Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

3 Kodi Tiyenela Kupemphela Bwanji?

3 Kodi Tiyenela Kupemphela Bwanji?

M’ZIPEMBEDZO zambili amakonda kuphunzitsa anthu mmene ayenela kukhalila popemphela, mawu amene ayenela kuchula komanso mwambo umene ayenela kutsatila. Koma Baibo imatithandiza kuona kuti zimenezi sizofunika kwenikweni. M’malomwake, imatilimbikitsa kuganizila cinthu cofunika kwambili pa funso lakuti, “Kodi tiyenela kupemphela bwanji?

Baibo imanena za atumiki a Mulungu amene anali kupemphela pamalo osiyana-siyana komanso atakhala mwa njila zosiyana-siyana. Anapemphela camumtima ndipo ena anapemphela mokweza malinga na mmene zinthu zinalili pa nthawi yopemphelayo. Anali kupemphela akuyang’ana kumwamba kapena atagwada. Iwo sanali kugwilitsa nchito mafano, mikanda kapena mabuku popemphela, koma anali kungopemphela mocokela pansi pamtima, ndipo anali kulankhula m’mawu awo-awo. Kodi n’ciani cinacititsa kuti mapemphelo awo amvedwe?

Monga tachulila kale m’nkhani yapita, iwo anali kupemphela kwa Mulungu mmodzi, Yehova. Palinso cinthu cina cofunika kwambili cimene anacita. Pa lemba la 1 Yohane 5:14 timaŵelenga kuti: “Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” Conco mapemphelo athu ayenela kukhala ogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Kodi zimenezi zikutanthauza ciani?

Kuti tizipemphela mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, coyamba tiyenela kudziwa kuti cifunilo cakeco n’ciani. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenela kuphunzila Baibo kuti mapemphelo athu akhale ogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo athu pokhapokha ngati ndife akatswili pa nkhani ya Baibo? Ayi, koma Mulungu amafuna kuti tiziphunzila cifunilo cake, kucimvetsa komanso kucita zinthu mogwilizana na cifunilo cakeco. (Mateyu 7:21-23) Conco, tifunika kupemphela mogwilizana na zimene timaphunzila m’Baibo

Mulungu amayankha mapemphelo amene timapemphela m’dzina la Yesu, mwacikhulupililo komanso mogwilizana na cifunilo cake

Tikapitiliza kuphunzila za Yehova na cifunilo cake, cikhulupililo cathu cidzakula. Zimenezi n’zofunika ngati tikufuna kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo athu. Yesu ananena kuti: “Cinthu ciliconse cimene mudzapempha m’mapemphelo anu, mudzalandila ngati muli ndi cikhulupililo.” (Mateyu 21:22) Kukhala na cikhulupililo sikutanthauza kungokhulupilila ciliconse popanda kuciganizila bwino-bwino. Koma kumatanthauza kukhulupilila cinacake coti ngakhale kuti n’cosaoneka na maso, pali umboni wamphamvu wakuti cinthuco cilipodi. (Aheberi 11:1) M’Baibo muli umboni wambili-mbili wosonyeza kuti Yehova, ngakhale kuti sitingamuone, alipo ndithu, ni wodalilika ndipo amayankhadi mapemphelo a anthu amene amamukhulupilila. Komanso, tingamupemphe kuti atithandize kuti tizimukhulupilila kwambili ndipo iye amasangalala kutipatsa zimene tikufunikila.—Luka 17:5; Yakobo 1:17..

Yesu anachula cinthu cinanso cofunika kwambili popemphela. Iye anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ni njila yotithandiza kuti mapemphelo athu afike kwa Atate, Yehova. N’cifukwa cake Yesu anauza otsatila ake kuti azipemphela m’dzina lake. (Yohane 14:13; 15:16) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tizipemphela kwa Yesu. M’malo mwake, tiyenela kupemphela m’dzina la Yesu podziwa kuti iye ni amene amacititsa kuti mapemphelo athu afike kwa Atate wathu wangwilo na woyela.

Nthawi ina otsatila a Yesu anam’pempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphela.” (Luka 11:1) Zikuoneka kuti popeleka pempho limeneli, iwo sanali kumupempha kuti awafotokozele mfundo zimene tangokambilana kumenezi, koma ankamupempha kuti awauze zinthu zimene ayenela kuchula popemphela. M’mawu ena, funso lawo kwenikweni linali lakuti, ‘Kodi tizipempha ciani?’