Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anatipatsa Ufulu Wosankha

Anatipatsa Ufulu Wosankha

Yandikirani Mulungu

Anatipatsa Ufulu Wosankha

2 MAFUMU 18:1-7

MAKOLO ayenera kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Khalidwe komanso chitsanzo chabwino cha makolo zingathandize kuti ana akhale ndi makhalidwe abwino. Zingathandizenso kuti azisankha zinthu mwanzeru pa moyo wawo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti makolo ambiri sapereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Kodi ndiye kuti ana oterewa ngakhale atayesetsa chotani, sangachite zabwino pa moyo wawo? Yankho la funso limeneli tikulipeza mu mfundo yolimbikitsa yakuti, Yehova Mulungu anapatsa munthu aliyense ufulu wosankha. Taganizirani nkhani ya Hezekiya yopezeka pa 2 Mafumu 18:1-7.

Hezekiya anali “mwana wa Ahazi, mfumu ya Yuda.” (Vesi 1) Ndipo Ahazi anachititsa anthu ake kusiya kulambira koyera. Mfumu imeneyi inkalambira Baala ndiponso inkachita miyambo yopereka anthu nsembe. Mfumuyi inapha ndi kupereka nsembe mmodzi kapena angapo mwa abale ake a Hezekiya. Komanso Ahazi anatseka zitseko za kachisi ndipo ‘anadzimangira maguwa a nsembe m’ngodya zilizonse za Yerusalemu.’ Zimenezi ‘zinautsa mkwiyo wa Yehova.’ (2 Mbiri 28:3, 24, 25) Izi zikusonyezeratu kuti bambo ake a Hezekiya anali munthu woipa kwambiri. Kodi Hezekiya akanatha kupewa kuchita zoipa zimene bambo ake anachita?

Hezekiya atangokhala mfumu, anasonyeza kuti sanatengere chitsanzo choipa cha bambo ake. Baibulo limati iye ‘anachita zowongoka pamaso pa Yehova.’ (Vesi 3) Hezekiya anakhulupirira Yehova ndipo “panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda.” (Vesi 5) M’chaka choyamba cha ulamuliro wake, mfumu yachinyamata imeneyi inayambitsa ntchito yothandiza kuti anthu ayambirenso kulambira Yehova m’njira yoyenera. Zotsatira zake zinali zakuti malo amene anthu ankalambirirapo mafano anachotsedwa. Kenako kachisi anatsegulidwanso ndipo anthu anayambiranso kulambira Mulungu m’njira yoyenera. (Vesi 4; 2 Mbiri 29:1-3, 27-31) Hezekiya ‘anaumilira Yehova ndipo Yehova anali naye.’​—Vesi 6, 7.

Kodi n’chiyani chinathandiza Hezekiya kuti apewe kutsatira chitsanzo choipa cha bambo ake? Sitikudziwa zambiri za Abiya, amene anali mayi ake a Hezekiya. Koma kodi n’kutheka kuti mayi akewa ndi amene anamuthandiza? Kapena kodi chitsanzo chabwino cha Yesaya, amene anayamba ntchito yake yonenera, Hezekiyayo asanabadwe n’chimene chinamuthandiza? * Baibulo silinena kuti chinamuthandiza ndi chiyani. Koma mfundo ndi yakuti, Hezekiya anasankha kuchita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene bambo ake anachita.

Chitsanzo cha Hezekiya n’cholimbikitsa kwambiri kwa anthu amene anakula movutika chifukwa cha khalidwe loipa la makolo awo. N’zoona kuti kale silibwerera ndipo sitingathe kusintha zinthu zoipa zimene zinachitika kale. Koma zimene tingasankhe panopa zingatithandize kuti tidzakhale ndi tsogolo labwino. Mofanana ndi Hezekiya, tingasankhe kukonda Mulungu woona Yehova ndiponso kumulambira. Zimenezi zingachititse kuti tizikhala mosangalala panopa komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Tiyenera kuyamikira kwambiri Mulungu wathu wachikondi chifukwa cha mphatso yamtengo wapatali imene watipatsa, yomwe ndi ufulu wosankha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Yesaya anali mneneri kuyambira mu 778 B.C.E. mpaka mu 732 B.C.E. kapena kupitirira pang’ono. Hezekiya anayamba kulamulira mu 745 B.C.E., ali ndi zaka 25.