Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Angathandize Anthu Ovutika?

Kodi Ndani Angathandize Anthu Ovutika?

Kodi Ndani Angathandize Anthu Ovutika?

“Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, . . . Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.”​—SAL. 72:1, 12.

1. Kodi zimene zinachitikira Davide zikutiphunzitsa chiyani za chifundo cha Mulungu?

MAWU amenewa, omwe mwina analemba ndi Mfumu Davide ya Isiraeli, ndi olimbikitsa kwambiri. Zaka zambiri iye asanalembe mawu amenewa, anamva chisoni kwambiri atachita chigololo ndi Bateseba. Pa nthawi imeneyi, Davide anapempha Mulungu kuti: “Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. . . . Ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. . . . Onani, ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Sal. 51:1-5) Chifukwa chakuti Yehova ndi wachifundo, amatiganizira podziwa kuti tinabadwa ndi uchimo.

2. Kodi Salmo 72 lingatithandize bwanji?

2 Yehova amadziwa kuti moyo wathu ndi womvetsa chisoni. Komabe, Baibulo linalosera kuti mfumu yodzozedwa ya Mulungu ‘idzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Idzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nidzapulumutsa moyo wa aumphawi.’ (Sal. 72:12, 13) Kodi anthu adzapulumutsidwa bwanji? Salmo 72 likufotokoza zimene zidzachitike. Salmo limeneli, lomwe ndi nyimbo yonena za ulamuliro wa Solomo mwana wa Davide, limapereka chithunzi cha mmene ulamuliro wa Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu udzathetsere mavuto a anthu.

Zimene Zidzachitike mu Ulamuliro wa Khristu

3. Kodi Solomo anapempha chiyani nanga Mulungu anamupatsa chiyani?

3 Davide, yemwe pa nthawiyo anali atakalamba, ananena kuti Solomo aikidwe kukhala mfumu ndipo anamupatsa malangizo. Solomo anatsatira mokhulupirika zonse zimene analangizidwa. (1 Maf. 1:32-35; 2:1-3) Kenako Yehova anaonekera kwa Solomo m’maloto ndipo anamuuza kuti: “Tapempha chimene ndikupatse.” Solomo anangopempha chinthu chimodzi kuti: “Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.” Chifukwa chakuti zimene Solomo anapemphazi zinasonyeza kuti anali wodzichepetsa, Yehova anam’patsa zimene anapemphazo ndiponso zinthu zina.​—1 Maf. 3:5, 9-13.

4. Kodi Mfumukazi ina inanena chiyani pofotokoza ulamuliro wa Solomo?

4 Yehova anadalitsa Solomo moti pa nthawi ya ulamuliro wake anthu ankakhala mwa mtendere ndipo zinthu zinkayenda bwino kwambiri kuposa ulamuliro wina uliwonse umene wakhalapo. (1 Maf. 4:25) Mmodzi mwa anthu amene anapita kukaona mmene ulamuliro wa Solomo unalili, ndi mfumukazi ya ku Seba limodzi ndi gulu la nduna zake. Mfumukaziyi inauza Solomo kuti: “Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa  . . . anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.” (1 Maf. 10:1, 6, 7) Koma Yesu ndi amene anasonyeza kuti anali wanzeru kwambiri ndipo mpake kuti ponena za iye mwini anati: “Tsopano wina woposa Solomo ali pano.”​—Mat. 12:42.

Padzakhala Mpumulo Solomo Wamkulu Akamadzalamulira

5. Kodi Salmo 72 limanena za chiyani, ndipo likutipatsa chithunzi chotani?

5 Tiyeni tsopano tikambirane mmene mfundo za mu Salmo 72 zikusonyezera madalitso amene adzakhalepo mu ulamuliro wa Yesu Khristu yemwe ndi Solomo Wamkulu. (Werengani Salmo 72:1-4.) Salmo limeneli limasonyeza mmene Yehova amaonera “ulamuliro” wa Mwana wake Yesu Khristu, yemwe ndi “Kalonga wa mtendere.” (Yes. 9:6, 7) Motsogoleredwa ndi Mulungu, Solomo wamkulu ‘adzanenera mlandu anthu ozunzika ndipo adzapulumutsa ana aumphawi.’ Ulamuliro wake udzakhala wamtendere ndiponso wachilungamo. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anasonyeza zimene zidzachitike mu ulamuliro wake wa zaka 1,000.​—Chiv. 20:4.

6. Kodi Yesu anapereka chithunzi chotani cha madalitso amene adzakhalepo mu Ufumu wake?

6 Taganizirani zinthu zimene Yesu anachita zimene zikutithandiza kudziwa zomwe iye adzachitire anthu pokwaniritsa Salmo 72. Mpake kuti timachita chidwi ndi mmene iye anasonyezera chifundo kwa anthu amene ankavutika. (Mat. 9:35, 36; 15:29-31) Mwachitsanzo, munthu wina wodwala khate anafika kwa Yesu n’kumupempha kuti: “Mukangofuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Ndipo nthawi yomweyo munthuyo anachira. (Maliko 1:40-42) Kenako Yesu anakumana ndi mayi wamasiye yemwe mwana wake anali atamwalira. Yesu “anamumvera chifundo” mayiyo ndipo anauza mwanayo kuti, “Tadzuka!” ndipo mwanayo anadzuka.​—Luka 7:11-15.

7, 8. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yesu anali ndi mphamvu zochiritsa.

7 Yehova anapatsa Yesu mphamvu yochita zozizwitsa. Chitsanzo cha zimenezi ndi nkhani yokhudza “mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12.” Ngakhale kuti “ochiritsa ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri, ndipo anawononga chuma chake chonse,” matendawo anangokulirakulira. Mayiyo analowa m’khamu la anthu n’kukhudza Yesu. Pochita zimenezi iye anaswa lamulo lokhudza munthu amene ‘anali ndi nthenda yakukha magazi.’ (Lev. 15:19, 25) Yesu anazindikira kuti mphamvu yatuluka mwa iye ndipo anafuna kudziwa amene anamukhudza. Mayiyo “anachita mantha nayamba kunjenjemera” ndipo ‘anagwada pamaso pake ndi kumuuza zoona zonse.’ Yesu anadziwa kuti Yehova wachiritsa mayiyu ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”​—Maliko 5:25-27, 30, 33, 34.

8 Yesu ankachiritsa anthu ndi mphamvu imene Mulungu anamupatsa ndipo anthu oona ankakhudzidwa kwambiri ndi zimenezi. Mwachitsanzo, anthu ambiri anachita chidwi pamene anaona Yesu akuchiritsa anthu asanayambe ulaliki wa paphiri. (Luka 6:17-19) Yohane M’batizi atatuma anthu awiri kukatsimikizira ngati Yesu analidi Mesiya, iwo anamupeza ‘akuchiritsa nthenda zambiri ndi matenda ambiri akayakaya ndi kutulutsa mizimu yoipa. Ndipo anapenyetsa akhungu ochuluka.’ Kenako Yesu anawauza kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mwaona ndi kumva: akhungu akuona, olemala akuyenda, akhate akuyeretsedwa ndipo ogontha akumva, akufa akuukitsidwa, ndi aumphawi akumva uthenga wabwino.” (Luka 7:19-22) Uthenga umenewu uyenera kuti unamulimbikitsa kwambiri Yohane.

9. Kodi zozizwitsa za Yesu zinapereka chithunzi cha chiyani?

9 N’zoona kuti zinthu zothandiza zimene Yesu anachitira anthu pa nthawi ya utumiki wake wa padziko lapansi, zinali za kanthawi kochepa. Anthu amene anawachiritsa kapena kuwaukitsa patapita nthawi anamwaliranso. Komabe, zozizwitsa zimene Yesu anachita padzikoli zinapereka chithunzi cha mpumulo wosatha umene anthu adzapeze mu ulamuliro wake monga Mesiya.

Dziko Lonse Lapansi Lidzakhala Paradaiso

10, 11. (a) Kodi madalitso a Ufumu adzakhalapo kwa nthawi yaitali bwanji, ndipo kodi ulamuliro wa Yesu udzakhala wotani? (b) Ndani adzakhala ndi Khristu m’Paradaiso, ndipo kodi iye adzayenera kuchita chiyani kuti adzakhale ndi moyo wosatha?

10 Taganizirani mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso padziko lapansi. (Werengani Salmo 72:5-9.) Anthu amene amalambira Mulungu woona adzakhala m’Paradaiso kwa nthawi yaitali ngati mmene dzuwa ndi mwezi zilili, kapena kuti adzasangalala ndi moyo kosatha. Mfumu Yesu Khristu adzatsitsimula anthu ngati mmene imachitira “mvula yakugwa pa udzu wosenga: Monga mvula yothirira dziko.”

11 Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukaganizira kukwaniritsidwa kwa salmo limeneli? Kodi simulakalaka kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi? N’zosakayikitsa kuti munthu wochimwa amene anapachikidwa pafupi ndi Yesu anasangalala kwambiri pamene Yesuyo anamuuza kuti: “Udzakhala nane m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Munthu ameneyu adzaukitsidwa mu ulamuliro wa Yesu wa zaka 1,000. Iye akadzagonjera ulamuliro wa Khristu adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi ndipo adzakhala wangwiro, wathanzi labwino ndiponso wosangalala.

12. Mu ulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000, kodi anthu osalungama amene adzaukitsidwe adzapatsidwa mwayi wotani?

12 Mu ulamuliro wa Yesu Khristu yemwe ndi Solomo Wamkulu, ‘olungama adzakhazikika’ kapena kuti zinthu zidzawayendera bwino kwambiri. (Sal. 72:7) Pa nthawi imeneyonso Yesu azidzakonda anthu ndiponso kuwasamalira ngati mmene ankachitira ali padziko lapansi. M’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza, ngakhale anthu “osalungama” adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wosankha ngati akufuna kutsatira mfundo zolungama za Yehova kuti akhale ndi moyo. (Mac. 24:15) Koma anthu amene adzakane kutsatira mfundo zolungama za Mulungu, sadzaloledwa kukhala ndi moyo wosatha n’kumasokoneza bata ndi mtendere m’dziko latsopano.

13. Kodi ulamuliro wa Khristu udzafika mpaka kuti, nanga n’chifukwa chiyani mtendere wake sudzasokonezedwa?

13 Mawu otsatirawa akusonyeza mmene ulamuliro wa Solomo Wamkulu padziko lonse udzakhalire: “Adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja. Ndi kuchokera ku Mtsinje [wa Firate] kufikira malekezero a dziko lapansi. Okhala m’chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka.” (Sal. 72:8, 9) Inde, Yesu Khristu adzalamulira dziko lonse. (Zek. 9:9, 10) Anthu onse amene amayamikira ulamuliro wa Khristu ndiponso madalitso a ufumu wake ‘adzagwada pamaso pake’ posonyeza kuti amamugonjera ndi mtima wonse. Koma ochimwa osalapa adzadulidwa ali ndi “zaka zana limodzi.” (Yes. 65:20) Iwo “adzaluma nthaka.”

Yesu Amatimvera Chifundo Ndipo Amatiganizira

14, 15. Tikudziwa bwanji kuti Yesu amadziwa mmene tikumvera ndiponso kuti “adzapulumutsa waumphawi wofuulayo”?

14 Anthu ochimwafe ndife omvetsa chisoni kwambiri ndipo tikufunika thandizo. Koma chiyembekezo chilipo. (Werengani Salmo 72:12-14.) Yesu, yemwe ndi Solomo Wamkulu, amatimvera chifundo chifukwa amadziwa kuti ndife opanda ungwiro. Yesu anavutika chifukwa cha chilungamo ndipo Yehova analola kuti iye akumane ndi mayesero. Yesu anavutika kwambiri maganizo moti “thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi likugwera pansi.” (Luka 22:44) Ndiyeno ali pamtengo wozunzikirapo anafuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” (Mat. 27:45, 46) Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, ndiponso ngakhale kuti Satana anayesetsa mmene akanathera kuti amuchititse kusiya Yehova, Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova Mulungu.

15 Tisakayike zoti Yesu amaona mavuto amene tikukumana nawo ndipo “adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.” Mofanana ndi Atate wake, Yesu amatikonda komanso kutiganizira. Iye ‘adzamvera aumphawi’ ndi ‘kuchiritsa osweka mtima ndiponso kumanga mabala awo.’ (Sal. 69:33; 147:3) Yesu ‘angatimvere chisoni pa zofooka zathu’ chifukwa chakuti “wayesedwa m’zonse ngati ifeyo, napezekabe wopanda uchimo.” (Aheb. 4:15) Ndi bwino kudziwa kuti Mfumu Yesu Khristu akulamulira kumwamba ndipo ndi wokonzeka kuthetsa mavuto onse a anthu.

16. N’chiyani chinathandiza Solomo kumvetsa bwino mavuto a anthu ake?

16 Popeza Solomo anali wanzeru ndiponso wozindikira, ayenera kuti ‘ankachitira chisoni wosauka.’ Ndipotu pa moyo wake anakumana ndi zinthu zokhumudwitsa komanso zoopsa kwambiri. Mwachitsanzo, m’bale wake Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara ndipo mchimwene wake Abisalomu anapha Amnoni chifukwa cha zimene anachitazi. (2 Sam. 13:1, 14, 28, 29) Abisalomu anakonza chiwembu chofuna kulanda Davide ufumu, koma zinalephereka ndipo Abisalomuyo anaphedwa ndi Yoabu. (2 Sam. 15:10, 14; 18:9, 14) Kenako mchimwene wake wa Solomo, Adoniya, anakonzanso chiwembu chofuna kulanda ufumu wa Solomo. Chiwembu chakechi chikanatheka, ndiye kuti iye akanapha Solomo. (1 Maf. 1:5) Pemphero la Solomo potsegulira kachisi wa Yehova linasonyeza kuti iye ankamvetsa bwino mavuto a anthu. Ponena za anthu ake, mfumuyi inapemphera kuti: ‘Akadziwa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake, inu Yehova mum’khululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse.’​—2 Mbiri 6:29, 30.

17, 18. Kodi atumiki ena a Mulungu amakumana ndi mavuto otani, ndipo n’chiyani chimawathandiza kupirira?

17 Nthawi zina munthu angamamve “chisoni” chifukwa cha zinthu zina zimene zinamuchitikira pa moyo wake. Mlongo wina wa zaka za m’ma 30, dzina lake Mary, * analemba kuti: “Ndili ndi zifukwa zambiri zokhalira wosangalala koma nthawi zina zinthu zimene zinandichitikira m’mbuyomu zimandichititsa manyazi ndiponso zimandinyansa. Ndikakumbukira zimenezi ndimakhumudwa kwambiri n’kuyamba kulira ndipo ndimangomva ngati zachitika dzulodzuloli. Zimenezi zimachititsa kuti ndizivutika maganizo kwambiri, kudziona ngati munthu wachabechabe ndiponso kudziimba mlandu.”

18 Umu ndi mmenenso atumiki ambiri a Mulungu amamvera. Kodi n’chiyani chingawathandize kupeza mphamvu kuti athe kupirira? Mary ananena kuti: “Anzanga a pamtima ndiponso abale anga auzimu amandithandiza kuti ndikhale wosangalala. Ndimayesetsanso kuganizira kwambiri zimene Yehova walonjeza ndipo ndikukhulupirira kuti kulira kwanga kudzasanduka chimwemwe.” (Sal. 126:5) Mulungu watipatsa Mwana wake yemwe wamuika kukhala Wolamulira ndipo tiyenera kumukhulupirira. Ponena za Mwanayu Baibulo linalosera kuti: “Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.” (Sal. 72:13, 14) Izitu ndi zolimbikitsa kwambiri.

Tikuyembekezera Dziko la Mwanaalirenji

19, 20. (a) Malinga ndi zimene Salmo 72 limanena, kodi ndi vuto liti limene lidzathetsedwa Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira? (b) Kodi ndani ayenera kutamandidwa chifukwa cha ulamuliro wa Khristu, ndipo kodi inuyo mukumva bwanji ndi zimene Ufumuwo udzachite?

19 Taganiziraninso za mmene moyo udzakhalire m’tsogolo kwa anthu olungama m’dziko latsopano mu ulamuliro wa Solomo Wamkulu. Baibulo limalonjeza kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Sal. 72:16) Nthawi zambiri m’mapiri simupezeka zokolola, choncho mawu amenewa akusonyeza kuti zokolola zidzakhala zambiri m’dzikomo. Zokolola zake zidzakhala “ngati za ku Lebano.” Lebano ndi dera limene linali la chonde kwambiri m’nthawi ya ulamuliro wa Solomo. Tangoganizani! Sikudzakhalanso njala, choncho sikudzakhalanso anthu onyentchera chifukwa chosowa chakudya. Anthu onse adzasangalala ndi “phwando la zinthu zonona.”​—Yes. 25:6-8; 35:1, 2.

20 Kodi ndani ayenera kutamandidwa chifukwa cha madalitso onsewa? Kwenikweni Yehova Mulungu yemwe ndi Mfumu Yosatha komanso Wolamulira wa chilengedwe chonse. Ndipo tonsefe tidzanena mosangalala mawu omaliza a salmo limeneli akuti: “Dzina lake [la Mfumu Yesu Khristu] lidzakhala kosatha: Momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu: Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; Amitundu onse adzamutcha wodala. Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, amene achita zodabwiza yekhayo: Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nawo ulemerero wake. Amen, ndi Amen.”​—Salmo 72:17-19.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Tasintha dzinali.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ulosi wa mu Salmo 72 umafotokoza za chiyani?

• Kodi Solomo Wamkulu ndani, ndipo ulamuliro wake udzafika mpaka kuti?

• Kodi ndi madalitso ati olembedwa mu Salmo 72 amene inuyo amakuchititsani chidwi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi madalitso a mu ulamuliro wa Solomo ankaimira chiyani?

[Chithunzi patsamba 32]

Mpake kuti tiyenera kuyesetsa kuti tidzapeze moyo m’Paradaiso mu ulamuliro wa Solomo Wamkulu