Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzifunafuna Madalitso a Yehova ndi Mtima Wonse

Muzifunafuna Madalitso a Yehova ndi Mtima Wonse

Muzifunafuna Madalitso a Yehova ndi Mtima Wonse

‘Mulungu amapereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.’​—AHEB. 11:6.

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri amachita chiyani kuti adalitsidwe ndi Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani ifeyo makamaka tiyenera kuyesetsa kuti tipeze madalitso a Yehova?

M’MADERA ena munthu akayetsemula amamuuza kuti “Mulungu akudalitse.” Iwo amanena mawu amenewa ngakhale kwa munthu wosamudziwa amene angokumana naye. Atsogoleri a zipembedzo zosiyanasiyana amadalitsa anthu, nyama ndi zinthu zina zopanda moyo. Anthu ena oyenda amakopeka kuti akaone malo ena achipembedzo n’cholinga choti adalitsidwe. Nthawi zambiri atsogoleri a ndale amapemphera kuti Mulungu adalitse dziko lawo. Kodi mukuganiza kuti kupempherera madalitso ngati amenewa n’koyenera? Kodi mapemphero oterewa amayankhidwa? Kodi ndani kwenikweni amene amalandira madalitso a Mulungu ndipo n’chifukwa chiyani?

2 Yehova ananeneratu kuti masiku otsiriza adzakhala ndi anthu oyera ndi amtendere kuchokera m’mitundu yonse. Iwo adzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu mpaka kumalekezero a dziko lapansi ngakhale kuti azidzadedwa ndiponso kutsutsidwa. (Yes. 2:2-4; Mat. 24:14; Chiv. 7:9, 14) Ngati tikufuna kuti moyo wathu ukhale wogwirizana ndi mawu ouziridwa amenewa tiyenera kupempha madalitso a Mulungu chifukwa kupanda kutero zinthu sizingatiyendere bwino. (Sal. 127:1) Koma kodi tingapeze bwanji madalitso a Mulungu?

Anthu Omvera Amalandira Madalitso

3. Kodi Aisiraeli akanakhala omvera zotsatira zake zikanakhala zotani?

3 Werengani Miyambo 10:6, 7Mtundu wa Isiraeli utatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anasonyeza kuti zinthu zidzawayendera bwino ndiponso adzatetezedwa ngati azimvera mawu ake. (Deut. 28:1, 2) Madalitso a Yehova akanagwera ndi ‘kupeza’ anthu a Mulungu. Choncho, zinali zosakayikitsa kuti Yehova akanadalitsa kwambiri anthu omvera.

4. Kodi munthu amene amamvera Mulungu amatani?

4 Kuti Aisiraeli akhale omvera kodi anafunika kukhala ndi mtima wotani? Chilamulo cha Mulungu chinanena kuti Mulungu akanakhala wosangalala ngati anthuwo akanam’tumikira “ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima.” (Werengani Deuteronomo 28:45-47.) Yehova safuna kuti anthu azimvera malangizo ake mokakamizika ngati mmene nyama kapena ziwanda zingachitire. (Maliko 1:27; Yak. 3:3) Munthu amamvera Mulungu ndi mtima wonse chifukwa chomukonda. Munthu wotereyu amasangalala kwambiri chifukwa chokhulupirira kuti malamulo a Yehova si olemetsa ndiponso amakhulupirira kuti Mulungu ‘amapereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.’​—Aheb. 11:6; 1 Yoh. 5:3.

5. Kodi kukhulupirira lonjezo la Yehova kukanathandiza bwanji munthu kuti azimvera lamulo la pa Deuteronomo 15:7, 8?

5 Tiyeni tione umboni wakuti kumvera kotereku kunali kofunika kuti munthu atsatire lamulo la pa Deuteronomo 15:7, 8. (Werengani.) Kumvera lamulo limeneli monyinyirika kukanathandiza anthu osauka koma sikukanachititsa kuti anthu a Mulungu azikondana ndiponso kugwirizana. Ndipo kodi kupereka monyinyirika kukanasonyeza kuti munthuyo amakhulupirira zoti Yehova amasamalira anthu ake? Kodi kukanasonyeza kuti munthuyo akutsanzira Mulungu yemwe ndi wowolowa manja? Ayi. Mulungu ankadziwa munthu amene ankapereka zinthu ndi mtima wonse ndipo analonjeza kuti adzadalitsa zochita zonse za munthu wotereyo. (Deut. 15:10) Kukhulupirira lonjezo limeneli kukanachititsa kuti anthu azithandizana ndipo akanadalitsidwa kwambiri.​—Miy. 28:20.

6. Kodi lemba la Aheberi 11:6 limatitsimikizira za chiyani?

6 Kuwonjezera pa kukhulupirira kuti Yehova amapereka mphoto, lemba la Aheberi 11:6 limasonyeza kuti palinso khalidwe lina lofunika kuti munthu alandire madalitso a Mulungu. Onani kuti Yehova amapereka mphoto kwa anthu “om’funafuna ndi mtima wonse.” Mawu amene anawamasulira kuti “om’funafuna ndi mtima wonse” amasonyeza kuti munthu amafunika kuchita khama ndiponso kuikapo maganizo ake onse. Zimenezitu zikusonyeza kuti pamafunika kuchita khama kuti tipeze madalitso. Mulungu woona, “amene sanganame,” ndi amene angatidalitse. (Tito 1:2) Kwa zaka zambiri, iye wasonyeza kuti malonjezo ake ndi odalirika. Mawu ake sapita pachabe, amakwaniritsidwa nthawi zonse. (Yes. 55:11) Choncho tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti ngati timukhulupirira, iye adzatipatsa mphoto.

7. Kodi tingatani kuti tipeze madalitso kudzera mu “mbewu” ya Abulahamu?

7 Yesu Khristu anasonyeza kuti iye ndi mbali yoyamba ya “mbewu” ya Abulahamu. Akhristu odzozedwa ndi mbali yachiwiri ya “mbewu” yolonjezedwa imeneyi. Iwo apatsidwa ntchito ‘yolengeza zabwino zopambana za amene anawaitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (Agal. 3:7-9, 14, 16, 26-29; 1 Pet. 2:9) N’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngati sitimvera anthu amene Yesu wawapatsa udindo wosamalira zinthu zake. Popanda thandizo la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” sitikanatha kumvetsa tanthauzo la zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu ndiponso mmene tingazigwiritsire ntchito pa moyo wathu. (Mat. 24:45-47) Tikamachita zimene timaphunzira m’Malemba tidzalandira madalitso a Mulungu.

Muziika Zofuna za Mulungu Patsogolo

8, 9. Fotokozani khama limene Yakobo anasonyeza mogwirizana ndi zimene ankapempherera?

8 Nkhani ya Yakobo imasonyeza bwino kufunika kochita khama kwambiri kuti tilandire madalitso a Mulungu. Iye sankadziwa mmene Mulungu adzakwaniritsire lonjezo lake kwa Abulahamu, koma ankakhulupirira kuti Yehova adzachulukitsa kwambiri mbewu za agogo ake ndipo mbadwazo zidzakhala mtundu waukulu. Choncho mu 1781 B.C.E., Yakobo anapita ku Harana kukafuna mkazi. Si kuti cholinga chake chinali kupeza mkazi amene angayenerane naye koma ankafuna mkazi wolambira Yehova ndiponso wokonda zinthu zauzimu amene angalere bwino ana ake.

9 Tonse tikudziwa kuti Yakobo anakumana ndi Rakele amene anali wachibale wake. Iye anam’konda kwambiri Rakele moti analolera kugwira ntchito kwa Labani, bambo ake a Rakele, kwa zaka 7 kuti amukwatire. Imeneyi si nkhani wamba yongonena za chikondi. Yakobo ankadziwa zimene Mulungu Wamphamvu yonse analonjeza agogo ake Abulahamu. Lonjezoli analibwerezanso kwa bambo ake Isake. (Gen. 18:18; 22:17, 18; 26:3-5, 24, 25) Kenako Isake anauza mwana wake Yakobo za lonjezoli kuti: “Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: Akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbewu zako pamodzi nawe: Kuti ulowe m’dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anam’patsa Abrahamu.” (Gen. 28:3, 4) Choncho khama limene Yakobo anachita pofuna mkazi woyenera n’kukhala ndi ana, linasonyeza kuti ankakhulupirira zimene Yehova ananena.

10. N’chifukwa chiyani Yehova anadalitsa Yakobo?

10 Koma si kuti Yakobo ankangofuna chuma kuti asamalire banja lake. Maganizo ake onse anali pa cholowa chake. Iye ankaganizira kwambiri za kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Yehova. Yakobo ankayesetsa kuchita zonse zimene akanatha kuti adalitsidwe ndi Mulungu ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ena. Iye sanasithe maganizo amenewa mpaka pamene anakalamba ndipo Yehova anamudalitsa chifukwa cha mtima umenewu.​—Werengani Genesis 32:24-29.

11. Mogwirizana ndi zimene Mulungu watiuza zokhudza chifuniro chake, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

11 Mofanana ndi Yakobo, ife sitidziwa tsatanetsatane wa mmene Yehova adzakwaniritsire cholinga chake. Koma tikamaphunzira Mawu a Mulungu timadziwa mfundo zikuluzikulu zokhudza zimene tiyenera kuyembekezera pa “tsiku la Yehova.” (2 Pet. 3:10, 17) Mwachitsanzo, sitidziwa kuti tsikuli lidzafika liti, koma tikudziwa kuti layandikira. Timakhulupirira zimene Mawu a Mulungu amanena kuti tikalalikira mokwanira pa kanthawi kamene katsalaka, tidzadzipulumutsa ifeyo ndiponso amene akutimvera.​—1 Tim. 4:16.

12. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

12 Tikudziwa kuti mapeto akhoza kufika nthawi ina iliyonse ndipo sikuti Yehova akudikira kuti tilalikire munthu aliyense padziko lapansili. (Mat. 10:23) Ndipotu timalandira malangizo otithandiza kulalikira mogwira mtima. Chifukwa cha chikhulupiriro, timagwira nawo ntchito imeneyi ndi mphamvu yathu yonse ndipo timagwiritsa ntchito zinthu zonse zimene tili nazo. Kodi tidzayesetsa kulalikira kulikonse kumene anthu asonyeza chidwi? Koma kodi tingadziwe bwanji anthu achidwi? (Werengani Mlaliki 11:5, 6.) Ntchito yathu ndi yolalikira ndipo tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatidalitsa. (1 Akor. 3:6, 7) Sitikayika zoti iye amaona khama lathu ndipo kudzera mwa mzimu wake woyera iye adzatipatsa malangizo amene tikufunikira.​—Sal. 32:8.

Muzipempha Mzimu Woyera

13, 14. Perekani umboni wotsimikizira kuti mzimu wa Mulungu umathandiza atumiki ake kukhala oyenera kugwira bwino ntchito?

13 Bwanji ngati timaona kuti sitingakwanitse ntchito ina yake kapena kugwira nawo ntchito yolalikira? Tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera kuti tipititse patsogolo luso limene tili nalo pa utumiki wake. (Werengani Luka 11:13.) Kaya munthu ali ndi maphunziro otani, mzimu wa Mulungu ungamuthandize kukhala woyenerera kugwira ntchito kapena kuchita utumiki winawake. Mwachitsanzo, kungoyambira pa nthawi imene Aisiraeli ananyamuka ku Igupto, mzimu wa Mulungu unathandiza abusa ndiponso akapolo kugonjetsa adani awo pochita nawo nkhondo ngakhale kuti analibe luso lomenya nkhondo. (Eks. 17:8-13) Kenako, mzimu womwewu unathandiza Bezaleli ndi Oholiabu kugwira bwino ntchito yaikulu kwambiri yokonza likasa potsatira mapulani amene Mulungu anawauza.​—Eks. 31:2-6; 35:30-35.

14 Mzimu wamphamvu umenewu unathandiza atumiki a Mulungu a masiku ano pa nthawi imene gulu lake linafunika kuyamba kusindikiza mabuku. M’bale R. J. Martin, amene ankayang’anira ntchito ya mufakitale yosindikizira mabuku, analemba m’kalata yake zinthu zimene zinali zitachitika pofika mu 1927. Iye analemba kuti: “Pa nthawi yoyenerera, Ambuye anatitsegulira khomo ndipo tinapeza makina aakulu osindikizira mabuku ngakhale kuti sitinkadziwa mmene tingawakonzere komanso mmene tingawagwiritsire ntchito. Koma Ambuye amapereka nzeru kwa anthu amene amadzipereka ndi mtima wonse. . . . Kwa masabata ochepa chabe, tinadziwa kuwagwiritsa ntchito ndipo akugwirabe ntchito imene ngakhale anthu amene anapanga makinawa sankadziwa kuti angachite.” Yehova wakhala akudalitsa anthu amene ali ndi khama lotereli mpaka masiku ano.

15. Kodi lemba la Aroma 8:11 lingalimbikitse bwanji anthu amene akukumana ndi mayesero?

15 Mzimu wa Yehova umagwira ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mzimu umenewu umathandiza atumiki onse a Mulungu kuti apirire mavuto akuluakulu. Bwanji ngati tikuona kuti mayesero enaake ndi aakulu kwambiri moti sitingapirire? Mawu a Paulo opezeka pa Aroma 7:21, 25 ndi pa 8:11 akhoza kutilimbikitsa. Inde “mzimu wa iye amene anaukitsa Yesu kwa akufa” ungatithandize ndiponso kutipatsa mphamvu kuti tipambane polimbana ndi zilakolako za thupi. Mawu amenewa analembera Akhristu odzozedwa koma mfundo zake zimagwiranso ntchito kwa atumiki onse a Mulungu. Tonsefe tingapeze moyo ngati tikhulupirira Khristu ndiponso ngati tiyesetsa kulimbana ndi zilakolako zoipa komanso ngati tilola kutsogoleredwa ndi mzimu pa moyo wathu.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atipatse mzimu wake woyera?

16 Kodi n’zotheka kulandira mzimu wa Mulungu popanda kuchita khama lililonse? Ayi. Kuwonjezera pa kupempha Mulungu kuti atipatse mzimuwo, tiyenera kuphunzira mwakhama Mawu ouziridwa a Mulungu. (Miy. 2:1-6) Komanso mzimu wa Mulungu umakhala pa mpingo wake wachikhristu. Tikamapezeka pa misonkhano nthawi zonse timasonyeza kuti tikufunitsitsa ‘kumva zimene mzimu ukunena ku mipingo.’ (Chiv. 3:6) Ndipotu tiyenera kutsatira modzichepetsa zimene timaphunzira. Lemba la Miyambo 1:23 limatilangiza kuti: “Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga.” Mulungu amapereka mzimu wake woyera “kwa anthu omvera iye monga wolamulira.”​—Mac. 5:32.

17. Kodi mmene Mulungu amadalitsira khama lathu tingaziyerekezere ndi chiyani?

17 Ngakhale kuti tiyenera kuyesetsa kuti Mulungu atidalitse, tiyenera kukumbukira kuti kungogwira ntchito mwakhama sikungatithandize kupeza zinthu zambiri zabwino zimene Yehova amapatsa anthu ake. Tingayerekezere madalitso amene Mulungu amatipatsa ndi mmene chakudya chabwino chimagwirira ntchito m’matupi athu. Mulungu anapanga matupi athuwa kuti tizisangalala ndi chakudya ndiponso kuti tizipeza zinthu zofunika m’thupi tikadya chakudyacho. Mulungu ndi amenenso amatipatsa chakudya. Ifeyo sitidziwa bwinobwino mmene zinthu zofunika m’thupi zimafikira m’chakudya chathu komanso ambirife sitingafotokoze mmene matupi athu amapezera mphamvu mu chakudya chimene timadya. Chomwe timadziwa n’chakuti, izi zimachitika ndipo ife timafunika kuti tizidya. Tikamadya chakudya chopatsa thanzi zinthu zimayenda bwino. Mofanana ndi zimenezi, Yehova wapereka malangizo kuti tikapeze moyo wosatha ndipo ndi wokonzeka kutithandiza kutsatira malangizo amenewa. Pamenepatu iye amachita zambiri ndipo tiyenera kum’tamanda. Choncho, kuti Mulungu atidalitse, tiyenera kumumvera ndiponso kuchita zinthu zogwirizana ndi zimene amafuna.​—Hag. 2:18, 19.

18. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani ndipo chifukwa chiyani?

18 Motero muzichita utumiki uliwonse umene mwapatsidwa ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muzipempha Yehova kuti zinthu zikuyendereni bwino. (Maliko 11:23, 24) Muzichita zimenezi ndi chikhulupiriro chakuti “aliyense wofunafuna amapeza.” (Mat. 7:8) Akhristu odzozedwa adzadalitsidwa mwa kulandira “kolona wa moyo” kumwamba. (Yak. 1:12) Akhristu a “nkhosa zina” amene akuyesetsa kuti akalandire madalitso kudzera mu mbewu ya Abrahamu, adzasangalala kumva Khristu akunena kuti: “Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga, lowani ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Yoh. 10:16; Mat. 25:34) Inde, anthu ‘amene akudalitsidwa ndi Mulungu adzalandira dziko lapansi; ndipo adzakhala momwemo kosatha.’​—Sal. 37:22, 29.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu akhaledi womvera?

• Kodi chofunika n’chiyani kuti munthu adalitsidwe ndi Mulungu?

• Kodi Mulungu angatipatse bwanji mzimu wake woyera ndipo kodi ungatithandize bwanji?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Yakobo analimbana ndi mngelo kuti adalitsidwe ndi Yehova.

Kodi inunso mumayesetsa kuchita khama?

[Chithunzi patsamba 10]

Mzimu wa Mulungu unathandiza Bezaleli ndi Oholiabu kuti agwire bwino ntchito