Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

2 Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Ndani?

2 Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Ndani?

KODI mapemphelo onse amapita kumalo amodzi, kaya wopemphelayo akuchula dzina la ndani? Anthu ambili masiku ano amaganiza conco. Ambili mwa anthuwa ni amene amafuna kuti zipembedzo zonse zizicitila zinthu pamodzi. Anthu amenewa amaona kuti zipembedzo zonse n’zovomelezeka kwa Mulungu ngakhale kuti zimasiyana zocita. Koma kodi n’kutheka kuti mwina mfundo imeneyi si yoona?

Baibo imanena kuti anthu ambili amapemphela kwa mulungu wolakwika. Kale-kale pamene Baibo inali kulembedwa, anthu ambili anali kupemphela kwa mafano osema. Koma nthawi zonse Mulungu anali kudzudzula khalidwe limenelo. Mwacitsanzo, pa Salimo 115:4-6, Mulungu ananena za mafano kuti: “Makutu ali nawo koma satha kumva.” Mfundo yake pamenepa ni yakuti, si cinthu canzelu kupemphela kwa mulungu amene saamva

M’Baibo muli nkhani inayake yosangalatsa yokhudza mfundo imeneyi. Mneneli woona Eliya anauza aneneli a Baala kuti apemphele kwa mulungu wawo ndipo kenako Eliyayo apemphelanso kwa Mulungu wake. Iye anawauza kuti Mulungu woona ni amene ayankhe pemphelo la olambila ake, pamene mulungu wonyenga sayankha. Aneneli a Baala anavomela kucita zimenezo, ndipo anapemphela kwa nthawi yaitali komanso mokuwa kwambili. Koma palibe cimene cinacitika. Nkhaniyo imati: “Palibe anawayankha kapena kuwamvela.” (1 Mafumu 18:29) Nangano kodi Eliya zinamuthela bwanji?

Eliya atapemphela, Mulungu anayankha pemphelo lake nthawi yomweyo mwa kutumiza moto kucokela kumwamba. Moto umenewo unanyeketsa nsembe yonse imene Eliya anaiika paguwa. Kodi n’ciani cinacititsa kuti pakhale kusiyana kumeneku? Pemphelo la Eliya, lolembedwa pa 1 Mafumu 18:36, 37, likusonyeza cimene cinacititsa. Pempheloli ni lalifupi ndipo m’Ciheberi coyambilila lili na mawu pafupifupi 30 basi. Koma m’mawu ocepa omwewo Eliya anachula dzina la Mulungu lakuti Yehova katatu konse.

Baala anali mulungu wa Akanani ndipo mawu akuti Baala amatanthauza “mwiniwake” kapena “mbuye.” Akananiwo anali kulambilanso milungu ya Baala ya mitundu yosiyana-siyana. Koma dzina lakuti Yehova ni la Mulungu mmodzi yekha basi m’cilengedwe conse. Mulungu ameneyu anauza anthu ake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapeleka ulemu wanga kwa wina aliyense.”—Yesaya 42:8.

N’cifukwa ciani pemphelo la Eliya linayankhidwa pamene mapemphelo a aneneli a Baala sanayankhidwe? Anthu opembedza Baala sanali kulemekeza moyo wa anthu cifukwa ina mwa miyambo ya cipembedzo cawo inali kuphatikizapo kucita uhule ngakhalenso kupeleka anthu nsembe. Mosiyana na zimenezi, kupembedza Yehova kunacititsa anthu ake, Aisiraeli, kukhala olemekezeka cifukwa kunawateteza kuti asamacite zinthu zonyansa ngati zimene opembedza Baala anali kucita. Ndiyeno taganizilani izi: Mutakhala kuti mwalembela kalata mnzanu wolemekezeka kwambili ndiponso wakhalidwe labwino, kodi mungaitumize kwa munthu wina amene dzina lake ni losiyana na la mnzanuyo, komanso khalidwe lake ni loipa kwambili? N’zodziwikilatu kuti simungatelo.

Zimene Eliya anacita potsutsana na aneneli a Baala, zikusonyeza kuti si mapemphelo onse amene amapita kwa Mulungu woona

Mukamapemphela kwa Yehova, ndiye kuti mukupemphela kwa Mlengi amene ni Atate wa anthu onse. Mneneli Yesaya popemphela ananena kuti:  * “Inuyo Yehova ndinu Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Atate ameneyu ni amene Yesu Khristu anali kunena pamene anauza otsatila ake kuti: “Ine ndikukwela kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Yehova ndiye Atate wake wa Yesu. Yesu anali kupemphela kwa Mulungu ameneyu, ndipo anaphunzitsanso otsatila ake kuti azipemphela kwa Yehova.—Mateyu 6:9

Ndiyeno kodi Baibo imanena kuti tizipemphela kwa Yesu, Mariya, oyela mtima kapena kwa angelo? Yankho ni lakuti ayi. Tiyenela kupemphela kwa Yehova yekha basi. Cifukwa ciani? Taganizilani zifukwa ziŵili izi: Coyamba, pemphelo ni mbali ya kulambila ndipo Baibo imati tiyenela kulambila Yehova yekha basi. (Ekisodo 20:5) Caciŵili, Baibo imanena kuti Mulungu ni “Wakumva pemphelo.” (Salimo 65:2) Ngakhale kuti Yehova anapatsa ena maudindo osiyana-siyana, kumvetsela mapemphelo ni udindo wake ndipo sanaupeleke kwa wina aliyense. Mulungu amalonjeza kuti iye ni amene azimvetsela mapemphelo athu

Conco ngati mukufuna kuti Mulungu azimva mapemphelo anu, kumbukilani malangizo a m’Baibo awa: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Machitidwe 2:21) Komabe kodi Yehova amayankha mapemphelo a munthu wina aliyense zivute zitani? Kapena kodi pali cinacake cimene tiyenela kucita kuti Yehova aziyankha mapemphelo athu?

^ ndime 9 M’zipembedzo zina amanena kuti kuchula dzina la Mulungu, ngakhale popemphela, n’kulakwa. Koma dzina limenelo limapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’zinenelo zoyambilila za Baibo. Kawili-kawili dzinali imapezeka m’mapemphelo na mu nyimbo zotamanda Mulungu za atumiki okhulupilika a Yehova.