Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mtsogoleri Wanu Ndi Mmodzi, Khristu”

“Mtsogoleri Wanu Ndi Mmodzi, Khristu”

“Mtsogoleri Wanu Ndi Mmodzi, Khristu”

“Musatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”​—MAT. 23:10.

1. Kodi Mboni za Yehova zimaona kuti Mtsogoleri wawo ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?

MATCHALITCHI Achikhristu ali ndi anthu amene amawatsogolera, monga papa ku Rome, abambo ndi atsogoleri a matchalitchi a Eastern Orthodox ndiponso abusa a zipembedzo zina. Pakati pa Mboni za Yehova, palibe munthu amene amaonedwa kuti ndi mtsogoleri. Mboni za Yehova si otsatira kapena ophunzira a munthu wina aliyense. Zimenezi n’zogwirizana ndi mawu a ulosi amene Yehova ananena okhudza Mwana wake kuti: “Taonani, ndam’pereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.” (Yes. 55:4) Mpingo wa padziko lonse wa Akhristu odzozedwa pamodzi ndi anzawo a “nkhosa zina” safuna kukhala ndi mtsogoleri wina koma amene Yehova wawapatsa. (Yoh. 10:16) Iwo amamvera mawu a Yesu akuti: “Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”​—Mat. 23:10.

Mngelo Amene Anali Kalonga wa Isiraeli

2, 3. Tchulani ntchito zofunika zimene Mwana wa Mulungu anachitira mtundu wa Isiraeli.

2 Zaka zambiri mpingo wachikhristu usanakhazikitsidwe, Yehova ankagwiritsa ntchito mngelo potsogolera Aisiraeli omwe anali anthu ake. Yehova atatulutsa Aisiraeli ku Iguputo anawauza kuti: “Taona, ndituma mthenga [mngelo] akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamalo pomwe ndakonzeratu. Musamalire iye, ndi kumvera mawu ake; musam’wawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa liri m’mtima mwake.” (Eks. 23:20, 21) N’zosakayikitsa kuti mngelo ‘amene anali ndi dzina la Yehova,’ anali Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu.

3 Mwana wa Mulungu ameneyu asanabadwe ngati munthu, ayenera kuti ankatchedwa Mikayeli. M’buku la Danieli, Mikayeli amatchedwanso ‘Kalonga wa anthu a Danieli,’ Aisiraeli. (Dan. 10:21) Yuda yemwe anali wophunzira wa Yesu anasonyeza kuti Mikayeli ankagwiritsidwanso ntchito pa nkhani zokhudza Aisiraeli isanafike nthawi ya Danieli. Mose atamwalira, Satana ankafuna kugwiritsa ntchito mtembo wake kuti akwaniritse zolinga zake. N’kutheka kuti iye ankafuna kuti augwiritse ntchito pochititsa Aisiraeli kulambira mafano. Mikayeli analowererapo kuti zimenezi zisachitike. Yuda analemba kuti: “Pamene Mikayeli mkulu wa angelo anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose, sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza, m’malo mwake anati: ‘Yehova akudzudzule.’” (Yuda 9) Pasanapite nthawi yaitali, Aisiraeli atatsala pang’ono kulanda mzinda wa Yeriko, “kazembe wa ankhondo a Yehova” anaonekera kwa Yoswa n’kumulimbikitsa kuti Mulungu amuthandiza. Kazembe ameneyu ayenera kuti analinso Mikayeli. (Werengani Yoswa 5:13-15.) Pamene chiwanda chomwe chinali kalonga chinkafuna kulepheretsa mngelo kuti asakapereke uthenga wofunika kwa mneneri Danieli, Mikayeli yemwe ndi mkulu wa angelo anabwera kudzathandiza mngeloyo.​—Dan. 10:5-7, 12-14.

Mtsogoleri Woloseredwayo Aonekera

4. Tchulani ulosi umene umanena za kubwera kwa Mesiya.

4 Zimenezi zisanachitike, Yehova anatumiza mngelo wake dzina lake Gabrieli kuti akauze mneneri Danieli za ulosi wokhudza kubwera kwa Mesiya Mtsogoleri. (Dan. 9:21-25) * Pa nthawi yeniyeni yomwe ulosiwu unanena, yomwe ndi m’chilimwe cha 29 C.E., Yesu anabatizidwa ndi Yohane. Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera n’kukhala Khristu kapena kuti Mesiya, kutanthauza Wodzozedwa. (Mat. 3:13-17; Yoh. 1:29-34; Agal. 4:4) Zitatere, iye anakhala Mtsogoleri woposa onse.

5. Kodi Khristu ankatsogolera bwanji anthu pa utumiki wake wa padziko lapansi?

5 Yesu anasonyeza kuti anali “Mesiya Mtsogoleri” kuyambira pa nthawi imene anayamba utumiki wake padziko lapansi. Patangopita masiku ochepa, anayamba kusonkhanitsa ophunzira ake ndipo anachita chozizwitsa chake choyamba. (Yoh. 1:35–2:11) Ophunzira ake ankamutsatira m’madera osiyanasiyana pamene ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 8:1) Anawaphunzitsa ntchito yolalikira ndipo ankatsogolera polalikira ndi kuphunzitsa. Chimenechi chinali chitsanzo chabwino. (Luka 9:1-6) Masiku ano, akulu Achikhristu amatengera chitsanzo cha Yesu pa nkhani imeneyi.

6. Kodi Khristu anasonyeza bwanji kuti anali M’busa ndiponso Mtsogoleri?

6 Pofotokoza zimene ankachita monga mtsogoleri, Yesu anadziyerekezera ndi m’busa wachikondi. Kale abusa ankatsogolera nkhosa zawo. M’buku lina, W. M. Thomson analemba kuti: “M’busa ndi amene ankakhala patsogolo. Iye sankangosonyeza njira koma ankaona ngati malowo ali abwino ndiponso otetezeka. Iye ankagwiritsa ntchito ndodo yake kutsogolera nkhosa zake ku udzu wobiriwira ndiponso poziteteza kwa adani.” (The Land and the Book) Yesu anasonyeza kuti ndi m’busa weniweni ndiponso mtsogoleri. Iye anati: “Ine ndine m’busa wabwino; m’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, ine ndimazidziwa, izonso zimanditsatira.” (Yoh. 10:11, 27) Posonyeza kuti zimene ananenazi ndi zoona, Yesu anafa imfa ya nsembe mmalo mwa nkhosa zake, koma Yehova “anamkweza . . . akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi.”​—Mac. 5:31; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu; Aheb. 13:20.

Woyang’anira Mpingo Wachikhristu

7. Kodi Yesu amagwiritsa ntchito chiyani kuyang’anira mpingo wachikhristu?

7 Yesu ataukitsidwa, komanso atatsala pang’ono kupita kumwamba, anauza ophunzira ake kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mat. 28:18) Atapita kumwamba, Yehova anagwiritsa ntchito Yesu kupereka mzimu woyera kwa ophunzira kuti akhale olimba m’choonadi. (Yoh. 15:26) Yesu anatsanulira mzimu kwa Akhristu oyambirira pa Pentekosite mu 33 C.E. (Mac. 2:33) Uku kunali kuyamba kwa mpingo wachikhristu. Yehova anapatsa Mwana wake udindo woyang’anira mpingo wa padziko lapansi. (Werengani Aefeso 1:22; Akolose 1:13, 18.) Masiku ano, Yesu akutsogolera mpingo wachikhristu pogwiritsa ntchito mzimu woyera wa Yehova ndipo angelo ‘okhala pansi pake’ akumutumikira.​—1 Pet. 3:22.

8. Mu nthawi ya atumwi, kodi Khristu ankagwiritsa ntchito ndani padziko lapansi pofuna kutsogolera ophunzira ake, nanga panopa akugwiritsa ntchito ndani?

8 Pogwiritsanso ntchito mzimu woyera, Khristu anapereka “mphatso za amuna” kuti ena akhale “monga abusa ndi aphunzitsi” mu mpingo. (Aef. 4:8, 11) Mtumwi Paulo analangiza oyang’anira achikhristu kuti: “Mudziyang’anire nokha ndi gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu.” (Mac. 20:28) Pamene mpingo wachikhristu unkayamba, oyang’anira onse anali odzozedwa. Atumwi ndiponso akulu a mpingo wa ku Yerusalemu ndi amene anali m’bungwe lolamulira. Khristu ankagwiritsa ntchito bungwe lolamulirali kutsogolera gulu lonse la “abale” odzozedwa padziko lapansi. (Aheb. 2:11; Mac. 16:4, 5) M’nthawi ya mapeto ino, Khristu wapereka udindo woyang’anira “zinthu zake zonse” kwa kapolo wake “wokhulupirika ndi wanzeru.” Kapolo ameneyu amaimiridwa ndi Bungwe Lolamulira lomwe ndi kagulu ka abale amene ndi Akhristu odzozedwa. Zinthu zake zonse zikuimira zinthu zonse zokhudza Ufumu padziko lapansi. (Mat. 24:45-47) Odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina amadziwa kuti akamatsatira malangizo amene Bungwe Lolamulira la masiku ano limapereka, ndiye kuti akutsatira Mtsogoleri wawo, Khristu.

Khristu Ndiye Anayambitsa Ntchito Yolalikira

9, 10. Kodi Yesu anachita chiyani, zimene zinachititsa kuti uthenga wabwino wa Ufumu ufalikire?

9 Atangoyamba utumiki wake, Yesu anali kutsogolera ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa padziko lonse. Iye anakhazikitsa dongosolo loyenera kutsatira polalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi. Pa nthawi ya utumiki wake, iye analangiza atumwi ake kuti: “Musapite mu msewu wa amitundu, ndipo musalowe mu mzinda wa Asamariya; m’malomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli. Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’” (Mat. 10:5-7) Atumwiwa anagwira ntchito imeneyi mwakhama pakati pa Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda, makamaka Pentekosite wa 33 C.E. atadutsa.​—Mac. 2:4, 5, 10, 11; 5:42; 6:7.

10 Yesu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti ntchito yolalikira Ufumu ifikire Asamariya ndipo kenako anthu a mitundu ina. (Mac. 8:5, 6, 14-17; 10:19-22, 44, 45) Pofuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe kwa anthu amitundu ina, Yesu anachititsa Saulo wa ku Tariso kuti akhale Mkhristu. Iye anauza wophunzira wake wina dzina lake Hananiya kuti: “Nyamuka, upite ku msewu wotchedwa Msewu Woongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi ukafunse za munthu wa ku Tariso, dzina lake Saulo. . . . Nyamuka uzipita, chifukwa munthu ameneyu ndi chiwiya changa chosankhika. Inde, chotengera dzina langa kwa amitundu, ngakhalenso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Mac. 9:3-6, 10, 11, 15) “Munthu ameneyu” anadzakhala mtumwi Paulo.​—1 Tim. 2:7.

11. Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, kodi Khristu anachita chiyani kuti ntchito yolalikira ifalikire?

11 Nthawi itakwana yoti Ufumu ulalikidwe kwa anthu amitundu ina, Yesu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kutsogolera Paulo pa maulendo ake aumishonale ku Asia Minor mpaka ku Ulaya. M’buku la Machitidwe, Luka analemba kuti: “Pamene [Akhristu amene anali aneneri ndiponso aphunzitsi a mumpingo wa Antiokeya wa ku Suriya] anali kutumikira Yehova ndi kusala kudya, mzimu woyera unati: ‘Mwa anthu onse mundipatulire Baranaba ndi Saulo kuti agwire ntchito imene ndinawaitanira.’ Pamenepo anasala kudya napemphera, ndipo anawaika manja ndi kuwalola kuti apite.” (Mac. 13:2, 3) Yesu anali ataitana Saulo wa ku Tariso kuti akhale ‘chiwiya chake chosankhika’ kuti akalalikire dzina la Yesuyo kwa anthu amitundu ina. Choncho, amene anachititsa kuti ntchito yolalikirayi ipite patsogolo mwamsanga anali Khristu yemwe ndi Mtsogoleri wa mpingo. Pa ulendo waumishonale wachiwiri wa pa Paulo, zinali zoonekeratu kuti Yesu akugwiritsa ntchito mzimu woyera kutsogolera ntchito yolalikira. Nkhaniyi imati: “Mzimu wa Yesu,” zimene zikutanthauza kuti Yesu kudzera mwa mzimu woyera, unatsogolera Paulo ndi anzake amene ankayenda naye. Mzimuwu unawathandiza posankha nthawi ndi malo oyenera kulalikira ndipo m’masomphenya anauzidwa kuti apite ku Ulaya.​—Werengani Machitidwe 16:6-10.

Kodi Yesu Akutsogolera Bwanji Mpingo Wake?

12, 13. Kodi buku la Chivumbulutso limasonyeza bwanji kuti Khristu amaonetsetsa mwachidwi zimene zikuchitika mu mpingo uliwonse?

12 M’nthawi ya atumwi, Yesu ankaonetsetsa mwachidwi zimene zinkachitika mu mpingo wa otsatira ake odzozedwa. Iye ankadziwa bwino za moyo wauzimu wa mpingo uliwonse. Zimenezi zimaonekera bwino tikawerenga buku la Chivumbulutso chaputala 2 ndi 3. Iye anatchula mipingo 7 ndipo yonse inali ku Asia Minor. (Chiv. 1:11) N’zosakayikitsa kuti iye ankadziwanso moyo wauzimu wa mipingo ina ya otsatira ake imene inalipo pa nthawiyo.​—Werengani Chivumbulutso 2:23.

13 Yesu anayamikira ina mwa mipingoyi chifukwa cha kupirira, kukhulupirika poyesedwa, kumvera mawu ake ndiponso kukana mpatuko. (Chiv. 2:2, 9, 13, 19; 3:8) Koma iye anaperekanso uphungu wamphamvu ku mipingo ingapo chifukwa chikondi chawo chimene anali nacho poyamba chinali chitazirala ndipo ankalekerera kulambira mafano, dama ndiponso mpatuko. (Chiv. 2:4, 14, 15, 20; 3:15, 16) Yesu anali woyang’anira wachikondi, ngakhale kwa anthu amene anawapatsa uphungu wamphamvu. Iye anati: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho, khala wachangu ndipo ulape.” (Chiv. 3:19) Ngakhale kuti anali kumwamba, Yesu ankatsogolera mpingo wa ophunzira ake padziko lapansi kudzera mwa mzimu woyera. Kumapeto kwa uthenga wake wopita ku mipingo, Yesu anati: “Ali ndi khutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.”​—Chiv. 3:22.

14-16. (a) Kodi Yesu wasonyeza bwanji kuti ndi Mtsogoleri wolimba mtima wa anthu a Yehova padziko lapansi? (b) Fotokozani zimene zachitika chifukwa chakuti Yesu ‘wakhala ndi’ ophunzira ake “masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (c) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

14 Tsopano taona kuti Mikayeli (Yesu) anasonyeza kuti anali mngelo wamphamvu amene ankatsogolera Aisiraeli. Kenako Yesu anadzakhala Mtsogoleri wolimba mtima ndiponso M’busa wachikondi wa ophunzira ake oyambirira. Pa nthawi ya utumiki wake wa padziko lapansi, ankatsogolera ntchito yolalikira ndiponso ataukitsidwa ankayang’anira bwinobwino kufalitsidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu.

15 Kudzera mwa mzimu woyera, Yesu anachititsa kuti ntchito yolalikira ifalikire mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Asanapite kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; werengani 1 Petulo 1:12.) Motsogozedwa ndi Khristu, umboni unaperekedwa m’nthawi ya atumwi.​—Akol. 1:23.

16 Koma Yesu anasonyeza kuti ntchito imeneyi, idzapitirira mpaka nthawi yamapeto. Atauza otsatira ake kuti azilalikira ndiponso kupanga ophunzira kwa anthu amitundu yonse, anawalonjezanso kuti: “Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 28:19, 20) Kuyambira pamene Khristu anapatsidwa mphamvu zolamulira mu 1914, mosiyana ndi kale lonse, iye ‘ali ndi’ ophunzira ake ndipo akugwira ntchito mwakhama monga Mtsogoleri wawo. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene ntchito yake yawonjezekera kuyambira mu 1914.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mudziwe zambiri za ulosi umenewu, onani mutu 11 wa buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli!

Kubwereza

• Kodi Mwana wa Mulungu anasonyeza bwanji kuti ndi Wolamulira wakhama wa Isiraeli?

• Kodi Khristu amatsogolera bwanji mpingo wake wa padziko lapansi?

• Kodi Khristu wakhala akutsogolera bwanji ntchito yolalikira uthenga wabwino?

• Perekani umboni wotsimikizira kuti Khristu amaona bwinobwino moyo wauzimu wa mpingo uliwonse.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

“Ndituma mthenga [mngelo] akutsogolere”

[Chithunzi patsamba 23]

Mofanana ndi nthawi yakale, Khristu akugwiritsa ntchito “mphatso za amuna” kutsogolera gulu la nkhosa