerekezera ndi zimene Aroma ankachita pa zionetsero zawo za kupambana. Pa zionetserozi anali kufukiza nsembe zonunkhira, kwinaku akuguba mumsewu.” Bukulo limanenanso kuti: “Kwa Aroma, fungo limenelo linali kutanthauza kuti apambana, pamene kwa akaidi ogwidwa kunkhondowo linali kungowakumbutsa za chilango cha imfa chimene anali kuyembekezera kulandira.” *​—The International Standard Bible Encyclopedia.

Kodi “misanje” kapena kuti malo okwezeka amene amatchulidwa kawirikawiri m’Malemba Achiheberi anali chiyani?

Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawauza kuti ayenera kuwononga malo onse amene Akanani anali kupembedzerapo milungu yawo. Mulungu anawalamula kuti: ‘Muwononge mafano awo onse a miyala, ndi kuwononga mafano awo onse oyenga, ndi kupasula misanje yawo yonse.’ (Numeri 33:52) Malo amenewa amene ankapembedzerapo milungu yonyenga ayenera kuti ankapezeka pamwamba pa mapiri kapena anali kumanga pulatifomu pamalo ena monga pansi pa mtengo kapena pamalo ena m’mizinda. (1 Mafumu 14:23; 2 Mafumu 17:29; Ezekieli 6:3) Pamalo amenewa pankapezeka zinthu monga maguwa ansembe, zoimiritsa, kapena kuti zipilala zopatulika, zifaniziro ndi zinthu zinanso zimene anali kuzigwiritsa ntchito popembedza.

Asanamange kachisi ku Yerusalemu, Aisrayeli ankapembedza Yehova pamalo amene iye ankawavomereza. M’Baibulo, malo amenewo amatchedwanso kuti “misanje,” kapena kuti malo okwezeka. Mwachitsanzo, Samueli, amene anali mneneri wa Mulungu, anapereka nsembe “pamsanje” mumzinda winawake m’dziko la Zufi. Koma kachisi atamangidwa, mafumu osiyanasiyana amene anali okhulupirika kwa Yehova anayesetsa kuchotsa ‘misanje’ imeneyi.​—2 Mafumu 21:3; 23:5-8, 15-20; 2 Mbiri 17:1, 6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziwe tanthauzo lauzimu la chitsanzo cha Paulo chimenechi, werengani Nsanja ya Olonda ya November 15, 1990, tsamba 27.

[Chithunzi patsamba 23]

Chithunzi chosonyeza Aroma akuchita chionetsero, m’zaka za m’ma 100 C.E.

[Mawu a Chithunzi]

Photograph taken by courtesy of the British Museum

[Chithunzi patsamba 23]

Zoimiritsa zakale za ku Gezeri